“Kuyenera Kuti Izi Zioneke”
“Yesu [a]nati kwa iwo, . . . Kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.”—MATEYU 24:4-6.
1. Kodi ndi nkhani iti imene tingafune kudziŵa?
N’ZOSAKAYIKITSA kuti mumafuna kudziŵa za moyo wanu ndi tsogolo lanu. Ndiye kuti mungafunenso kudziŵa nkhani imene inachititsa chidwi C. T. Russell kalelo mu 1877. Russell, amene anadzayambitsa Watch Tower Society, analemba kabuku kakuti The Object and Manner of Our Lord’s Return (Cholinga cha Kubweranso kwa Ambuye Wathu ndi Mabweredwe Ake). Kabuku ka masamba 64 kameneka kanafotokoza kubweranso kwa Yesu, kapena kuti kudza kwake kwa m’tsogolo. (Yohane 14:3) Nthaŵi ina yake ali pa Phiri la Azitona, atumwi anam’funsa za kubweranso kumeneko kuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?”—Mateyu 24:3.
2. N’chifukwa chiyani pali kusiyana maganizo ponena za zimene Yesu analosera?
2 Kodi yankho la Yesu mumalidziŵa ndi kulimvetsa? Limapezeka m’Mauthenga Abwino atatu. Polofesa D. A. Carson anati: “Pali machaputala angapo m’Baibulo amene abweretsa mkangano kwambiri pakati pa omasulira malemba kuposa mmene Mateyu 24 ndi nkhani zofanana nazo za m’Marko 13 ndi Luka 21 zachitira.” Ndiyeno anapereka lingaliro lake—nalonso lozunguza malingaliro a anthu. M’zaka za zana lapitalo, malingaliro ochuluka oterowo anasonyeza kupanda chikhulupiriro. Eni malingalirowo ankanena kuti Yesu sananenepo zimene timaŵerenga m’Mauthenga Abwino, ndi kuti mawu ake anapotozedwa pambuyo pake, kapena kuti ulosi wake unalephera—malingaliro osonkhezeredwa ndi maphunziro apamwamba a ofufuza Baibulo. Wothirira ndemanga wina anafika pofufuza Uthenga Wabwino wa Marko ‘malinga ndi filosofi yachibuda cha Mahayana’!
3. Kodi Mboni za Yehova zimauona motani ulosi wa Yesu?
3 Mosiyana ndi zimenezo, Mboni za Yehova zimaona Baibulo kukhala loona ndi lodalirika, kuphatikizapo zimene Yesu anauza atumwi anayi amene anali naye pa Phiri la Azitona masiku atatu imfa yake isanachitike. Kuyambira m’masiku a C. T. Russell, anthu a Mulungu akhala akuumvetsa mowonjezereka ulosi umene Yesu anapereka pamenepo. M’zaka zingapo zapitazo, Nsanja ya Olonda yawongolerabe kamvedwe kawo ka ulosiwu. Kodi mwachimvetsa bwino chidziŵitso chimenecho ndi kuona mmene chikukhudzira moyo wanu?a Tiyeni tibwereremonso.
Kukwaniritsidwa Kwake Koopsa Kuli Pafupi
4. Kodi chingakhale chifukwa chiyani chimene atumwi anafunsira Yesu za m’tsogolo?
4 Atumwi anali kudziŵa kuti Yesu ndiye Mesiya. Choncho atamumva akutchula za imfa yake, kuukitsidwa, ndi kubwerera kumwamba, iwo ayenera kuti anadabwa kuti, ‘Ngati Yesu adzafa ndi kuchoka, adzachita bwanji zinthu zodabwitsa zimene Mesiya ayenera kuchita?’ Ndiponso, Yesu ananenapo za mapeto a Yerusalemu ndi kachisi wake. Mwina atumwi anali kuganiza kuti, ‘Kodi zimenezo zidzachitika liti ndipo zidzachitika motani?’ Poyesa kumvetsa zinthu zimenezi, atumwi anafunsa kuti: “Zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?”—Marko 13:4; Mateyu 16:21, 27, 28; 23:37–24:2.
5. Kodi zimene Yesu ananena zinakwaniritsidwa motani m’zaka za zana loyamba?
5 Yesu analosera kuti kudzakhala nkhondo, njala, miliri, zivomezi, kudedwa ndi kuzunzidwa kwa Akristu, amesiya onama, ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu ponseponse. Pomwepo chikafika chimaliziro. (Mateyu 24:4-14; Marko 13:5-13; Luka 21:8-19) Yesu ananena zimenezi kuchiyambiyambi kwa chaka cha 33 C.E. M’zaka zotsatira, ophunzira ake atcheru anaona kuti zinthu zoloseredwazo zinali kuchitikadi m’njira yochititsa chidwi. Inde, mbiri yakale ikupereka umboni wakuti chizindikiro chimenecho chinakwaniritsidwa panthaŵiyo, mpaka dongosolo la zinthu lachiyuda linawonongedwa ndi Aroma mu 66-70 C.E. Kodi zimenezo zinachitika bwanji?
6. N’chiyani chinachitika pakati pa Aroma ndi Ayuda mu 66 C.E.?
6 M’nyengo yotentha ku Yudeya mu 66 C.E., Azelote achiyuda anaukira alonda achiroma pa nsanja yoyandikana ndi kachisi ku Yerusalemu. Zimenezi zinayambitsa chiwawa m’malo ena m’dzikolo. M’buku lakuti History of the Jews (Mbiri ya Ayuda), Polofesa Heinrich Graetz anasimba kuti: “Cestius Gallus amene, pokhala Kazembe wa Aramu, inali ntchito yake yochirikiza ulemerero wa asilikali achiroma, . . . sanathenso kulekerera chipanduko chikufalikira m’dera lakelo osachitapo kanthu kuti achithetse. Anasonkhanitsa asilikali ake, ndipo akalonga oyandikana naye anatumiza asilikali awo modzifunira.” Gulu la asilikali 30,000 limeneli linazinga Yerusalemu. Atamenyana, Ayuda anabwerera m’mbuyo ndikukaima kuseri kwa linga pafupi ndi kachisi. “Pamasiku otsatira asanu Aroma anali kuomba lingalo, koma nthaŵi zonse anali kubwerera m’mbuyo chifukwa cha mivi ya Ayuda. Patsiku lachisanu ndi chimodzi mpamene anatha kugwetsa mbali ya linga la kumpoto kutsogolo kwa Kachisi.”
7. N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu anaona zinthu mosiyana ndi Ayuda ambiri?
7 Tangolingalirani mmene Ayuda anasokonezekera, popeza kwa nthaŵi yaitali anali kuganiza kuti Mulungu adzawateteza ndi kutetezanso mzinda wawo wopatulika! Koma ophunzira a Yesu anali atachenjezedwa kale kuti Yerusalemu adzakumana ndi tsoka. Yesu analosera kuti: “Masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake.” (Luka 19:43, 44) Koma kodi Akristu amene anali m’Yerusalemu mu 66 C.E. anali kudzafera momwemo?
8. Kodi Yesu analosera za tsoka liti, ndipo “osankhidwa” amene anali kudzafupikitsidwira masiku anali ayani?
8 Poyankha atumwi pa Phiri la Azitona, Yesu ananeneratu kuti: “Masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso nthaŵi zonse. Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.” (Marko 13:19, 20; Mateyu 24:21, 22) Choncho masiku anali kudzafupikitsidwa ndipo “osankhidwa” kupulumutsidwa. Kodi ameneŵa anali ayani? Ndithudi sanali Ayuda opandukawo amene anali kunena kuti akulambira Yehova koma anakana Mwana wake. (Yohane 19:1-7; Machitidwe 2:22, 23, 36) Amene analidi osankhidwa panthaŵiyo anali Ayuda ndi anthu amene sanali Ayuda amene anasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu monga Mesiya ndi Mpulumutsi. Mulungu anasankha oterowo, ndipo pa Pentekoste wa 33 C.E., anali atawapanga kukhala mtundu watsopano wauzimu, “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16; Luka 18:7; Machitidwe 10:34-45; 1 Petro 2:9.
9, 10. Kodi masiku a kuukira kwa Aroma ‘anafupikitsidwa’ motani, ndipo panatsatira zotani?
9 Kodi masikuwo ‘anafupikitsidwadi’ ndipo osankhidwa odzozedwa m’Yerusalemu kodi anapulumutsidwadi? Polofesa Graetz akupereka lingaliro lakuti: “[Cestius Gallus] anaona kuti si bwino kupitiriza kumenyana ndi anthu otengeka maganizo ndi opanda manthawo ndi kuyamba chintchito chadzaoneni m’nyengoyo, mvula ili pafupi kuyamba . . . imene ikanapangitsa kuti gulu la asilikalilo lisamalandire zofunika. Mwina pazifukwa zimenezo anaona kuti kuli bwino kubwerera.” Kaya n’zimenezidi zomwe Cestius Gallus anali kuganiza, gulu lankhondo la Aroma linabwerera kuchoka ku mzindawo, ndipo anavulazidwa kwambiri ndi Ayuda amene anali kuwapitikitsa.
10 Kubwerera kosayembekezereka kwa Aroma kumeneko kunapatsa mpata ‘anthu’—ophunzira a Yesu amene anali pangozi m’Yerusalemu—kuti apulumutsidwe. Mbiri yakale imati patapezeka mpata umenewu, Akristu anathaŵa m’deralo. Zimenezotu zinasonyeza mphamvu ya Mulungu yodziŵiratu za m’tsogolo ndi kuonetsetsa kuti olambira ake adzapulumuke! Nangano bwanji za Ayuda osakhulupirirawo amene anakhalabe m’Yerusalemu ndi m’Yudeya?
Anthu Okhalako Panthaŵiyo Anali Kudzaona Chisautsocho
11. Kodi Yesu anati bwanji ponena za “mbadwo uwu”?
11 Ayuda ambiri anali kuganiza kuti kulambira kwawo, kochitikira pa kachisi, sikudzatha. Koma Yesu anati: ‘Phunzirani ndi mkuyu . . . ; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa. Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi.’—Mateyu 24:32-35.
12, 13. Kodi ophunzira ayenera kuti anawamva motani mawu a Yesu akuti “mbadwo uno”?
12 M’zaka zoyambirira chisanafike chaka cha 66 C.E., Akristu anaona mbali zambiri zoyambirira za chizindikiro chachiungwe zikukwaniritsidwa—nkhondo, njala, ngakhale kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu ponseponse. (Machitidwe 11:28; Akolose 1:23) Komano kodi mapeto anali kudzafika liti? Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti: “Mbadwo uwu [Chigiriki, ge·ne·aʹ] sudzatha kuchoka”? Nthaŵi zambiri Yesu anatcha makamu a Ayuda om’tsutsa, kuphatikizapo atsogoleri achipembedzo kuti ‘obadwa oipa, achigololo.’ (Mateyu 11:16; 12:39, 45; 16:4; 17:17; 23:36) Choncho, atanenanso za “mbadwo uwu” pa Phiri la Azitona, mwachionekere sanali kutanthauza fuko lonse la Ayuda m’mbiri yonse ya anthu; sanalinso kutanthauza otsatira ake, ngakhale kuti anali “mbadwa yosankhika.” (1 Petro 2:9) Komanso Yesu sanali kutanthauza kuti “mbadwo uwu” ndi nyengo inayake.
13 M’malo mwake, Yesu anali kunena za Ayuda otsutsa a panthaŵiyo amene anali kudzaona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chimene anapereka. Ponena za mawuwo “mbadwo uno” opezeka pa Luka 21:32, Polofesa Joel B. Green anati: “Mu Uthenga Wabwino Wachitatu, ‘mbadwo uno’ (ndi mawu ena ofanana nawo) nthaŵi zonse amatanthauza gulu la anthu amene akutsutsana ndi cholinga cha Mulungu. . . . [Amatanthauza] anthu amene akufulatira zolinga za Mulungu mouma khosi.”b
14. Kodi “mbadwo” umenewo unaona zotani, koma kodi Akristu anakhala motani ndi chotsatirapo chosiyana?
14 Mbadwo woipawo wa Ayuda otsutsa amene anali kuona chizindikiro chikukwaniritsidwa anali kudzaonanso chimaliziro. (Mateyu 24:6, 13, 14) Ndipo anachionadi! Mu 70 C.E., gulu lankhondo la Aroma linabweranso, lotsogozedwa ndi Titus, mwana wa Mfumu Vespasian. Kuzunzika kwa Ayuda amene anatsekeredwanso m’mzindawo n’kosaneneka.c Flavius Josephus, mboni yoona ndi maso, anasimba kuti podzafika nthaŵi imene Aroma amasakaza mzindawo, Ayuda pafupifupi 1,100,000 anali atamwalira ndipo enanso 100,000 anali atatengedwa ukapolo, ndipo ambiri a iwo anafa momvetsa chisoni ndi njala kapena anaphedwa m’mabwalo a maseŵero ku Roma. Ndithudi, chisautso cha mu 66-70 C.E. ndicho chinali chachikulu kwambiri chimene Yerusalemu ndi dongosolo lachiyuda linali lisanaonepo kapena linali kudzaonanso. Komatu zinali zosiyana kotheratu kwa Akristu amene anamvera ulosi wochenjeza wa Yesu natuluka m’Yerusalemu pambuyo poti magulu ankhondo a Aroma achoka mu 66 C.E.! Akristu “osankhidwawo” odzozedwa ‘anapulumuka,’ kapena anasungidwa amoyo, mu 70 C.E.—Mateyu 24:16, 22.
Kukwaniritsidwa Kwina Kudzakhalapo
15. Tingatsimikizire motani kuti ulosi wa Yesu unali kudzakwaniritsidwa pamlingo waukulu pambuyo pa 70 C.E.?
15 Komabe, sizinathere pomwepo. Pachiyambi, Yesu anasonyeza kuti pambuyo poti mzindawo wawonongedwa, iye adzabwera m’dzina la Yehova. (Mateyu 23:38, 39; 24:2) Kenako anafotokoza zowonjezeka mu ulosi wake wa pa Phiri la Azitona. Atatchula za kudza kwa ‘chisautso chachikulu,’ ananena kuti pambuyo pake padzakhala a Kristu onama, ndipo Yerusalemu adzaponderezedwa ndi amitundu kwa nthaŵi yaitali. (Mateyu 24:21, 23-28; Luka 21:24) Kodi mwina kukwaniritsidwa kwinanso kwakukulu kunali m’tsogolo? Zochitika zikuyankha kuti inde. Tikayerekeza Chivumbulutso 6:2-8 (cholembedwa chisautso cha ku Yerusalemu cha mu 70 C.E. chitachitika) ndi Mateyu 24:6-8 komanso ndi Luka 21:10, 11, tikuona kuti nkhondo, njala, ndi miliri zinali kudzachitika pamlingo waukulu m’tsogolo. Kukwaniritsidwa kwakukulu kumeneku kwa mawu a Yesuŵa kwakhala kukuchitika chiyambire Nkhondo Yadziko I mu 1914.
16-18. Kodi tikuyembekezera chiyani kuti chichitike?
16 Kwa zaka zambiri tsopano, Mboni za Yehova zakhala zikuphunzitsa kuti kukwaniritsidwa kwamakono kwa chizindikirocho kukusonyeza kuti ‘chisautso chachikulu’ chili m’tsogolo. “Mbadwo” woipa umene ulipowu udzaona chisautsocho. Zikuoneka kuti padzakhalanso mbali yoyamba (kuukiridwa kwa zipembedzo zonse zonyenga), monga momwe kuukira kwa Gallus mu 66 C.E. kunali mbali yoyamba ya chisautso cha Yerusalemu.d Ndiyeno, patapita nthaŵi yautali wosadziŵika, chimaliziro chidzafika—chiwonongeko cha padziko lonse, chofanana ndi chija cha mu 70 C.E.
17 Ponena za chisautso chimene chili patsogolo pathupa, Yesu anati: “Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo [kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga], dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuŵala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka: ndipo pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pamitambo yakumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.”—Mateyu 24:29, 30.
18 Choncho, Yesu iyemwini akunena kuti “atapita masauko a masiku awo,” kudzaoneka zinthu zachilendo kuthambo. (Yerekezani ndi Yoweli 2:28-32; 3:15.) Zimenezi zidzazizwitsa ndi kusokoneza anthu osamvera moti ‘adzadziguguda pachifuŵa.’ Ambiri ‘adzakomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi.’ Koma Akristu oona sadzatero! Iwo ‘adzatukula mitu yawo, chifukwa chiwomboledwe chawo chayandikira.’—Luka 21:25, 26, 28.
Chiweruzo Chikudza!
19. Tingadziŵe motani nthaŵi imene fanizo la nkhosa ndi mbuzi lidzakwaniritsidwa?
19 Onani kuti Mateyu 24:29-31 akuneneratu kuti (1) Mwana wa munthu akudza, (2) pakudza kumeneku adzadza ndi ulemerero waukulu, (3) angelo adzakhala naye, ndipo (4) mitundu yonse padziko lapansi idzamuona. Yesu anabwereza mbali zimenezi m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Mateyu 25:31-46) Choncho, titha kunena kuti fanizo limeneli likunena za nthaŵi, mbali yoyamba ya chisautso chachikulu itachitika, pamene Yesu adzadza ndi angelo ake ndi kukhala pampando wake wachifumu kuti apereke chiweruzo. (Yohane 5:22; Machitidwe 17:31; yerekezani ndi 1 Mafumu 7:7; Danieli 7:10, 13, 14, 22, 26; Mateyu 19:28.) Kodi ndani adzaweruzidwa, ndipo chigamulo chake chidzakhala chotani? Fanizolo likusonyeza kuti Yesu adzayang’anira mitundu yonse, monga kuti yasonkhana patsogolo pa mpando wake wachifumu wakumwamba.
20, 21. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikira nkhosa za m’fanizo la Yesu? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikira mbuzi m’tsogolo?
20 Amuna ndi akazi onga nkhosa adzaikidwa kudzanja lamanja lachiyanjo la Yesu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anagwiritsa ntchito mwayi wawo kuchitira zabwino abale ake—Akristu odzozedwa, amene adzalamulira ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. (Danieli 7:27; Ahebri 2:9–3:1) Mogwirizana ndi fanizolo, Akristu mamiliyoni ambiri onga nkhosa azindikira abale auzimu a Yesu ndipo akhala akugwira ntchito yowachirikiza. Chotero, “khamu lalikulu” lili ndi chiyembekezo cha m’Baibulo chopulumuka ‘chisautso chachikulu’ kenako kudzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso, bwalo la padziko lapansi la Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 7:9, 14; 21:3, 4; Yohane 10:16.
21 Komatu zidzakhala zosiyana kotheratu ndi mbuzi! Otchedwa mbuziwo akufotokozedwa pa Mateyu 24:30 kuti ‘akudziguguda pachifuŵa’ pamene Yesu akudza. Ndipo ayeneradi kutero, popeza adzakhala atadzipangira mbiri yokana uthenga wabwino wa Ufumu, kutsutsa ophunzira a Yesu, ndi kukonda dziko lomwe likupitali. (Mateyu 10:16-18; 1 Yohane 2:15-17) Yesu—osati wophunzira wake aliyense padziko lapansi—ndiye adzanena amene ali mbuzi. Ponena za amenewo anati: “Ameneŵa adzachoka kumka kuchilango cha nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:46.
22. Kodi ndi mbali iti ya ulosi wa Yesu yofunika kuti tiipendenso kwambiri?
22 Kuwonjezera kumvetsa kwathu ulosi wa m’Mateyu chaputala 24 ndi 25 kwakhala kosangalatsa. Komabe, pali mbali ya ulosi wa Yesu yofunika kuti tiipendenso kwambiri—‘chonyansa cha kupululutsa chitaima m’malo oyera.’ Yesu analimbikitsa otsatira ake kugwiritsa ntchito kuzindikira ponena za chimenechi ndi kuti akhale okonzeka kuchitapo kanthu. (Mateyu 24:15, 16) Kodi “chonyansa” chimenechi n’chiyani? Kodi chikuima liti m’malo oyera? Ndipo kodi ziyembekezo zathu za panthaŵi ino ndi m’tsogolo zikukhudzidwa motani? Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani zophunzira m’makope a Nsanja ya Olonda a February 15, 1994; October 15 ndi November 1, 1995; ndi August 15, 1996.
b Katswiri wamaphunziro wa ku Britain G. R. Beasley-Murray anati: “Omasulira sayenera kuvutika ndi mawu akuti ‘mbadwo uno.’ Pamenedi n’zoona kuti mawu akuti genea m’Chigiriki chakale anali kutanthauza kubadwa, mbadwa, chonchonso fuko, . . . mu [Septuagint yachigiriki] nthaŵi zambiri anagwiritsidwa ntchito potembenuza mawu achihebri akuti dôr, otanthauza nyengo, mbadwo wa anthu, kapena mbadwo kutanthauza anthu okhalako panthaŵiyo. . . . M’mawu onenedwa ndi Yesu mawuwo akuoneka kuti akutanthauza zinthu ziŵiri: choyamba nthaŵi zonse amatanthauza anthu amene analiko panthaŵiyo, ndipo chachiŵiri, nthaŵi zonse amasonyeza bwino lomwe kuti pali chidzudzulo.”
c M’buku lakuti History of the Jews, Polofesa Graetz ananena kuti nthaŵi zina Aroma anali kupachika akaidi 500 patsiku. Ayuda ena amene anatengedwa ukapolo anadulidwa manja kenako n’kuwabwezera kumzindawo. Kodi moyo unali wotani kumeneko? “Ndalama inatheratu mphamvu, popeza sinalinso kugula mkate. Amuna m’misewu anali kumenyanirana chakudya chonyansa kwadzaoneni, timapesi touma, kachikopa, kapena matumbo otayidwa kuti agalu adye. . . . Kuwonjezeka kwakukulu kwa mitembo yosaikidwa m’manda kunapangitsa mpweya wotentha wa m’chilimwewo kukhala ngati mliri, ndipo anthu ambiri anafa ndi matenda, njala, ndi lupanga.”
d Nkhani yotsatira idzafotokoza mfundo imeneyi yokhudza chisautso cham’tsogolo.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Mateyu 24:4-14 anakwaniritsidwa motani m’zaka za zana loyamba?
◻ M’nthaŵi ya atumwi, monga momwe Mateyu 24:21, 22 ananeneratu, kodi masiku anafupikitsidwa motani ndipo anthu anapulumutsidwa bwanji?
◻ Kodi n’chiyani chikudziŵikitsa “mbadwo” wotchulidwa pa Mateyu 24:34?
◻ Tikudziŵa bwanji kuti ulosi woperekedwa pa Phiri la Azitona unali kudzakwaniritsidwanso pamlingo waukulu?
◻ Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi lidzakwaniritsidwa liti ndiponso motani?
[Chithunzi patsamba 12]
Chithunzi cha Arch of Titus ku Roma, chosonyeza bwino zofunkha Yerusalemu atawonongedwa
[Mawu a Chithunzi]
Soprintendenza Archeologica di Roma