Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?
“Chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?”—MAT. 24:3.
1. Kodi ndi funso lochititsa chidwi lotani limene atumwi a Yesu anamufunsa?
PAFUPIFUPI zaka 2,000 zapitazo, atumwi anayi a Yesu anali kukambirana mwamseri ndi Mbuye wawo m’Phiri la Maolivi, ndipo anamufunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha [“mathedwe,” Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu] a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:3) Pafunso limeneli, atumwi anagwiritsa ntchito mawu awiri ochititsa chidwi kwambiri. Mawuwo ndi “kukhalapo kwanu” ndiponso “mathedwe a dongosolo lino la zinthu.” Kodi mawu amenewa amanena za chiyani?
2. Kodi mawu akuti “mathedwe” amatanthauza chiyani kwenikweni?
2 Tiyeni tiyambe ndi mawu achiwiriwa akuti “mathedwe.” Mawuwa amasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki akuti syn·teʹlei·a. Mawu a Chigiriki ofananako ndi amenewa ndi te’los, ndipo amamasuliridwa kuti “mapeto.” Tingayerekeze kusiyana kwa mawu awiriwa ndi mmene zimakhalira pa nkhani yokambidwa m’Nyumba ya Ufumu. Tingati mathedwe a nkhaniyo ndi chigawo chake chomalizira, pamene wokamba nkhaniyo kwa nthawi yochepa amakumbutsa omvera mfundo za m’nkhani yake ndi kuwasonyeza mmene mfundozo zikuwakhudzira. Mapeto a nkhani ndi pamene wokambayo akuchoka pa pulatifomu. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mathedwe a dongosolo lino la zinthu,” kutanthauza nyengo yonse imene imakafika ku mapeto kuphatikizapo mapetowo.
3. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zikuchitika pa nthawi ya kukhalapo kwa Yesu?
3 Nanga bwanji za “kukhalapo” kumene atumwi aja anafunsa? Mawu amenewa amasuliridwa ku mawu a Chigiriki akuti pa·rou·siʹa.a Pa·rou·siʹa wa Khristu, kapena kuti kukhalapo kwake, kunayamba pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba mu 1914, ndipo kukupitirirabe mpaka pa “chisautso chachikulu,” pamene adzabwera kudzawononga oipa. (Mat. 24:21) Zinthu zambiri zosiyanasiyana, monga “masiku otsiriza” a dongosolo loipa ili la zinthu, kusonkhanitsidwa kwa osankhidwa ndi kuuka kwawo kuti akakhale ndi moyo kumwamba, zikuchitika pa nthawi ya kukhalapo kwa Yesu. (2 Tim. 3:1; 1 Akor. 15:23; 1 Ates. 4:15-17; 2 Ates. 2:1) Tinganene kuti nyengo ya “mathedwe a dongosolo lino la zinthu” (syn·teʹlei·a) ndi imodzimodzi ndi nyengo yotchedwa kukhalapo kwa Khristu (pa·rou·siʹa).
Nthawiyi ndi Yaitali
4. Kodi kukhalapo kwa Yesu kukufanana bwanji ndi zochitika za m’nthawi ya Nowa?
4 Mfundo yakuti mawu a pa·rou·siʹa amanena za nthawi yaitali ikugwirizana ndi zimene Yesu ananena za kukhalapo kwake. (Werengani Mateyo 24:37-39.) Onani kuti apa Yesu sanayerekeze kukhalapo kwake ndi nthawi yaifupi imene Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chinachitika. M’malo mwake, anayerekezera kukhalapo kwake ndi nthawi yaitali kwambiri imene inakathera pa Chigumula. Panyengo imeneyo, panachitika zinthu monga ntchito ya Nowa yomanga chingalawa ndi ntchito yake yolalikira, ndipo nyengoyo inapitirira mpaka nthawi imene Chigumulacho chinafika. Zinthu zimenezo zinachitika pa zaka zambirimbiri. Mofanana ndi zimenezi, kukhalapo kwa Khristu kumaphatikizapo zochitika zokathera pachisautso chachikulu, kuphatikizaponso chisautso chachikulucho.—2 Ates. 1:6-9.
5. Kodi mawu olembedwa pa Chivumbulutso chaputala 6, amasonyeza motani kuti kukhalapo kwa Yesu ndi nthawi yaitali?
5 Ulosi wina m’Baibulo umasonyeza kuti mawu akuti kukhalapo kwa Khristu amanena za nthawi yaitali osati chabe za kubwera kwake kudzawononga oipa. Buku la Chivumbulutso limanena za Yesu atakwera hatchi yoyera ndipo akupatsidwa kolona. (Werengani Chivumbulutso 6:1-8.) Atavekedwa kolonayo n’kukhala Mfumu mu 1914, Yesu akusonyezedwa akupita “kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake.” Lembalo likusonyeza kuti iye akutsatiridwa ndi okwera pamahatchi okhala ndi maonekedwe ena. Malinga ndi ulosi, zimenezi zikuimira nkhondo, njala ndi miliri ndipo zonsezi zakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali yomwe imatchedwanso “masiku otsiriza.” Kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu tikukuona masiku ano.
6. Kodi buku la Chivumbulutso chaputala 12 likutithandiza kumvetsa chiyani za kukhalapo kwa Khristu?
6 Buku la Chivumbulutso chaputala 12 limafotokoza mfundo zinanso zonena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu kumwamba. M’chaputala chimenechi tikuwerenga za nkhondo kumwamba. Mikayeli yemwe ndi Yesu Khristu paudindo wake wa kumwamba limodzi ndi angelo ake, akumenyana ndi Mdyerekezi limodzi ndi ziwanda zake. Mapeto ake, Satana Mdyerekezi ndi gulu lake lonse akuponyedwa ku dziko lapansi. Chaputala chimenechi chikutiuza kuti, zitatero, Mdyerekezi akukhala ndi mkwiyo waukulu “podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Werengani Chivumbulutso 12:7-12.) Apa zikuonekeratu kuti Ufumu wa Khristu utakhazikitsidwa kumwamba, pakutsatira nthawi ya “tsoka” lalikulu padziko lapansi ndi anthu okhalamo.
7. Kodi salmo lachiwiri limanena za chiyani, ndipo limafotokoza za mpata wotani?
7 Nalonso salmo lachiwiri lili ndi ulosi wonena za kukhazikitsidwa kwa Yesu kukhala Mfumu paphiri la Ziyoni kumwamba. (Werengani Salmo 2:5-9; 110:1, 2.) Salmo lomweli limasonyezanso kuti pali nthawi imene olamulira a dzikoli limodzi ndi anthu awo, akupatsidwa mpata wogonjera ulamuliro wa Khristu. Akuuzidwa ‘kuchita mwanzeru’ ndi kulola kuti ‘alangike.’ Panthawi imeneyo, ndi “odala onse akumukhulupirira Iye [Mulungu]” mwa kutumikira Yehova ndi Mfumu imene iye anasankha. Zimenezi zikutanthauza kuti iwo akupatsidwa mpata panthawi ya kukhalapo kwa Yesu mu Ufumu wake.—Sal. 2:10-12.
Kuona Chizindikiro
8, 9. Kodi ndani amene akanatha kuona chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu ndi kumvetsa tanthauzo lake?
8 Afarisi atafunsa kuti Ufumu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti sudzabwera “mwa maonekedwe ochititsa chidwi” kwa iwo. (Luka 17:20, 21) Anthu osakhulupirira sakanazindikira. Kodi iwo akanazindikira bwanji zimenezo pamene ngakhale Yesuyo sanamuzindikire kuti ndi Mfumu yawo ya m’tsogolo? Nanga ndani amene akanatha kuona chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu ndi kumvetsa tanthauzo lake?
9 Yesu anapitiriza kunena kuti ophunzira ake adzaona chizindikirocho bwinobwino ngati mmene angaonere “mphezi, mwa kung’anima kwake, [imene] imawala kuchokera mbali ina pansi pa thambo kukafika mbali ina pansi pa thambo.” (Werengani Luka 17:24-29.) N’zochititsa chidwi kuti lemba la Mateyo 24:23-27 limagwirizanitsa mfundo imeneyi ndi chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu.
M’badwo Umene Ukuona Chizindikiro
10, 11. (a) Kodi m’mbuyomu panafotokozedwa zotani zokhudza “m’badwo” wotchulidwa pa Mateyo 24:34? (b) Kodi ophunzira a Yesu mosakayikira ayenera anadziwa kuti ndaninso amene adzakhala “m’badwo” umenewo?
10 M’mbuyomu, magazini ino inafotokoza kuti m’nthawi ya Yesu, “m’badwo uwu” wotchulidwa pa Mateyo 24:34 unali kutanthauza ‘m’badwo wa Ayuda osakhulupirira wokhala m’nyengo imodzi.’b Kafotokozedwe kameneka kanaoneka ngati komveka chifukwa chakuti m’malo ena onse amene Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “m’badwo,” ananena za kuipa kwa m’badwo umenewo. Ndipo kawirikawiri Yesu anagwiritsa ntchito mawu monga “woipa” kufotokoza m’badwo umenewo. (Mat. 12:39; 17:17; Maliko 8:38) Chifukwa cha zimenezi, panali maganizo akuti pakukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosiwo, Yesu anali kunena za “m’badwo” woipa wa anthu osakhulupirira amene adzaona zochitika zimene zidzakhala chizindikiro cha “mathedwe a dongosolo lino la zinthu” (syn·teʹlei·a) ndi mapeto (teʹlos) ake.
11 Kunena zoona, pamene Yesu anagwiritsa ntchito mawu ofotokoza kuipa kwa “m’badwo,” anali kulankhula ndi anthu oipa kapena za anthu oipa a m’nthawi yake. Koma kodi zinalinso choncho ndi mawu ake olembedwa pa Mateyo 24:34? Musaiwale kuti ophunzira anayi a Yesu anafika kwa iye “mwamseri.” (Mat. 24:3) Popeza kuti Yesu sanagwiritse ntchito mawu ofotokoza kuipa kwa m’badwo powauza za “m’badwo uwu,” atumwiwo mosakayikira ayenera kuti anadziwa kuti iwo ndi ophunzira anzawo adzakhala “m’badwo” umene sudzatha wonse kuchoka “kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”
12. Kodi nkhani yonse ikusonyeza chiyani za amene Yesu anali kutanthauza ponena mawu akuti “m’badwo”?
12 Kodi tikunena zimenezi chifukwa chiyani? Tiyeni tione bwinobwino nkhani yake yonse. Pa Mateyo 24:32, 33, Yesu anati: “Tsopano phunzirani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Pamene nthambi yake yanthete yaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti chilimwe chili pafupi. Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo penipeni.” (Yerekezerani ndi Maliko 13:28-30; Luka 21:30-32.) Kenako, pa Mateyo 24:34 pamati: “Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”
13, 14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ophunzira a Yesu ayenera kuti ndi amene anali “m’badwo” umene iye anali kunena?
13 Yesu ananena kuti ophunzira ake, amene anali pafupi kudzozedwa ndi mzimu woyera, ndi amene akanatha kumvetsa ataona “zinthu zonsezi” zikuchitika. Choncho Yesu ayenera kuti anali kunena za ophunzira ake pamene ananena mawu akuti: “M’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”
14 Mosiyana ndi anthu osakhulupirira, ophunzira a Yesu anatha kuona chizindikirocho n’kumvetsanso tanthauzo lake. Iwo anatha ‘kuphunzirapo’ pa zochitika za chizindikirocho ndi ‘kudziwa’ tanthauzo lake lenileni. Anazindikiradi kuti ‘iye ali pakhomo penipeni.’ Ngakhale kuti Ayuda osakhulupirira ndiponso Akhristu odzozedwa okhulupirika anaona kukwaniritsidwa kochepa kwa mawu a Yesu nthawi imeneyo, ndi otsatira ake odzozedwa okha amene kalelo anatha kuphunzira pa zochitika zimenezi. Iwo okha ndi amene anamvetsa tanthauzo lenileni la zimene anaona.
15. (a) Kodi “m’badwo” wamakono umene Yesu anali kunena ndani? (b) N’chifukwa chiyani sitingawerengetse zaka zenizeni za “m’badwo uwu”? (Onani bokosi patsamba 25.)
15 Masiku ano, anthu osazindikira zinthu zauzimu amaganiza kuti palibe “maonekedwe ochititsa chidwi” a chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Iwo amati zinthu zonse zikupitirirabe monga mmene zinalili kale. (2 Pet. 3:4) Koma abale a Khristu odzozedwa ndiponso okhulupirika amene ndi gulu la Yohane lamakono, aona chizindikiro chimenechi ngati mmene angaonere kung’anima kwa mphezi ndipo amvetsa tanthauzo lake lenileni. Monga gulu, odzozedwa amenewa ndiwo “m’badwo” wamakono wa anthu okhala panyengo imodzi, umene sudzatha wonse kuchoka “kufikira zinthu zonsezi zitachitika.”c Zimenezi zikusonyeza kuti abale ena a Khristu odzozedwa adzakhala ali amoyo padziko lapansi pamene chisautso chachikulu chomwe chinaloseredwa chidzayamba.
“Khalani Maso”
16. Kodi ophunzira onse a Khristu ayenera kuchita chiyani?
16 Kungoona chizindikirocho si kokwanira. Yesu anapitiriza kunena kuti: “Zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.” (Maliko 13:37) Kaya ndife odzozedwa kapena a khamu lalikulu, zimenezi ndi zofunika kwambiri kwa ife. Padutsa zaka zoposa 90 kuchokera pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba mu 1914. Zivute zitani, tiyenera kukhala okonzeka ndi kukhala maso. Kudziwa kuti Khristu wakhalapo monga Mfumu ngakhale sakuoneka, kumatithandiza kuchita zimenezi. Kumatikumbutsanso mfundo yakuti posachedwapa iye abwera kudzawononga adani ake ‘pa ola limene sitikuliganizira.’—Luka 12:40.
17. Kodi kumvetsa tanthauzo la kukhalapo kwa Khristu kuyenera kutithandiza motani, ndipo tiyenera kulimbikira kuchita chiyani?
17 Kumvetsa tanthauzo la kukhalapo kwa Khristu kumatithandiza kusaiwala kuti nthawi yatha. Tikudziwa kuti kukhalapo kwa Yesu kunayamba kale ndipo ngakhale sakuoneka, akulamulira monga Mfumu kumwamba kuyambira 1914. Posachedwapa abwera kudzawononga oipa ndi kusintha zinthu kwambiri padziko lonse lapansili. Choncho kuposa kale lonse, tiyeni tilimbikire kugwira nawo ntchito mwakhama imene Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto [teʹlos] adzafika.”—Mat. 24:14.
[Mawu a M’munsi]
a Tanthauzo la pa·rou·siʹa lingadziwike poona kusiyana pakati pa mawu akuti ‘kukhalapo’ kwa mtumwi Paulo ndi akuti “kulibe” opezeka pa 2 Akorinto 10:10, 11 ndi Afilipi 2:12. Kuti mumve zambiri, onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 676-679.
c Zikuoneka kuti nthawi imene “m’badwo uwu” ulipo ndi imodzimodzi ndi nthawi ya kukwaniritsidwa kwa masomphenya oyamba a m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 1:10–3:22) Mbali imeneyi ya tsiku la Ambuye ikuyambira mu 1914 mpaka tsiku limene wodzozedwa wokhulupirika womaliza adzamwalira ndi kuukitsidwa.—Onani Revelation—Its Grand Climax At Hand! tsamba 24, ndime 4.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi tikudziwa bwanji kuti nthawi ya kukhalapo kwa Yesu ndi yaitali?
• Kodi ndani amaona chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu ndi kumvetsa tanthauzo lake?
• Kodi m’badwo wamakono wotchulidwa pa Mateyo 24:34 ndani?
• N’chifukwa chiyani sitingawerengetse zaka zenizeni za “m’badwo uwu”?
[Bokosi patsamba 25]
Kodi Tingawerengetse Zaka za “M’badwo Uwu”?
Nthawi zambiri mawu akuti “m’badwo” amanena za anthu amisinkhu yosiyanasiyana amene amakhala ndi moyo panyengo inayake kapena pazochitika zinazake. Mwachitsanzo, lemba la Eksodo 1:6 limatiuza kuti: ‘Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi m’badwo uwo wonse.’ Yosefe ndi abale ake anali osiyana msinkhu, koma onse anakumana ndi zochitika zimodzimodzi panyengo yofanana. ‘M’badwo uwo’ unaphatikizapo abale ake ena a Yosefe amene anabadwa iye asanabadwe. Ena mwa amenewa anakhala ndi moyo wautali kuposa Yosefe. (Gen. 50:24) Ena, a “m’badwo uwo,” monga Benjamini, anabadwa Yosefe atabadwa kale ndipo ayenera kuti anakhalabe ndi moyo Yosefe atamwalira.
Motero, pamene mawu akuti “m’badwo” agwiritsidwa ntchito ponena za anthu okhala ndi moyo panthawi inayake, n’zosatheka kunena zaka zenizeni za nthawi imeneyo komabe nthawiyo imakhala ndi mapeto ake ndipo sikhala yaitali mopitirira muyeso. Choncho, pogwiritsa ntchito mawu akuti “m’badwo uwu” olembedwa pa Mateyo 24:34, Yesu sanapatse ophunzira ake njira yowerengetsera nthawi pamene “masiku otsiriza” adzatha. M’malo mwake, Yesu anatsindikanso mfundo yakuti iwo sadzadziwa “za tsikulo ndi ola lake.”—2 Tim. 3:1; Mat. 24:36.
[Chithunzi pamasamba 22, 23]
Kuyambira pamene anavekedwa kolona kukhala Mfumu mu 1914, Yesu akufotokozedwa kuti ‘akugonjetsa’
[Chithunzi patsamba 24]
“M’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika”