Yehova Amayamikira Utumiki Wanu wa Mtima Wonse
“Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima [“ndi mtima wonse,” NW], monga kwa Ambuye [“Yehova,” NW], osati kwa anthu ayi.”—AKOLOSE 3:23.
1, 2. (a) Kodi mwaŵi waukulu kwambiri umene tingakhale nawo ngwotani? (b) Nchifukwa ninji nthaŵi zina tingalephere kuchita zonse zimene timafuna kuchita potumikira Mulungu?
KUTUMIKIRA Yehova ndiwo mwaŵi waukulu kwambiri umene tingakhale nawo. Pachifukwa chabwino, magazini ino kuyambira kale yalimbikitsa Akristu kutengamo mbali mu utumiki, ngakhale kutumikira “mokwanira” ngati kungatheke. (1 Atesalonika 4:1, NW) Komabe, si nthaŵi zonse pamene timatumikira Mulungu monga momwe mtima wathu umafunira. “Cholinga changa ndicho kugwira ntchito nthaŵi zonse,” akufotokoza motero mlongo wina wosakwatiwa amene anabatizidwa pafupifupi zaka 40 zapitazo. “Chifukwa changa chogwirira ntchito sindicho kupeza zovala zapamwamba kapena kuwononga ndalama zambiri kutchuthi, koma kuti ndizipeza zofunika, kuphatikizapo ndalama zogulira mankhwala ndi zolipirira kuchipatala cha mano. Ndikuona monga ndikupatsa Yehova zinthu zotsala.”
2 Chifukwa chakuti timakonda Mulungu timafuna kuchita zambiri monga momwe tingathere m’ntchito yolalikira. Koma zochitika m’moyo mwathu nthaŵi zambiri zimalepheretsa zimene timafuna kuchita. Kusamalira maudindo ena a Malemba, kuphatikizapo kusamalira apabanja, kungatidyere nthaŵi yathu ndi mphamvu yathu yaikulu. (1 Timoteo 5:4, 8) Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino moyo wafika pothetsa nzeru. (2 Timoteo 3:1) Pamene tilephera kuchita zonse zimene timafuna kuchita mu utumiki, mtima wathu ungavutike. Tingafune kudziŵa ngati Mulungu amakondwera ndi kulambira kwathu.
Kukongola kwa Utumiki wa Mtima Wonse
3. Kodi Yehova amayembekezanji kwa tonsefe?
3 Pa Salmo 103:14, Baibulo likutitsimikizira bwino lomwe kuti Yehova “adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” Iye adziŵa kulephera kwathu kuposa wina aliyense. Safuna kuti tipereke zimene tilibe. Nanga amayembekezanji? Chinachake chimene aliyense, mosasamala kanthu za mikhalidwe yake m’moyo, angapereke: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima [“ndi mtima wonse,” NW], monga kwa Ambuye [“Yehova,” NW], osati kwa anthu ayi.” (Akolose 3:23) Inde, Yehova amafuna kuti ife—tonsefe—timtumikire ndi mtima wonse.
4. Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauzanji?
4 Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauzanji? Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “ndi mtima wonse” kwenikweni limatanthauza “kuchokera mumtima.” “Mtima” umatanthauza munthu weniweniyo, ndi luso lake lonse lakuthupi ndi lamaganizo. Choncho, kutumikira ndi mtima wonse kumatanthauza kudzipereka ife eni, kugwiritsira ntchito nzeru zathu ndi mphamvu zathu zonse moyenerera monga momwe tingathere m’kutumikira Mulungu. Kunena mwachidule, kumatanthauza kuchita zonse zimene ifeyo tingathe.—Marko 12:29, 30.
5. Kodi chitsanzo cha atumwi chimasonyeza motani kuti onse sangachite mofanana mu utumiki?
5 Kodi kutumikira ndi mtima wonse kumatanthauza kuti tiyenera kutero pamlingo wofanana? Zimenezo sizingatheke nkomwe, popeza kuti mikhalidwe ndi kukhoza zimasiyanasiyana pakati pa wina ndi mnzake. Talingalirani za atumwi okhulupirika a Yesu. Iwo sanali kuchita zofanana. Mwachitsanzo, timadziŵa zochepa kwambiri ponena za atumwi ena, monga Simoni Mkanani ndi Yakobo mwana wa Alifeyo. Mwinamwake anali kuchita zochepa m’ntchito zawo monga atumwi. (Mateyu 10:2-4) Mosiyana ndi zimenezo, Petro anavomereza maudindo ambiri ovuta—inde, mpaka Yesu anampatsa “mafungulo a Ufumu”! (Mateyu 16:19) Komabe, Petro sanaikidwe monga wamkulu kuposa anzakewo. Pamene Yohane anaona masomphenya a Yerusalemu Watsopano m’Chivumbulutso (cha m’ma 96 C.E.), iye anaona maziko 12 pamene panalembedwa “maina khumi ndi aŵiri a atumwi khumi ndi aŵiri.”a (Chivumbulutso 21:14) Yehova anayamikira utumiki wa atumwi onse, ngakhale kuti mwachionekere ena anachita zambiri kuposa anzawo.
6. M’fanizo la Yesu la wofesa, kodi chikuchitika nchiyani ndi mbewu zofesedwa “panthaka yabwino,” ndipo pakubuka mafunso otani?
6 Mofananamo, Yehova safuna kuti tonse tizilalikira pamlingo umodzi. Yesu anasonyeza zimenezi m’fanizo la wofesa, limene linayerekezera ntchito yolalikira ndi kufesa mbewu. Mbewu zinagwa panthaka zosiyanasiyana, kuchitira fanizo mikhalidwe ya mtima yosiyanasiyana ya amene amamva uthenga. “Iye amene afesedwa panthaka yabwino,” anafotokoza motero Yesu, “uyu ndiye wakumva mawu nawadziŵitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.” (Mateyu 13:3-8, 18-23) Kodi zipatso zimenezi nchiyani, ndipo nchifukwa ninji zikubala pamlingo wosiyanasiyana?
7. Kodi zipatso za mbewu zofesedwa ndizo chiyani, ndipo nchifukwa ninji zikubala muunyinji wosiyanasiyana?
7 Popeza kuti mbewu imene ifesedwa ndiyo “mawu a Ufumu,” kubala zipatso kumeneku kukutanthauza kufalitsa mawu amenewo, kuuza anthu ena. (Mateyu 13:19) Kuchuluka kwa kabalidwe ka zipatso nkosiyanasiyana—kuchokera pa makumi atatu mpaka pa makumi khumi—chifukwa chakuti kukhoza ndi mikhalidwe m’moyo imasiyanasiyana. Munthu amene ali ndi thanzi labwino ndiponso wolimba mwakuthupi angathere nthaŵi yochuluka m’ntchito yolalikira kuposa amene alibe mphamvu chifukwa cha kudwaladwala kapena chifukwa cha ukalamba. Wachinyamata wosakwatira kapena wosakwatiwa amene alibe udindo wosamalira banja angachite zambiri kuposa amene amagwira ntchito nthaŵi zonse pofuna kusamalira banja.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:29.
8. Kodi Yehova amawaona motani amene amapereka ndi mtima wawo wonse?
8 Kodi munthu wogwira ntchito ndi mtima wonse wobala zipatso makumi atatu ali wodzipereka pang’ono pamaso pa Mulungu kusiyana ndi wobala zipatso makumi khumi? Kutalitali! Kuchuluka kwa zipatso kungakhale kosiyana, koma Yehova amayamikira malinga ngati utumiki umene timachitawo timauchita ndi mtima wathu wonse. Kumbukirani, zipatso zonse zosiyanasiyanazo zimachokera m’mitima imene ili “nthaka yabwino.” Liwu lachigiriki (ka·losʹ) lotembenuzidwa kuti “chabwino” limanena za chinthu chimene chili “chokongola” ndiponso chimene “chimakondweretsa mtima, ndi kusangalatsa maso.” Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti pamene tiyesetsa mmene tingathere, mtima wathu umakhala wokongola pamaso pa Mulungu!
Sayerekezera Wina ndi Mnzake
9, 10. (a) Kodi mtima wathu ungatipangitse kuganiza zolakwa zotani? (b) Kodi fanizo la pa 1 Akorinto 12:14-26 limasonyeza motani kuti Yehova satiyerekezera ndi ena pa zimene timachita?
9 Komabe, mtima wathu wopanda ungwirowu ungatichititse kuona zinthu molakwa. Tingayerekezere utumiki wathu ndi wa anthu ena. Tingaganize kuti, ‘Ena akuchita zambiri mu utumiki kuposa mmene ndikuchitira. Kodi Yehova angakondwere ndi utumiki wanga?’—Yerekezerani ndi 1 Yohane 3:19, 20.
10 Maganizo ndi njira za Yehova nzapamwamba kwambiri kupambana zathu. (Yesaya 55:9) Timazindikira mmene Yehova amaonera zoyesayesa zathu aliyense payekha kuchokera pa 1 Akorinto 12:14-26, pamene mpingo ukuyerekezeredwa ndi thupi la ziŵalo zosiyanasiyana—maso, manja, mapazi, makutu, ndi zina. Tangolingalirani za thupi lenilenilo. Kungakhale kupusa chotani nanga kuyerekezera maso anu ndi manja anu kapena kuyerekezera mapazi anu ndi makutu anu! Chiŵalo chilichonse chili ndi ntchito yake yosiyana, komabe ziŵalo zonsezo zimagwira ntchito zofunika ndipo zimayamikiridwa. Mofananamo, Yehova amayamikira utumiki wanu wa mtima wonse mosasamala kanthu kuti kaya ena akuuchita pamlingo waukulu kapena akuuchita pamlingo wochepa.—Agalatiya 6:4.
11, 12. (a) Nchifukwa ninji ena angaganize kuti ali “ofooka” kapena “ochepa ulemu”? (b) Kodi Yehova amauona motani utumiki wathu?
11 Pamene tilephera kuchita zochuluka chifukwa cha matenda, ukalamba, kapena zochitika zina, nthaŵi zina enafe tingaganize kuti ndife “ofooka” kapena kuti ndife anthu “ochepa ulemu.” Koma si mmene Yehova amaganizira. Baibulo likutiuza kuti: “Ziŵalozo zoyesedwa zofooka m’thupi, zifunika; ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu . . . pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; . . . koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosoŵacho.” (1 Akorinto 12:22-24) Choncho munthu aliyense angakhale wamtengo wapatali kwa Yehova. Iye amayamikira utumiki wathu ngakhale kuti timalephera kuchita zina. Kodi mtima wanu sukusonkhezerani kuchita zambiri monga momwe mungathere m’kutumikira Mulungu womvetsetsa ndiponso wachikondi ameneyo?
12 Choncho, chimene Yehova amayamikira sindicho kuti muzichita zofanana ndi ena ayi koma zimene inuyo—ndi mtima wanu wonse—mungathe kuchita panokha. Zonena kuti Yehova amayamikira zoyesayesa zathu aliyense payekha zinasonyezedwa mogwira mtima ndi mmene Yesu anachitira ndi akazi aŵiri osiyana kwambiri kumapeto kwa moyo wake wa padziko lapansi.
Mphatso ya “Mtengo Wapatali” ya Mkazi Woyamika
13. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitika pamene Mariya anadzoza mutu ndi mapazi a Yesu ndi mafuta onunkhira bwino? (b) Kodi mafuta a Mariya anali a ndalama zingati?
13 Lachisanu madzulo, Nisani 8, Yesu anafika ku Betaniya, mudzi waung’ono chakummaŵa m’mphepete mwa Phiri la Azitona, pafupifupi makilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu. Yesu anali ndi mabwenzi ake okondedwa m’tauni imeneyi—Mariya, Marita, ndi mbale wawo, Lazaro. Yesu anali mlendo kunyumba kwawo, mwinamwake mobwerezabwereza. Koma Loŵeruka madzulo, Yesu ndi mabwenzi akewa anaitanidwa kuchakudya m’nyumba ya Simoni, amene khate lake mwina linachiritsidwa ndi Yesu kumbuyoku. Pamene Yesu anaseyama pagome, Mariya modzichepetsa anachita chinachake chimene chinasonyeza chikondi chake chochokera pansi pa mtima kwa mwamuna amene anaukitsa mbale wake. Anatsegula nsupa yokhala ndi mafuta onunkhira bwino, “a mtengo wapatali.” Analidi a mtengo wapatali! Mafutawo anali okwanira malupiya a theka 300, ndalama zofanana ndi malipiro a chaka chonse. Iye anadzoza mutu ndi mapazi a Yesu ndi mafuta onunkhirawo. Inde mpaka iye anapukuta mapazi a Yesu ndi tsitsi lake.—Marko 14:3; Luka 10:38-42; Yohane 11:38-44; 12:1-3.
14. (a) Kodi ophunzira anachitanji ataona zimene Mariya anachita? (b) Kodi Yesu anatetezera Mariya motani?
14 Ophunzira anavutika mtima! ‘Nkutayiranji mafutawa?’ anafunsa motero. Yudasi, pobisa chikhumbo cha kuba, ananyengezera kuti anali ndi malingaliro ofuna kuthandiza osauka, nanena kuti: “Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi malupiya a theka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?” Mariya anakhalabe chete. Komabe, Yesu anauza ophunzirawo nati: “Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira ine ntchito yabwino [mtundu wa ka·losʹ]. . . . Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m’manda. Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.” Mawu a Yesu okomawo anatonthoza mtima wa Mariya chotani nanga!—Marko 14:4-9; Yohane 12:4-8.
15. Nchifukwa ninji Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anachita Mariya, ndipo tikuphunzirapo chiyani ponena za utumiki wa mtima wonse?
15 Yesu anasangalala kwambiri ndi zimene anachita Mariya. Malinga nkunena kwake, iye anachita ntchito yabwino. Sikunali kukwera kwa mtengo wa mphatsoyo kumene Yesu anayamikira ayi koma chifukwa chakuti ‘anachita chimene anakhoza.’ Anagwiritsira ntchito mwaŵiwo napereka chimene anakhoza kupereka. M’mabaibulo ena mawu ameneŵa atembenuzidwa kuti, “Wachita zonse zimene angachite,” kapena, “Wachita chimene iye anatha kuchita.” (An American Translation; The Jerusalem Bible) Mariya anapereka ndi mtima wonse chifukwa chakuti anapereka zimene anali nazo. Zimenezo nzimene utumiki wa mtima wonse umatanthauza.
“Tindalama Tiŵiri Tating’ono” ta Mkazi Wamasiye
16. (a) Kodi Yesu anachidziŵa bwanji chopereka cha mkazi wamasiye waumphaŵi? (b) Kodi timakobiri ta mkazi wamasiyeyo tinali ndalama zingati?
16 Masiku angapo zitatha izi, pa Nisani 11, Yesu anakhala tsiku lonse lathunthu m’kachisi, kumene anatsutsa ulamuliro wake ndi kuyankha mosapita mbali mafunso ovuta onena za misonkho, chiukiriro, ndi nkhani zina. Iye anadzudzula alembi ndi Afarisi chifukwa chakuti, mwa zina, ‘analusira nyumba za akazi amasiye.’ (Marko 12:40) Kenaka Yesu anakhala pansi, mwachionekere m’Bwalo la Akazi, kumene, monga mwa mwambo wachiyuda, kunali mabokosi a zopereka okwanira 13. Anakhala pamenepo kanthaŵi ndithu, kupenyerera anthu pamene anali kupereka zopereka zawo. Panabwera anthu olemera ambiri, mwinamwake ena okhala ndi maonekedwe odzilungamitsa, ngakhalenso mwina odzitukumula. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:2.) Yesu anasumika maso pa mkazi wina. Maso wamba mwinamwake sakanaona chilichonse chachilendo kwa mkaziyo kapena mphatso yake. Koma Yesu, amene anatha kudziŵa mitima ya ena, anadziŵa kuti iye anali “mkazi wamasiye waumphaŵi.” Anadziŵanso bwino lomwe kuchuluka kwa mphatso imene anapereka—“tindalama tiŵiri tating’ono, tofa kakobiri kamodzi.”b—Marko 12:41, 42.
17. Kodi Yesu anachiona motani chopereka cha mkazi wamasiye, ndipo motero tikuphunzirapo chiyani ponena za kupereka kwa Mulungu?
17 Yesu anaitana ophunzira ake, chifukwa chakuti anafuna kuti iwo akhale oyambirira kuzindikira phunziro limene anali pafupi kuphunzitsa. Iye “anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo,” Yesu anatero. Malinga ndi mmene iye anaonera, mkaziyo anaponyamo ndalama zoposa zimene enawo anaponyamo kuziphatikiza pamodzi. Anapereka “zonse anali nazo”—ndalama zake zonse. Mwa kutero, anadziika m’manja mwa Yehova. Choncho, munthu amene anakhala monga chitsanzo cha kupereka kwa Mulungu anali amene mphatso yake inali yochepa kwambiri mwakuthupi. Komabe, pamaso pa Mulungu, mphatsoyo inali ya mtengo wapatali koposa!—Marko 12:43, 44; Yakobo 1:27.
Kuphunzirira pa Kaonedwe ka Yehova ka Utumiki wa Mtima Wonse
18. Kodi tikuphunzirapo chiyani ponena za mmene Yesu anachitira ndi akazi aŵiriwo?
18 Malinga ndi mmene Yesu anachitira ndi akazi aŵiriwa, tikuphunzirapo maphunziro otonthoza mtima a mmene Yehova amaonera utumiki wa mtima wonse. (Yohane 5:19) Yesu sanayerekezere mkazi wamasiyeyo ndi Mariya. Anayamikira timakobiri tiŵiri ta mkazi wamasiyeyo mofanana ndi mmene anayamikirira mafuta “a mtengo wapatali” a Mariya. Popeza kuti mkazi aliyense anapereka mmene anathera, mphatso zonsezo zinali za mtengo wapatali pamaso pa Mulungu. Choncho, ngati muganiza kuti ndinu wopanda pake chifukwa chakuti mukulephera kuchita mmene mumafunira potumikira Mulungu, musade nkhaŵa. Yehova amakondwera kulandira zonse zimene mungathe kupereka. Kumbukirani, Yehova “ayang’ana mumtima,” choncho iye amadziŵa bwino zokhumba za mtima wanu.—1 Samueli 16:7.
19. Nchifukwa ninji sitiyenera kuweruza anzathu ponena za mmene akutumikirira Mulungu?
19 Lingaliro la Yehova pa utumiki wa mtima wonse liyenera kusonkhezera mmene timaonerana ndi mmene timachitira kwa wina ndi mnzake. Kungakhale kupanda chikondi kotani nanga kusuliza zoyesayesa za ena kapena kuyerekezera utumiki wa munthu wina ndi mnzake! Mwachisoni, Mkristu wina analemba kuti: “Nthaŵi zina ena amapereka lingaliro lakuti ngati sindiwe mpainiya ndiwe wopanda pake. Ife amene timachita kuvutikira kuti tikhale ofalitsa ‘wamba’ a nthaŵi zonse a Ufumu tiyenera kuyamikiridwanso.” Tikumbukire kuti tilibe mphamvu yoweruza Mkristu mnzathu ponena za mmene angachitire utumiki wa mtima wonse. (Aroma 14:10-12) Yehova amayamikira utumiki wa mtima wonse wa aliyense wa miyandamiyanda ya ofalitsa Ufumu okhulupirika, ndipo ifenso tiyenera kutero.
20. Kodi kumakhala bwino kulingalira chiyani ponena za alambiri anzathu?
20 Nanga bwanji ngati ena aoneka kuti akuchita zochepa kuposa mmene angachitire mu utumiki? Kupita pansi kwa ntchito ya wokhulupirira mnzathu kungasonyeze bwino kwa akulu okhudzidwa kuti pafunika thandizo kapena chilimbikitso. Panthaŵi imodzimodziyo, tisaiŵale kuti kwa ena, utumiki wa mtima wonse ungafanane ndendende ndi timakobiri tiŵiri tating’ono ta mkazi wamasiye osati ndi mafuta a mtengo wapatali a Mariya. Kumakhala bwino kulingalira kuti abale ndi alongo athu amakonda Yehova ndipo kuti chikondi chimenecho chidzawapangitsa kuchita zochuluka—osati zochepa—malinga ndi mmene angathere. Zoonadi palibe mtumiki wachikumbumtima chabwino wa Yehova amene angafune kuchita zochepa kuposa mmene angathere m’kutumikira Mulungu!—1 Akorinto 13:4, 7.
21. Kodi ndi ntchito yopindulitsa iti imene ambiri akulondola, ndipo ndi mafunso ati amene akubuka?
21 Komabe, kwa anthu ambiri a Mulungu, utumiki wa mtima wonse watanthauza kulondola ntchito yopindulitsa kwambiri—utumiki waupainiya. Kodi iwo amalandira madalitso otani? Ndipo bwanji nanga ponena za enafe amene sitinachitepo upainiya—kodi tingasonyeze bwanji mzimu waupainiya? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Popeza kuti Matiya analoŵa m’malo mwa Yudase monga mtumwi, dzina lake—osati la Paulo—liyenera kuti linaonekera pakati pa maziko 12 amenewo. Ngakhale kuti Paulo anali mtumwi, iye sanali mmodzi wa 12 amenewo.
b Kalikonse ka tindalama timeneti kanali ka lepton, ndalama yaing’ono koposa yachiyuda imene inali kugwiritsiridwa ntchito nthaŵi imeneyo. Ma lepton aŵiri anali ofanana ndi gawo limodzi mwa magawo 64 a malipiro a tsiku limodzi. Malinga nkunena kwa Mateyu 10:29, ndi kobiri la assarion (lofanana ndi ma lepton asanu ndi atatu), munthu anali kugula mpheta ziŵiri, zimene zinali zina mwa mbalame zotsika mtengo kwambiri zimene osauka anali kudya. Choncho, mkazi wamasiye ameneyu analidi wosauka, chifukwa chakuti anali ndi theka la ndalama yogulira mpheta imodzi, yosakwanira nkomwe kudyera chakudya.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauzanji?
◻ Kodi fanizo la pa 1 Akorinto 12:14-26 likusonyeza motani kuti Yehova satiyerekezera ndi ena?
◻ Kodi tikuphunzirapo chiyani ponena za kupereka ndi mtima wonse kuchokera m’ndemanga za Yesu zonena za mafuta a mtengo wapatali a Mariya ndi timakobiri tiŵiri ta mkazi wamasiye?
◻ Kodi njira imene Yehova amaonera utumiki wa mtima wonse ingatithandize bwanji ponena za mmene tiyenera kuonerana?
[Chithunzi patsamba 15]
Mariya anapereka mmene anathera, kudzoza thupi la Yesu ndi mafuta “a mtengo wapatali”
[Chithunzi patsamba 16]
Timakobiri ta mkazi wamasiye—pafupifupi topanda pake mwakuthupi koma tamtengo wapatali koposa pamaso pa Yehova