“Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
“Atayamika, anaunyemanyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’”—1 AKOR. 11:24.
1, 2. Kodi Atumwi ayenera kuti anazindikira chiyani za Yesu ndipo n’chifukwa chiyani?
ALONDA a ku Yerusalemu anali ataona kuti mwezi ukuoneka. Ndiyeno Khoti Lalikulu la Ayuda linali litauzidwa zimenezi ndipo linalengeza kuti mwezi wa Nisani wayamba. Kenako anthu ena anatumidwa kuti akafalitse uthengawu kapenanso kuyatsa moto wosonyeza kuti izi zachitika. Atumwi ankadziwa kuti nthawi ya Pasika inali itayandikira. Choncho ayenera kuti anazindikira zoti Yesu angafune kunyamuka kupita ku Yerusalemu kuti akafike kumeneko tsiku la Pasika lisanakwane.
2 Pa nthawiyi, Yesu anali ndi atumwi ake ku Pereya kutsidya la Yorodano. Iye anali pafupi kunyamuka ulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu. (Mat. 19:1; 20:17, 29; Maliko 10:1, 32, 46) Tsiku loyamba la mwezi wa Nisani likadziwika, anthu ankadziwa kuti achita Pasika pakangodutsa masiku 13, pa Nisani 14 dzuwa litalowa.
3. Kodi deti la Pasika ndi lofunika bwanji kwa Akhristu?
3 Deti la Pasika limagwirizana ndi deti la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndipo lidzakhala pa April 14, 2014 dzuwa litalowa. Tsiku limeneli ndi lofunika kwambiri kwa Akhristu oona komanso anthu ofuna kuphunzira Baibulo. Tikutero chifukwa cha zimene timawerenga pa 1 Akorinto 11:23-25. Lembali limati: “Yesu, usiku umene anali kukaperekedwa anatenga mkate. Ndipo atayamika, anaunyemanyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’ Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu.”
4. (a) Kodi tingakhale ndi mafunso ati okhudza Chikumbutso? (b) Kodi deti la Chikumbutso limadziwika bwanji chaka chilichonse? (Onani bokosi lakuti “Chikumbutso cha 2014.”)
4 Sitikukayikira kuti mudzapezeka pa mwambowu umene Yesu anauza otsatira ake kuti azichita chaka chilichonse pomukumbukira. Panopa ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingakonzekere bwanji mwambowu? Nanga udzachitika bwanji? Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzagwiritsidwe ntchito? Nanga mwambowu komanso zinthu zimene zidzagwiritsidwe ntchito n’zofunika bwanji kwa ineyo?’
ZIZINDIKIRO ZA PA CHIKUMBUTSO
5. Kodi Yesu anauza atumwi ake kuti akakonzekere zinthu ziti kuti achitire limodzi Pasika womaliza?
5 Pamene Yesu anauza atumwi ake kuti akakonze chipinda choti adzachitire Pasika, sananene za kukongoletsa kwambiri chipindacho. Zikuoneka kuti ankangofuna kuti chikhale choyera komanso choti anthu onse amene anaitanidwa akwanemo. (Werengani Maliko 14:12-16.) Pokonzekera mwambowu, atumwi anayenera kupeza zinthu ngati mkate wopanda chofufumitsa ndiponso vinyo wofiira. Atadya chakudya cha Pasika, Yesu anagwiritsa ntchito zinthu ziwirizi poyambitsa mwambo wa Chakudya cha Madzulo cha Ambuye.
6. (a) Kodi Yesu ananena chiyani za mkate atamaliza Pasika? (b) Kodi ndi mkate uti umene uyenera kugwiritsidwa ntchito pa Chikumbutso?
6 Mtumwi Mateyu analipo pa mwambowu ndipo anadzanena kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: ‘Eni, idyani.’” (Mat. 26:26) Mkatewu unali wopanda chofufumitsa ngati umene ankagwiritsa ntchito pa Pasika. (Eks. 12:8; Deut. 16:3) Ankauphika pongogwiritsa ntchito ufa wa tirigu ndi madzi. Sankaikamo zinthu ngati yisiti kapena mchere. Choncho mkatewu unali wosafufuma, wouma komanso wosavuta kubenthula. Masiku ano, akulu angapemphe munthu pasadakhale kuti aphike mkatewu pogwiritsa ntchito ufa wa tirigu ndi madzi ndipo angaike mafuta pang’ono m’chophikiracho. Ngati ufa wa tirigu sukupezeka, akhoza kugwiritsa ntchito ufa wa zinthu monga mpunga, balere kapena chimanga.
7. (a) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito vinyo wotani? (b) Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito vinyo wotani pa Chikumbutso?
7 Mateyu ananenanso kuti: “[Yesu] anatenga kapu ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu.’” (Mat. 26:27, 28) Kapu imene Yesu anatenga inali ya vinyo wofiira. Sakanagwiritsa ntchito madzi a mphesa chifukwa nyengo yokolola mphesa inali itadutsa kalekale. Ngakhale kuti pa Pasika woyamba ku Iguputo sanagwiritse ntchito vinyo, Yesu sananene kuti asagwiritsidwe ntchito. Iye anagwiritsanso ntchito vinyoyu pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Nawonso Akhristu amagwiritsa ntchito vinyo pa Chikumbutso. Magazi a Yesu anali amtengo wapatali ndipo sanafunike kuwawonjezera mphamvu. Choncho si bwino kuthira zinthu zowonjezera mphamvu kapena zokometsera mu vinyo wa pa Chikumbutso. Ndi bwino kungofulula kapena kugula vinyo wosasakaniza chilichonse (monga Beaujolais, Burgundy kapena Cabernet).
KODI ZIZINDIKIROZI ZIMAIMIRA CHIYANI?
8. N’chifukwa chiyani Akhristu amaganizira kwambiri zimene mkate ndi vinyo zimaimira?
8 Mtumwi Paulo anasonyeza kuti si atumwi okha amene ayenera kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, koma Akhristu onse. Iye analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Zimene ndinalandira kwa Ambuye n’zimene inenso ndinakupatsirani, zakuti Ambuye Yesu . . . anatenga mkate. Ndipo atayamika, anaunyemanyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’” (1 Akor. 11:23, 24) Chifukwa chakuti Akhristu analamulidwa kuchita mwambowu chaka ndi chaka, amaganizira kwambiri zimene mkate ndi vinyo zimaimira.
9. Kodi ena amalakwitsa n’kumaganiza chiyani za mkate umene Yesu anagwiritsa ntchito?
9 Anthu a m’matchalitchi ena amanena kuti Yesu anati: ‘Mkate uwu ndi thupi langa.’ Choncho amakhulupirira kuti mkatewo unasintha mozizwitsa n’kukhala thupi lake lenileni. Koma zimenezi si zoona.a Tikutero chifukwa chakuti pa nthawiyo thupi la Yesu linalipo ndipo mkate woti adyewo unaliponso. Choncho Yesu ankangonena zinthu mophiphiritsira ngati mmene ankachitiranso nthawi zina zambiri.—Yoh. 2:19-21; 4:13, 14; 10:7; 15:1.
10. Kodi mkate wa pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye umaimira chiyani?
10 Mkate umene anagwiritsa ntchito pa nthawiyo umaimira thupi la Yesu. Koma kodi thupi lake ndi liti? Poyamba atumiki a Mulungu ankaganiza kuti mkate umaimira mpingo wa odzozedwa, womwe umatchedwanso “thupi la Khristu.” Ankaganiza choncho chifukwa chakuti Yesu ananyemanyema mkate koma pamene ankaphedwa sanathyoledwe fupa lililonse. (Aef. 4:12; Aroma 12:4, 5; 1 Akor. 10:16, 17; 12:27) Koma atumiki a Mulunguwo ataganizira mozama n’kufufuza m’Malemba, anazindikira kuti mkatewo umaimira thupi la Yesu limene Mulungu anamukonzera. Yesu “anavutika m’thupi” mpaka kupachikidwa. Choncho mkate wa pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye umaimira thupi la Yesu limene ‘linanyamula machimo athu.’—1 Pet. 2:21-24; 4:1; Yoh. 19:33-36; Aheb. 10:5-7.
11, 12. (a) Kodi Yesu ananena zotani zokhudza vinyo? (b) Kodi vinyo amene amagwiritsidwa ntchito pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye amaimira chiyani?
11 Izi zingatithandizenso kumvetsa zimene Yesu ananena zokhudza vinyo. Baibulo limati: “Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu atadya chakudya chamadzulo, ndipo anati: ‘Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga.’” (1 Akor. 11:25) M’Mabaibulo ena monga Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu analemba mawuwa kuti: ‘Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga.’ Ndiyeno funso n’kumati, kodi chikhocho ndi chimene chinali pangano latsopano? Ayi. Mawu oti “kapu” kapena “chikho” akuimira vinyo amene anali mkatimo. Ndiyeno Yesu ananena kuti vinyoyo akuimira magazi ake amene anakhetsedwa.
12 M’buku la Maliko mawu a Yesuwa analembedwa kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri.” (Maliko 14:24) Magazi a Yesu anakhetsedwa “chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo awo akhululukidwe.” (Mat. 26:28) Choncho vinyo wofiira amaimira magazi enieni a Yesu. Chifukwa cha magazi amenewa tikhoza kumasulidwa ndi dipo ndiponso ‘kukhululukidwa machimo athu.’—Werengani Aefeso 1:7.
MWAMBO WOKUMBUKIRA IMFA YA KHRISTU
13. Kodi mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu umachitika bwanji?
13 N’kutheka kuti mukufuna kudzachita nawo mwambo wa Chikumbutso limodzi ndi Mboni za Yehova. Kodi mungakonde kudziwa mmene mwambowu udzachitikire? Choyamba, mwambowu udzachitikira pamalo oyera ndiponso abwino kukhalapo. Mwina adzaika timaluwa pang’ono koma sikuti adzachita kukongoletsa mogometsa ayi. Mkulu woyenerera adzafotokoza momveka bwino ndiponso mwaulemu zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mwambowu. Iye adzathandiza aliyense kumvetsa komanso kuyamikira zimene Khristu anatichitira. Yesu anafa n’kupereka dipo kuti tipeze moyo. (Werengani Aroma 5:8-10.) Wokamba nkhaniyo adzafotokozanso ziyembekezo ziwiri za Akhristu zimene zili m’Baibulo.
14. Kodi wokamba nkhani ya Chikumbutso adzafotokoza ziyembekezo ziwiri ziti?
14 Chiyembekezo choyamba n’chokalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba. Akhristu ochepa chabe, kuphatikizapo atumwi okhulupirika, ndi amene ali ndi chiyembekezochi. (Luka 12:32; 22:19, 20; Chiv. 14:1) Koma Akhristu ambiri amene akutumikira Mulungu mokhulupirika masiku ano akuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansili. Izi zikadzachitika ndiye kuti chifuniro cha Mulungu chidzakhala chitachitika kumwamba ndiponso pansi pano. Izi n’zimene Akhristu akhala akuzipempherera kwa nthawi yaitali. (Mat. 6:10) Baibulo limafotokoza bwino zinthu zosiyanasiyana zimene adzasangalale nazo kwamuyaya.—Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23.
15, 16. Kodi pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, mkate amachita nawo chiyani?
15 Ndiyeno chakumapeto, wokamba nkhaniyo adzasonyeza kuti yafika nthawi yoti tichite zimene Yesu anauza atumwi ake kuti azichita. Monga tanena kale, padzakhala mkate ndi vinyo. Mwina zidzaikidwa patebulo chapafupi ndi wokamba nkhani. Ndiyeno wokambayo adzafotokoza mavesi a m’Baibulo osonyeza zimene Yesu ananena ndiponso kuchita poyambitsa mwambowu. Mwachitsanzo, timawerenga m’buku la Mateyu kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.’” (Mat. 26:26) Yesu ananyema mkate wopanda chofufumitsa kuti apereke kwa ophunzira ake. Ndiyeno pa April 14, mikate yotereyi adzainyemanyema n’kuiika m’mbale.
16 Padzakhala mbale zokwanira, kuti ntchito yoyendetsa mbalezo kwa anthu onse isatenge nthawi yaitali. Sikuti padzakhala mwambo winawake wochititsa kaso ayi. Padzangoperekedwa pemphero kenako mbalezo zidzayendetsedwa mwadongosolo malinga ndi mmene malowo alili. Mofanana ndi chaka cha 2013, n’kutheka kuti m’mipingo yambiri anthu ochepa adzadya ndipo mwina palibe aliyense amene adzadye.
17. Kodi chidzachitike n’chiyani pa Chikumbutso potsatira malangizo a Yesu okhudza vinyo?
17 Kenako padzachitika zimene zafotokozedwa pa Mateyu 26:27, 28, zakuti: “Kenako [Yesu] anatenga kapu ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu. Vinyoyu akuimira “magazi anga a pangano,” amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.’” Potsatira zimenezi, padzaperekedwa pemphero lina kenako ‘makapu’ a vinyo wofiira adzayendetsedwa.
18. Popeza akudya ndi ochepa mwinanso sadzakhalapo, n’chifukwa chiyani tiyenera kupezekabe pa mwambowu?
18 Ambiri amene adzapezeke pa mwambowu sadzadya mkate kapena kumwa vinyo chifukwa chomvera zimene Yesu ananena zoti oyenera kudya ndi okhawo amene adzakalamulire naye limodzi kumwamba. (Werengani Luka 22:28-30; 2 Tim. 4:18) Choncho iwo adzangoonerera mwaulemu. Komabe kupezeka pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye n’kofunika kwambiri. Mukatero mumasonyeza kuti mumaona nsembe ya Yesu kukhala yamtengo wapatali kwambiri. Anthu akafika pa mwambowu amaganizira kwambiri madalitso amene angapeze chifukwa cha nsembe ya dipo imene Yesu anapereka. Amadziwa kuti akhoza kukhala m’gulu la “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. Anthu odzapulumukawa ndi amene “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 14-17.
19. Kodi tingachite chiyani pokonzekera Chikumbutso ndiponso kuti tidzapindule kwambiri?
19 Mboni za Yehova padziko lonse zimakonzekera mwambo wapaderawu. Kukatsala milungu ingapo kuti uchitike, padzakhala ntchito yoitana anthu kuti adzapezekepo. Ndiyeno kutatsala masiku angapo, tizidzawerenga nkhani za m’Baibulo zosonyeza zimene Yesu anachita komanso zimene zinachitika pa madeti ofananawo mu 33 C.E. Ndi bwino kuchita zonse zimene tingathe pokonzekera pasadakhale kuti tidzapezeke pa mwambowu. Tingachite bwino kudzafika nthawi ya nyimbo ndi pemphero isanakwane n’cholinga choti tidzalandire alendo komanso kuti mbali ina ya mwambowu isadzatipite. Kaya ndife Mboni kapena ayi, tidzapindula kwambiri ngati tizidzatsatira m’Mabaibulo athu pamene wokamba nkhaniyo akutchula malemba. Chofunika kwambiri n’chakuti tikadzapezeka pa mwambo wa Chikumbutso tidzasonyeza kuti timayamikira ndi mtima wonse nsembe imene Yesu anapereka. Tidzasonyezanso kuti tikumvera lamulo lake lakuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—1 Akor. 11:24.
a Katswiri wina wa ku Germany ananena kuti: “Popeza . . . Yesu analipo ndipo thupi lake lonse linali labwinobwino komanso magazi ake anali asanakhetsedwe, palibe aliyense mwa atumwiwo amene akanaganiza . . . zoti akudya thupi lenileni kapena kumwa magazi enieni a Ambuye. Choncho Yesu anagwiritsa ntchito mawu osavuta pofotokoza zimenezi ndipo sakanafuna kuti ophunzira ake amve zina.”