Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Yohane 18:15 amatchula wophunzira wodziŵika kwa mkulu wansembe. Kodi ameneyu ndi wophunzira mmodzimodzi yemwe poyamba anathaŵa ‘wamaliseche,’ monga momwe zasimbidwira pa Marko 14:51, 52?
Ayi, zikuwoneka kuti munthu wodziŵika kwa mkulu wansembe anali mtumwi Yohane, pamene kuli kwakuti anali wophunzira Marko yemwe anathaŵa ‘wamaliseche.’
Kuzitsatira nkhanizi mwadongosolo lanthaŵi pamene zinachitika, tiyambira pa munda wa Getsemane. Atumwiwo anachita mantha pamene Yesu Kristu anagwidwa. ‘Ndipo iwo onse anamsiya iye, nathaŵa.’ Vesi lotsatira lenilenilo m’cholembedwa cha Marko likusonyeza kusiyana motere: ‘Ndipo mnyamata wina anamtsata iye, nafundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira; koma iye anasiya bafutayo, nathaŵa wamaliseche.’—Marko 14:50-52.
Chotero, kachitidwe koyambirira ka atumwi 11 amenewo kakusiyanitsidwa ndi ka wophunzira wosatchulidwa dzina, chotero nkwanzeru kugamula kuti iye sanali mmodzi wa atumwiwo. Chochitikachi chasimbidwa kokha mu Uthenga Wabwino wolembedwa ndi wophunzira woyambirira Yohane wotchedwa Marko, msuwani wa Barnaba. Chotero, pali chifukwa chonenera kuti Marko ndiye anali “mnyamata wina” yemwe anayamba kutsatira Yesu wogwidwayo koma yemwe anathaŵa popanda chovala chake chofunda pamene gulu linayesa kumgwira iyenso.—Machitidwe 4:36; 12:12, 25; Akolose 4:10.
Panthaŵi ina usikuwo, mtumwi Petro anatsatiranso Yesu, pamtunda wabwino. M’lingaliroli pali kufanana; wophunzira wachichepere (Marko) anayamba kutsatira Yesu koma anaima, pamene kuli kwakuti pambuyo pake aŵiri a atumwi ake omwe anathaŵa anayamba kutsatira Ambuye wawo wogwidwayo. Mu Uthenga Wabwino wa mtumwi Yohane, timaŵerenga kuti: ‘Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziŵika kwa mkulu wansembe, naloŵa pamodzi ndi Yesu, m’bwalo la mkulu wansembe.’—Yohane 18:15.
Mtumwi Yohane akugwiritsira dzina lakuti “Yohane” kusonya kwa Yohane Mbatizi koma sakudzitchula yekha ndi dzina. Mwachitsanzo, iye akulemba za ‘wophunzira wakuchitira umboni za izi; ndipo analemba izi.’ Mofananamo: ‘Iye amene anawona, wachita umboni, ndi umboni wake uli wowona; ndipo iyeyu adziŵa kuti anena zowona.’ (Yohane 19:35; 21:24) Onaninso Yohane 13:23: ‘Mmodzi wa akuphunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pachifuŵa cha Yesu.’ Apo panali nthaŵi pang’ono Yesu asanagwidwe. Pambuyo pake tsiku lomwelo Yesu wopachikidwayo anapatulapo wophunzira mmodzi, amene Yohane akumtchula m’mawu ofanana kuti: ‘Pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, ali kuimirirako, [Yesu] ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!’—Yohane 19:26, 27; yerekezerani ndi Yohane 21:7, 20.
Mkhalidwe wofananawu wosadzitchula dzina ukuoneka pa Yohane 18:15. Ndiponso, Yohane ndi Petro akugwirizanitsidwa m’cholembedwa chapambuyo pa chiukiriro pa Yohane 20:2-8. Zisonyezero zimenezi zimapereka lingaliro lakuti mtumwi Yohane ndiye anali ‘wophunzira amene anali wodziŵika kwa mkulu wansembe.’ Baibulo silimapereka chidziŵitso chakumbuyo chosonyeza mmene mtumwi (Yohane) wa ku Galileya angakhale anadziŵira, ndikudziŵidwa, ndi mkulu wansembeyo. Koma kudziŵika kwake ndi banja la mkulu wansembeyo kunamkhozetsa Yohane kupyola pa wosunga pakhomo ndikuloŵa m’bwalomo ndikuloŵetsanso Petro.