MUTU 126
Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa Kayafa
MATEYU 26:69-75 MALIKO 14:66-72 LUKA 22:54-62 YOHANE 18:15-18, 25-27
PETULO ANAKANA YESU
Yesu atagwidwa m’munda wa Getsemane atumwi anathawa chifukwa ankachita mantha. Koma mtumwi Petulo “ndiponso wophunzira wina” anayamba kutsatira gulu lomwe linagwira Yesu. Zikuoneka kuti wophunzira winayo anali mtumwi Yohane. (Yohane 18:15; 19:35; 21:24) N’kutheka kuti atumwi awiriwa anakumana ndi gulu lomwe linagwira Yesu pamene ankapita kunyumba kwa Anasi. Anasi atalamula kuti gulu la anthulo lipite ndi Yesu kunyumba kwa Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, Petulo ndi Yohane ankawatsatira chapatali. Atumwiwo ayenera kuti anali ndi mantha poganizira zimene zikanawachitikira komanso ankadera nkhawa Mbuye wawo.
Yohane ankadziwana ndi Kayafa choncho sanavutike kulowa pageti la kunyumba kwa Kayafa. Koma Petulo anadikirirabe panja pa geti mpaka pamene Yohane anabwera kudzapempha mtsikana yemwe ankagwira ntchito ngati mlonda kuti amulowetse. Kenako mtsikanayo analola kuti Petulo alowe.
Chifukwa choti usiku umenewo kunkazizira kwambiri, anthu amene anasonkhana panja pa nyumba ya Kayafa ankawotha moto. Petulo ankawotha nawo motowo podikirira “kuti aone zotsatira” za mlandu wa Yesu. (Mateyu 26:58) Chifukwa cha kuwala kwa motowo, mtsikana uja anazindikira Petulo ndipo ananena kuti: “Kodi inunso si inu mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” (Yohane 18:17) Koma si mtsikana yekhayo amene anazindikira Petulo, panalinso anthu ena amene anamuzindikira n’kunena kuti ankayenda ndi Yesu.—Mateyu 26:69, 71-73; Maliko 14:70.
Petulo atadziwa kuti anthuwo amuzindikira, anakhumudwa kwambiri chifukwa sankafuna kuti anthu amudziwe moti anachoka n’kukakhala pageti. Petulo anakana zoti ankayenda ndi Yesu, moti munthu wina atamufunsa iye ananena kuti: “Ngakhale kumudziwa, sindikumudziwa ameneyo, ndipo sindikumvetsa kuti ukunena chiyani.” (Maliko 14:67, 68) Petulo anayambanso “kutemberera ndi kulumbira,” zomwe zikutanthauza kuti anali wokonzeka kulumbira kuti zimene ankanenazo zinali zoona komanso kuti anali wokonzeka kukumana ndi mavuto aliwonse ngati zomwe ankanenazo zikanadziwika kuti si zoona.—Mateyu 26:74.
Pamene zimenezi zinkachitika, n’kuti mlandu wa Yesu uli mkati m’chipinda cham’mwamba cha nyumba ya Kayafa. Petulo komanso anthu ena amene ankadikirira pa bwalo la nyumbayo ankangoona anthu akutuluka komanso kulowa kukapereka umboni.
Petulo akamalankhula ankamveka kuti ndi wa ku Galileya choncho zinkachita kuonekeratu kuti zimene ankanena zinali zabodza. Komanso munthu wina pa gululo anali wachibale wake wa Makasi, yemwe Petulo anamudula khutu uja. Munthuyo anafunsa Petulo kuti: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” Petulo atakananso kachitatu tambala analira ngati mmene Yesu ananenera.—Yohane 13:38; 18:26, 27.
Zikuoneka kuti pamene tambala ankalira, Yesu anali ataima pakhonde la chipinda cham’mwamba lomwe linali moyang’anizana ndi pa bwalo pa nyumbayo. Yesu atatembenuka anaphana maso ndi Petulo. Petulo ayenera kuti anadzimvera chisoni kwambiri mumtima mwake chifukwa anakumbukira zimene Yesu ananena ali m’chipinda chomwe anadyeramoPasika chija. Ndiyeno tangoganizani mmene Petulo anamvera atazindikira kuti wakanadi Yesu katatu. Nthawi yomweyo anatuluka mumpandawo ndipo analira mopwetekedwa mtima kwambiri.—Luka 22:61, 62.
Koma chinachitika n’chiyani kuti Petulo, yemwe ankadziona kuti ndi wolimba mwauzimu komanso wokhulupirika, akane Mbuye wake? Pa nthawiyi anthu ankapotoza choonadi komanso ankachita zinthu zoti Yesu aoneke ngati chigawenga choopsa. Choncho m’malo moti Petulo aikire kumbuyo munthu amene anali wosalakwa, iye anakana Munthu ‘amene anali ndi mawu amoyo wosatha.’—Yohane 6:68.
Zimene zinachitikira Petulo zikutithandiza kudziwa kuti ngati munthu sanakonzekere bwinobwino, ngakhale atakhala wodzipereka kwambiri komanso atakhala ndi chikhulupiriro cholimba, akhoza kugwa mwauzimu atakumana ndi mavuto kapena zinthu zomwe zingayese chikhulupiriro chake mwadzidzidzi. Choncho atumiki onse a Mulungu ayenera kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Petulo.