MUTU 34
Yesu Anasankha Atumwi 12
ATUMWI 12
Panali patangodutsa chaka chimodzi ndi hafu kuchokera pamene Yohane M’batizi anauza anthu kuti Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. Yesu atayamba ntchito yolalikira, anthu ena okhulupirika anakhala ophunzira ake. Ena mwa anthuwa mayina awo anali Andireya, Simoni Petulo, Yohane, Yakobo (mchimwene wake wa Yohane), Filipo, ndi Batolomeyo (yemwe ankadziwikanso kuti Natanayeli). Patapita nthawi, anthu enanso anakhala otsatira a Khristu.—Yohane 1:45-47.
Tsopano Yesu anali wokonzeka kuti asankhe atumwi. Atumwiwa anadzakhala anzake apamtima komanso anawaphunzitsa mwapadera ntchito yolalikira. Koma asanasankhe atumwiwa Yesu anapita kuphiri, mwina lomwe linali pafupi ndi nyanja ya Galileya chakufupi ndi ku Kaperenao. Iye anakhala kumeneko usiku wonse akupemphera ndipo n’kutheka kuti ankapempha nzeru komanso kuti Mulungu amuthandize. Tsiku lotsatira, anaitana ophunzira ake ndipo anasankhapo anthu 12 kuti akhale atumwi ake.
Yesu anasankha anthu 6 amene tawatchula kumayambiriro kwa nkhani ino kukhala atumwi ake kuphatikizapo Mateyu, yemwe anamuitana ali mu ofesi ya okhometsa msonkho uja. Anthu ena 5 amene anasankhidwa, mayina awo anali Yudasi (yemwe ankadziwikanso kuti Tadeyo komanso amene anali “mwana wa Yakobo”), Simoni Kananiya, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Yudasi Isikariyoti.—Mateyu 10:2-4; Luka 6:16.
Pa nthawiyi, atumwi 12 amenewa anali atayenda ndi Yesu kwa kanthawi ndithu ndipo iye ankawadziwa bwino. Ena mwa atumwiwa anali achibale ake. Mwachitsanzo, Yakobo ndi Yohane anali ana a mchemwali wake wa Mariya, omwe anali mayi ake a Yesu. Komanso ngati zimene anthu ena amanena zili zoona kuti Alifeyo anali mchimwene wake wa Yosefe (omwe anali bambo ake a Yesu omulera), ndiye kuti mtumwi Yakobo yemwe anali mwana wa Alifeyo analinso m’bale wake wa Yesu.
Yesu sankavutika kukumbukira mayina a atumwi ake. Koma kodi inuyo mukhoza kukumbukira mayina a atumwi onse? Muzingokumbukira kuti panali a Simoni awiri, a Yakobo awiri ndi a Yudasi awiri. Ndiyeno Simoni (Petulo) anali ndi m’bale wake dzina lake Andireya ndipo Yakobo (mwana wa Zebedayo) anali ndi m’bale wake dzina lake Yohane. Njira imeneyi ingakuthandizeni kukumbukira mayina a atumwi 8. Atumwi 4 otsalawo anali Mateyu (yemwe anali wokhometsa msonkho), Tomasi (yemwe anakayikira kuti Yesu waukitsidwa), Natanayeli (yemwe anaitanidwa ali pansi pa mtengo) komanso Filipo (yemwe anali mnzake wa Natanayeli).
Atumwi 11 anali ochokera ku Galileya, komwe kunalinso kwawo kwa Yesu. Natanayeli anali wochokera ku Kana. Kwawo kwenikweni kwa Filipo, Petulo ndi Andireya kunali ku Betsaida. Patapita nthawi Petulo ndi Andireya anasamukira ku Kaperenao, kumene Mateyu ankakhala. Yakobo ndi Yohane ankakhala ku Kaperenao kapena chakufupi ndi ku Kaperenao ndipo ankagwira ntchito ya usodzi chakufupi ndi kumene ankakhalako. Zikuoneka kuti Yudasi Isikariyoti, yemwe kenako anadzapereka Yesu, ndi mtumwi yekhayo amene anali wochokera ku Yudeya.