Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Asangalatsidwa ndi Mfarisi Wotchuka
YESU ndi mlendo m’nyumba ya Mfarisi wotchuka, kumene iye wangochiritsa kumene munthu wodwala mbulu. Tsopano, pamene Yesu akuwona alendo anzake akumasankha malo apamwamba pa chakudya, iye aphunzitsa phunziro pa kudzichepetsa.
“Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati,” Yesu akukpereka uphungu, “usaseyama pa mpando waulemu. Kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye, ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu adzati kwa iwe, ‘Mpatse uyu malo.’ Ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.”
Chotero Yesu akuchenjeza: “Koma pamene paliponse pamene waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo, kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe akanena nei iwe, ‘Bwenzi langa, sendera kwera kuno.’ Pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseyama pachakudya pamodzi ndi iwe.” Akumagogomezera phunzirolo, Yesu akumaliza kuti: “Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”
Potsatira, Yesu akulankhula ndi Mfarisi yemwe wamuitana iye ndi kulongosola mmene angaperekere chakudya chokhala ndi chivomerezo chenicheni cha Mulungu. “Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako kapena abale ako kapena a fuko lako kapena anansi ako eni chuma. Kuti kapena iwonso angabwezere kuitana iwe ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando, uitane aumphaŵi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe cha kubwezera iwe mphotho.”
Kupereka chakudya choterocho kaamba ka opanda mwaŵiwo kudzabweretsa chimwemwe kwa woperekayo chifukwa chakuti monga mmene Yesu akulongosolera kwa wochereza wake: “Udzabwezeredwa mphotho pa kuwuka kwa olungama.” Kulongosola kwa Yesu kwa chakudya cha ulemu chimenechi kumaitanira ku maganizo a mlendo mnzake za mtundu wina wa chakudya. “Wodala iye amene adzadya mkate mu ufumu wa Mulungu,” mlendo ameneyu akutero. Komabe, si onse amene moyenerera amayamikira chiyembekezo cha chimwemwe chimenecho, monga momwe Yesu akupitirizira kusonyeza mwa fanizo.
“Munthu wina anakonza phwando lalikulu, naitana anthu ambiri. Ndipo anatumiza kapolo wake . . . kukanena kwa oitanidwawo, ‘Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano.’ Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, ‘Ine ndagula munda ndipo ndiyenera ndituluke kukawuwona; ndikupempha, Undilole ine ndisafika.’ Ndipo anati wina, ‘Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha, Undilole ine ndisafika.’ Ndipo anati wina, ‘Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.’”
Ndi kupempha chikhululukira kopanda pake chotani nanga! Munda kapena ng’ombe mwachibadwa zimasanthulidwa zisanagulidwe, chotero sipamakhala kufunikira kwenikweni kwa kuyang’ana pa izo pambuyo pake. Mofananamo, ukwati wa munthu sufunikira kumuletsa iye kulandira chiitano chofunika koposa choterocho. Chotero pamene amva za kupempha chikhululukira kumeneku, mbuyeyo akwiya nalamulira kapolo wake:
“‘Tuluka msanga pita kumakwalala ndi ku njira za mudzi, nubwere nawo muno aumphwaŵi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.’ Ndipo kapoloyo anati, ‘Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo.’ Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, ‘Tuluka nupite ku misewu ndi njira za kuminda, nuwawumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale. . . . Kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.’”
Ndi mkhalidwe wotani umene ukulongosoledwa ndi fanizoli? Chabwino, “mbuye” wopereka chakudyayo akuimira Yehova Mulungu; “kapolo” wopereka chiitanoyo, Yesu Kristu; ndipo “phwando lamadzulo,” mwaŵi wa kukhala mu mzere kaamba ka Ufumu wa kumwamba.
Oyambirira kulandira chiitano kubwera mu mzere kaamba ka Ufumuwo anali, pamwamba pa ena onse, atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’tsiku la Yesu. Ngakhale kuli tero, iwo anakana chiitanocho. Chotero, kuyambira makamaka pa Pentekoste wa 33 C.E., chiitano chachiŵiri chinaperekedwa kwa onyazitsidwa ndi odzichepetsa a mtundu Wachiyuda. Koma si okwanira omwe anavomereza kudzaza malo 144,000 mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Chotero mu 36 C.E., zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, chiitano chachitatu ndi chomalizira chinafutukulidwa kwa osakhala Ayuda osadulidwa, ndipo kusonkhanitsidwa kwa oterowo kunapitiriza kufikira m’zana la 20. Luka 14:1-24.
◆ Ndi phunziro lotani m’kudzichepetsa limene Yesu akuphunzitsa?
◆ Ndimotani mmene wochereza angaperekere phwando lokhala ndi chivomerezo cha Mulungu, ndipo nchifukwa ninji ilo likamubweretsera chimwemwe?
◆ Nchifukwa ninji kupempha zikhululukiro kwa alendo oitanidwa kuli kopanda pake?
◆ Nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi fanizo la Yesu la “phwando lalikulu la madzulo”?