Tsanzirani Chifundo cha Mulungu Lerolino
‘Tigwe m’dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu.’—2 SAMUELI 24:14.
1. Kodi Davide analingalira motani za chifundo cha Mulungu, ndipo nchifukwa ninji?
MFUMU DAVIDE anadziŵa mwa zokumana nazo kuti Yehova ali wachifundo kwambiri kuposa anthu. Ndichidaliro kuti njira za Mulungu, kapena mabande ake, ngabwino koposa, Davide anafuna kuphunzira njira Zake ndikuyenda m’chowonadi Chake. (1 Mbiri 21:13; Salmo 25:4, 5) Kodi nanunso mumalingalira monga momwe anachitira Davide?
2. Kodi Yesu anapereka uphungu wotani pa Mateyu 18:15-17 ponena za kusamalira tchimo lalikulu?
2 Baibulo limapereka chidziŵitso cha kulingalira kwa Mulungu, ngakhale pankhani zonga ngati chimene tingachite ngati munthu wina atichimwira. Yesu anauza atumwi ake, omwe pambuyo pake anadzakhala oyang’anira Achikristu kuti: ‘Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.’ Kuchimwa komwe kukutchulidwa pano sikunaphatikizepo kusamvana wamba koma tchimo lalikulu, monga ngati chinyengo kapena kusinjirira. Yesu ananena kuti ngati sitepe limeneli lilephera kuthetsa nkhaniyo ndipo ngati pali mboni, wochimwiridwayo ayenera kuzitenga kuti zikatsimikizire kuti panali cholakwa. Kodi ili ndilo sitepe lomalizira? Ayi. ‘Ngati [wochimwayo] samvera iwo, uuze mpingo; ndipo ngati iye samveranso mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.’—Mateyu 18:15-17.
3. Kodi Yesu anatanthauzanji ponena kuti wochimwa wosalapa anayenera kukhala “monga wakunja ndi wamsonkho”?
3 Pokhala Ayuda, atumwiwo anamvetsetsa chimene chinatanthauza kumuchitira wochimwa “monga wakunja ndi wamsonkho.” Ayuda anapeŵa kuyanjana ndi anthu akunja, ndipo iwo ananyoza Ayuda omwe ankagwira ntchito monga amisonkho Achiroma.a (Yohane 4:9; Machitidwe 10:28) Chotero, Yesu ankalangiza ophunzirawo kuti ngati mpingo unakana wochimwa, iwo anayenera kuleka kuyanjana naye. Komabe, kodi zimenezo zikugwirizana motani ndi kuyanjana kwa Yesu ndi amisonkho panthaŵi zina?
4. Polingalira mawu ake a pa Mateyu 18:17, kodi nchifukwa ninji Yesu akanayanjana ndi amisonkho ndi ochimwa ena?
4 Luka 15:1 akuti: ‘Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva iye.’ Sikuti wamsonkho aliyense ndi wochimwa anali kumeneko, koma “onse” kutanthauza ambiri. (Yerekezerani ndi Luka 4:40.) Atiwo? Awo amene anali okondweretsedwa kuti machimo awo akhululukidwe. Ena oterowo anamva uthenga wa kutembenuka mtima wa Yohane Mbatizi. (Luka 3:12; 7:29) Chotero pamene ena anadza kwa Yesu, kulalikira kwake kwa iwo sikunatsutsane ndi uphungu wake wa pa Mateyu 18:17. Onani kuti ‘amisonkho ndi ochimwa ambiri [anamva Yesu] . . . ndipo anamtsata iye.’ (Marko 2:15) Aŵa sanali amene anafuna kupitiriza njira yoipa ya moyo, akumakana thandizo lirilonse. Mmalomwake, iwo anamva uthenga wa Yesu ndipo mitima yawo inakhudzidwa. Ngakhale kuti iwo ankachimwabe, pamene panthaŵi imodzimodziyo ankayesayesa kupanga masinthidwe, mwakulalikira kwa iwo, ‘mbusa wabwinoyo’ ankatsanzira Atate wake wachifundo.—Yohane 10:14.
Kukhululuka, Thayo la Mkristu
5. Kodi nkati komwe kali kaimidwe ka Mulungu ka kukhululukira?
5 Tiri ndi zitsimikizo zabwino izi za kufunitsitsa kwa Atate wathu kutikhululukira: ‘Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chirichonse.’ ‘Izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.’ (1 Yohane 1:9; 2:1) Kodi munthu wochotsedwa angakhululukiridwe?
6. Kodi munthu wochotsedwa angakhululukidwe ndi kubwezeretsedwa motani?
6 Inde. Panthaŵi yochotsa munthu chifukwa cha kuchimwa osalapa, akulu amene amaimira mpingo amamulongosolera kuti nkotheka kwa iye kutembenuka mtima ndi kulandira chikhululukiro cha Mulungu. Iye angamapezekepo pamisonkhano Panyumba Yaufumu, kumene angamve malangizo a m’Baibulo omwe angamuthandize kutembenuka mtima. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 14:23-25.) M’kupita kwanthaŵi iye angafune kubwezeretsedwa mumpingo woyerawo. Pamene akulu akumana naye, iwo adzayesayesa kutsimikiza kaya ngati iye walapadi ndikuleka njira yake yochimwa. (Mateyu 18:18) Ngati ziri choncho, iye angabwezeretsedwe, mogwirizana ndi dongosolo la pa 2 Akorinto 2:5-8. Ngati iye wakhala wochotsedwa kwa zaka zambiri, iye angafunikire kupanga kuyesayesa kwamphamvu kuti apange kupita patsogolo. Iye angafunikirenso thandizo lalikulu pambuyo pake kuti akulitse chidziŵitso chake cha Baibulo ndi chiyamikiro kotero kuti akhale Mkristu wolimba mwauzimu.
Kubwerera kwa Yehova
7, 8. Kodi Mulungu anakhazikitsa chitsanzo chotani m’chigwirizano ndi anthu ake okhala muukapolo?
7 Koma kodi akulu iwo eni angakhale oyamba kufikira munthu wochotsedwa? Inde. Baibulo limasonyeza kuti chifundo chingasonyezedwe osati kokha mwakusapereka chilango koma kaŵirikaŵiri mwakuchitapo kanthu moyenera. Tiri ndi chitsanzo cha Yehova. Asanatumize muukapolo anthu ake osakhulupirika, mwaulosi anapereka chiyembekezo cha kubwerera kwawo motere: ‘Kumbukirani zinthu izi, Yakobo; ndi Israyeli, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; . . . Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako, bwerera kwa ine, pakuti ndakuombola.’—Yesaya 44:21, 22.
8 Kenaka, mkati mwa ukapolowo, Yehova anatenga masitepe owonjezereka, akumachitapo kanthu m’njira yoyenera. Iye anatumiza aneneri, oimira ake, kukaitana Israyeli ‘kumfuna ndi kumpeza iye.’ (Yeremiya 29:1, 10-14) Pa Ezekieli 34:16, iye anadzifanizira yekha ndi mbusa ndipo anthu a mtundu wa Israyeli ku nkhosa yotaika: “Ndidzafuna yotayika, ndikubweza yopitikitsidwa.” Pa Yeremiya 31:10, Yehova anagwiritsiranso ntchito fanizo la kukhala mbusa wa Aisrayeli. Ayi, iye sanadzisonyeze kukhala mbusa wodikirira pakhola la nkhosa kaamba ka yotaika kuti ibwerere; mmalomwake, iye anadzisonyeza kukhala mbusa wofunafuna zotaika. Onani kuti ngakhale kuti mwachisawawa anthuwo anali osalapa ndiponso muukapolo, Mulungu anayambitsa zoyesayesa zakufuna kubwerera kwawo. Ndipo mogwirizana ndi Malaki 3:6, Mulungu sakasintha kachitidwe kake ndi makonzedwe Achikristu.
9. Kodi chitsanzo cha Mulungu chinatsatiridwa motani mumpingo Wachikristu?
9 Kodi izi sizikupereka lingaliro lakuti pangakhale chifukwa choyambitsira masitepe kwa ena omwe ngochotsedwa ndipo amene tsopano angakhale olapa? Kumbukirani kuti mtumwi Paulo anapereka malangizo akuchotsa munthu woipayo mu mpingo wa Korinto. Pambuyo pake iye anachenjeza mpingowo kukhala wolimba m’chikondi chawo kwa munthuyo chifukwa cha kutembenuka mtima kwake, kotsogolera ku kubwezeretsedwa kwake mu mpingo.—1 Akorinto 5:9-13; 2 Akorinto 2:5-11.
10. (a) Kodi ndi cholinga chotani chimene chiyenera kusonkhezera kupanga kuyesayesa kulikonse kwa kufikira anthu ena ochotsedwa? (b) Kodi nchifukwa ninji achibale Achikristu safunikira kukhala amene angayambitse kufikirako?
10 Bukhu lanazonse logwidwa mawu poyambirirapo linanena kuti: ‘Chifukwa chenicheni chochotsera munthu m’tchalitchi chinali kuchinjiriza miyezo ya gululo: ‘chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse’ (1 Akor. 5:6). Cholinga chimenechi m’chowonekera bwino m’ndime zambiri Zabaibulo ndi zosakhala za m’Baibulo, koma kudera nkhaŵa munthuyo, ngakhale pambuyo pa kuchotsedwa, ndiko kunali maziko a kuchonderera kwa Paulo pa 2 Akor. 2:7-10.’ (Kanyenye ngwathu.) Chotero, kudera nkhaŵa kofananaku kuyenera kusonyezedwa moyenerera lerolino ndi abusa a gulu. (Machitidwe 20:28; 1 Petro 5:2) Mabwenzi akale ndi achibale a munthuyo angayembekezere kuti wochotsedwayo akabwerera; komabe chifukwa cha ulemu kaamba ka lamulo la pa 1 Akorinto 5:11, iwo samayanjana ndi munthu wochotsedwa.b Iwo amasiyira abusa oikidwa kukhala oyamba kuwona ngati munthu woteroyo ngokondweretsedwa kubwerera.
11, 12. Kodi ndi ochotsedwa otani amene ngakhale akulu sangaŵafikire, koma kodi ndi ati amene angaŵachezere?
11 Sikukakhala koyenera ngakhale kwa akulu kukhala oyamba kufikira ochotsedwa ena, monga ngati ampatuko, omwe ‘amalankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira aŵatsate.’ Iwo ndiwo ‘aphunzitsi onama . . . amene adzaloŵa nayo m’tseri mipatuko yotaikitsa ndipo m’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mawu onyenga.’ (Machitidwe 20:30; 2 Petro 2:1, 3) Baibulo silimaperekanso maziko alionse ofunira anthu ochotsedwa omwe ngandewu kapena amene amalimbikitsa mokangalika kuchita zoipa.—2 Atesalonika 2:3; 1 Timoteo 4:1; 2 Yohane 9-11; Yuda 4, 11.
12 Komabe, anthu ambiri ochotsedwa sali otero. Munthu wina angakhale analeka kale kuchita cholakwa chomwe anachotsedwera. Ndipo wina angakhale ankagwiritsira ntchito fodya, kapena ankamwa mopambanitsa, koma iye tsopano sakuyesayesa kutsogolera ena nkuchita zoipa. Kumbukirani kuti ngakhale Aisrayeli okhala muukapolowo asanabwerere kwa Mulungu, iye anatumiza oimira kukaŵafulumiza kubwerera. Kaya Paulo kapena akulu a mpingo wa Korinto anakhala oyamba kufikira munthu wochotsedwayo, Baibulo silinena kalikonse. Pamene munthuyo analapa naleka chisembwere chake, Paulo analangiza mpingowo kumbwezeretsa iye.
13, 14. (a) Kodi nchiyani chomwe chikusonyeza kuti ochotsedwa ena angavomereze makonzedwe akufikiridwa kwachifundo? (b) Kodi bungwe la akulu lingapange motani makonzedwe a kumfikira?
13 M’nthaŵi zaposachedwapa pakhala zochitika pamene mkulu anakumana ndi munthu wochotsedwa.c Pamene kunali koyenera, mbusayo anafotokoza mwachidule masitepe oyenera kutengedwa kaamba ka kubwezeretsedwa. Ena a anthu onga ameneŵa analapa ndipo anabwezeretsedwa. Zotulukapo zosangalatsa zoterozo zimasonyeza kuti pangakhale anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa omwe angavomereze kufikira kwachifundo kopangidwa ndi abusa. Koma kodi akuluwo angasamalire motani nkhani yotereyi? Pafupifupi kamodzi pachaka, bungwe la akulu liyenera kulingalira ngati pali anthu oterowo omwe akukhala m’gawo lawo.d Akuluwo akasumika chidwi pa awo amene akhala ochotsedwa kwa nyengo yoposa pa chaka chimodzi. Mogwirizana ndi mikhalidweyo, ngati nkoyenerera, iwo akagaŵira akulu aŵiri (makamaka awo ozoloŵerana ndi mkhalidwewo) kukachezera munthuyo. Sadzachezera munthu aliyense amene akupereka umboni wosuliza, wa mkhalidwe wowopsa kapena amene adziŵitsiratu kuti sakufuna thandizo.—Aroma 16:17, 18; 1 Timoteo 1:20; 2 Timoteo 2:16-18.
14 Abusa aŵiriwo angatumize telefoni kufunsa zakupanga ulendo wokacheza wachidule, kapena angapiteko panthaŵi yoyenera. M’kuchezetsako, safunikira kukhala aukali kapena osamasuka koma ayenera kusonyeza mwachisangalalo kudera nkhaŵa kwachifundo. Mmalo mobwereramo mu nkhani yakale, iwo angakambitsirane malemba a Baibulo onga ngati Yesaya 1:18 ndi 55:6, 7 ndi Yakobo 5:20. Ngati munthuyo akufunadi kubwerera ku gulu la Mulungu, iwo angalongosole mwachifundo masitepe amene ayenera kutenga, monga ngati kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsidwa za Watch Tower Society ndikupezeka pamisonkhano ku Nyumba Yaufumu.
15. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukumbukiridwa ndi akulu opita kukachezera munthu wochotsedwayo?
15 Akulu ameneŵa akafunikira nzeru ndi kuzindikira kuti atsimikize kaya ngati pali chisonyezero cha kutembenuka mtima ndiponso kaya ngati akafunikira kubwererako. Komabe, iwo ayenera kukumbukira kuti anthu ena ochotsedwa sangakhoze ‘kukonzedwanso kuti atembenuke mtima.’ (Ahebri 6:4-6; 2 Petro 2:20-22) Pambuyo pakuchezetsako, aŵiriwo akapereka lipoti lachidule lapakamwa ku Komiti Yampingo ya Utumiki. Kenaka, iwo akadziŵitsa bungwe la akulu pa kukumana kwawo kotsatira. Kudziyambira kwachifundo kwa akuluwo kukasonyeza lingaliro la Mulungu ili: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.”—Malaki 3:7.
Thandizo Lina Lachifundo
16, 17. Kodi tiyenera kuwawona motani achibale Achikristu a munthu wochotsedwa?
16 Kodi bwanji ponena za ife amene sindife oyang’anira ndipo sitidzakhala oyamba kulankhula ndi anthu ochotsedwawo? Kodi tingachitenji chomwe chidzakhala chogwirizana ndi makonzedwe ameneŵa ndi kutsanzira Yehova?
17 Malinga ngati munthu ngochotsedwa kapena wodzilekanitsa, tifunikira kutsatira malangizo aŵa: ‘Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.’ (1 Akorinto 5:11) Koma chilangizo Chabaibulo chimenechi sichiyenera kuyambukira kawonedwe kathu ka ziŵalo za banja Lachikristu zomwe zimakhala ndi munthu wochotsedwayo. Ayuda akale anachita mwamphamvu ndi amisonkho kotero kuti chidani chawo chinayambukira ngakhale banja la wamsonkhoyo. Yesu sanayambitse zimenezo. Iye ananena kuti wochimwa amene akana thandizo anayenera kuwonedwa “monga wakunja ndi wamsonkho”; iye sananene kuti ziŵalo zabanja Lachikristu limenelo zinayenera kuchitiridwa mofananamo.—Mateyu 18:17.
18, 19. Kodi ndinjira zina ziti zimene tingasonyezere Chikristu chathu kwa achibale okhulupirika a munthu wochotsedwa?
18 Tiyenera kuchilikiza mwapadera ziŵalo zabanja zomwe ziri Akristu okhulupirika. Iwo angakhale akuyang’anizana kale ndi kupweteka ndi zopinga chifukwa chakukhala panyumba ndi munthu wochotsedwa yemwe angamalefule zolondola zawo zauzimu. Iye angakonde kuti Akristu asamacheze kunyumba kwake; kapena ngati abwera kudzawona ziŵalo zabanja zokhulupirika, sangakhale ndi ulemu wakuchoka pakati pa alendowo. Iye angamatsekerezenso zoyesayesa zabanjalo za kupita kumisonkhano yonse Yachikristu. (Yerekezerani ndi Mateyu 23:13.) Chotero Akristu opanda mwawi oterowo amafunikiradi chifundo chathu.—2 Akorinto 1:3, 4.
19 Njira ina imene tingasonyezere chifundo chokoma mtima ndiyo ‘kulankhula motonthoza’ ndikukhala ndi makambitsirano olimbikitsa ndi okhulupirika oterowo okhala m’banjalo. (1 Atesalonika 5:14, NW) Palinso mwaŵi wabwino wakupereka chilikizo misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake, pamene tiri muutumiki wakumunda, kapena pamene tiri pamodzi nthaŵi zina. Sitifunikira kutchula za kuchotsedwa koma tingakambitsirane zinthu zambiri zomangirira. (Miyambo 25:11; Akolose 1:2-4) Pamene kuli kwakuti akulu adzapitiriza kuŵeta Akristu okhala m’banjalo, tingapeze kuti nafenso tingakhoze kuwachezera popanda kukambitsirana ndi munthu wochotsedwayo. Ngati munthu wochotsedwayo ayankha pamene tapita kukacheza kapena tatumiza telefoni, tingangofunsa za wachibale Wachikristu amene tikufunayo. Nthaŵi zina ziŵalo zabanja Zachikristu zingakhale zokhoza kuvomereza chiitano chakubwera kunyumba kwathu kudzacheza. Mfundo njakuti: Iwo—aang’ono ndi akulu omwe—ndi atumiki anzathu, ziŵalo zokondeka za mpingo wa Mulungu, zosayenera kupatulidwa.—Salmo 10:14.
20, 21. Kodi tiyenera kulingalira ndikuchita motani ngati munthu wina wabwezeretsedwa?
20 Mbali ina yosonyezera chifundo imatseguka pamene wochotsedwayo abwezeretsedwa. Fanizo la Yesu limagogomezera chimwemwe chimene chimakhala kumwamba pamene ‘wochimwa mmodzi atembenuka mtima.’ (Luka 15:7, 10) Paulo analembera Akorinto motere ponena za munthu yemwe adachotsedwa: ‘Mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chochulukacho. Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.’ (2 Akorinto 2:7, 8) Tiyeni tigwiritsire ntchito uphungu umenewo modzichepetsa ndiponso mwachikondi m’masiku ndi milungu yotsatirapo pambuyo pa kubwezeretsedwa kwa munthuyo.
21 Fanizo la Yesu la mwana woloŵerera limasonyeza ngozi imene tiyenera kuipeŵa. Mbale wamkuluyo sanasangalale ndi kubwerera kwa woloŵererayo koma anaipidwa. Lolani kuti tisakhale ngati iye, kusunga chidani chifukwa cha zolakwa zakale kapena kuipidwa ndi kubwezeretsedwa kwa munthuyo. Mmalomwake, chonulirapo chathu chiyenera kukhala ngati tateyo, yemwe anachitira fanizo chivomerezo cha Yehova. Tateyo anali wachimwemwe kuti mwana wake, yemwe anataika nakhala monga wakufa, anapezeka, kapena kukhalanso wamoyo. (Luka 15:25-32) Mofananamo, tidzalankhula momasuka kwa mbale wobwezeretsedwayo ndi kumlimbikitsa m’njira zina. Inde, tiyenera kuchimveketsa kuti tikusonyeza chifundo, monga mmene amachitira Atate wathu wakumwamba wokhululuka ndi wachifundo.—Mateyu 5:7.
22. Kodi nchiyani chomwe chikuloŵetsedwamo m’kutsanzira kwathu Yehova Mulungu?
22 Palibe chikaikiro chirichonse kuti ngati tikufuna kutsanzira Mulungu wathu, tiyenera kusonyeza chifundo mogwirizana ndi malamulo ake ndi chiweruzo cholungama. Wamasalmo anamfotokoza bwino motere: ‘Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.’ (Salmo 145:8, 9) Ha, nchitsanzo chachikondi chotani nanga choti Akristu achitsanzire!
[Mawu a M’munsi]
a “Amisonkho ankanyozedwa makamaka ndi anthu Achiyuda a ku Palestina kaamba ka zifukwa zingapo izi: (1) iwo ankasonkhanitsira ndalama ulamuliro wachilendo womwe unatenga dziko la Israyeli, chotero ankapereka chilikizo losakhala lachindunji kwa achiŵembuwa; (2) anali odziŵika kukhala osawona mtima, ankakhala ndi chuma mwakudyerera anthu awo; ndipo (3) ntchito yawo inaloŵetsamo kuyanjana mokhazikika ndi Amitundu, kuwapangitsa kukhala odetsedwa mwamwambo. Kuipidwa ndi amisonkho kukupezeka ponse paŵiri m’C[hipangano] C[hatsopano] ndi mabuku a arabi . . . Mogwirizana ndi kunena kwa omalizirawo, chidani chinayenera kufutukulidwira ngakhale ku banja la wamsonkhoyo.”—The International Standard Bible Encyclopedia.
b Ngati m’banja Lachikristu muli wachibale wochotsedwa, iye akakhalabe ndi phande m’zochitika zanthaŵi zonse zatsiku ndi tsiku zabanjalo. Ichi chikaphatikizapo kupezekapo pamene zinthu zauzimu zikukambitsiridwa pabanjapo.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, masamba 19-20.
c Onani 1991 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 53-4.
d Ngati Mboni iriyonse, pamene ikulalikira kunyumba ndi nyumba kapena mwanjira ina, yadziŵa kuti munthu wochotsedwa akukhala m’gawolo, iyenera kupereka chidziŵitso choterocho kwa akulu.
Kodi Munamvetsetsa Mfundo Izi?
◻ Kodi Ayuda ankaŵachitira motani amisonkho ndi ochimwa, koma kodi nchifukwa ninji Yesu anayanjana ndi ena oterowo?
◻ Kodi ndi maziko Amalemba otani omwe alipo kaamba ka kukhala woyamba kusonyeza chifundo kwa otaika ambiri?
◻ Kodi mabungwe a akulu angakhale bwanji oyamba kutero, ndipo kulinga kwa yani?
◻ Kodi tiyenera kusonyeza motani chifundo kwa anthu obwezeretsedwa ndi mabanja a anthu ochotsedwa?
[Bokosi patsamba 23]
Aliyense yemwe anali mbali ya mpingo woyera ndi wachimwemwe wa Mulungu koma tsopano ngwochotsedwa kapena wodzilekanitsa safunikira kukhalabe mumkhalidwe umenewo. Mmalomwake, iye angatembenuke mtima nkukhala woyamba kukambitsirana ndi akulu a mumpingomo. Njira yobwererera idakali yotseguka.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Garo Nalbandian