-
‘Kondanani Wina ndi Mnzake’Nsanja ya Olonda—2003 | February 1
-
-
6 Fanizo lachiŵiri limanena za mkazi. Yesu anati: “Mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo mmene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”—Luka 15:8-10.
-
-
‘Kondanani Wina ndi Mnzake’Nsanja ya Olonda—2003 | February 1
-
-
Yotayika Komabe Yofunika
8. (a) Kodi mbusa ndi mkazi anachita bwanji zinthu zawo zitatayika? (b) Kodi zimene anachita zikutiuza chiyani za mmene ankaonera chinthu chotayikacho?
8 M’mafanizo aŵiriwa zinthu zinatayika, koma taonani mmene eni ake zinthuzo anachitira. Mbusayo sananene kuti: ‘Nkhosa imodzi ndi ya ntchito yanji popeza ndikadali nazo nkhosa 99? Ndi yosafunika nkhosayo.’ Ndipo mkaziyo sananene kuti: ‘N’kuvutikiranji chifukwa cha ndalama imodzi? Ndalama nayini zomwe ndili nazo n’zondikwanira.’ M’malo mwake, mbusa anafunafuna nkhosa yake yotayika ngati kuti anali ndi nkhosa imodzi yokhayo. Ndipo mkazi anakhudzidwa kwambiri ndi kutayika kwa ndalama yakeyo ngati kuti analibe ndalama zina. Pa zochitika ziŵirizi zinthu zotayikazo zinali za mtengo wapatali kwa eni ake. Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?
-
-
‘Kondanani Wina ndi Mnzake’Nsanja ya Olonda—2003 | February 1
-
-
9. Kodi nkhaŵa imene mbusa ndi mkaziyo anali nayo ikusonyeza chiyani?
9 Taonani mawu omaliza a Yesu m’mafanizo aŵiriwa. Iye anati: “Kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima,” ndiponso “chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.” Chotero, nkhaŵa imene mbusa ndi mkazi anali nayo ikusonyeza pang’ono chabe, nkhaŵa imene Yehova ndi zolengedwa zake zakumwamba amakhala nayo. Monga mmene zotayika zinakhalirabe zamtengo wapatali kwa mbusa ndi mkaziyo, anthunso amene apatuka ndipo sakugwirizana ndi anthu a Mulungu amakhalabe amtengo wapatali pamaso pa Yehova. (Yeremiya 31:3) Anthu otero angakhale ofooka mwauzimu, koma sikuti apanduka. Ngakhale kuti ndi ofooka, mwina angakhale akutsatirabe zimene Yehova amafuna. (Salmo 119:176; Machitidwe 15:29) Chotero, mofanana ndi m’nthaŵi zakale, Yehova safulumira ‘kuwatayiratu pankhope pake.’—2 Mafumu 13:23.
10, 11. (a) Kodi tifunika kuwaona bwanji amene apatuka kuchoka mu mpingo? (b) Kodi tingawasonyeze bwanji kuti timawadera nkhaŵa, malinga ndi mafanizo aŵiri a Yesu?
10 Mofanana ndi Yehova ndiponso Yesu, ifenso timadera nkhaŵa kwambiri amene ali ofooka ndipo sakupezeka pampingo wachikristu. (Ezekieli 34:16; Luka 19:10) Timaona munthu wofooka monga nkhosa yotayika osati yosatheka kubwerera. Sitimanena kuti: ‘Nkuderanji nkhaŵa za munthu wofooka? Mpingo ukuyenda bwino kwambiri popanda iye.’ M’malo mwake, mofanana ndi Yehova , timaona anthu amene apatuka koma akufuna kubwerera kukhala ofunika.
-