Achichepere Akufunsa Kuti
Kodi Ndingakonze Motani Moyo Wanga?
“SINDINATHE kuloŵa mkati,” anatero John. Iye anangoima kunja kwa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova. Akali wachichepere iye analeka Chikristu ndi kulondola moyo wa upandu, wa anamgoneka, ndi wachisembwere. Pambuyo pa zaka zambiri za moyo wotero, sanaiŵale za Baibulo, chotero anapita ku Nyumba Yaufumu—komano anachita mantha kwambiri kuti aloŵe. “Simukudziŵa bwino,” iye anatero kwa winawake amene anamlimbikitsa kuloŵa. “Ndachita machimo ambiri. Sindiganiza kuti pali njira iliyonse imene Yehova adzandikhululukira pa zimene ndachita.”
Achichepere osaŵerengeka amapandukira malamulo, chipembedzo, ndi makhalidwe a makolo awo. Kuli kochititsa kakasi ndi kwatsoka makamaka pamene achichepere oleredwa ndi makolo owopa Mulungu achita zimenezi. Ngakhale kuli kwakuti ambiri atenga njira imeneyo, m’kupita kwa nthaŵi, ena amayamba kukhala ndi chikumbumtima chowavuta cha mkhalidwe wa kupanda pake umene ngakhale moyo wosalamulirika sungauphimbe. (Miyambo 14:13) Achichepere ena, pokhala atasautsidwa ndi dziko loipali, amafuna kukonza miyoyo yawo ndi kubwerera ku choonadi cha Baibulo chimene anaphunzira pamene anali ana. Koma kodi nkothekadi kwa iwo kuchita motero?
Mwana Wopanduka Achoka Kwawo
Fanizo la Yesu la mwana woloŵerera, kapena womwaza, lopezeka pa Luka 15:11-32 limapereka chidziŵitso chambiri pankhaniyi. Cholembedwacho chimati: “Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri; ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigaŵirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagaŵira za moyo wake. Ndipo pakupita masiku oŵerengeka mwana wamng’onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake ku dziko lakutali.”
Ndithudi mnyamata ameneyu sanapanduke chifukwa chakuti atate ake anali aukali, ankhanza, kapena oletsa kwambiri! Malinga ndi Chilamulo cha Mose, mwana wamwamuna anali woyenerera kupatsidwa choloŵa chokwanira cha chuma cha atate ake, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri zimenezi zinafunikira kuchitidwa atate ake atamwalira. (Deuteronomo 21:15-17) Kunali kupimbidzala mtima chotani nanga kuti iye anapempha kupatsidwa choloŵa chake pasadakhale! Komabe, atate achikondiwo anavomera. (Yerekezerani ndi Genesis 25:5, 6.) Pamenepa, mwachionekere, mkhalidwe wamaganizo wa mnyamatayo—osati wa atate ake—unali wolakwika. Monga momwe katswiri wina Alfred Edersheim akunenera, iye mwina mwake anaipidwa ndi “dongosolo ndi chilango cha panyumba pawo” ndipo anali ndi “chikhumbo chadyera cha kumasuka ndi chisangalalo.”
Monga momwe nkhani yapitayo mu mpambo uno inavomerezera, si makolo onse amene ali okoma mtima ndi olingalira.a Komabe, pamene kholo lili laukali kapena losalingalira ena, kupanduka sindiko yankho lake; potsirizira pake kumakhala kudziwononga. Kachiŵirinso, lingalirani za fanizo la Yesu. Atamka kutali ndi kwawo, mnyamatayo “anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko. Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusoŵa.” Zimenezi sizinamchititse kuzindikira. Akali wodzidalira, “anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaŵeta nkhumba. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.”
Katswiri wina wa Baibulo Herbert Lockyer akuti: “Ayuda amene anali kumvetsera Yesu ayenera kukhala ataipidwa ndi mawu awa, ‘kudyetsa nkhumba,’ pakuti kwa Myuda, panalibenso kutsitsidwa kwina kwakukulu kuposa kumeneku.” Mofananamo lerolino, awo amene amasiya choonadi cha Baibulo kaŵirikaŵiri amaloŵa m’mavuto, kapena ngakhale m’mikhalidwe yochititsa manyazi. Msungwana wina Wachikristu amene anathaŵa panyumba akuulula motere: “Ndalama zanga zonse zinathera pa anamgoneka, ndipo ndinalibe ndalama yogulira zilizonse. Chotero ndinayamba kuba kanthu kalikonse m’masitolo kuti ndichirikize chizoloŵezi changacho.”
“Anakumbukira Mumtima”
Komabe, kodi ndimotani mmene mwana woloŵererayo anachitira ndi mikhalidwe ya iyemwini yovutayo? Yesu anati potsirizira pake iye “anakumbukira mumtima.” Mawu Achigiriki choyambirira amatanthauza, “nzeru zitabwereramo.” M’mawu ena, iye “sanali iyemwini” ndipo anali m’dziko la maloto, wochititsidwa khungu pa kuipa kwa mkhalidwe wake.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:24-26.
Mofananamo lerolino achichepere ena opanduka adzidzimutsidwa ndi mkhalidwe weniweniwo woipa. Kututa zotulukapo zoipa za moyo wachiwawa—ndende, kuvulala kwakukulu, matenda opatsirana mwakugonana—kungakhaledi chokumana nacho chovutitsa maganizo. Potsirizira pake mawu a pa Miyambo 1:32 amazindikiridwa mopweteka: “Kubwerera m’mbuyo kwa achibwana kudzawapha.”
Talingalirani za Elizabeth wachichepere, amene anathaŵa makolo ake nadziloŵetsa mu anamgoneka. “Ndinaiŵaliratu za Yehova,” iye akutero. Komabe, pamene anakayenda ku New York, anadzera pa malikulu a Mboni za Yehova. Chiyambukiro chake? “Ndinapwetekedwa m’maganizo ndi mumtima,” iye akukumbukira motero. “Ha, ndinachitanji ine? Kodi ndinaloleranji moyo wanga kuwonongeka mofulumira chotero?”
Potsirizira pake pamene mwana woloŵererayo anazindikira choonadi, anapanga chosankha molimba mtima—kumka kwawo ndi kukakonzanso moyo wake! Koma kodi ndimotani mmene atate ake anachitira pambuyo pa kupweteketsedwa mtima ndi kugwiritsidwa mwala ndi mwana wawoyo? Cholembedwacho chikuyankha kuti: “Koma pakudza iye kutali, atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.” Inde, mnyamatayo asananene mawu ake olinganizidwa bwino opempha chikhululukiro, atate ake anayambirira kusonyeza chikondi ndi chikhululukiro!
Kuwongolera Zinthu ndi Mulungu
Ngakhale zinali choncho, mwana woloŵererayo anati kwa atate ake: “Ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu.” Phunziro lake? Achichepere amene achoka m’njira za Mulungu sangathe kukonza miyoyo yawo kufikira ‘atawongolera zinthu’ ndi Mulungu mwini! (Yesaya 1:18, NW) Ndife oyamikira kuti Yehova amapangitsa kuyanjanitsidwa kotero kukhala kotheka. Ndithudi, atate wa m’fanizo la Yesu amaimira Yehova Mulungu. Ndipo Mulungu amasonyeza mkhalidwe umodzimodziwu wa kukhululukira mwa kuuza ochimwa kuti: “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.” (Malaki 3:7; yerekezerani ndi Salmo 103:13, 14.) Koma monga momwe analili Ayuda ochimwa m’nthaŵi za Baibulo, oterowo ayenera kupanga chosankha chotsimikiza chakuti: “Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.”—Maliro 3:40.
Zimenezi zikutanthauza kupenda mwamphamvu khalidwe lauchimo la munthuwe. Pamene wachichepere wochimwa achita zimenezi, ayenera kusonkhezeredwa kuulula machimo ake pamaso pa Yehova Mulungu. Wamasalmo anati: “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. . . . Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. . . . Ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”—Salmo 32:3-5.
Bwanji nanga ngati wachichepere waloŵa m’zolakwa zazikulu kwambiri—mwinamwake kutaya mimba, uchiwerewere, anamgoneka, kapena mchitidwe wina wa upandu? Zoonadi, woteroyo angamve kukhala wosayenerera chikhululukiro. John, wotchulidwa pachiyambiyo, anamva motero. Nchifukwa chake anangoima chiriri kunja kwa Nyumba Yaufumu kufikira mkulu wina wa mpingo wokoma mtima atamkumbutsa kuti Mfumu Manase wa Israyeli wakale nayenso anali ndi liwongo la machimo aakulu—kuphatikizapo mbanda! Komabe, Yehova anamkhululukira. (2 Mbiri 33:1-13) “Mkulu ameneyo anandipulumutsa,” akutero John. Podziŵa kuti chikhululukiro chinali chothekera, John anapeza nyonga ya kuloŵa m’Nyumba Yaufumu ndi kupempha thandizo.b
Achichepere ambiri a mumkhalidwe wotero mofananamo afunikira thandizo kuti akonze zinthu ndi Mulungu, ndipo akulu ampingo wakumaloko angathandize kwambiri pankhaniyi. Angamvetsere mwachifundo ndi moleza mtima pamene wachichepere ‘avomereza machimo ake.’ Angaperekenso chilango ndi thandizo labwino. Mwachitsanzo, iwo angalinganize kuti wachichepereyo akhale ndi winawake kuti ‘amphunzitse zoyamba za chiyambidwe’ za Mawu a Mulungu mwanjira ya phunziro la Baibulo la panyumba. Ndipo ngati wochimwayo ali ndi vuto la kupemphera, mkulu angampempherere. “Pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo,” Baibulo limatitsimikizira motero.—Yakobo 5:14-16; Ahebri 5:12.
Kulambulira Njira ya Mapazi Anu
Ndithudi, kukonza zinthu ndi Mulungu kwangokhala chiyambi. Monga momwedi mwana woloŵererayo anapepesera kwa atate ake, achichepere ochimwa ayenera kuyesayesa kupempha chikhululukiro kwa makolo awo. Kupepesa koona mtima kungathandize kwambiri pa kuchepetsa kupwetekedwa mtima kumene akhala nako ndi pa kupezanso chichirikizo chawo. Wachichepere wina wothaŵa kwawo amene anabwereranso ali ndi khanda lapathengo akukumbukira kuti: “Amayi ndi Atate anasonyeza chikondi chachikulu.”
Wachichepere amene akufuna kukondweretsa Mulungu afunikira ‘kulambulira misewu yolunjika yoyendamo mapazi ake.’ (Ahebri 12:13) Zimenezi zingatanthauze kusintha mkhalidwe wake wa moyo, zizoloŵezi, ndi mabwenzi. (Salmo 25:9; Miyambo 9:6) Kukhazikitsa ndandanda ya phunziro laumwini kulinso kofunika. Yemwe kale anali msungwana wopanduka akuti: “Ndimaŵerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo ndimaŵerenga nkhani zonse zotengedwa m’Baibulo zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndikuthokoza Mulungu kaamba ka kundipatsa mpata wina.”
John akusimba bwino nkhaniyo mwachidule, akumati: “Ndimakumbukira za nthaŵi imene ndawawanya kumbuyoku. Ndimaganiza za mmene zinthu zikanakhalira, komano palibe njira imene ndingafafanizire zimene zinachitika.” Mwamwaŵi, ife timalambira Mulungu wachifundo amene mwachikondi amapempha awo amene amamsiya kuti abwerere. Bwanji osavomera pempho lake?
[Mawu a M’munsi]
a Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kumvera Makolo Anga?”
b Ngati simunaleredwe monga Mkristu komabe mukuona kufunika kwa kusintha moyo wanu, kupita ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova ndiko chiyambi chabwino. Pemphani phunziro la Baibulo la panyumba laulere. Mwanjira imeneyi mungakhale ndi thandizo laumwini m’kukonza moyo wanu.
[Chithunzi patsamba 29]
Akristu okhwima maganizo angakuthandizeni kukonza moyo wanu