Kodi Ndinu Wokhulupirika M’zinthu Zonse?
“Amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.”—LUKA 16:10.
1. Kodi imodzi mwa njira zimene Yehova alili wokhulupirika ndi iti?
KODI munaona zimene umachita mthunzi wa mtengo dzuwa likamakwera? Umasintha kukula kwake ndiponso mbali. Zimene anthu amayesetsa kuchita ndiponso malonjezo awo, kawirikawiri zimakhala zosakhazikika ngati mthunzi. Mosiyana ndi anthu, Yehova Mulungu sasintha nthawi zonse. Pomutchula kuti “Atate wa mauniko,” wophunzira Yakobo anati: “Alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” (Yakobo 1:17) Yehova sasintha ndipo ndi wodalirika ngakhale pa zinthu zazing’ono kwambiri. Iye ndi “Mulungu wokhulupirika.”—Deuteronomo 32:4.
2. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudzipenda kuti tione ngati tili okhulupirika? (b) Kodi tikambirana mafunso ati okhudza kukhulupirika?
2 Kodi Mulungu amaona bwanji kudalirika kwa anthu om’pembedza? Amawaona monga mmene Davide anali kuwaonera. Iye anati: “Maso anga ayang’ana okhulupirika m’dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m’njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.” (Salmo 101:6) Inde, Yehova amakondwera ndi kukhulupirika kwa atumiki ake. M’pomveka kuti mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Chofunika kwa adindo n’chakuti munthu akhale wokhulupirika.’ (1 Akorinto 4:2) Kodi kukhala wokhulupirika kumaphatikizapo chiyani? Ndi mbali ziti pamoyo wathu zimene tiyenera kukhala okhulupirika? Kodi pali madalitso otani a ‘kuyenda mwangwiro’?
Kodi Kukhala Wokhulupirika N’kutani?
3. Kodi n’chiyani chimene chimasonyeza kuti ndife okhulupirika?
3 Monga mtumiki, Mose anali wokhulupirika, limatero Baibulo pa Ahebri 3:5. N’chifukwa chiyani Mose anatchedwa wokhulupirika? Pomanga chihema, ‘Mose anachita monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.’ (Eksodo 40:16) Monga opembedza Yehova, timaonetsa kukhulupirika mwa kum’tumikira momvera. Zimenezi zikuphatikizapo kukhala wokhulupirika kwa Yehova tikakumana ndi mayesero ovuta ndiponso aakulu. Komabe, kupambana pa mayesero aakulu si umboni wokha wa kukhulupirika. Yesu anati: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Tiyenera kukhala okhulupirika ngakhale pa nkhani zimene zimaoneka zazing’ono.
4, 5. Kodi tikakhala okhulupirika “m’chaching’onong’ono,” timasonyeza chiyani?
4 Kukhala omvera tsiku lililonse “m’chaching’onong’ono” n’kofunika pa zifukwa ziwiri. Choyamba, kumasonyeza mmene timaonera ulamuliro wa Yehova. Taganizirani mayeso a kukhulupira amene anthu awiri oyambirira aja, Adamu ndi Hava, anapatsidwa. Lamulo limene anapatsidwa silinali lovuta kulisunga. Iwo anali ndi ufulu wakudya chakudya chilichonse m’munda wa Edene, koma anafunika kupewa kudya zipatso za mtengo umodzi wokha basi, “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:16, 17) Akanamvera mokhulupirika lamulo laling’onolo, anthu awiri oyambirirawo akanasonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Kutsatira malangizo a Yehova pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, kumasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova.
5 Chachiwiri, khalidwe lathu pa ‘chaching’onong’ono’ limasonyeza zimene tingachite pa ‘chachikulu,’ pankhani zazikulu m’moyo. Pamfundoyi, taganizirani zimene zinachitikira Danieli ndi Ahebri anzake atatu okhulupirika, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. Iwo anagwidwa ukapolo kupita ku Babulo mu 617 B.C.E. adakali aang’ono, mwina a zaka zosakwana 20. Anyamata anayiwa anawatengera ku nyumba yachifumu ya Mfumu Nebukadinezara. Kumeneko, ‘anawaikira gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pake aimirire pamaso pa mfumu.’—Danieli 1:3-5.
6. Kodi ndi mayesero otani amene Danieli ndi anzake achihebri atatu anakumana nawo kunyumba yachifumu ya ku Babulo?
6 Koma kunali kovuta kwa anyamata anayi achihebri aja kudya chakudya cha mfumu ya ku Babulo. Kawirikawiri pachakudya cha mfumucho pankakhala zakudya zoletsedwa ndi Chilamulo cha Mose. (Deuteronomo 14:3-20) Mwina nyama yake inkakhala yosazinga bwinobwino, ndipo kudya nyama yotero kukanakhala kulakwira Chilamulo cha Mulungu. (Deuteronomo 12:23-25) Mwinanso chakudyacho ankayamba achipereka nsembe kwa mafano, pakuti umenewo ndiwo unali mwambo wachipembedzo wa Ababulo pachakudya chimene anthu ambiri anali kudyera limodzi.
7. Kodi kumvera kwa Danieli ndi anzake atatu aja kunasonyezanji?
7 Kupewa zakudya zina, siinali nkhani yaikulu kwa anthu okhala kunyumba ya mfumu ku Babulo. Komabe, Danieli ndi anzake aja, anali otsimikiza mtima kusadziipitsa ndi chakudya choletsedwa m’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisrayeli. Nkhaniyi inakhudza kudalirika ndi kukhulupirika kwawo kwa Mulungu. Chotero, iwo anapempha kuti aziwapatsa zamasamba ndi madzi, ndipo anawalola. (Danieli 1:9-14) Anthu ena masiku ano angaone kuti zimene anyamata anayiwa anachita zinali zazing’ono. Komabe mwa kumvera Mulungu, iwo anasonyeza mmene anali kuonera ulamuliro wa Yehova.
8. (a) Ndi mayesero aakulu ati a kukhulupirika amene Ahebri atatu aja anakumana nawo? (b) Kodi zotsatira za mayeserowo zinali zotani, ndipo zimenezi zikusonyeza chiyani?
8 Kukhala okhulupirika pankhani imene mwina inaoneka yaing’ono, kunathandiza anzake a Danieli atatuwo kupambana pa mayesero aakulu. Tatsegulani Baibulo lanu pa chaputala 3 cha buku la Danieli, mudziwerengere nokha mmene Ahebri atatu amenewa analili okonzeka kufa m’malo molambira fano lagolidi limene Mfumu Nebukadinezara inaimika. Atawatengera kwa mfumu, iwo molimba mtima ananena maganizo awo kuti: “Taonani, Mulungu wathu amene tim’tumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira fano lagolidi mudaliimikalo.” (Danieli 3:17, 18) Kodi Yehova anawapulumutsa? Alonda amene anaponya anyamatawo m’ng’anjo yamotoyo anapserera ndi motowo, koma Ahebri atatu okhulupirikawo anatulukamo amoyo, sanatenthedwe n’komwe ndi moto wa m’ng’anjoyo. Chizolowezi chawo cha kukhulupirika chinawathandiza kukhala okhulupirika pamayesero aakulu amenewa. Kodi nkhaniyi sikusonyeza kufunika kwa kukhulupirika pa zinthu zazing’ono?
Kukhala Okhulupirika pa “Chuma Chosalungama”
9. Kodi Yesu anali kunena za chiyani pamene ananena mawu opezeka pa Luka 16:10?
9 Asananene mfundo yakuti wokhulupirika m’chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu, Yesu analangiza anthu amene anali kumumvetsera kuti: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.” Kenako ananena za kukhulupirika m’chaching’ono. Ndiyeno anati: “Chifukwa chake ngati simunakhala okhulupirika m’chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? . . . Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.”—Luka 16:9-13.
10. Kodi tingasonyeze bwanji kukhulupirika pogwiritsa ntchito ‘chuma chathu chosalungama’?
10 Malinga ndi nkhani yake, mfundo ya Yesu pa Luka 16:10, ikunena za kugwiritsa ntchito “chuma chosalungama,” kutanthauza chuma kapena katundu wathu. Chuma chimenechi chikutchedwa chosalungama chifukwa chakuti chumachi, makamaka ndalama, chimayendetsedwa ndi anthu ochimwa. Komanso, chilakolako chofuna chuma chingapangitse munthu kuchita zinthu zosalungama. Timasonyeza kuti ndife okhulupirika mwa kugwiritsa ntchito zinthu zathu mwanzeru. M’malo mogwiritsa ntchito chuma chathu modzikonda, tiyenera kuchigwiritsa ntchito kupititsira patsogolo ntchito za Ufumu ndiponso kuthandizira osowa. Pokhala okhulupirika mwa njira imeneyi, timapanga ubwenzi ndi Yehova Mulungu ndiponso Yesu Kristu, eni ake a “mahema osatha.” Adzatilandira m’malo amenewa, mwa kutipatsa moyo wosatha kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi pano.
11. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulephera kuuza eni nyumba kuti angathe kupereka ndalama zothandizira ntchito ya Mboni za Yehova imene ikuchitika padziko lonse?
11 Taganiziraninso mwayi umene timapatsa anthu amene timawapatsa mabaibulo kapena mabuku ofotokoza Baibulo polalikira uthenga wa Ufumu. Timawafotokozera kuti akhoza kupereka ndalama zothandizira ntchito ya anthu a Yehova imene ikuchitika padziko lonse. Tikamatero, kodi sitiwapatsa mwayi wakuti agwiritse ntchito chuma chawo mwanzeru? Ngakhale kuti kwenikweni nkhani ya pa Luka 16:10 imanena za kugwiritsa ntchito chuma, mfundo imene ili pamenepo imagwiranso ntchito m’mbali zina pamoyo.
Kuona Mtima N’kofunikadi
12, 13. Kodi ndi pa zochitika ziti pamene tingasonyeze kuona mtima?
12 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino [kapena kuti, kuona mtima].” (Ahebri 13:18) Mawu akuti “zonse” akunena nkhani zonse zokhudza ndalama. Timapereka ngongole zathu ndiponso misonkho mofulumira ndi moona mtima. Chifukwa chiyani? Timachita zimenezo chifukwa cha chikumbumtima chathu, ndipo makamakanso chifukwa chokonda Mulungu ndi kumvera malangizo ake. (Aroma 13:5, 6) Kodi timatani tikapeza chinthu chomwe si chathu? Timayesetsa kuchipereka kwa mwini wake. Zimenezitu zimatipatsa mpata wochitira umboni wabwino kwambiri tikamafotokoza chifukwa chake tikupereka chinthucho kwa mwini wake.
13 Kukhala wokhulupirika ndi woona mtima m’zinthu zonse kumaphatikizapo kukhala woona mtima pantchito. Kuona mtima pantchito kumapangitsa ena kuganizira za Mulungu amene timamuimira. ‘Sitiba’ nthawi mwa kukhala aulesi. Koma timagwira ntchito mwakhama ngati kuti ntchitoyo tikugwirira Yehova. (Aefeso 4:28; Akolose 3:23) M’dziko lina ku Ulaya, akuti pafupifupi wantchito mmodzi mwa atatu aliwonse amakatenga mwachinyengo chilolezo kwa dokotala chotsanzikira kuntchito kuti akudwala. Atumiki enieni a Mulungu sapeka tizifukwa tojombera kuntchito. Nthawi zina mabwana amaganizira zokweza pantchito Mboni za Yehova chifukwa cha kuona mtima ndi kukhulupirika kwawo.—Miyambo 10:4.
Kukhulupirika mu Utumiki Wathu Wachikristu
14, 15. Kodi zina mwa njira zimene tingasonyezere kukhulupirika mu utumiki wachikristu ndi ziti?
14 Kodi timasonyeza motani kukhulupirika mu utumiki umene taikizidwa? Baibulo limati: “Tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Njira yofunika kwambiri imene tingasonyezere kukhulupirika mu utumiki ndiyo kuchita utumikiwo nthawi zonse. Kodi tingalolerenji mwezi kutha osachitira umboni za Yehova ndi chifuniro chake? Kulalikira nthawi zonse kumatithandizanso ifeyo kupititsa patsogolo luso lathu ndi kukhala alaliki ogwira mtima.
15 Tingasonyezenso kukhulupirika mu utumiki wakumunda mwa kugwiritsa ntchito malangizo amene amapezeka mu Nsanja ya Olonda ndi mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kodi utumiki wathu sukhala wopindulitsa tikaukonzekera ndi kugwiritsa ntchito maulaliki amene timapatsidwa ndiponso maulaliki ena othandiza? Tikapeza munthu wachidwi ndi uthenga wa Ufumu, kodi timabwererako mwamsanga kukakulitsa chidwicho? Nanga bwanji za maphunziro a Baibulo a panyumba amene timayambitsa ndi anthu achidwi? Kodi ndife odalirika ndi okhulupirika pochititsa maphunzirowo? Kukhala wokhulupirika mu utumiki kungadzatipezetse moyo ifeyo ndiponso anthu amene amatimvetsera.—1 Timoteo 4:15, 16.
Kukhala Osiyana ndi Dziko
16, 17. Kodi tingasonyeze kuti ndife osiyana ndi dziko m’njira ziti?
16 Popemphera kwa Mulungu, Yesu ananena za otsatira ake kuti: “Ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:14-16) Tingakhale otsimikiza mtima kukhala osiyana ndi dziko pankhani zikuluzikulu monga kusalowerera m’zandale, maholide ndi miyambo ya zipembedzo, ndiponso chiwerewere. Koma bwanji pa nkhani zing’onozing’ono? Kodi zingatheke kutengera njira za dziko mosazindikira? Mwachitsanzo, ngati sitisamala, kavalidwe kathu kakhoza kukhala kosadzilemekeza ndi kosayenera. Kukhala wokhulupirika kumaphatikizapo kuvala ndi kudzikongoletsa “mwaulemu ndi modzichepetsa.” (1 Timoteo 2:9, 10, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Inde, “osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.”—2 Akorinto 6:3, 4.
17 Pofuna kulemekeza Yehova, timavala modzilemekeza popita kumisonkhano ya mpingo. Tiyeneranso kutero pa misonkhano yadera ndi yachigawo. Tiyenera kuvala zovala zoyenera ndi zooneka bwino. Zimenezi zimapereka umboni kwa anthu amene amationa. Ngakhale angelo amaona zochita zathu, pajatu ankaonanso zochita za Paulo ndi Akristu anzake. (1 Akorinto 4:9) Choncho, tiyenera kuvala moyenera nthawi zonse. Ena angaone kuti kukhulupirika pa kavalidwe ndi nkhani yaing’ono, komatu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu.
Madalitso a Kukhulupirika
18, 19. Kodi kukhala wokhulupirika kumabweretsa madalitso otani?
18 Akristu oona amatchedwa “adindo okoma a chisomo chamitundumitundu cha Mulungu.” Motero, amadalira ‘mphamvu imene Mulungu amapereka.’ (1 Petro 4:10, 11) Kuwonjezera apo, monga adindo, taikizidwa zinthu zimene si zathu. Zinthuzo ndi njira zimene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwake, kuphatikizapo utumiki wathu. Potsimikizira kuti ndife adindo abwino, timadalira mphamvu imene Mulungu amapereka, mphamvu yoposa yachibadwa. (2 Akorinto 4:7) Kusamalira udindo wathuwu kumatiphunzitsa kukonzekera mayesero aliwonse amene tingakumane nawo m’tsogolo.
19 Wamasalmo anaimba kuti: “Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake: Yehova asunga okhulupirika.” (Salmo 31:23) Tiyeni titsimikize mtima kukhala okhulupirika, tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova ali ‘Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirika.’—1 Timoteo 4:10.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ‘okhulupirika m’chaching’onong’ono’?
• Tingasonyeze bwanji kukhulupirika
pankhani ya kuona mtima?
mu utumiki?
pokhala osiyana ndi dziko?
[Zithunzi patsamba 26]
Wokhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu
[Chithunzi patsamba 29]
‘Chitani zonse moona mtima’
[Chithunzi patsamba 29]
Njira yabwino yosonyezera kukhulupirika ndiyo kukonzekera bwino utumiki wakumunda
[Chithunzi patsamba 30]
Valani ndi kudzikongoletsa mwaulemu