“Ndithandizeni M’mene Ndisoŵa Chikhulupiriro!”
“Atate wa mwanayo ananena kuti: ‘Ndiri nacho chikhulupiriro! Ndithandizeni m’mene ndiso ŵa chikhulupiriro!’”—MARKO 9:24, NW.
1. Kodi nchiyani chimene chinapangitsa tate wina kufuula kuti, “Ndithandizeni m’mene ndisoŵa chikhulupiriro”?
ATATE wa mnyamata wogwidwa ndi chiŵanda adaimirira pamaso pa Yesu Kristu. Ha, analakalaka motani nanga mwamunayo kuti mwana wake achiritsidwe! Ophunzira a Yesu anasoŵa chikhulupiriro chokwanira chotulutsira chiŵandacho, koma tateyo anafuula kuti: “Ndiri nacho chikhulupiriro! Ndithandizeni m’mene ndisoŵa chikhulupiriro!” Mwamphamvu yopatsidwa ndi Mulungu, Yesu pamenepo anachitulutsa chiŵandacho, zimene mosakaikira zinalimbitsa chikhulupiriro cha tate wa mnyamatayo.—Marko 9:14-29, NW.
2. Kodi Akristu samachita manyazi ndi chikhulupiriro mwa njira ziŵiri ziti?
2 Mofanana ndi chikhulupiriro cha atate wa mnyamatayo, mtumiki wokhulupirira wa Yehova samachita manyazi kunena kuti: “Ndiri nacho chikhulupiriro!” Otonza angatsutse kukhalapo kwa mphamvu ya Mulungu, kuwona kwa Mawu ake, ndipo ngakhale kukhalapo kwake kwenikweniko. Koma Akristu owona amavomereza mosavuta kuti iwo ali nacho chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu. Komabe, polankhula mwamseri m’pemphero kwa Atate wawo wakumwamba, anthu amodzimodziŵa angachonderere kuti: “Ndithandizeni m’mene ndisoŵa chikhulupiriro!” Iwo amachita chimenechi popanda manyazi, podziŵa kuti ngakhale atumwi a Yesu Kristu anapempha kuti: ‘Mutiwonjezere chikhulupiriro.’—Luka 17:5.
3. Kodi chofunika nchiyani ponena za mmene Yohane anagwiritsirira ntchito liwu lakuti ‘chikhulupiriro’ mu Uthenga wake Wabwino, ndipo nchifukwa ninji chimenechi chinali choyenerera?
3 Makamaka Malemba Achikristu Achigiriki amanena zambiri pa chikhulupiriro. Kwenikweni, Uthenga Wabwino wa Yohane umagwiritsira ntchito mawu Achigiriki osiyanasiyana ofanana ndi liwu lakuti “chikhulupiriro” koposa pa 40 peresenti mobwerezabwereza kuposa mmene amachitira Mauthenga Abwino atatu enawo ataphatikizidwa pamodzi. Yohane anagogomezera kuti kukhala ndi chikhulupiriro sikokwanira; kuchisonyeza kuli kofunika. Pamene analikulemba, pafupifupi 98 C.E., iye anawona mzimu wakupha wa mpatuko ukuloŵerera kufuna kufooketsa Akristu m’chikhulupiriro. (Machitidwe 20:28-30; 2 Petro 2:1-3; 1 Yohane 2:18, 19) Chotero kunali kofunika kusonyeza chikhulupiriro, kupereka umboni wake mwa machitidwe a kudzipereka kwaumulungu. Nthaŵi zovuta zidali patsogolo.
4. Kodi nchifukwa ninji palibe chosatheka kwa awo okhala ndi chikhulupiriro?
4 Chikhulupiriro chimawatheketsa Akristu kulaka zovuta zirizonse. Yesu anauza ophunzira ake kuti ngati akhala nacho ‘chikhulupiriro monga kambewu kampiru,’ palibe chimene sichikatheka kwa iwo. (Mateyu 17:20) Mwanjirayo, iye anagogomezera mphamvu ya chikhulupiriro, chipatso cha mzimu woyera. Motero Yesu anagogomezera, osati chimene anthu angakhoze kuchita, koma chimene mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, ingakhoze kuchita. Amene amatsogozedwa nawo samakulitsa mavuto aang’ono. Kugwiritsira nzeru imene mzimu wa Mulungu umapereka kumaŵathandiza kukhala ndi lingaliro loyenera la zinthu. Ngakhale mavuto aakulu amachepa pamene aikidwa pansi pa mphamvu yochirikiza ya chikhulupiriro.—Mateyu 21:21, 22; Marko 11:22-24; Luka 17:5, 6.
Kupempherera Kuti Chikhulupiriro Chisalephere
5-7. (a) Kodi ndimawu achenjezo otani onena za chikhulupiriro amene Yesu analankhula pamene anakhazikitsa Chikumbutso? (b) Kodi chikhulupiriro chake Petro chinamtheketsa motani kulimbitsa abale ake?
5 Mu 33 C.E., Yesu anachita phwando la Paskha ndi ophunzira ake kwa nthaŵi yomalizira. Ndiyeno, atachotsapo Yudasi Iskariote, anakhazikitsa phwando la Chikumbutso, akumati: “Ndikupanga pangano la ufumu ndi [amuna] inu, monga momwe Atate anapangira pangano la ufumu ndi ine . . . Simoni, Simoni, tawona! Satana anafunsa kukutenga kuti akupete ngati tirigu. Koma ndakupempherera kuti chikhulupiriro chako chisazime; ndipo iweyo, pamene ubwerera, limbitsa abale ako.”—Luka 22:28-32, NW.
6 Yesu anapemphera kuti chikhulupiriro cha Simoni Petro chisazime. Ngakhale kuti chifukwa chodzidalira mopambanitsa Petro anadzitama kuti sakamkana konse Yesu, pasanapite nthaŵi yaitali iye anamkana katatu konse. (Luka 22:33, 34, 54-62) Kwenikwenidi, chifukwa cha kukanthidwa ndi imfa kwa Mbusa konenedweratu, nkhosa zinabalalika. (Zekariya 13:7; Marko 14:27) Komabe, pamene Petro anachira mwakuuka mumsampha wa mantha umene anagweramo, analimbitsa abale ake auzimu. Iye anabweretsa nkhani ya kufuna munthu woloŵa m’malo Yudasi Isikariote. Pokhala wolankhulira wa atumwi pa Pentekoste wa 33 C.E., Petro anagwiritsira ntchito yoyamba ya “mafungulo” amene Yesu adampatsa, kutsegulira njira Ayuda kuti akhale ziŵalo za Ufumuwo. (Mateyu 16:19; Machitidwe 1:15–2:41) Satana anafuna atumwiwo kotero kuti awapete ngati tirigu, koma Mulungu anawathandiza kuti chikhulupiriro chawo chisalephere.
7 Tangoyerekezerani mmene Petro analingalirira pamene anamva Yesu akunena kuti: “Ndakupempherera kuti chikhulupiriro chako chisazime.” Taganizirani! Ambuye wake ndi Mtsogoleri adapemphera kuti chikhulupiriro cha Petro chisalephere. Ndipo sichinalephere, kapena kuzima. Kwenikwenidi, patsiku la Pentekoste, Petro ndi ena anakhala anthu oyamba kudzozedwa ndi mzimu woyera ndikukhala ana auzimu a Mulungu, oloŵa nyumba pamodzi ndi Kristu oyembekezeredwa muulemerero wakumwamba. Pokhala ndi mzimu woyera ukugwira ntchito pa iwo mokulira kuposa ndi kalelonse, iwo anakhoza kusonyeza zipatso zake, kuphatikizapo chikhulupiriro, kuposa ndi kalelonse. Ha, linali yankho lodabwitsa chotani nanga la kuchonderera kwawo kwakuti: ‘Mutiwonjezere chikhulupiriro’!—Luka 17:5; Agalatiya 3:2, 22-26; 5:22, 23.
Kuyang’anizana ndi Ziyeso Zakutsogolo ndi Chikhulupiriro
8. Kodi ndichenjezo lapanthaŵi yake lotani limene gulu latipatsa ponena za kukwaniritsidwa kwa 1 Atesalonika 5:3?
8 Kukwaniritsa ulosi wa Baibulo, posachedwapa tidzamva mfuu yakuti “Mtendere ndi chisungiko!” (1 Atesalonika 5:3, NW) Kodi chimenechi chingaike chikhulupiriro chathu pachiyeso? Inde, popeza kuti tikhoza kutengeka mosadziŵa ndi chipambano chowonekera chimene mitundu ingakhale nacho chakubweretsa mtendere. Koma sitidzagaŵanako malingaliro a olengeza mtendere oterowo ngati tikumbukira kuti Yehova Mulungu sakugwiritsira ntchito lirilonse la mabungwe a dziko lino kuti akwaniritse cholinga chimenecho. Iye ali ndi njira yakeyake yobweretsera mtendere weniweni, ndipo njira yokhayo ndiyo mwa Ufumu wake pansi pa Yesu Kristu. Chifukwa chake, mosasamala kanthu za chipambano chirichonse chimene mitundu ingakhale nacho m’kukhazikitsa mtendere, uwo udzakhala wakanthaŵi ndipo wachiphamaso. Kuti atithandize kukhala maso m’nkhani imeneyi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” adzapitirizabe kufalitsa machenjezo apanthaŵi yake kotero kuti atumiki a Yehova sadzatengeka mosadziŵa ndi chilengezo chachinyengo chikudzacho cha “Mtendere ndi chisungiko” choperekedwa ndi mitundu ya dongosolo la zinthu lakale lino.—Mateyu 24:45-47.
9. Kodi nchifukwa ninji kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzatifunikiritsa kukhala olimba mtima ndi chikhulupiriro?
9 Mfuu yakuti “Mtendere ndi chisungiko!” idzakhala chizindikiro cha “chiwonongeko chadzidzidzi” chomwe chidzagwera Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chibvumbulutso 17:1-6; 18:4, 5) Ichinso chidzayesa chikhulupiriro Chachikristu. Pamene chipembedzo chonyenga chidzagwa, kodi Mboni za Yehova zidzachirimika m’chikhulupiriro? Ndithudi zidzatero. Chochitika chimenechi—chosayembekezeredwa ndi chodabwitsa kwa anthu ambiri—sichidzachitidwa ndi munthu. Anthu ayenera kudziŵa kuti icho chiridi chiweruzo cha Yehova, cholemekezera dzina limene chipembedzo chonyenga chalitonza kwa nthaŵi yaitali. Koma kodi anthu adzadziŵa motani popanda wina kuwauza? Ndipo kodi ndani pambali pa Mboni za Yehova amene angayembekezeredwe kuwauza zimenezo?—Yerekezerani ndi Ezekieli 35:14, 15; Aroma 10:13-15.
10. Kodi ndimotani mmene kuukira kwa Gogi pa anthu a Yehova kudzakhaliranso chiyeso cha chikhulupiriro?
10 Mboni zodzozedwa za Yehova ndi atsamwali awo okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi akhala ndi kulimbika mtima kofunikira kwa kuuza ena ponena za chiweruzo cha Yehova choyandikiracho motsutsana ndi Babulo Wamkulu ndi dongosolo la zinthu lonse la Satana. (2 Akorinto 4:4) M’malo ake monga Gogi wa Magogi, kutanthauza malo otsitsidwa omwe iye alipo, Satana adzasonkhanitsa magulu ake apadziko lapansi kupanga kuukira kotheratu pa anthu a Mulungu. Chikhulupiriro m’mphamvu zaumulungu zotetezera Mboni za Yehova chidzaikidwa pachiyeso. Koma tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti monga momwe Mawu a Mulungu ananeneratu, Yehova adzapulumutsa anthu ake.—Ezekieli 38:16; 39:18-23.
11, 12. (a) Kodi nchiyani chimene chinatsimikiziritsa chipulumutso cha Nowa ndi banja lake mkati mwa Chigumula? (b) Kodi sitiyenera kudera nkhaŵa ponena za chiyani mkati mwa chisautso chachikulu?
11 Lerolino, sitikudziŵa kwenikweni mmene Yehova adzatetezerera anthu ake mkati mwa ‘chisautso chachikulu,’ koma chimenechi sichifukwa chokaikirira kuti kaya iye adzatero. (Mateyu 24:21, 22) Mkhalidwe wa atumiki a Mulungu a lerolino udzafanana ndi wa Nowa ndi banja lake mkati mwa Chigumula. Otsekeredwa m’chingalawa ndi madzi osefukira a chiwonongeko akuwazinga, mwachiwonekere anagwidwa ndi mantha kaamba ka chisonyezero chimenechi cha mphamvu yaumulungu ndipo ayenera kuti anapemphera ndi mtima wonse. Palibe chisonyezero cha Malemba chakuti iwo anadera nkhaŵa ndikudzifunsa kuti: ‘Kodi chingalawachi ncholimbadi moti sichidzawonongeka ndi mphamvu ya chigumula? Kodi tiri nacho chakudya chokwanira kutifikitsa ku mapeto a Chigumula? Kodi tidzakhala okhoza kuchita ndi mikhalidwe yosintha ya padziko lapansi pambuyo pake?’ Zochitika zotsatirapo zinatsimikizira kuti nkhaŵa zoterozo zikadakhala zopanda pake.
12 Kuti atsimikizire chipulumutso chawo, Nowa ndi banja lake anafunikira kusonyeza chikhulupiriro. Ichi chinatanthauza kutsatira malangizo ndi zitsogozo za mzimu woyera wa Mulungu. Mkati mwa chisautso chachikulu, kudzakhala kofunika mofananamo kwa ife kutsatira zitsogozo za mzimu woyera ndi kumvera malangizo a Yehova kupyolera m’gulu lake. Pamenepo sitidzakhala ndi chifukwa chodera nkhaŵa ndi kufunsa kuti: ‘Kodi zosoŵa zathu zauzimu ndi zakuthupi zidzakwaniritsidwa motani? Kodi padzakhala makonzedwe otani kaamba ka okalamba kapena awo ofunikira chisamaliro chapadera chamankhwala? Kodi Yehova adzatitheketsa motani kupulumuka kuloŵa m’dziko latsopano?’ Pokhala ndi chikhulupiriro cholimba, atumiki okhulupirika onse a Yehova adzasiya zonse m’manja ake okhoza zonse.—Yerekezerani ndi Mateyu 6:25-33.
13. Pamene chisautso chachikulu chiyamba, kodi nchifukwa ninji tidzafunikira chikhulupiriro chonga cha Abrahamu?
13 Chisautso chachikulu chitayamba, mosakaikira chikhulupiriro chathu mwa Mulungu chidzalimbitsidwa mokulira. Ndiiko komwe, tidzawona kuti Yehova akuchita zimene ananena kuti adzachita. Tidzawona ndi maso athu pamene adzakhala akupereka chiweruzo chake! Koma kodi ife mwaumwini tidzakhala nacho chikhulupiriro chokwanira chakukhulupirira kuti pamene adzakhala akuwononga oipa, Mulungu adzapulumutsa anthu ake? Kodi tidzakhala ngati Abrahamu, yemwe anali ndi chikhulupiriro chakuti ‘Woweruza wa dziko lonse lapansi adzachita zoyenera,’ kusawononga olungama pamodzi ndi oipa?—Genesis 18:23, 25.
14. Kodi ndimafunso otani amene ayenera kutipangitsa kupenda chikhulupiriro chathu ndi kugwira ntchito mwamphamvu kuchilimbitsa?
14 Ha, kuli kofunika motani nanga kuti tsopano tikulitse chikhulupiriro chathu! Popeza kuti mapeto a dongosolo la zinthu loipali ayandikira kwenikweni, tiyeni tilole mzimu wa Mulungu kutisonkhezera ku “machitidwe oyera a mayendedwe ndi ntchito za kudzipereka kwaumulungu.” (2 Petro 3:11-14, NW) Pamenepo sitidzavutitsidwa m’nthaŵi ya chisautso chachikulu ndi malingaliro onga aŵa: ‘Kodi ndine woyenerera kulandira chitetezero cha Yehova? Kodi ndinayenera kuchita zowonjezereka muutumiki wake? Kodi ndinagwiradi ntchito mokwanira kuvala “umunthu watsopano”? Kodi ndine mtundu wa munthu amene Yehova amafuna m’dziko latsopano?’ Mafunso osamalitsa otereŵa ayenera kutipangitsa kupenda chikhulupiriro chathu ndi kugwira ntchito zolimba kuchilimbitsa tsopano lino!—Akolose 3:8-10, NW.
Chikhulupiriro Chotichiritsa
15. Kodi nchiyani chimene Yesu nthaŵi zina anauza aja omwe anawachiritsa, koma kodi nchifukwa ninji chimenechi sichimachirikiza kuchiritsa kwa chikhulupiriro kwamakono?
15 Yesu sanachiritse anthu okhala ndi chikhulupiriro okha. (Yohane 5:5-9, 13) Chotero zochita zake sizimachirikiza konse chiphunzitso chopanda malemba cha kuchiritsa kwa chikhulupiriro. Nzowona, Yesu nthaŵi zina anauza ochiritsidwawo kuti: ‘Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.’ (Mateyu 9:22; Marko 5:34; 10:52; Luka 8:48; 17:19; 18:42) Koma mwakunena zimenezi, iye anali kungosonyeza chowonadi chowonekeratu chakuti: Ngati odwalawo analibe chikhulupiriro m’mphamvu ya Yesu yakuchiritsa, iwo sakanabwera nkubwera komwe kwa iye kuti awachiritse.
16. Kodi ndiprogramu yakuchiritsa yotani imene Yesu akuitsogoza lerolino?
16 Lerolino, Yesu Kristu akutsogoza programu ya kuchiritsa kwauzimu, ndipo anthu oposa 4,000,000 adziika pamzera wakupindula nayo. Monga Mboni za Yehova, iwo akusangalala ndi thanzi lauzimu mosasamala kanthu za mavuto alionse athupi amene angakhale nawo. Akristu odzozedwa pakati pawo ali ndi chiyembekezo chakumwamba, ndipo ‘apenyerera zinthu zosatha zosawoneka.’ (2 Akorinto 4:16-18; 5:6, 7) Ndipo Akristu okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi amayang’ana kutsogolo ku machitidwe ozizwitsa akuchiritsa omwe adzachitika m’dziko latsopano la Mulungu.
17, 18. Kodi ndimakonzedwe a Yehova otani amene akulongosoledwa pa Chibvumbulutso 22:1, 2, ndipo kodi chikhulupiriro nchofunika motani kwa ife kuti tipindule nawo?
17 Mtumwi Yohane anasonya ku makonzedwe a Mulungu a moyo wamuyaya m’mawu awa opezeka pa Chibvumbulutso 22:1, 2: ‘Anandiwonetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.’ “Madzi a moyo” amenewo amaphatikizapo Mawu a Mulungu a chowonadi ndi makonzedwe ena onse a Yehova ochiritsira anthu omvera ku uchimo ndi imfa ndi kuwapatsa moyo wamuyaya pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu. (Aefeso 5:26; 1 Yohane 2:1, 2) Pamene adakali pa dziko lapansi, otsatira a Yesu odzozedwa a 144,000 amamwa madzi a makonzedwe a moyo a Mulungu kupyolera mwa Kristu ndipo amatchedwa ‘mitengo ya chilungamo.’ (Yesaya 61:1-3; Chibvumbulutso 14:1-5) Iwo abala zipatso zauzimu zochuluka pa dziko lapansi. Pamene adzaukitsidwira kumwamba, mkati mwa Ulamuliro wa Kristu Wazaka Chikwi, adzakhala ndi phande lakugaŵira makonzedwe adipo omwe adzakhala ‘ochiritsa amitundu’ ku uchimo ndi imfa.
18 Ngati chikhulupiriro chathu ncholimba m’makonzedwe a Mulungu ameneŵa, tidzakhala ndi kufunitsitsa kwakukulu kwa kutsatira zitsogozo za mzimu wake wa kugaŵanamo. Mwachiwonekere ungwiro wakuthupi udzabwera pamene munthu asonyeza chikhulupiriro mwa Kristu ndi kupanga kupita patsogolo kwauzimu. Ngakhale kuti munthu adzakhala atachiritsidwa mavuto aakulu akuthupi mozizwitsa, iye adzakhala akuyandikira ungwiro pamene achita zolungama. Iye nthaŵi zonse adzakhala akumwa m’makonzedwe a Mulungu akuchiritsa kupyolera m’nsembe ya Kristu. Chotero chikhulupiriro chidzasonkhezera kuchiritsidwa kwathu ndi kukhalitsidwa angwiro mwakuthupi.
‘Kupulumutsidwa Mwa Chikhulupiriro’
19. Kodi chofunika nchiyani kuti tikhalebe olimba m’chikhulupiriro?
19 Kufikira pamene mbandakucha wa dziko latsopano la Mulungu uchotseratu kosatha mdima wa dziko loipa liripoli, kuli kofunika motani nanga kuti atumiki a Yehova achirimikebe m’chikhulupiriro! Anthu ‘opanda chikhulupiriro’ adzaponyedwa ‘m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure,’ imfa yachiŵiri. Potsirizira penipeni, izi zidzachitika pambuyo pa chiyeso chomalizira pamapeto a Ulamuliro wa Kristu Wazaka Chikwi. (Chibvumbulutso 20:6-10; 21:8) Chidzakhala chotulukapo chodalitsika chotani nanga kwa awo opitiriza kusonyeza chikhulupiriro ndi kupulumuka kukasangalala ndi mtsogolo mosatha!
20. Kodi ndimotani mmene 1 Akorinto 13:13 adzakhalira ndi tanthauzo lapadera kumapeto kwa Ulamuliro wa Kristu Wazaka Chikwi?
20 Pamenepo mawu aŵa a Paulo pa 1 Akorinto 13:13 adzakhala ndi thanthauzo lapadera: ‘Zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.’ Sitidzafunikiranso kusonyeza chikhulupiriro chakuti lonjezo laulosi la pa Genesis 3:15 lidzakhala lenileni kapena kuyembekezera kuti lidzakwaniritsidwa. Izo zidzakhala zitachitika. Monga osunga umphumphu, tidzapitirizabe kuyembekezera mwa Yehova, kukhala ndi chikhulupiriro mwa iye ndi Mwana wake, ndi kuwakonda monga amene anachititsa kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu. Kuwonjezerapo, chikondi chakuya ndi chiyamikiro cha mtima wonse kaamba ka chipulumutso chathu zidzatimangirira kwa Mulungu m’kudzipereka kosakhoza kusweka ku umuyaya wonse.—1 Petro 1:8, 9.
21. Kodi ife lerolino tiyenera kuchitanji kuti ‘tipulumutsidwe mwa chikhulupiriro’?
21 Kupyolera m’gulu lake lowoneka, Yehova wapanga makonzedwe ozizwitsa olimbitsira chikhulupiriro. Utengeni mwaŵi wakuwagwiritsira ntchito onse mokwanira. Pezekani mokhazikika ndi kukhala ndi phande pamisonkhano ya anthu a Mulungu. (Ahebri 10:24, 25) Phunzirani mwakhama Mawu ake ndi zofalitsidwa Zachikristu. Mpempheni Yehova mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Tsanzirani chikhulupiriro cha amene amatsogolera modzichepetsa mumpingo. (Ahebri 13:7) Kanizani ziyeso zakudziko. (Mateyu 6:9, 13) Inde, ndipo zamitsani unansi wanu waumwini ndi Yehova mwanjira iriyonse yotheka. Choposa zonse, pitirizani kusonyeza chikhulupiriro. Pamenepo mukhoza kukhala pakati pa amene amakondweretsa Yehova ndi kukhala panjira yomka ku chipulumutso, popeza kuti Paulo anati: ‘Muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chiri mphatso ya Mulungu.’—Aefeso 2:8.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi ndiziyeso za chikhulupiriro zotani zimene ziri kutsogolo kwathu?
◻ Kodi ndimwanjira ziŵiri zotani zimene chikhulupiriro chathu chingatichiritsire?
◻ Malinga ndi 1 Petro 1:9, kodi tiyenera kusunga chikhulupiriro chathu kwautali wotani?
◻ Kodi ndimakonzedwe otani amene tiri nawo olimbitsira chikhulupiriro chathu?
[Chithunzi patsamba 15]
Mofanana ndi atate wa mwana amene Yesu anachiritsa, kodi mumadzimva kukhala wofunikira chikhulupiriro chowonjezereka?
[Chithunzi patsamba 17]
Chikhulupiriro chonga cha Nowa ndi banja lake chidzakhala chofunika kuti tipulumuke ‘chisauto chachikulu’