Mutu 13
Boma la Mulungu la Mtendere
1. Kodi nchiyani chimene maboma aanthu alephera kuchita?
KODI MWAWONA kuti maboma aanthu, ngakhale awo okhala ndi zolinga zabwino, alephera kukwaniritsa zosowa zenizeni za anthu? Palibe lirilonse limene lathetsa mavuto a upandu ndi kudana kwa mafuko kapena lagawira chakudya choyenera ndi nyumba anthu awo onse. Iwo sanachotsere nthenda kotheratu nzika zawo. Ngakhale boma liri lonse silinakhale lokhoza kuletsa kukalamba kapena imfa kapena kubwezeretsa akufa ku moyo kachiwiri. Palibe limodzi limenedi ladzetsa mtendere ndi chisungiko zosatha kwa nzika zake. Maboma aanthu ngosakhoza konse kuthetsa mavuto aakulu oyang’anizana ndi anthu.
2. Kodi nchiyani chimene chiri uthenga waukulu wa Baibulo?
2 Mlengi wathu amadziwa mmene tikufunikirira kwambiri boma lolungama limene lidzatheketsa anthu onse kukhala ndi moyo wokwanira ndi wosangalatsa. Motero ndicho chifukwa chake Baibulo limasimba boma lotsogozedwa ndi Mulungu. Kunena zowona, boma lolonjezedwa ndi Mulungu limeneli ndilo uthenga waukulu wa Baibulo.
3. Kodi Yesaya 9:6, 7amanenanji ponena za boma la Mulungu?
3 Koma mungafunse kuti: ‘Kodi Baibulo limatchula pati boma la Mulungu?’ Limatero, mwa chitsanzo, pa Yesaya 9:6, 7. Malinga ndi kunena kwa King James Version, mavesi amenewa amati: “Pakuti kwa ife mwana wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa: ndipo boma lidzakhala pa phewa lake: ndipo dzina lake lidzatchedwa Wodabwitsa, Phungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Sipadzakhala mapeto a kuwonjezeka kwa boma lake ndi mtendere.”
4. Kodi ndani amene ali mwana amene akukhala wolamulira wa boma la Mulungu?
4 Panopo Baibulo likusimba kubadwa kwa mwana, kalonga. M’kupita kwa nthawi ‘mwana wamwamuna wa mfumu’ ameneyu anayenera kukhala wolamulira wamkulu, “Karonga wa Mtendere.” Iye akakhala ndi ulamuliro wa boma lodabwitsa kwenikweni. Boma limeneli lidzadzetsa mtendere kudziko lonse lapansi, ndipo mtenderewo udzakhala kosatha. Mwanayo, amene kubadwa kwake kunanenedweratu m’Yesaya 9:6, 7, anali Yesu. Polengeza kubadwa kwake kwa namwali wosadziwa mwamunayo Maliya, mngelo Gabriyeli anati ponena za Yesu: “Adzalamulira monga mfumu . . . ndipo sipadzakhala mapeto a ufumu wake.”—Luka 1:30-33, NW.
KUGOGOMEZERA KUFUNIKA KWA UFUMUWO
5. (a) Kodi ndimotani mmene kufunika kwa Ufumu kukusonyezedwera m’Baibulo? (b) Kodi ufumu wa Mulungu nchiyani, ndipo kodi udzachitanji?
5 Pamene iwo anali padziko lapansi, ntchito yaikulu ya Yesu Kristu ndi omchirikiza inali kulalikira ndi kuphunzitsa ponena za ufumu wa Mulungu ulinkudza. (Luka 4:43; 8:1) Iwo akutchula ufumu umenewo kokwanira 140 m’Baibulo. Yesu anaphunzitsadi omtsatira kupempha kwa Mulungu kuti: “Ufumu wan udze. Chifuniro chanu chichitidwe m’dziko lapansi, monga momwe chachitidwira kumwamba.” (Mateyu 6:10, King James Version) Kodi ufumu umenewu umene Akristu amapempha ndiwodi boma? Mungakhale musanauganizire motero, koma ndiwo. Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ali Mfumu ya Ufumuwo. Ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala malo pa amene iye akulamulira. Kudzakhala bwino kwambiri chotani nanga pamene anthu onse adzagwirizana mu mtendere pansi pa boma Laufumu wa Mulungu!
6. Pamene Yesu anali padziko lapansi, kodi nchifukwa ninji Ufumuwo unanenedwa kukhala uli “pafupi” ndi “mkati mwa inu”?
6 Yohane Mbatizi anayamba kulalikira boma limeneli, akuuza anthu kuti: “Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 3:1, 2) Kodi nchifukwa ninji Yohane adanena zimenezi? Chifukwa chakuti Yesu, Uyo amene akakhala wolamulira wa boma lakumwamba la Mulungu, anali pafupi kubatizidwa ndi iye ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Motero mungazindikire chifukwa chake Yesu pambuyo pake anauza Afarisi kuti: “Tawonani, Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.” (Luka 17:21) Chinali chifukwa chakuti Yesu, amene Mulungu adamuika kukhala mfumu, anali pamenepo limodzi nawo. Mkati mwa zaka zake zitatu ndi theka za kulalikira ndi kuphunzitsa, Yesu, mwa kukhulupirika kwake kwa Mulungu kufikira imfa, anatsimikizira kuyenera kwake kwa kukhala mfumu.
7. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Ufumuwo unali nkhani yofunika pamene Yesu anali padziko lapansi?
7 Kuti tisonyeze kuti ufumu wa Mulungu unali nkhani yofunika mkati mwa uminisitala wa Kristu, tiyeni tilingalire zimene zinachitika pa tsiku lotsiriza imfa yake isanakhale. Baibulo limatiuza kuti anthu ananeneza Yesu, kuti: “Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisala, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Kristu mfumu.” Atamva zimenezi, kazembe Wachiromayo Pontiyo Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?”—Luka 23:1-3.
8. (a) Kodi Yesu anayankha motani pamene iye anafunsidwa ngati iye anali mfumu? (b) Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti ufumu wake sunali “wochokera konkuno”?
8 Yesu sanayankhe funso la Pilato molunjika, koma anati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” Yesu anayankha motere chifukwa chakuti ufumu wake sunati ukakhale wapadziko lapansi. Iye anayenera kulamulira ali kumwamba, osati monga munthu ali pampando wina wachifumu padziko lapansi. Popeza kuti nkhani inali yakuti kaya Yesu anali ndi kuyenera kwa kulamulira monga mfumu kapena ayi, Pilato kachiwirinso anafunsa Yesu kuti: “Nanga kodi ndiwe mfumu?”
9. (a) Kodi ndichowonadi chodabwitsa chotani chimene Yesu anadziwikitsa? (b) Kodi mafunso akulu ndiotani lerolino?
9 Mwachiwonekere, Yesu anali pa mlandu wakuti aphedwe chifukwa chakuti analinkulalikira ndi kuphunzitsa boma latsopano. Motero Yesu anayankha Pilato kuti: “Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowondi.” (Yohane 18:36, 37) Inde, Yesu adathera moyo wake padziko lapansi akuuza anthu chowonadi chodabwitsa ponena za boma Laufumu la Mulungu. Chinali uthenga wake waukulu. Ndipo Ufumu udakali nkhani yofunika koposa lerolino. Komabe, mafunso ano, akutsalirabe: Kodi ndiboma liti limene liri lofunika koposa m’moyo wa munthu? Kodi ndilo boma lina la anthu, kapena kodi ndilo ufumu wa Mulungu wokhala ndi Kristu monga wolamulira?
KULINGANIZA BOMA LATSOPANO LA DZIKO LAPANSI
10. (a) Kodi ndiliti pamene Mulungu anawona kufunikira kwa boma latsopano? (b) M’Baibulo, kodi kutchulidwa koyamba kwa boma limeneli kunapangidwa pati? (c) Kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi chinjoka?
10 Kunali pamene Satana anachititsa Adamu ndi Hava kugwirizana naye m’chipanduko chake chakuti Yehova anawona kufunika kwa boma latsopano pa anthu. Motero nthawi yomweyo Mulungu anafotokoza chifuno chake cha kukhazikitsa boma loterolo. Iye anatchula boma limeneli pamene iye anapereka chiweruzo pa chinjoka, kwenikweni akumauza Satana Mdyerekezi kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Iyo idzakunzunzunda mutu ndipo iwe udzaizunzunda chitende.”—Genesis 3:14, 15, NW.
11. Kodi panayenera kukhala udani pakati pa yani?
11 Koma mungafunse kuti: ‘Kodi chirichonse ponena za boma chanenedwa kuti pano?’ Tiyeni tiyang’anitsitse pa mawu amenewa ndipo tidzawona. Lembalo likunena kuti kudzakhala chivuwa, kapena udani, pakati pa “mbewu” ya Satana, kapena ana, ndi “mbewu” ya mkazi, kapena ana. Choyambirira, tifunikira kudziwa amene “mkaziyo” ali.
12. Kodi nchiyani chimene chikunenedwa ponena za “mkaziyo” m’Chivumbulutso chaputala 12?
12 Iye simkazi wapadziko lapansi. Satana sanakhale ndi udani wapadera uliwonse ndi mkazi aliyense waumunthu. M’malo mwake, ameneyu ndimkazi wophiphiritsira. Ndiko kuti, iye akuphiphiritsira kanthu kena kake. Zimenezi zikusonyezedwa m’bukhu lotsirizira la Baibulo, Chivumbulutso, m’mene chidziwitso chowonjezereka chikuperekedwa ponena za iye. M’menemo “mkaziyo” akufotokozedwa kukhala “akukometseredwa ndi dzuwa, akuimirira pamwezi, ndipo ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri pa mutu pake.” Kuti atithandize kudziwa amene “mkazi” ameneyu amaphiphiritsira, wonani chimene Chivumbulutso chikupitiriza kunena ponena za mwana wake: “Mkaziyo analowetsa m’dziko mwana wamwamuna, mwana wamwamuna amene anayenera kulamulira mitundu yonse ndi ndodo yachifumu yachitsulo, ndipo mwanayo anatengeredwa mwachindunji kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.”—Chivumbulutso 12:1-5, The Jerusalem Bible.
13. Kodi “mwana wamwamunayo” ndi “mkaziyo” amaphiphiritsira yani kapena chiyani?
13 Kudziwa amene kapena chimene “mwana wamwamunayo” ali kudzatithandiza kuzindikira amene kapena chimene “mkaziyo” amaphiphiritsira. Mwanayo sali munthu weniweni, monga momwedi mkaziyo saliri mkazi waumunthu weniweni. Lembalo likusonyeza kuti “mwana wamwamuna” ameneyu ayenera “kulamulira mitundu yonse.” Motero “mwanayo” amaphiphiritsira boma la Mulungu lokhala ndi Yesu Kristu wolamulira monga Mfumu. “Mkaziyo,” chifukwa cha chimenecho, amaphiphiritsira gulu la Mulungu la zolengedwa zakumwamba zokhulupirika. Monga momwedi kuliri kuti “mwana wamwamunayo” anatuluka kuchokera mwa “mkazi,” momwemonso Mfumuyo, Yesu Kristu, anachokera m’gulu lakumwamba, khamu la zolengedwa zauzimu zokhulupirika kumwamba limene limagwira ntchito limodzi kuchita chifuno cha Mulungu. Agalatiya 4:26 amatcha gulu limeneli “Yerusalemu wakumwamba.” Motero, pamenepa, pamene Adamu ndi Hava choyamba anapandukira ulamuliro wa Mulungu, Yehova anapanga makonzedwe a boma Laufumu limene likatumikira monga chiyembekezo kwa okonda chilungamo.
YEHOVA AMAKUMBUKIRA LONJEZO LAKE
14. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera kuti anakumbukira lonjezo lake lonena za “mbewu” imene ikuzanzunda Satana? (b) Kodi “mbewu” yolonjezedwayo ndani?
14 Yehova sanaiwale lonjezo lake la kutumiza “mbewu” imene ikakhala wolamulira wa boma la Mulungu. Wolamulira ameneyu akapha Satana mwa kuphwanya mutu wake. (Aroma 16:20; Ahebri 2:14) Pambuyo pake, Yehova ananena kuti mbewu yolonjezedwayo ikadzera mwa munthu wokhulupirikayo Abrahamu. Yehova anauza Abrahamu kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:18) Kodi “mbewu” imeneyi ndani imene inalonjezedwa kudzera mumzera wa Abrahamu? Baibulo likupereka yankho pambuyo pake, kuti: “Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbewu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbewu yako, ndiye Kristu.” (Agalatiya 3:16) Yehova anauzanso mwana wamwamuna wa Abrahamu Isake ndi mdzukulu wake Yakobo kuti “mbewu” ya “mkazi” wa Mulungu ikadzera mumzera wawo wa mbadwa.—Genesis 26:1-5; 28:10-14.
15, 16. Kodi nchiyani chimene chimatsimikiziritsa kuti “mbewuyo” inayenera kukhala mfumu yolamulira?
15 Pomveketsa bwino lomwe kuti “mbewu” imeneyi ikakhala mfumu yolamulira, Yakobo ananena mawu awa kwa mwana wake wamwamuna Yuda, kuti: “Ndodo yachifumu [kapena, mphamvu yolamulira] siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Yesu Kristu anachokera m’fuko la Yuda. Iye anatsimikizira kukhala “Silo” ameneyu kwa amene “anthu adzamvera.”—Ahebri 7:14.
16 Pafupifupi zaka 700 pambuyo pa mawuwo kwa Yuda,. Yehova ponena za Davide wa fuko la Yuda anati: “Ndapeza Davide mtumiki wanga . . . Ndidzakhalitsanso mbewu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba.” (Salmo 89:20, 29) Pamene Mulungu akuti “mbewu” ya Davide idzakhazikitsidwa “chikhalire” ndi kuti “mpando wake wachifumu” udzakhalako ngati “masiku a m’mwamba,” “kodi akutanthauzanji? Yehova Mulungu akutanthauza chenicheni chakuti boma Laufumu lokhala m’manja mwa wolamulira wake woikidwa, Yesu Kristu, lidzakhala chikhalire. Kodi tikudziwa motani?
17. Kodi tikudziwa motani kuti wolamulira wolonjezedwayo ndiYesu Kristu?
17 Chabwino, kumbukirani zimene mngelo wa Yehova Gabriyeli anauza Maliya ponena za mwana amene anali pafupi kubadwa kwa iye. Iye anati: “Uyenera kumtcha dzina lake Yesu.” Koma Yesu sanati angokhalabe mwana, kapena ngakhale mwamuna, padziko lapansi. Gabriyeli anapitiriza kuti: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba; ndipo Yehova Mulungu adzampatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo iye adzalamulira monga mfumu pabanja la Yakobo kosatha, ndipo sipadzakhala mapeto a ufumu wake.” (Luka 1:31-33, NW) Kodi sikodabwitsadi kuti Yehova wapanga makonzedwe okhazikitsa boma lolungama kaamba ka phindu losatha la awo amene akumkonda ndi kumkhulupirira?
18. (a) Kodi Baibulo limafotokoza motani mapeto a maboma apadziko lapansi? (b) Kodi nchiyani chimene boma la Mulungu lidzachitira anthu?
18 Nthawi tsopano ikuyandikira pamene boma Laufumu la Mulungu lidzachitapo kanthu kuchotsa maboma onse a dziko. Pa nthawi imeneyo Yesu Kristu adzayamba kugwira ntchito monga Mfumu yolakika. Pofotokoza nkhondo imeneyi, Baibulo limati: “M’masiku a mafumu amemewo Mulungu wa kumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa konse . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu onsewa, ndipo uwo wokha udzakhala kosatha.” (Danieli 2:44, NW; Chivumbulitso 19:11-16) Maboma ena onse atachoka, boma la Mulungu lidzakwaniritsa zosowa zenizeni za anthu. Wolamulirayo, Yesu Kristu, adzatsimikizira kuti palibe nzika yake yokhulupirika ikudwala, kukalamba kapena kufa. Upandu, nyumba zoipa, njala ndi mavuto ena onse oterowo adzathetsedwa. Kudzafikira kukhala mtendere weniweni ndi chisungiko padziko lonse lapansi. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3-5) Komabe, tifunikira kuphunzira zambiri ponena za awo amene adzakhala olamulira m’boma Laufumu la Mulungu limeneli.
[Chithunzi pamasamba 112, 113]
Yesu anatuna omtsatira kukachita ntchito yofunika yolalikira za ufumu wa Mulungu
[Chithunzi patsamba 114]
Pamene anali pamlandu wakuti aphedwe, Yesu anapitiriza kulalikira ufumu wa Mulungu
[Chithunzi patsamba 119]
Kodi mumawona Yesu motani—monga mfumu yolakika kapena monga khanda losadzithandiza?