Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kufunika kwa Pemphero ndi Kudzichepetsa
POYAMBIRIRA, pamene iye anali m’Yudeya, Yesu ananena fanizo lonena za kufunika kwa kukhala wolimbikira m’pemphero. Tsopano, paulendo wake womalizira wopita ku Yerusalemu, iye akugogomezeranso kufunika kwa kusaleka m’kupemphera. Yesu mwinamwake adakali m’Samariya kapena Galileya pamene akuwuza ophunzira ake fanizo lowonjezereka iri:
“M’mudzi mwakuti munali woweruza wosawopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Ndipo m’mudzimo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane. Ndipo sanafuna nthaŵi; koma bwino bwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu; koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake.”
Yesu kenaka akupanga kugwira ntchito kwa nkhani yake, akumati: “Tamverani chonena woweruza wosalungama. Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima?”
Yesu sakutanthauza kuti Yehova Mulungu ali m’njira iriyonse wofanana ndi woweruza wosalungamayo. M’malomwake, ngakhale kuti woweruza wosalungama angayankhe ku kuchonderera kolimbikira, sipayenera kukhala kukaikira kuti Mulungu, yemwe ali ponse paŵiri wolungama ndi wabwino, adzayankha ngati anthu ake sakuleka kupemphera. Chotero Yesu akupitiriza kuti: “Ndinena ndi inu [Mulungu], adzawachitira chilungamo posachedwa.”
Chilungamo mobwerezabwereza chimamanidwa kwa odzichepetsa ndi osauka, pamene kuli kwakuti amphamvu ndi olemera kaŵirikaŵiri amachitiridwa mokomera. Mulungu, ngakhale kuli tero, sadzangowona ku icho kuti oipa alangidwa mwachilungamo komanso adzatsimikizira kuti atumiki ake achitiridwa mwachilungamo mwa kuwapatsa iwo moyo wosatha. Koma kodi ndi anthu angati omwe molimba mtima amakhulupirira kuti Mulungu adzachititsa chilungamo kuchitidwa posachedwa?
Akulozera makamaka ku chikhulupiriro chogwirizanitsidwa ku mphamvu ya pemphero, Yesu akufunsa kuti: “Koma Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?” Ngakhale kuti funsolo lasiyidwa losayankhidwa, tanthauzo lake lingakhale lakuti chikhulupiriro choterocho sichikakhala chofala pamene Kristu afika mu mphamvu ya Ufumu. Komabe, ife sitingamalize kuti icho sichikakhalako. Kodi inu mukuchichita icho?
Pakati pa awo omvetsera kwa Yesu pali ena ake omwe akudzimva odzitsimikizira kwenikweni m’chikhulupiriro chawo. Iwo amadzidalira iwo eni kuti ali olungama, ndipo amapeputsa ena. Amenewa angaphatikizepo ngakhale ena ake a ophunzira a Yesu. Chotero iye akulunjikitsa fanizo lotsatirali kwa oterowo:
“Anthu aŵiri anakwera kunka kukachisi kukapemphera; Winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; ndisala chakudya kaŵiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo.”
Afarisi akudziŵidwa kaamba ka zisonyezero zawo zapoyera za chilungamo kuti akondweretse ena. Masiku awo a nthaŵi zonse kaamba ka kusala kudya kodzipangira ali Lolemba ndi Lachinayi, ndipo mosamalitsa amapereka limodzi la magawo khumi la ngakhale zitsamba za m’munda zazing’ono. Miyezi yoŵerengeka poyambirira, kuipidwa kwawo ndi anthu wamba kunawonekera mkati mwa Phwando la Misasa pamene iwo anati: “Koma khamu iri losadziŵa Chilamulo [ndiko kuti, kumasulira kwa Chifarisi koperekedwa kwa icho] likakhala lotembereredwa.”
Akupitiriza fanizo lake, Yesu akunena za munthu “wotembereredwa” woteroyo kuti: “Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.” Chifukwa chakuti wamsonkhoyo wavomereza kuphophonya kwake modzichepetsa, Yesu akunena kuti: “Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ayi; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.”
Chotero Yesu akugogomezeranso kufunika kwa kukhala wodzichepetsa. Pokhala ataleredwa m’chitaganya chimene Afarisi odzilungamitsa ali a chisonkhezero koposa ndipo malo ndi ntchito zimagogomezeredwa nthaŵi zonse, nchosadabwitsa kuti ngakhale ophunzira a Yesu ayambukiridwa. Komabe, ndi maphunziro abwino chotani nanga m’kudzichepetsa amene Yesu akuphunzitsa! Luka 18:1-14; Yohane 7:49.
◆ Nchifukwa ninji woweruza wosalungama akuyankha pempho la mkazi wamasiyeyo, ndipo ndi phunziro lotani lomwe likuphunzitsidwa ndi fanizo la Yesu?
◆ Kodi ndi chikhulupiriro chotani chomwe Yesu adzafuna pamene afika?
◆ Ndi kwa ndani komwe Yesu akulunjikitsa fanizo lake lonena za Mfarisi ndi wamsonkho?
◆ Kodi ndi mkhalidwe wotani wa Afarisi womwe ufunikira kupeŵedwa?