Chipilala Chomwe Chimasonyeza Kuti Maulosi A M’baibulo Ndi Olondola
CHAPAKATIKATI PA MZINDA WA ROME KU ITALY KULI CHIPILALA CHOMWE CHIMAKOPA ALENDO OCHOKERA M’MADERA OSIYANASIYANA PADZIKO LONSE. CHIPILALACHI CHINAMANGIDWA POKUMBUKIRA WOLAMULIRA WINA WACHIROMA DZINA LAKE TITO.
Pachipilala cha Tito panajambulidwa mochita kugoba zithunzi ziwiri zosonyeza zochitika zikuluzikulu zomwe zinachitika kale. Anthu ambiri sadziwa kuti pali kugwirizana pakati pa chipilalachi ndi ulosi wina wa m’Baibulo: Chipilalachi chimapereka umboni wosonyeza kuti maulosi a m’Baibulo ndi olondola.
MZINDA WOMWE UNKAYENERA KUWONONGEDWA
Isanafike nthawi ya atumwi, ufumu wa Roma unakula kwambiri kukafika ku Britain komanso ku Gaul (komwe panopa ndi ku France) mpaka ku Egypt, ndipo anthu a m’chigawochi ankakhala mwabata ndi mtendere. Koma panali dera lina lakutali lomwe Aroma ankavutika nalo. Dera lake linali la Yudeya ndipo munkakonda kuchitika zachisokonezo.
Buku lina linati: “Panali madera ochepa omwe ankalamulidwa ndi ufumu wa Roma amene ankadedwa kwambiri ndipo limodzi mwa madera amenewa linali Yudeya. Ayuda ankadana kwambiri ndi Aroma chifukwa ankawalamulira mowapondereza. Komanso Aroma ankaona kuti Ayuda ndi anthu osamvera.” (Encyclopedia of Ancient Rome) Ayuda ambiri ankayembekezera kuti kudzabwera Mesiya yemwe adzawalanditse m’manja mwa Aroma n’kubwezeretsa ufumu wa Isiraeli. Koma m’chaka cha 33 C.E., Yesu ananena kuti mzinda wa Yerusalemu udzawonongedwa.
Yesu anati: “Masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira. Adaniwo adzakutsekereza ndi kukusautsa kuchokera kumbali zonse. Iwo adzakuwononga limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake mwa iwe.”—Luka 19:43, 44.
N’kutheka kuti mawu a Yesuwa anadabwitsa kwambiri ophunzira ake. Patadutsa masiku awiri, Yesu ndi ophunzira ake akuyang’ana kachisi wa ku Yerusalemu, wophunzira wina anati: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!” Zoonadi miyala ina yomwe anamangira kachisiyo inali yaikulu kuposa mamita 11 m’litali, mamita 5 m’lifupi ndiponso mamita atatu kupita m’mwamba. Yesu anayankha kuti: “Kunena za zinthu izi mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzakhala mwala wosiyidwa pano pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”—Maliko 13:1; Luka 21:6.
Yesu anapitiriza kuwafotokozera kuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Kodi zimene Yesu ananenazi zinachitikadi?
KUWONONGEDWA KWA MZINDA WA YERUSALEMU
Zaka 33 zinadutsa ndipo Ayuda anali adakali pansi pa ulamuliro wa Aroma. Ndiyeno m’chaka cha 66 C.E., bwanamkubwa wachiroma yemwe ankayang’anira Yudeya, dzina lake Gessius Florus, analanda ndalama za kukachisi. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri Ayuda. Pasanapite nthawi, zigawenga zachiyuda zinalowa mumzinda wa Yerusalemu n’kuyamba kupha asilikali achiroma ndipo zinalengeza kuti Ayuda achoka pansi pa ulamuliro wa Roma.
Patadutsa miyezi pafupifupi itatu, asilikali achiroma oposa 30,000, omwe ankatsogoleredwa ndi Seshasi Galasi anapita ku Yerusalemu kuti akalimbane ndi zigawenga zachiyuda zija. Asilikali achiroma analowa mumzindawo mpaka kukafika pampanda wakachisi n’kuyamba kuukumba. Koma pachifukwa chosadziwika bwino, asilikaliwo anabwerera. Zigawenga zachiyuda zija zitaona kuti asilikali achiroma akubwerera, zinasangalala ndipo zinayamba kuwathamangitsa. Popeza asilikali achiroma komanso zigawenga zachiyuda anali atachoka mumzindamo, Akhristu anali ndi mpata womvera chenjezo limene Yesu anapereka loti athawire kumapiri omwe anali kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano.—Mateyu 24:15, 16.
M’chaka chotsatira, gulu la nkhondo la Roma linabweranso ku Yudeya ndipo pa nthawiyi linkatsogoleredwa ndi Vasipashani ndi mwana wake Tito. Koma Mfumu Nero itangomwalira mu 68 C.E., Vasipashani anabwerera ku Roma kuti akakhale mfumu. Iye anasiya udindo wake wotsogolera asilikali pafupifupi 60,000 m’manja mwa mwana wake Tito.
Mu June 70 C.E., Tito analamula asilikali ake kuti ayambe kugwetsa mitengo m’chigawo china cha Yudeya. Mitengo imeneyi anaigwiritsira ntchito pomanga mpanda wazisonga wautali makilomita 7 kuzungulira mzinda wa Yerusalemu. Pofika mu September, Aroma anatenga katundu komanso kuwotcha mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake ndipo anagumula kachisiyo moti sanasiye mwala uliwonse pamwamba pa unzake monga mmene Yesu ananenera. (Luka 19:43, 44) Akatswiri ena amanena kuti “anthu pafupifupi 250,000 kapena 500,000 anaphedwa pamene Yerusalemu ankawonongedwa.”
CHIPILALA CHOKUMBUKIRA MFUMU TITO
Mu 71 C.E., Tito anabwerera kwawo ndipo anthu anamulandira mwaulemerero. Anthu onse a mumzinda anapita kukamulandira ndipo anachita chikondwerero chomwe chinali chisanachitikepo chiyambire.
Anthu anasangalala kwambiri kuona Tito ndi asilikali ake atanyamula chuma chosaneneka pamene ankadutsa m’misewu ya mumzinda wa Roma. Anasangalalanso kuona zombo zomwe analanda, zithunzi zosonyeza katundu komanso zinthu zambirimbiri zomwe anafunkha kuchokera kukachisi wa ku Yerusalemu.
Tito anakhala mfumu ya Roma mu 79 C.E. ndipo analowa m’malo mwa bambo ake a Vasipashani. Koma atangolamulira zaka ziwiri zokha, Tito anamwalira mwadzidzidzi. Ndiyeno mng’ono wake Domitani anayamba kulamulira monga mfumu ya Roma ndipo posakhalitsa anamanga chipilala chokumbukira Tito.
MMENE ANTHU AMAONERA CHIPILALACHI MASIKU ANO
Masiku ano anthu ambiri amasangalala akapita ku Rome n’kukaona chipilala cha Tito. Ena akaona chipilalachi amaona kuti chinamangidwa mwaluso zedi. Ena chimawakumbutsa za ulamuliro wakale wamphamvu wa Roma ndipo ena amakumbukira kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake.
Koma anthu amene amawerenga Baibulo mosamala amaona kuti chipilala cha Tito ndi chofunika kwambiri. Chipilalachi chimapereka umboni wotsimikizira kuti maulosi a m’Baibulo ndi odalirika komanso olondola. Zimenezi zimasonyeza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.—2 Petulo 1:19-21.