PHUNZIRO 55
Muzithandiza Mpingo Wanu
Padziko lonse atumiki a Yehova amasangalala kutumikira Yehova m’mipingo yam’dera lomwe akukhala. Iwo amasangalala ndi malangizo omwe amalandira ndipo amayesetsa kuthandiza mpingo wawo m’njira zosiyanasiyana. Kodi mukuona kuti nanunso mukufunika kumathandiza mpingo wanu?
1. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji nthawi ndi mphamvu zanu pothandiza mpingo?
Tonsefe tingathandize mumpingo m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kodi mumpingo mwanu muli anthu enaake amene ndi achikulire komanso amene akudwala? Kodi mungawathandize kuti azipezeka pamisonkhano? Kapena kodi mungawathandize zinthu zina monga kukawagulira zinthu, kapenanso kukawathandiza kugwira ntchito zapakhomo? (Werengani Yakobo 1:27.) Tingadziperekenso kukathandiza kukonza ndi kuyeretsa Nyumba ya Ufumu yathu. Palibe amene amatikakamiza kuti tizigwira ntchito zimenezi. Koma chifukwa chakuti timakonda Yehova ndi abale athu, ‘timadzipereka mofunitsitsa.’—Salimo 110:3.
A Mboni za Yehova obatizidwa angathandize mpingo m’njira zinanso. Abale amene akwaniritsa mfundo za m’Malemba zowathandiza kuti ayenerere udindo mumpingo, angasankhidwe kuti atumikire monga atumiki othandiza ndipo m’kupita kwa nthawi angayenerere kukhala akulu. Abale komanso alongo angawonjezere zomwe amachita pa ntchito yolalikira potumikira monga apainiya. A Mboni ena angathandize pogwira nawo ntchito yomanga malo olambirira kapena angasamukire mumpingo wina womwe ukufunikira anthu oti akathandize.
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji ndalama ndi zinthu zathu zina pothandiza mpingo?
Tingathe ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miyambo 3:9) Timasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito ndalama ndi zinthu zina kuti zithandizire mpingo wathu komanso ntchito yolalikira yomwe imachitika padziko lonse. (Werengani 2 Akorinto 9:7.) Zinthu zimene timapereka zimagwiritsidwanso ntchito pakachitika ngozi zam’chilengedwe. Anthu ambiri amasankha kuti nthawi zonse “aziika kenakake pambali” kuti akwanitse kupereka. (Werengani 1 Akorinto 16:2.) Tikhoza kupereka ndalama zathu pogwiritsa ntchito mabokosi a zopereka omwe amapezeka m’malo athu olambirira kapena tingathe kupereka kudzera pa donate.jw.org. Yehova watipatsa mwayi wosonyeza kuti timamukonda ndipo tingachite zimenezi popereka zinthu zimene tili nazo.
FUFUZANI MOZAMA
Ganizirani njira zina zomwe mungathandizire mpingo.
3. Tingagwiritse ntchito zinthu zimene tili nazo
Yehova ndi Yesu amakonda anthu amene amapereka mosangalala. Mwachitsanzo, Yesu anayamikira mayi wamasiye yemwe ngakhale kuti anali ndi tindalama tochepa kwambiri, anatipereka kwa Yehova. Werengani Luka 21:1-4, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi tingapereke kwa Yehova pokhapokha ngati tili ndi ndalama zambiri?
Kodi Yehova ndi Yesu amamva bwanji tikapereka mochokera pansi pa mtima?
Kuti muone mmene zopereka zathu zimagwirira ntchito, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane funso lotsatirali:
Kodi zopereka zimagwiritsidwa ntchito bwanji kuti zithandize mipingo padziko lonse?
4. Tingadzipereke kugwira ntchito zina
Atumiki a Yehova akale ankadzipereka pogwira ntchito yokonza malo awo olambirira. Iwo ankachita zimenezi ngakhale kuti anali atapereka kale ndalama zothandizira pa ntchitoyi. Werengani 2 Mbiri 34:9-11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mtumiki wa Yehova aliyense ku Isiraeli ankathandiza nawo bwanji posamalira nyumba ya Yehova kapena kuti malo olambirira?
Kuti muone mmene a Mboni za Yehova amachitira zinthu mogwirizana ndi chitsanzo cha m’Baibulo chimenechi, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani timafunikira kugwira nawo ntchito yokonza komanso kuyeretsa Nyumba ya Ufumu yathu?
Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite pothandiza kusamalira malo olambirira?
5. Abale angawonjezere zimene amachita kuti ayenerere kupatsidwa maudindo ena
Malemba amalimbikitsa abale kuti aziyesetsa kuchita zonse zomwe angathe pothandiza mpingo. Kuti muone chitsanzo cha zimene angachite, onerani VIDIYO. Kenako muyankhe mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, kodi Ryan anachita zotani kuti azichita zambiri pothandiza mpingo?
Baibulo limafotokoza zimene abale angachite kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza komanso akulu. Werengani 1 Timoteyo 3:1-13, kenako mukambirane mafunso awa:
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi a Mboni za Yehova amapeza kuti ndalama zoyendetsera ntchito yawo?”
Kodi mungayankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova amayamikira kwambiri zonse zomwe timachita pogwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu komanso zinthu zimene tili nazo pothandiza mpingo.
Kubwereza
Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nthawi yathu ndi mphamvu zathu pothandiza mpingo?
Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zinthu zomwe tili nazo pothandiza mpingo?
Kodi ndi zinthu ziti zomwe inuyo mukufuna kuchita pothandiza mpingo?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake Mulungu safuna kuti anthu amene amamulambira azipereka chakhumi masiku ano.
“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopereka Chakhumi?” (Nkhani yapawebusaiti)
Baibulo limapereka maudindo ena kwa amuna obatizidwa. Koma kodi zimakhala bwanji ngati pakufunika kuti maudindowa asamaliridwe ndi mkazi wobatizidwa?
“Udindo Umene Akulu Ali Nawo Mumpingo” (Nsanja ya Olonda, February 2021)
Onerani vidiyoyi kuti muone zimene a Mboni ena olimba mtima ankachita kuti akapereke mabuku kwa Akhristu anzawo.
Onani njira yomwe timapezera ndalama zoyendetsera ntchito yathu yomwe ndi yosiyana kwambiri ndi zipembedzo zina.
“Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yanu Zimachokera Kuti?” (Nkhani yapawebusaiti)