Chizindikiro—Sichiri Kokha Mbiri Yakale
MU Yerusalemu, mu Middle East, pali malo ozizwitsa a m’mbiri omwe amafunikira chisamaliro cha anthu olingalira lerolino. Iwo ali malo okwezedwa pamene paima “kachisi wa chuma chachikulu,” m’mawu a wodziŵa mbiri yakale wa m’zana loyambirira Wachiroma Tacitus. Palibe kudziŵidwa kwa chimango cha kachisi komwe kulipo, koma pulatiformu imatero. Ilo limachitira umboni kuwona kwa chizindikiro cha ulosi chomwe chimakuyambukirani inu.
Akatswiri ofukula zofotseredwa pansi apanga kufufuza kochulukira kum’mwera kwa pulatiformu ya kachisi. “Chimodzi cha zopezedwa zokondweretsa,” walongosola tero J.A. Thompson mu The Bible and Archaeology, “chinali unyinji wa njerwa za ntchito ya miyala za Herodiya mwachiwonekere zoikidwa kuchokera pamwamba pa khoma la Kachisi panthaŵi ya kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu A.D.70.”
Chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake chinanenedweratu zaka 37 chisanachitike. Osachepera pa akatswiri a mbiri yakale atatu analemba mawu a Yesu Kristu akuti “sudzasiidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa.” (Luka 21:6; Mateyu 24:1, 2; Marko 13:1, 2) Kukambitsirana kunatsatira kumene kumayambukira aliyense lerolino, kuphatikizapo inu.
“Mphunzitsi,” ophunzira ake anamfunsa tero, “chizindikiro nchiyani pamene izi ziti zichitike?” Mogwirizana ndi Yesu, nyengo yotsogolera ku kuwonongedwa kwa kachisi ikazindikiritsidwa ndi nkhondo, zivomezi, kuperewera kwa zakudya, ndi miliri. “Mbadwo uno,” iye akuwonjezera tero, “sudzapitirira kufikira zonsezi zitachitika.”—Luka 21:7, 10, 11, 32.
Kodi mbadwo umenewo unakumana ndi kukwaniritsidwa kwa “chizindikiro”? Inde. Baibulo limalozera ku “njala yaikulu” limodzinso ndi zivomezi zitatu, ziŵiri za izo ‘zivomezi zazikulu.’ (Machitidwe 11:28; 16:26; Mateyu 27:51; 28:1, 2) Mogwirizana ndi mbiri ya kudziko, zivomezi zina ndi kuperewera kwa zakudya kunachitika mkati mwa nyengo imeneyo. Inalinso nthaŵi ya nkhondo, ziŵiri za zimenezi zinamenyedwa ndi magulu ankhondo a Chiroma molimbana ndi nzika za Yerusalemu. Kulaliridwa kwachiŵiri kwa Yerusalemu kunatulukapo njala yovuta ndi mliri, chikumatsogolera ku kuwonongedwa kwa mzinda ndi kachisi wake m’chaka cha 70 C.E. Malo m’Yerusalemu kumene kachisi inali amaimirira kukhala mboni yeniyeni ku zochitika zoipa za m’zana loyamba zimenezo.
‘Chosangalatsa,’ wina anganene tero, ‘koma kodi ndimotani mmene icho chimandiyambukirira ine?’ Mu chakuti chizindikiro sichiri kokha mbiri yopita. Icho chinakwaniritsidwa kokha mwambali m’zana loyamba. Mwachitsanzo, Yesu ananeneratunso nthaŵi pamene mtundu wa anthu ukakhala m’mantha okulira chifukwa cha “zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi” ndi “mkukumo wa nyanja.” Mbali imeneyi ya chizindikiro ikazindikiritsa kuyandikira kwa “ufumu wa Mulungu”—boma lomwe lidzabweretsa chipulumutso chosatha kuchokera ku nsautso yadziko.—Luka 21:25-31.
Zinthu zoterezi sizinachitike m’zana loyamba. Lerolino, zaka 1,900 pambuyo pake, mtundu wa anthu ukuyembekezerabe chipulumutso kuchokera ku nkhondo, zivomezi, kuperewera kwa zakudya, ndi miliri. Chotero, chizindikiro chiyenera kukhala ndi kukwaniritsidwa kwachiŵiri kotheratu. Kulongosola pa ichi, bukhu la Chivumbulutso liri ndi zithunzi za ulosi zomwe zimagwirizana ndi chizindikiro, ndipo komabe linalembedwa pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu. (Chivumbulutso 6:1-8) Chotero, funso lofunika limabuka: Kodi chizindikirocho chawonedwa m’tsiku lathu?