Chizindikiro—Kodi Mwachiwona Icho?
“PANSI pakuya kunsi kwa nyanja, sitima ya pansi pa madzi yaitali, yokhala ndi kutsogolo kozungulira iri yolenjekeka zolimba, yosakhoza kugwedezeka ndi mafunde omwe amagunda m’mbali ya m’kuntho wa nyanja. Mpata m’sitima ya pansi pa madzi utseguka ndipo ndege ya utali wa mamita 9 ndi yochindikala mamita 1.4 ituluka mwaliwiro kupita chakunja. Ndegeyo iyamba ulendo wake wopita pamwamba ndi mpweya wosunkha, koma pofika pamwamba pa nyanja, injini yake iyatsa moto ndipo ndegeyo iphulika pa madzipo ndi phokoso lalikulu.”
Kulongosola koteroko kwa mamissile aliwiro koposa oponyedwa ndi sitima ya m’madzi, kuchokera mu bukhu la Rockets, Missiles and Spacecraft, lolembedwa ndi Martin Keen, limapereka tanthauzo ku ulosi wakale woneneratu nthaŵi ya nsautso yadziko chifukwa cha “mkukumo wanyanja.” (Luka 21:25) Kodi chiwopsyezo cha ndege za m’madzi za mamissile aliŵiro koposa chiri chachikulu motani?
Mogwirizana ndi bukhu lakuti Jane’s Fighting Ships 1986-87, Britain, China, France, the Soviet Union, ndi United States ali ndi masitima a pansi pa madzi onyamulira mamissile aliŵiro koposa 131 ogwira ntchito mokangalika. Palibe mzinda womwe sungakhoze kufikirika ndi iwo, ndipo zida zankhondo zimafikira chifupifupi mkati mwa kilomita imodzi ndi theka ya mnkholeyo. Ena amanyamula zida zankhondo zokwanira “kusakaza dziko lirilonse mkati mwa [makilomita 8,000],” mogwirizana ndi The Guinness Book of Records. Ngakhala choipirako, ena adzinenera kuti zida zankhondo m’kokha sitima ya pansi pa madzi imodzi yonyamula mamissile a liŵiro koposa ingakhoze kupangitsa nyengo yachisanu ya nyukliya yomwe ikakhoza kuipitsa miyoyo yonse padziko lapansi! Kulamulira kwa ndege za m’madzi zakutali kulinso vuto. Chikuwopedwa kuti kachitidwe kothamangira m’sitima ya m’madzi imodzi kangakhoze kudzetsa nkhondo ya nyukliya yakupha.
Ambiri akugwirizanitsa ziyembekezo zodzetsa mantha zoterozo ndi chizindikiro cha ulosi wa Yesu. Kodi chingakhale kuti mbadwo wathu ukukumana ndi kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chimenecho? Zenizeni zikuyankha inde. Ndipo chimatanthauza kuti chipulumutso kuchokera ku chiwopsyezo cha nkhondo ya nyukliya chiri pafupi. (Luke 21:28, 32) Ndi chiyembekezo cholondola choterocho, tikuitanani kulingalira umboni wa kukwaniritsidwa kwa chizindikirocho. Mbali zina zapadera za chizindikirocho zaikidwa pnsipa limodzi ndi kukwaniritsidwa kwawo kwamakono.
“Mitundu idzawukirana ndimitundu ina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Luka 21:10)
Chiyambire 1914 anthu oposa 100,000,000 afa ndi nkhondo. Nkhondo ya Dziko 1 inayamba mu 1914 ndipo inaphatikiza maiko 28, osaŵerenga maiko achilendo osiyanasiyana a Europe a tsiku limenelo. Maiko oŵerengeka anakhala achete. Inawononga miyoyo yoposa 13,000,000 ndi asilikari ovulazidwa oposa pa 21,000,000. Kenaka inadza Nkhondo ya Dziko II, yomwe inali yakupha koposa. Ndipo chiyambire pamenepo? Mu nkhani yakuti “Nkhondo za Dziko,” nyuzipepala ya ku South Africa The Star inagwira mawu a Times ya ku London ya pa Sande kukhala ikunena kuti: “Kota ya mitundu ya dziko pakali pano yagwidwa m’kukanthana.”
“Ndipo padzakhala zivomezi zazikulu.” (Luka 21:11)
Mu bukhu lawo Terra Non Firma, maprofesa a pa Stanford Yuniversite Gere ndi Shah andandalitsa tsatanetsatane wa “zivomezi za dziko zapadera” 164 zochitika zaka zoposa zikwi zitatu kupita kumbuyo. Pa chiwonkhetso chonsechi, 89 zinchitika chiyambire 1914, zikumatenga kuyerekeza kwa miyoyo 1,047,944. Ndandandayi inaphatikiza kokha zivomezi zazikulu, ndipo chiyambire chofalitsidwa cha Terra Non Firma mu 1984, zivomezi zakupha zachitika mu Chile, Soviet Union, ndi Mexico, zikumatulukapo zikwi za imfa zowonjezereka.
“Padzakhala . . . miliri.” (Luka 21:11)
Mu 1918 mliri wakupha unakantha mtundu wa anthu. Wotchedwa Spanish flu, iwo unafalikira kumalo onse okhalidwa ndi anthu kusiyapo kokha chisumbu cha St. Helena ndipo unapha anthu ochulukira kuposa omwe anaphedwa m’zaka zinayi zankhondo. Sayansi ya zamankhwala yapanga kupita patsogolo kokulira chiyambire nthaŵi imeneyo, ndipo komabe pali kusiyanako. Yalongosola tero The Lancet: “kuwumirira kwa matenda opatsirana mwa kugonana (STD) monga gulu lofala la kuyambukira kodziŵidwa kuli chozizwitsa cha mankhwala amakono. . . . Kulamulira kwa nthenda zopatsirana mwa kugonana kunawoneka panthaŵi imodzi kukhala m’kusamalira kwathu koma kwatipambana m’zaka za posachedwapa.”
Pali miliri ina imene mankhwala amakono akhala osakhoza kulamulira, yonga ngati kansa ndi nthenda za mtima. Yomwe yangotchulidwa pambuyopo, mogwirizana ndi S[outh] A[frica] Family Practice, “iri mbali yatsopano. . . . Iri chotulukapo cha pambuyo pa nkhondo yoyamba ya chitaganya.” Mu Britain, nthenda ya mtima ndi mwazi “ziri zochititsa imfa zokulira,” mogwirizana ndi bukhu la Cardiovascular Update—Insight Into Heart Disease. Ikumawonjezera kuti “kupita patsogolo kochepera kwenikweni kwapangidwa ku kulamulira kwawo.”
M’maiko otukuka kumene, mamiliyoni angapo akuvutika ndi malungo, matenda a tulo, likodzo, ndi matenda ena. Mmodzi wakupha woipitsa wadziko ali kutseguka m’mimba. Yalongosola tero magazini ya Medicine International: “Chayerekezedwa kuti zochitika 500 miliyoni za kutseguka m’mimba [pa] chaka mwachidziŵikire zimachitika pakati pa makanda ndi ana achichepere a ku Asia, Africa ndi Latin America, zokhala ndi imfa za pakati pa 5 ndi 18 miliyoni.”
“Padzakhala . . . kuperewera kwa zakudya.” (Luke 21:11)
Kuperewera kwa zakudya mwachibadwa kumatsatira nkhondo. Nkhondo ya Dziko I siinali yosiyanako. Njala zowopsya zinatsatira kudzuka kwake. Ndipo chiyambire pamenepo? Likusimba tero pepala lapadera la The Challenge of Internationalism—Forty Years of the United Nations (1945-1985): “Pamene kuli kwakuti panali anthu chifupifupi mamiliyoni 1,650 osadyetsedwa bwino mu 1950 panali mamiliyoni 2,250 mu 1983; m’mawu ena, kuwonjezeka kwa 600 miliyoni kapena kuwonjezeka kwa 36 peresenti.” Njala yosakaza inatsatira chilala chaposachedwapa cha ku Africa. “M’chaka chimodzi,” yalongosola tero magazini ya Newsweek, “ochulukira ofika ku anthu a ku Ethiopia 1 miliyoni ndi ana a ku Sudan 500,000 anafa.” Zikwi zingapo kuchokera ku maiko ena zinafanso.
“Ndipo kudzakhala zowopsya ndi zizindikiro zazikulu za kumwamba. Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.” (Luka 21:11, 25, 26)
Nkhondo ya Dziko I inayambitsa zida zankhondo zowopsya zatsopano. Kuchokera kumwamba, ndege za m’mlengalenga ndi masitima a mumlengalenga anaika mabomba ndi zipolopolo. Ngakhale chowopsya kwenikweni chinali nkhondo yomwe inadzera anthu wamba opanda chiyembekezo m’Nkhondo ya Dziko II, kuphatikizapo ija ya mabomba a atomu aŵiri.
Nyanja inakhalanso malo a zowopsya zatsopano. Pamene Nkhondo ya Dziko I inayambika, masitima a m’nyanja analingaliridwa kukhala zopanda pake, koma podzafika kumapeto kwa Nkhondo ya Dziko II, iwo anali anamiza ziŵiya zoposa pa zikwi khumi. “Kumiza masitima a zamalonda, kuphatikizapo masitima [onyamula anthu], popanda kuchenjeza kunawoneka kukhala mbali ya kachitidwe katsopano ndi kowopysa ka ‘nkhondo yotheratu,’” walongosola tero Norman Friedman mu bukhu lake Submarine Design and Development.
Lerolino ambiri akulingalira masitima a m’madzi a mamissile a liŵiro koposa kukhala masitima okulira a m’dziko. Ziŵiya zakupha zimanyamulidwanso ndi sitima ya liŵiro kwambiri ya m’madzi ya mamissile, ndege zonyamula, ndi masitima ena ankhondo. Mogwirizana ndi bukhu lakuti Jane’s Fighting Ships 1986-87, pali tsopano masitima a m’madzi 929, onyamula ndege 30, aliŵiro 84, akupha 367, masitima aliŵiro 675, zida zokakamiza 276, ndege zowukira mofulumira 2,024, nd ziŵiya zina zikwi zingapo zankhondo mu ntchito yokangalika ya mitundu 52. Wonjezerani ku ichi zida zochepera koma zakupha. Palibe ndi kalelonse kumene kunakhala “mkukumo” wowopsya wa nyanja wochitidwa ndi munthu woterowo.
Munthu wafikiranso m’dera la “dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi. Mamissile a liŵiro koposa amapita m’mwamba asanakanthe pa nthaka ya mnkhole wawo. Ndege za mumlengalenga zalowerera dongosolo la kumwamba ndi kulipyola. Mitundu yakhala yodalira mokulira pa masatellite opangidwa ndi munthu ozungulira dziko lapansi. Masatellite oyendayenda ndi ofufuza nyengo amawatheketsa iwo kulinganiza mamissile owukira ndi kulongosoka kwakupha. Kugwiritsira ntchito kwakuya kukupangidwanso kwa kulankhuzana ndi masatellite ozonda. “Masatellite,” walongosola tero Michael Sheehan mu bukhu lake The Arms Race, “akhala maso, makutu ndi mawu a magwero ankhondo amphamvu zazikulu zadziko.”
Chitsanzo chaposachedwapa chinali kuwukira kwa mumlengalenga pa Libya. Ikuchitira ripoti tero Aviation Week & Space Technology: “Zithunzithunzi za U.S. . . . za satellite zinagwiritsiridwa ntchito m’kukonzekera kuwukira ndi kufufuza kwa pambuyo pa kuwukira. Defense Meteorological Satellite Program inapereka ndandanda ya mphepo kaamba ka kuwukira ndipo kukambitsirana kwa ndege za nkhondo kunaphatikizidwa m’kupereka lamulo ndi kulamulira.” Chifukwa cha thayo lofunika lochitidwa ndi masatellite ankhondo, mphamvu zadziko zonsezo ziri nd zida zolimbana ndi masatellite. Kuzikidwa kwa zida mumlengalenga kuli chikhumbo chotseguka champhamvu ya dziko imodzi m’programu yotchedwa mofala Nkhondo Zotchuka. Kaya mphamvu zazikulu m’chenicheni zimadzilowetsa m’nkhondo za mumlengalenga kapena ayi, nthaŵi yokha idzalongosola.
Pakali pano, monga momwe kunanenedweratu, “anthu akukomoka nd mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.” Upandu, uchigawenga, kugwa kwa zachuma, kuipitsa kwa zamankhwala, ndi mbaliwali zaululu zochokera ku makapani amphamvu a nyukliya, limodzinso ndi kuchulukira kwa chiwopsyezo cha nkhondo ya nyukliya, zonsezo ziri zochititsa za “mantha.” Magazini ya ku Britain New Statesmen yachitira ripoti kuti “oposa theka” a achichepere a zaka za pakati pa 13 ndi 19 a m’dzikolo “amadzimva kuti nkhondo ya nyukliya idzachitika m’nthaŵi yawo ya moyo, ndipo 70 peresenti amakhulupirira kuti iri yothekera tsiku lina.”
[Bokosi patsamba 7]
Chizindikiro—Kodi icho Chimatanthauzanji?
Mamiliyoni angapo, pambuyo pa kusanthula chizindikiro m’chiyang’aniro cha mbiri ya m’zaka za zana la 20, akhala okhutiritsidwa za kukwaniritsidwa kwake. (Onaninso mateyu, mutu 24 ndi Marko, mutu 13.) Mbadwo wa 1914 ndithudi uli wozindikiritsidwa. Uli umene waphatikizidwa m’kukwaniritsidwa kwachiŵiri kwa mawu a Yesu akuti: “Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” (Luka 21:32) “Zinthu zonsezi” zimaphatikizapo kuwomboledwa kuchokera ku mavuto othetsa nzeru a mtundu wa anthu.
Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti: “Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu, chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira. . . . . Pa kuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.” Ufumu wa Mulungu, boma ladziko losakhala laumunthu, lidzasintha dziko lapansi iri kukhala paradaiso wa chiwunda chonse. Chotero, motsimikizirika monga mmene chizindikiro chakhalira chowona choteronso chiwomboledwe chidzabweranso.—Luka 21:28, 31; Salmo 72:1-8.
Mwinamwake simunalingalirepo chizindikiro cha ulosi ndi kalelonse. Tikukulimbikitsani inu kupitirizabe kusanthula Mawu a Mulungu. Kuchita tero kudzakutheketsani inu kumvetsetsa zochulukira ponena za zifuno za Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Chotero mudzaphunzira chimene Yehova Mulungu amafuna kwa awo omwe iye ‘adzapulumutsa’ kulowa m’dziko lapansi la Paradaiso likudzalo.—Salmo 37:10, 11; Zefaniya 2:2, 3; Chivumbulutso 21:3-5.
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
Courtesy of German Railroads Information Office, New York
Eric Schwab/WHO
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Jerry Frank/United Nations
U.S. Air Force photo