Masiku Otsiriza—Chochitika Chapadera
“Oppenheimer [yemwe anathandiza kupanga bomba la atomu] anali wolondola m’ganizo lake la maziko kuti mbiri yakale inasintha kachitidwe kake mu 1945. Kulibenso kumene nkhondo yaikulu ingamenyedwe mu mkhalidwe wa Nkhondo ya Dziko ya II.”—Weapons and Hope, lolembedwa ndi Freeman Dyson.
KUGWIRITSIRA ntchito kwa bomba la atomu mu 1945 kunasintha dziko. Iko kunadziŵikitsa posinthira pena m’mbiri ya nkhondo. Mmenemo ndi mmene mmodzi wa opanga bombayo, Robert Oppenheimer, anawonera mkhalidwewo. Pamene kuphulika koyesa kunachitika mu New Mexico, Oppenheimer anagwira mawu mu Bhagavad Gita ya chiHindu, akumanena kuti, “Ndakhala imfa, wosakaza wa dziko.” Oppenheimer analongosolanso kuti, “Anthu a dziko lino afunikira kugwirizana, ngati sitero adzatha psyiti.”
Mu 1949 bungwe lothandiza la asayansi ku Atomic Energy Commission ya ku U.S., lomwe linaphatikizapo Oppenheimer, linachenjeza molimbana ndi kupanga bomba lina la hydrogen losakaza kwenikweni. Ripoti lawo linanena kuti: “Ichi chiri chida chachikulu kwambiri; icho chiri m’mkhalidwe wosiyanako kotheratu ndi bomba la atomiki.” Ichi chinali chifukwa chakuti mphamvu za kuwononga kwa bomba la hydrogen zikakhoza kuchulukitsidwa mwa kuwonjezera mafuta a zinthu zotsika mtengo. Mu kokha zaka zinayi, bomba la atomu linangokhala chidoli chokha.
Enrico Fermi ndi Isidor Rabi, omwenso anali ziwalo za komiti yothandizayo, anapereka ngakhale chenjezo lamphamvu. “Chenicheni chakuti palibe malekezero omwe alipo ku kuwononga kwake kwa chida chimenechi kumapangitsa kukhalapo kwake kwenikweni ndi chidziŵitso cha kupangidwa kwake kukhala ngozi ku mtundu wa anthu wonse. Chiri moyenerera chinthu choipa cholingaliridwa m’kawonedwe kalikonse.” (Kanyenye ngwathu.) Iwo anadziŵa kuti munthu tsopano akakhoza kudziwononga iyemwini. Uphungu wawo motsutsana ndi kupanga bomba la hydrogen unanyalanyazidwa.
‘Maulosi a Chiŵeruzo Okhala ndi Maziko a Sayansi’
Mphamvu zodabwitsa za kuwononga zimene munthu tsopano ali nazo zachitiridwa chitsanzo m’nsonga imodzi yogwidwa mawu ndi Dr. Lown, prezidenti wothandiza wa International Physicians for the Prevention of Nuclear War: “Sitima ya m’madzi yamakono imodzi iri chifupifupi ndi nthaŵi zisanu ndi zitatu za mphamvu zokantha kotheratu za Nkhondo ya Dziko II—Yokwanira kuwononga mzinda waukulu uliwonse mu Northern Hemisphere.” Chonde dziŵani—kumeneko kuli kuthekera kwa mphamvu ya kuwononga ya kokha sitima yam’madzi imodzi! Mphamvu zazikulu ziri ndi unyinji wa masitima a m’madzi ndi masitima apamwamba pamadzi onyamula zida za nyukliya. Kuwonjezera ku amenewa ziri zida zoyenda nazo pa mtunda ndi mlengalenga, chimapanga chiwonkhetso chonse cha zida za nyukliya zoposa pa 50,000!
Ndiliti ndi kalelonse m’mbiri pamene munthu wakhala ndi mphamvu zowopsya zodzetsa mantha zoterezi m’manja ake? Dr. Lown akuvomereza kuti nyengo iriyonse ya m’mbiri yakhala ndi aneneri ake osalabadiridwa. Kodi ndi kusiyana kotani tsopano? Iye akulongosola kuti: “Nyengo yathu iri yoyamba mu imene maulosi a chiŵeruzo akuchokera ku kufufuza kotsutsa kwa usayansi.” Ngati pangakhale kuwononga kwa moto wa nyukliya, iye akutero, “kuli kudzidalira kopanda pake [kudzitama] kuyerekeza kuti pangadzakhale kupulumuka kwa anthu pambuyo pa ngozi yopangidwa ndi munthu yoteroyo.”
Kuwonjezereka kwa “Chisauko cha Mitundu”
Mu 1945 munthu anatulutsa chipatso choipa cha nkhondo ya nyukliya kuchokera ku unyinji wake wodabwitsa wa chidziŵitso cha za sayansi ndipo alibe njira iriyonse ya kuchibwezeranso icho m’mbuyo. Iye angakhoze kuwononga zida zake za nyukliya, koma kodi ndimotani mmene iye adzachotsera chidziŵitso chimene nthaŵi zonse chingatsogolerenso ku zimenezo? Chotero, zochitika zenizeni za Hiroshima ndi Nagasaki kuphatikizapo kugwiritsiridwa ntchito kwa zida za nyukliya zokulira kwawonjezera ukulu kaamba ka “zinthu zowopsya” ndi “zizindikiro zazikulu” kuchokera kumwamba, za “chisauko cha amitundu . . . osadziŵa kotulukira” chiyambire 1945.—Luka 21:11, 25.
Chisauko cha amitundu chawonjezekanso ndi kuyesayesa kwathu kwa kufikiritsa kukambitsirana kwa mwamsanga. Kokha m’zana lino la 20 ndi mmene dongosolo latsopano la kukambitsirana (wailesi, TV, makopyuta, masetilaiti) zalola mtundu wa anthu wonse kudziŵa mwamsanga za nkhondo ndi ngozi, mwakutero kufalitsa mantha ndi chisauko cha amitundu m’njira imene sinali yothekera ndi kalelonse. Osati kokha kuti unyinji wa dziko umadziŵa ponena za izo koma mwa TV iwo angakhoze kupenyerera nkhondo ndi kukhetsa mwazi pamene iko kukuchitika!
Zipsyera za Nkhondo
M’chaka chino cha 1988, pali mamiliyoni a mabanja angapo kuzungulira dziko lonse omwe akumana ndi mbali ya chizindikiro chakuti tiri m’masiku otsiriza. Tero motani? Iwo ataikiridwa ndi wokondedwa mmodzi kapena ochulukira mu nkhondo ziŵiri kapena mu imodzi ya kukanthana kokulira (Korea, Vietnam, Iraq-Iran, Lebanon, ndi zina zotero) zomwe zasakaza mtundu wa anthu. Mwinamwake banja lanu liri limodzi la awo omwe angakumbukire kutaikiridwa atate, agogo achimuna, amalume, kapena mbale. Ndiponso, mamiliyoni angapo a amayi, agogo achikazi, alongo, ndi azakhali afa mu nkhondo ndi m’chipiyoyo cha ku Europe.
M’kuwonjezerapo, mkati mwa mbadwo wathu, magulu ankhondo amenyera uku ndi uko modutsa Europe ndi ku Far East, akumagwirira chigololo ndi kuwopsyeza chiŵerengero cha anthu wamba. Chotero, opulumuka, makamaka akazi, amakhala ndi zipsyera za kuchitidwa moipa ndi iwo kufikira ku tsiku lino. Kodi munthu amapitirizabe kufika mu mkhalidwe wa kuipitsa makhalidwe abwino ndi kupusa?
Kavalo wofiira wa chivumbulutso wa nkhondo ndi kupha ndi kavalo wotumbuluka wa imfa apyola motsimikizirika modutsa dziko lapansi m’njira yosayerekezeka chiyambire 1914.—Chivumbulutso 6:4.
Koma bwanji ponena za “kavalo wakuda” wa njala? (Chivumbulutso 6:5) Kodi iye wakantha mbadwo wathu?
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Monga mmene zinthu zikuwonekera tsopano, nkhondo ya dziko ingachitike kokha kachiŵirinso—monga nkhondo ya nyukliya. Kenaka sipadzakhala mitundu kapena maufumu. Nsonga imodzi imeneyi imapangitsa nthaŵi yathu kukhala yapadera ndi kuwonjezera mphamvu ku kulongosolako “masiku otsiriza.”—2 Timoteo 3:1
[Mawu Otsindika patsamba 8]
“Sitima ya nkhondo yam’madzi imodzi yamakono iri ndi mphamvu chifupifupi nthaŵi zisanu ndi zitatu zotheratu za Nkhondo ya Dziko II—zokwanira kuwononga mzinda waukulu uliwonse mu Northern Hemisphere”