Munthu Aliyense Adzakhala Patsinde pa Mkuyu Wake
MTHUNZI umafunika kwambiri nthaŵi yotentha kumadera a ku Middle East. Mtengo uliwonse umene uli ndi mthunzi umakhala wofunika kwambiri, makamaka ngati wamera pafupi ndi nyumba ya munthu. Chifukwa chakuti mtengo wa mkuyu uli ndi masamba akuluakulu ofutukuka komanso nthambi zotambalala bwino, umakhala ndi mthunzi wabwino kwambiri kuposa mtengo wina uliwonse m’dera limeneli.
Buku lotchedwa Plants of the Bible linati, “mthunzi wa [mtengo wa mkuyu] akuti ndi wotsitsimula komanso wozizira bwino kuposa mthunzi wa hema.” Mitengo ya mkuyu imene kale inkamera m’mphepete mwa minda ya mpesa ku Israyeli inali malo abwino opumirapo anthu olima m’munda.
Pamapeto pa tsiku lotopetsa ndi lotentha, mabanja ankatha kukhala pansi pa mtengo wawo wa mkuyu n’kumacheza mosangalala. Komanso, mtengo wa mkuyu ndi waphindu kwa mwiniwake chifukwa umabereka zipatso zambiri zopatsa thanzi. Choncho, kuyambira pa nthaŵi ya Mfumu Solomo, kukhala pansi pa mtengo wa mkuyu kunatanthauza kuti anthu ali pa mtendere, ali ndi moyo wotukuka, komanso ali ndi zinthu za mwanaalirenji.—1 Mafumu 4:24, 25.
Zaka mazana angapo m’mbuyomo, mneneri Mose anafotokoza kuti Dziko Lolonjezedwa linali ‘dziko la mikuyu.’ (Deuteronomo 8:8) Azondi khumi ndi aŵiri anasonyeza kuti dzikolo linali lachonde pobweretsa nkhuyu ndi zipatso zina kumalo kumene kunali Aisrayeli. (Numeri 13:21-23) Zaka zopitirira 100 zapitazo, munthu wina amene anakayenda ku madera otchulidwa m’Baibulo ananena kuti mtengo wa mkuyu ndi umodzi mwa mitengo yofala kwambiri kumeneko. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Malemba amatchula kwambiri nkhuyu ndi mitengo ya mkuyu!
Mtengo Wobala Kaŵiri Pachaka
Mtengo wa mkuyu ukhoza kumera m’dothi losiyanasiyana, ndipo chifukwa chakuti mizu yake imapita patali, umatha kupirira nyengo yotentha yaitali ya ku Middle East. Mtengowu ndi wodabwitsa chifukwa umabereka zipatso zoyamba mu June, kenaka zipatso zambiri zomaliza kuyambira mwezi wa August kumapita m’tsogolo. (Yesaya 28:4) Aisrayeli nthaŵi zambiri ankadya zipatso zoyambirirazo zisanaume. Zipatso zomalizazo ankaziumitsa kuti azigwiritse ntchito chaka chonse. Nkhuyu zouma ankazisinja n’kupanga ntchintchi, ndipo nthaŵi zina ankathirako mtedza wamtundu wa katungulume. Ntchintchi zimenezi zinali zosungika, zopatsa thanzi, komanso zokoma.
Mkazi wanzeru Abigayeli anapatsa Davide ntchintchi za nkhuyu 200, ndipo mwachidziŵikire amadziŵa kuti chimenechi chinali chakudya chabwino kupatsa anthu amene akuthaŵa. (1 Samueli 25:18, 27) Ntchintchi za nkhuyu anali kuzigwiritsanso ntchito ngati mankhwala. Ntchintchi za nkhuyu zouma ataziika pa kansalu anazigwiritsa ntchito pothowa chithupsa chimene chinatsala pang’ono kupha Mfumu Hezekiya, ngakhale kuti chifukwa chenicheni chimene Hezekiya anachirira pambuyo pake chinali chakuti Mulungu analoŵererapo.a—2 Mafumu 20:4-7.
Kale, nkhuyu zouma zinali zofunika kwambiri m’madera onse ozungulira nyanja ya Mediterranean. Munthu wodziŵa nkhani za boma wotchedwa Cato ananyamula nkhuyu n’kumaionetsa kwa anthu a m’bungwe loyendetsa dziko la Rome powanyengerera kuti akamenye nkhondo yachitatu ndi mzinda wa Carthage. Nkhuyu zouma zabwino kwambiri mu dera lonse la Rome zinkachokera ku Caria, ku Asia Minor. N’chifukwa chake dzina lachilatini la nkhuyu zouma linadzakhala carica. Dera limeneli masiku ano lili m’dziko la Turkey ndipo kumachokerabe nkhuyu zabwino kwambiri.
Alimi a ku Israyeli nthaŵi zambiri ankadzala mitengo ya mkuyu m’minda ya mpesa, koma ankadula mitengo yosabereka. Dothi labwino linali losoŵa, choncho samafuna kuti aliwonongere mitengo yosabereka. M’fanizo la Yesu la mtengo wa mkuyu wosabereka, mwini wake wa munda wa mpesa anauza munthu wosamalira mundawo kuti: “Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake?” (Luka 13:6, 7) Pa nthaŵi ya Yesu anthu ankalipira msonkho pa mitengo ya zipatso, choncho kukhala ndi mtengo wosabereka kukanakhala kungotaya ndalama pachabe.
Nkhuyu zinali chakudya chofunika kwambiri kwa Aisrayeli. Choncho, kukolola nkhuyu zochepa, mwina chifukwa cha chilango chochokera kwa Yehova, linali tsoka lalikulu. (Hoseya 2:12; Amosi 4:9) M’neneri Habakuku anati: “Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m’minda m’mosapatsa chakudya; . . . Koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.”—Habakuku 3:17, 18.
Chizindikiro cha Mtundu Wosakhulupirika
Malemba nthaŵi zina amatchula nkhuyu kapena mitengo ya mkuyu mophiphiritsira. Mwachitsanzo, Yeremiya anayerekezera anthu okhulupirika amene anapita ku ukapolo kuchokera ku Yuda ndi mtanga wa nkhuyu zabwino, nkhuyu zoyamba kucha zimene nthaŵi zambiri ankazidya zisanaume. Koma anthu osakhulupirika amene anali ku ukapolo anawayerekezera ndi nkhuyu zoipa, zimene sakanatha kuzidya ndipo zinali zongofunika kutaya.—Yeremiya 24:2, 5, 8, 10.
M’fanizo lake la mtengo wa mkuyu wosabereka, Yesu anasonyeza kuleza mtima kumene Mulungu anaonetsera mtundu wa Ayuda. Monga tanena kale, Yesu anafotokoza za munthu wina amene anali ndi mtengo wa mkuyu m’munda wake wa mpesa. Mtengowo sunabereke kwa zaka zitatu, ndipo mwiniwakeyo anafuna kuti udulidwe. Koma munthu wosamalira mundawo anati: “Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iyayi, mudzaulikhatu.”—Luka 13:8, 9.
Pamene Yesu anapereka fanizo limeneli nkuti atalalikira kale kwa zaka zitatu, kuyesayesa kuti akulitse chikhulupiriro cha anthu a mtundu wachiyuda. Yesu anachita khama kwambiri pa ntchito yake, “kuthira feteleza” mtengo wa mkuyu wophiphiritsirawo, mtundu wachiyuda, ndiponso kuupatsa mpata woti ubale zipatso. Koma patatsala mlungu umodzi kuti Yesu aphedwe, zinaonekeratu kuti mtunduwo wam’kana Mesiya.—Mateyu 23:37, 38.
Kenako, Yesu anagwiritsanso ntchito mtengo wa mkuyu kuti ayerekezere mmene mtunduwo unalili woipa mwauzimu. Akupita ku Yerusalemu kuchoka ku Betaniya kutatsala masiku anayi kuti aphedwe, Yesu anaona mtengo wa mkuyu umene unali ndi masamba ambiri koma unalibe chipatso n’chimodzi chomwe. Chifukwa chakuti nkhuyu zoyamba zimabereka masamba akamaphuka, ndipo nthaŵi zina masamba asanaphuke kumene, kupanda zipatso kwa mtengowo kunaonetsa kuti unali wachabechabe.—Marko 11:13, 14.b
Mofanana ndi mtengo wa mkuyu wosabereka uja umene unali kuoneka ngati wabwinobwino, mtundu wachiyuda nawonso unali ndi maonekedwe abwino onamizira. Koma sunabale zipatso zabwino, ndipo pamapeto pake unakana ngakhale Mwana wa Yehova amene. Yesu anatemberera mtengo wa mkuyu wosaberekawo, ndipo tsiku lotsatira, ophunzira ake anaona kuti mtengowo unali utauma. Mtengo wouma umenewo unaphiphiritsira bwino kwambiri zimene zinali kudzachitika m’tsogolo, zoti Mulungu adzawakana Ayuda kuti si anthu ake osankhika.—Marko 11:20, 21.
‘Phunzirani ku Mtengo wa Mkuyu’
Yesu anagwiritsanso ntchito mtengo wa mkuyu pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza kukhalapo kwake. Iye anati: “Phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo.” (Mateyu 24:32, 33) Masamba obiriŵira kwambiri a mkuyu ndi chizindikiro chooneka bwino komanso chosasokoneza cha kuyandikira kwa chilimwe. Chimodzimodzinso, ulosi waukulu wa Yesu wolembedwa mu Mateyu chaputala 24, Marko chaputala 13, ndi Luka chaputala 21 umapereka umboni wooneka bwino wa kukhalapo kwa Yesu tsopano lino monga wolamulira wa Ufumu wakumwamba.—Luka 21:29-31.
Chifukwa chakuti tikukhala panthaŵi yofunika kwambiri, ndithudi tiyenera kuphunzira ku mtengo wa mkuyu. Ngati titero n’kukhala maso mwauzimu, tingayembekezere kudzaona lonjezo labwino kwambiri ili likukwaniritsidwa: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Mika 4:4.
[Mawu a M’munsi]
a Munthu wofufuza zinthu zachilengedwe dzina lake H.B. Tristram amene anapita ku madera otchulidwa m’Baibulo chapakati pa zaka za m’ma 1800 anati anapeza kuti anthu kumeneko akugwiritsabe ntchito ntchintchi za nkhuyu pothowa zithupsa.
b Izi zinachitika pafupi ndi mudzi wa Betefage. Dzinali limatanthauza “Nyumba ya Nkhuyu Zoyambirira Kucha.” Dzina limeneli likhoza kusonyeza kuti derali linali lotchuka chifukwa cha nkhuyu zake zabwino zoyambirira kucha.