Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Chidaliro Mkati mwa Masiku Otsiriza
PAMENE lachiŵiri, Nisani 11, liyandikira, Yesu ali ndi atumwi ake pa Phiri la Azitona. Angochoka kumene kuchigawo cha kachisi, chimene angathe kuwona chamunsi, ndipo Yesu anali kukambitsirana nawo za chizindikiro cha kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu ndi chamapeto a dongosolo la zinthu.
Popitirizabe ndemanga zake, Yesu akuwachenjeza za kuthamangitsana ndi Akristu onama. Kuyesayesa kudzapangidwa, iye akutero, kuti “akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.” Koma, mofanana ndi ziwombankhanga zowona patali, osankhidwa amenewa adzasonkhana kumene chakudya chauzimu chowona chikapezeka, ndiko kuti, ndi Kristu wowona m’kukhalapo kwake kosawoneka. Iwo sadzasochezedwa ndi kusonkhanitsidwira kwa Kristu wonama.
Akrisu onama angawonekere kokha mowoneka. Mosiyana, kukhalapo kwa Yesu kudzakhala kosawoneka. Kudzachitika mkati mwa nthaŵi yochititsa mantha m’mbiri ya anthu, monga momwe Yesu akunenera kuti: “Dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake.” Inde, imeneyi idzakhala nyengo ya mdima koposa m’mbiri yonse ya anthu. Kudzakhala ngati kuti dzuwa ladetsedwa m’nthaŵi yamasana, ndipo ngati kuti mwezi sunaŵale usiku.
“Mphamvu ziri mmwamba zidzagwedezeka,” akupitiriza motero Yesu. Mwakutero akusonyeza kuti miyamba yeniyeni idzakhala ndi mawonekedwe osonyeza vuto. Miyamba sidzakhala kokha malo okhala mbalame, koma idzadzazidwa ndi ndege zankhondo, maroketi, ndi kufufuza kutali m’mlengalenga. Mantha ndi chiwawa zidzapitirira muyezo wa kanthu kalikonse kodziŵika m’mbiri ya papitapo ya anthu.
Yesu akuti, monga chotulukapo, padzakhala “kuvutika maganizo kwa mitundu, yosadziwa njira yoturukira chifukwa cha mkokomo wa nyanja ndi mafunde ake, pamene anthu akukomoka ndi mantha ndi chiyembekezo cha zinthu zakudza padziko lapansi lokhalidwa ndi anthu.” Ndithudi, nyengo ya mdima koposa imeneyi ya kukhalapo kwa anthu idzatsogolera ku nthaŵi pamene, monga momwe Yesu akunenera, kuti “kudzakhala chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa.”
Komatu si onse amene adzakhala akulira pamene ‘Mwana wa munthu adza ndi mphamvu’ yodzawononga dongosolo la zinthu loipa lino. “Osankhidwawo” a 144,000 amene adzakhala ndi mbali limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wa kumwamba, sadzalira, choteronso atsamwari awo, awo amene Yesu poyambirirapo anawatcha “nkhosa zina” zakezo. Mosasamala kanthu kukhala ndi moyo mkati mwa nyengo ya mdima waukulu koposa m’mbiri ya anthu, amenewa amalabadira chilimbikitso cha Yesu chakuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani, mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”
Kuti ophunzira ake amene akhala ndi moyo mkati mwa masiku otsiriza akadziŵe kuyandikira kwamapeto, Yesu akupereka fanizo iri: “Onani mkuyu ndi mitengo yonse: pamene iphukira, muipenya nimuzindikira panokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuwona zinthu izi ziri kuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndi inu, mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika.”
Chotero, pamene ophunzira ake awona mbali zosiyanasiyana za chizindikiro zikukwaniritsidwa, ayenera kuzindikira kuti mapeto a dongosolo la zinthu ali pafupi ndikuti mwamsanga Ufumu wa Mulungu udzasesa kuipa konse. Kwenikweni, mapetowo adzachitika mkati mwa nthaŵi ya moyo wa anthu amene amawona kukwaniritsidwa kwa zinthu zonse zimene Yesu akuneneratu! Akumachenjeza za ophunzira amene akakhala ndi moyo mkati mwa nthaŵi yosaiŵalika ya masiku otsiriza, Yesu akuti:
“Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, kuti tsku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse okhala pankhope padziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.” Mateyu 24:23-51; Marko 13:21-37; Luka 21:25-36; Chivumbulutso 14:1, 3; Yohane 10:16.
◆ Kodi ndi mikhalidwe yapadziko yotani imene idziŵikitsa kukhalako kwa Kristu?
◆ Kodi ndiliti pamene ‘mitundu yonse yapadziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa,’ koma kodi otsatira a Kristu adzakhala akuchita chiyani?
◆ Kodi ndi fanizo lotani limene Yesu akupereka kuthandiza ophunzira ake amtsogolo kuzindikira pamene mapeto ayandikira?
◆ Kodi ndi chenjezo lotani limene Yesu akupereka kwa ophunzira ake amene akhala ndi moyo mkati mwa masiku otsiriza?