Kuthandiza Mwana Kuti Akule mu Nzeru ya Umulungu
ANTHU OLINGALIRA amitundu yosiyanasiyana ndi mayambidwe osiyanasiyana amavomereza kuti Yesu anali mphunzitsi wodabwitsa ndi munthu wa makhalidwe abwino. Koma kodi zinthu zina mkuphunzitsidwa kwake kwa unyamata zinaphatikiza ku ichi? Kodi ndi maphunziro otani amene makolo lerolino amaphunzira kuchokera ku moyo wake wa banja ndi kuleredwa?
Baibulo limatiuza ife zochepa kwambiri ponena za ubwana wa Yesu. Poyambirira, zaka zake zoyambirira 12 zinakwaniritsidwa mu maversi awiri: “Ndipo pamene [Yosefe ndi Mariya] anatha zonse monga mwa chilamulo cha Yehova, anabwerera ku Galileya kumudzi kwawo ku Nazareti. Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa iye.” (Luka 2:39, 40) Koma pano pali maphunziro kaamba ka makolo kuphunzira.
Mwana wachichepereyo “anapitirizabe kukula nalimbika.” Chotero, makolo ake anali kusamalira iye mwakuthupi. Ndiponso, iye mopitiriza “analikudzala ndi nzeru.”a Kodi linali thayo landani kumuphunzitsa iye nzeru ndi kumvetsetsa komwe kukanakhala maziko kaamba ka nzeru yoteroyo?
Pansi pa Chilamulo cha Mose, makolo ake anali ndi thayo limenelo. Lamulo linauza makolo a Chiisrayeli: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero adzikhala pa mtima panu; ndipo mudziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi mu nyumba zanu ndipoyenda inu pa njira ndi pogona inu pansi ndi pouka inu.” (Deutronomo 6: 6, 7) Chenicheni chakuti Yesu anapitiriza “kukhala wodzazidwa ndi nzeru,” ndi kutinso “chiyanjo cha Mulungu chinapitiriza pa iye,” chimasonyeza kuti Yosefe ndi Mariya anali kumvera lamulo limeneli.
Ena angadzimve kuti popeza Yesu anali mwana wangwiro, kuleredwa kwake sikukupereka chitsanzo chenicheni kaamba ka kulera ana ena. Komabe, Yosefe ndi Mariya sianali anthu angwiro. Komabe mwachiwonekere anapitiriza kupereka zosowa zake za kuthupi ndi za kuuzimu, ndipo anachita tero mosasamala kathu za chitsenderezo cha banja lomakula. (Mateyu 13:55, 56) Ndiponso, Yesu, angakhale anali wangwiro, anafunikirabe kukula kuchoka ku ukhanda kufika ku ubwana ndi unamwali ndi kufika ku ukulu. Panali ntchito yaikulu ya kudziwitsa yomwe makolo ake anayenera kuichita, ndipo mwachiwonekere iwo anaichita bwino.
Yesu pa Msinkhu wa Zaka 12
Ndipo atate wake ndi amake akamka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paskha.” (Luka 2:41) Malinga ndi Lamulo la Mulungu, mwamuna aliyense anafunikira kukawonekera mu Yerusalemu kaamba ka phwandolo. (Deutronomo 16:16) Koma zolembedwa zikunena kuti “makolo ake akamka.” Yosefe anatenga Mariya, ndipo mwachiwonekere banja lonse, pa ulendo umenewo wa mamailosi oposa 60 (100 km) ku Yerusalemu kaamba ka nthawi ya chikondwerero. (Deutronomo 16:6, 11) Unali mwambo wawo —mbali yokhazikika ya miyoyo yawo. Ndiponso, sanali kupanga kuwonekera kwa chiphamaso; iwo anatsalira kaamba ka masiku onse aphwando.—Luka 2: 42, 43.
Ichi chimapereka phunziro labwino kaamba ka makolo lerolino. Maphwando a chaka ndi chaka amenewa mu Yerusalemu anali nthawi ya kusonkhana ndi kusangalala. (Levitiko 23:4, 36) Iwo anapereka chokumana nacho chodzutsa maganizo chauzimu kwa Yosefe, Mariya ndi Yesu wachichepere. Lerolino, makolo amachita bwino kufunafuna nthawi yofananayo kaamba ka ana awo achichepere kukhala ndi masinthidwe osangalatsa limodzi ndi kumangiliridwa kosangalatsa kwa uzimu. Makolo amene ali Mboni za Yehova amachita ichi mwakutenga ana awo ku misonkhano ndi misonkhano yaikulu imene imachitidwa mokhazikika nthawi ndi nthawi mkati mwa chaka. Mwakutero, ana angakhale ndi chokumana nacho chosangalatsa cha kuyenda ndi kukhala okhoza kusakanizana ndi mazana kapena zikwi za akhulupiriri anzawo kwa masiku ochepa. Tate amene mwachipambano analera ana oposa khumi anali kupereka chiyamikiro cha chipambano chake ku chenicheni chakuti kuyambira pamene anabatizidwa monga Mkristu zaka 45 zapita, iye sanaphonyepo gawo limodzi la msonkhano uli wonse. Ndipo iye walimbikitsa banja lake kusaphonya uli wonse.
Kuyang’anira Kosamalitsa
Pamene Yesu anali wachichepere, iye mosakaikira anakhala chifupi ndi makolo ake mkati mwa maulendo apachaka amenewo ku mzinda waukulu wa Yerusalemu. Komabe, pamene anali kukula iye mwina mwake angakhale atapatsidwa ufulu wokulirapo. Pamene iye anali wa zaka 12, anali chifupifupi pa msinkhu umene Ayuda anauwona monga wofunika kwambiri munjira ya ku ukulu. Mwina mwake chifukwa cha kusintha koyenera ndi kwachibadwa kumeneku, kuyang’anira kosamalitsa kunawoneka pamene nthawi inafika kaamba ka banja la Yosefe kuchoka ku Yerusalemu ndi kubwerera ku mudzi. Nkhaniyo imakamba kuti: “Pakubwerera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m’mbuyo ku Yerusalemu, ndipo atate ndi amake sanadziwa. Iwo anayesa kuti iye anali m’chipiringu chaulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi ndipo anayamba kufunafuna iye mwa abale awo ndi mwa anansi awo.”—Luka 2: 43, 44.
Pali mbali za chochitika ichi zomwe ponse pawiri makolo ndi achichepere angazindikire. Komabe, pali kusiyana kumodzi: Yesu anali wangwiro. Popeza iye anali momvera wogonjera kwa Yosefe ndi Mariya, sitingalingalire kuti iye analephera kumvera makonzedwe ena ake omwe anapanga ndi iye. (Luka 2:52) Chingakhale chotheka kuti panali mpata mu kulankhulana. Makolowo anaganiza kuti Yesu anali m’chipiringu cha abale ndi anansi awo. (Luka 2:44) Chiri chapafupi kuganiza kuti, mkuchoka kotanganidwa mu Yerusalemu, iwo akanapereka chisamaliro choyamba kwa ana awo achichepere ndi kuganiza kuti mwana wawo wamkulu kwambiri, Yesu, anali kubwera nayenso.
Komabe, Yesu mwachidziwikire anaganiza kuti makolo ake adzadziwa kumene iye anali. Ichi chikulingaliridwa mu yankho lake: “Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera ine ndikhale m’zache za Atate wanga?” Iye sanali kuchita mwamwano. Mawu ake anangovumbulutsa chabe kudabwa kwake pa chenicheni chakuti makolo ake sanadziwe kumene iwo akanamupeza iye. Inali nkhani yofala ya kusamvana yomwe makolo ambiri a ana okula kumene amayamikira.—Luka 2:49.
Taganizirani za kudera nkhawa kwa Yosefe ndi Mariya pamapeto a tsiku loyamba, pamene anapeza kuti Yesu anali kusowa. Ndipo tangolingalirani kudera nkhawa kwawo kowonjezereka mkati mwa masiku awiri omwe iwo anali kufunafuna Yesu ku Yerusalemu. Komabe, chinapezeka kuti kumphunzitsa kwawo Yesu kunalipira mu kudera nkhawa kopambanitsa kumeneko. Yesu sanapite mu mayanjano oipa. Iye sanali kudzetsa manyazi pa makolo ake. Pamene iwo anamupeza Yesu, iye anali “mkachisi, anali kukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake.”—Luka 2:46, 47.
Chenicheni chakuti iye anawononga nthawi yake mu njira imeneyi, chiri chitsimikiziro chabwino cha kumvetsetsa kwake maprinsipulo a Malemba, ndiponso chimanena bwino ponena za kumphunzitsa kwa Yosefe ndi Mariya kufika ku nsonga imeneyo. Komabe, kachitidwe ka Mariya kamawoneka kofala kaamba ka mayi wodera nkhawa: poyamba, mpumulo pokhala atampeza mwana wake ali bwino; kenaka kulongosola malingaliro ake akudera nkhawa ndi kuvutika maganizo: “Mwanawe, wachitiranji ife chotero? Taona atate wako ndi ine tinalikufunafuna iwe ndi kuda nkhawa.” (Luka 2:48) Sichiri chosayembekezereka kuti Mariya analankhula izi pamaso pa Yosefe mkulongosola kudera nkhawa kwa makolo onse awiri. Achichepere ambiri owerenga nkhaniyi mwachiwonekere anganene kuti: “Amenewo alidi monga mayi wanga!”
Maphunziro Ophunziridwa
Kodi ndi maphunziro otani amene tingaphunzire kuchokera ku chokumana nacho ichi? Achichepere ali oyedzamira ku kuganiza kuti makolo awo amadziwa zimene iwo akulingalira. Iwo kawirikawiri amamvedwa akunena kuti: “Koma ndinaganiza kuti munadziwa.” Makolo, ngati mwana wanu wachichepere anayamba wanenapo zimenezi pamene panali kusamvana, inu simuli woyamba kukhala nalo vutolo.
Pamene ana akufika ku msinkhu wa unamwali, mokulira amakhala osadalira kwenikweni pa makolo awo. Kusintha kumeneku kuli kwachibadwa, ndipo makolo akafunikira kupanga masinthidwe kulola kaamba ka iko. Komabe ngakhale ndi maphunziro apamwamba kwambiri, kusamvana kungabuke ndipo makolo adzagawanamo mkudandaula. Koma, ngati atsatira chitsanzo chabwino cha Yosefe ndi Mariya, pamene chisokonezo chitabuka, maphunziro awo abwino adzaimika ana awo ku mbali yabwino.
Mwachiwonekere makolo a Yesu anapitiriza kugwira ntchito limodzi naye mpaka mu zaka zake za unyamata. Pambuyo pachochitika chomwe tangochilingaliracho, iye mogonjera “anatsika nawo pamodzi” ku mzinda wake wa ku mudzi ndipo “anapitirizabe kugonjera kwa iwo.” Ndi chotulukapo chotani? “Yesu anakulabe mu nzeru ndi msinkhu, ndi mchiyanjo cha Mulungu ndi cha anthu.” Chotero nkhaniyi inali ndi mapeto osangalatsa. (Luka 2:51, 52) Makolo amene amatsatira chitsanzo cha Yosefe ndi Mariya, omwe akuthandiza ana awo kukula mu nzeru ya umulungu omwe akuwapatsa iwo mkhalidwe wabwino wa panyumba ndi kuwawonetsa iwo ziyambukiro zabwino za mayanjano a umulungu, zimawonjezera kuyenerera kwakuti chinthu chofananacho chidzachitika kumbadwa zawo. Ana otero mokulira ali oyenerera kusangalala ndi moyo wachimwemwe pamene akula mu thayo, laukulu wa Chikristu.
Mawu a M’munsi
a Chigriki choyambirira pano chimatenga lingaliro lakuti “kudzazidwa ndi nzeru” kwa Yesu kunali kachitidwe kopitiriza, kopita patsogolo.