Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Paskha Womalizira wa Yesu Ali Pafupi
PAMENE Lachiŵiri, Nisani 11, likuyandikira kumapeto, Yesu amaliza kuphunzitsa atumwi ake pa Phiri la Azitona. Linali tsiku lotanganitsa, ndi lotopetsa chotani nanga! Tsopano, mwinamwake pobwerera ku Betaniya kukagona, iye awuza atumwi ake kuti: “Mudziwa kuti akapita masiku aŵiri, Paskha ufika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kupachikidwa.”
Tsiku lotsatira, Lachitatu, Nisani 12, mwachiwonekere Yesu akukhala m’malo abata ndi atumwi ake. Dzulo lake, anali adadzudzula poyera atsogoleri achipembedzo, ndipo iye akuzindikira kuti iwo akufunafuna kumupha. Chotero pa Lachitatu sakuwonekera poyera, popeza kuti safuna chirichonse kusokoneza kukondwerera kwake Paskha ndi atumwi ake madzulo otsatira.
Pakali pano, akulu ansembe ndi akulu a anthuwo asonkhana m’bwalo la mkulu wansembe, Kayafa. Pokhala okwiitsidwa ndi kuwukira kwa Yesu ladzulo, iwo akupanga makonzedwe omgwira mwanjira yamachenjera ndikuti amuphe. Komabe iwo apitiriza kuti: “Pa dzuwa la chakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.” Iwo akuwopa anthu, amene akumkonda Yesu.
Pamene atsogoleri achipembedzo apanga chiwembu choipa chakupha Yesu, iwo akulandira mlendo. Mowadabwitsa, iye ali mmodzi wa atumwi a Yesu, Yudase Isikariote, mwa amene Satana waika lingaliro lalikulu la kupereka Mbuye wake! Iwo akondwera motani nanga pamene Yudase awafunsa kuti: “Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu?” Iwo mwachimwemwe avomerezana kumlipira ndalama zasiliva 30, mtengo wa kapolo mmodzi mogwirizana ndi pangano la Chilamulo cha Mose. Kuyambira pamenepo, Yudase afunafuna mpata wabwino wakumperekera Yesu kwa iwo popanda khamu la anthu.
Nisani 13 iyamba Lachitatu dzuŵa litaloŵa. Yesu anafika kumene kuchokera ku Yeriko pa Lachisanu, motero uwu ndi usiku wachisanu ndi chimodzi ndi womalizira umene akukhala mu Betaniya. Tsiku lotsatira, Lachinayi, makonzedwe omalizira a Paskha adzayenera kupangidwa, imene iyambika pa kuloŵa kwa dzuŵa, pamene mwana wa nkhosa wa Paskha ayenera kuphedwa kenaka nkuwotchedwa wathunthu. Kodi nkuti kumene adzachitira phwandolo, ndipo kodi ndani adzapanga makonzedwewo?
Yesu sanapereke tsatanetsatane wa zimenezo, mwinamwake kuwopera kuti Yudase angadziŵitse akulu ansembe kotero kuti amgwire Yesu mkati mwa phwando la Paskha. Koma tsopano, mwinamwake kuchiyambi kwa Lachinayi masana, Yesu atumiza Petro ndi Yohane kuchokera ku Betaniya, akumati: “Pitani mutikonzere ife Paskha, kuti tidye.”
Iwo amufunsa kuti: “Mufuna tikakonzere kuti?”
Yesu awalongosolera nati: “Mutaloŵa m’mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akaloŵako iye. Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mpunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chiri kuti, m’mene ndikadye Paskha pamodzi ndi ophunzira anga? Ndipo iyeyo adzakuwonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.”
Mosakaikira mwini nyumbayo ngophunzira wa Yesu amene mwinamwake akuyembekezera Yesu kuti amupemphe kugwiritsira ntchito nyumba yake kaamba ka chochitika chapadera chimenechi. Momvana ndi izi, pamene Petro ndi Yohane afika mu Yerusalemu, iwo apeza zonse ziri ndendende monga mmene Yesu ananeneratu. Chotero aŵiriwo atsimikizira kukonza mwana wankhosa ndi kupanga makonzedwe ena onse kusamalira zofunika za anthu 13 okondwerera Paskhayo, Yesu ndi atumwi ake 12. Mateyu 26:1-5, 14-19; Marko 14:1, 2, 10-16; Luka 22:1-13; Eksodo 21:32.
◆ Kodi Yesu akuchitanji mwachiwonekere pa Lachitatu, ndipo nchifukwa ninji?
◆ Kodi ndimsonkhano wanji umene ukuchitidwira kunyumba ya mkulu wansembe, ndipo n’chifuno chanji chimene Yudase akuchezera atsogoleri achipembedzowo?
◆ Kodi ndani amene Yesu akuwatumiza mu Yerusalemu pa Lachinayi, ndipo kaamba ka chifuno chanji?
◆ Kodi otumidwawa akupezanji zimene zikuvumbulanso mphamvu zozizwitsa za Yesu?