Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Mkangano Ubuka
POYAMBIRIRA madzulowo, Yesu anaphunzitsa phunziro labwino la utumiki wodzichepetsa mwa kusambitsa mapazi a atumwi ake. Pambuyo pake, anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake yoyandikirayo. Tsopano, makamaka polingalira za zimene zangochitika kumene, chochitika chodabwitsa chikuwonekera. Atumwi ake akuyamba kukangana kopsetsana mtima ponena zakuti ndani pakati pawo akuwonekera kukhala wamkulu! Mwachiwonekere, uwu uli mbali ya mkangano wosatha.
Kumbukirani kuti pambuyo pa kusandulika kwa Yesu paphiripo, atumwiwo anatsutsana za amene anali wamkulu pakati pawo. Ndiponso, Yakobo ndi Yohane anapempha malo aulemu mu Ufumuwo, zomatulukira mumkangano wowonjezereka pakati pa atumwiwo. Tsopano, pausiku wake womalizira limodzi nawo, Yesu ayenera kukhala wachisoni motani nanga kuwona iwo akukangananso! Kodi iye akuchitanji?
Mmalo modzudzula atumwiwo pa kudzisungira kwawoko, kachiŵirinso Yesu akulingalira nawo moleza mtima: “Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, ochitira zabwino. Koma sipadzatero ndi inu; . . . pakuti wamkulu ndani, iye wakuseyama pachakudya kapena wakutumikirapo? Sindiye wakuseyama pachakudya kodi?” Kenaka, akuwakumbutsa za chitsanzo chake, akuti: “Koma ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.”
Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwawo, atumwiwo amamatira kwa Yesu mkati mwa ziyeso zake. Chotero iye akuti: ‘Ndikupanga pangano ndi inu, monga mmene Atate wapangira pangano ndi ine, la Ufumu.’ Pangano laumwini limeneli pakati pa Yesu ndi atsatiri ake okhulupirika limawagwirizanitsa kwa iye kukhala ndi phande muulamuliro wake wachifumu. Chiŵerengero chochepa chabe cha 144,000 pomalizira pake ndicho chikuloŵetsedwa m’pangano la Ufumu limeneli.
Ngakhale kuti atumwiwo akupatsidwa chiyembekezo chapadera chimenechi cha kugaŵana ndi Kristu muulamuliro wa Ufumu, iwo pakali pano ali ofooka mwauzimu. “Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha ine usiku uno,” akutero Yesu. Akuuza Petro kuti Iye wampempherera, Yesu akulangiza kuti: “Pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.”
“Tiana,” Yesu akulongosola, “katsala kanthaŵi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndimkako ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano. Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati mulinacho chikondano wina ndi mnzake.”
Petro akufunsa kuti: “Ambuye, mumuka kuti?”
“Kumene ndimukako sungathe kunditsata ine tsopano,” akuyankha motero Yesu, “koma, udzanditsata bwino lomwe.”
“Ambuye, sindingathe kukutsatani inu tsopano chifukwa ninji?” Petro afuna kudziŵa. “Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha inu.”
“Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha ine?” Yesu akufunsa. “Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, asanalire tambala udzandikana ine katatu.”
Petro akutsutsa naati: “Ngakhale ine ndikafa ndi inu, sindidzakukanani inu iyayi.” Ndipo pamene atumwi ena akugwirizana naye kunena zofananazo, Petro akudzitama naati: “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha inu, ine sindidzakhumudwa nthaŵi zonse.”
Akumasonya kunthaŵi pamene anatumiza atumwiwo paulendo wokalalikira ku Galileya popanda thumba la ndalama kapena kamba, Yesu akufunsa: “Munasoŵa kanthu kodi?”
“Iyayi,” akuyankha motero.
“Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe,” iye akutero “ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga. Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwaniritsidwa mwa ine, ndipo anaŵerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa ine ziri nacho chimaliziro.”
Yesu akusonya kunthaŵi pamene adzapachikidwa limodzi ndi ochita zoipa, kapena osayeruzika. Iye akusonyezanso kuti pambuyo pake atsatiri ake adzayang’anizana ndi chizunzo choopsa. “Ambuye, tawonani, malupanga aŵiri siawa,” iwo akutero.
“Chakwanira,” iye akuyankha. Monga mmene tidzawonera, kukhala kwawo ndi malupanga kudzalola Yesu kuphunzitsa phunziro lina lofunika pasanapite nthaŵi yaitali. Mateyu 26:31-35; Marko 14:27-31; Luka 22:24-38; Yohane 13:31-38; Chivumbulutso 14:1-3.
◆ Kodi nchifukwa ninji mkangano wa atumwiwo uli wodabwitsa kwambiri?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akusamalirira mkanganowo?
◆ Kodi nchiyani chimene chikukwaniritsidwa ndi pangano limene Yesu akulipanga ndi ophunzira ake?
◆ Kodi Yesu akupereka lamulo latsopano lotani, ndipo kodi nlofunika motani?
◆ Kodi Petro akusonyeza chidaliro chopambanitsa chotani, ndipo kodi Yesu akunenanji?
◆ Kodi nchifukwa ninji malangizo a Yesu onena za kunyamula thumba la ndalama ndi thumba la kamba ali osiyana ndi aja amene anawapereka poyambirira?