Kodi Mumakhala Wokonzeka Kusintha?
1. Popeza zinthu padzikoli zikusintha, kodi nafenso tikufunika kuchita chiyani?
1 Pa 1 Akorinto 7:31, Baibulo limayerekezera dzikoli ndi zinthu zochitika pabwalo la sewero pomwe ochita sewero osiyanasiyana akubwera n’kumachita zigawo zosiyanasiyana za sewero. Popeza zinthu padzikoli zikusintha, nafenso nthawi zonse tifunika kumasintha njira zolalikirira komanso nthawi imene timalalikira. Kodi inuyo mumakhala wokonzeka kusintha?
2. Kuti tiziyendera limodzi ndi gulu, n’chifukwa chiyani tiyenera kusintha?
2 Njira Zolalikirira: Kuyambira kale, Akhristu akhala akusintha njira zimene amalalikirira. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankatumiza ophunzira ake pa ulendo woyamba kuti akalalikire, anawauza kuti asatenge chakudya kapena ndalama. (Mat. 10:9, 10) Komabe kenako Yesu anasintha malangizowo. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti ophunzira akewo adzatsutsidwa komanso ntchito yolalikira idzafalikira kumadera ena. (Luka 22:36) Zaka za m’mbuyomu gulu la Yehova linkagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana polalikira malinga ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Mwachitsanzo, linkagwiritsa ntchito galimoto zokhala ndi zokuzira mawu, makadi olalikirira, ndiponso kuulutsa mawu pawailesi. Masiku ano popeza anthu ambiri sapezeka pakhomo, gulu limatilimbikitsa kuti kuwonjezera pa kulalikira kunyumba ndi nyumba, tizilalikiranso m’malo amene mumapezeka anthu ambiri komanso mwamwayi. Timalimbikitsidwanso kuti ngati anthu a m’gawo lathu amakhala kuntchito masana, tizipita kunyumba za anthu nthawi yamadzulo. Pamene galeta la Yehova likuyenda, kodi inunso mukuyenda nalo limodzi?—Ezek. 1:20, 21.
3. Kodi kusintha kumatithandiza bwanji kuti tizilalikira mogwira mtima m’gawo lathu?
3 Ulaliki Wanu: Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu a m’gawo lanu akuda nazo nkhawa kwambiri? Kodi ndi mavuto azachuma, am’banja kapena nkhondo? Ndi bwino kumadziwa mmene zinthu zilili m’dera lathu komanso mavuto amene anthu ambiri akukumana nawo n’cholinga choti tikonzekere ulaliki umene ungawagwire mtima. (1 Akor. 9:20-23) Eninyumba akamafotokoza maganizo awo, si bwino kuwadula n’kumangopitiriza kufotokoza ulaliki umene tinakonza. M’malomwake tiyenera kusintha ulaliki wathuwo kuti ugwirizane ndi zinthu zomwe iwo akuda nazo nkhawa.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha mwamsanga njira zolalikirira?
4 Posachedwapa “zochitika” za padzikoli zifika kumapeto ndipo chisautso chachikulu chiyamba. Baibulo limati: “Nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:31) Choncho m’pofunikadi kuti tizikhala okonzeka kusintha n’cholinga choti tithe kuthandiza anthu ambiri pa nthawi yochepa imene yatsalayi.