Mutu 12
Kulemekeza Ulamuliro Nkofunika kaamba ka Moyo Wamtendere
1-3. (a) Kodi nchiyani chimene chachititsa kufalikira kwakukulu kwa kukanidwa kwa ulamuliro m’tsiku lathu? (b) Kodi mkhalidwewo umasonyezedwa m’njira zosiyanasiyana zotani? (c) Kodi nkuti kumene ziyambukirozo zimamvedwa?
PALI mzimu wakudzigangira umene uli wofalikira m’dziko lamakono. Kusadalira ulamuliro kofalikira kwabuka, makamaka pakati pa awo obadwa chiyambire Nkhondo Yadziko II. Chifukwa ninji? Choyamba, makolo awo anawona chitsenderezo pamlingo wosafanana ndi wina uliwonse, kudzanso njira zotsendereza ndi zoipa zochitidwa ndi awo okhala muulamuliro. Anayambitsa lingaliro lokaikira ulamuliro. Chifukwa cha chimenecho, ambiri a iwo, atakhala makolo, sanakhomereze mwa ana awo kulemekeza ulamuliro. Ndiponso zosalungama za akuluakulu aboma zowonedwa ndi anawo sizinawongole mkhalidwe. Monga choturukapo, kusalemekeza ulamuliro kwakhala kofala.
2 Kupanda ulemu kumeneku kukusonyezedwa m’njira zosiyanasiyana. Nthawi zina kumasonyezedwa mwa mtundu wakavalidwe kapena kapesedwe kamene kamasonyeza kukanidwa kwamiyezo yovomerezedwa. Kungalowetsemo kunyozera poyera apolisi, kapena ngakhale chiwawa ndi kukhetsa mwazi. Koma sikumalekezera pa zimenezi. Ngakhale pakati pa awo amene samasonyeza poyera njira zowonekera kwambiri izi, ochuluka amanyalanyaza kapena kulumpha malamulo ngati samavomereza malamulo otero kapena kuwapeza kukhala ovutitsa.
3 Mkhalidwewu waipitsa kwambiri khalidwe m’banja, m’masukulu, pamalo antchito, ndi pokumana ndi akuluakulu aboma. Mowonjezerekawonjezereka, anthu safuna kuti munthu aliyense awauze chochita. Amalakalaka kuchita chimene amakhulupilira kukhala ufulu wokulirapo. Mutayang’anizana ndi mkhalidwewo, kodi mudzachitanji?
4. Mwazimene timachita m’nkhani imeneyi, kodi timasonyeza lingaliro lathu pankhani yotani?
4 Njira yanu idzasonyeza pamene mwaima ponena za nkhani yaufumu wachilengedwe chonse ya Yehova. Kodi mumalemekezadi Yehova monga Magwero amtendere weniweni ndi chisungiko? Kodi mudzafunafuna ndi kugwiritsira ntchito m’moyo wanu chimene Mawu ake amalangiza? Kapena kodi mudzayendera limodzi ndi awo amene modzigangira amapanga zosankha zawo ponena za chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa?—Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9.
5. (a) Kodi nchiyani chimene kawirikawiri chimatulukapo m’kutsatira chitsogozo cha anthu amene amalonjeza “ufulu”? (b) Kodi munthu amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhala waufulu motani?
5 Chidziŵitso cholongosoka Chabaibulo chingakutetezereni kukusokeretsedwa ndi awo amene, pamene kuli kwakuti ‘amalonjeza ufulu, iwo eniwo akukhala monga akapolo achivundi.’ Kutsatira chitsogozo cha anthu otero kukangokuikani chabe mu mkhalidwe waukapolo umodzimodziwo. (2 Petro 2:18, 19) Ufulu weniweni ungapezedwe kokha mwakuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Lamulo lake laumulungu liri “lamulo langwiro limene liri laufulu.” (Yakobo 1:25, NW) Ichi chinganenedwe chifukwa chakuti Yehova samatiletsa mosayenelera, kutipanikiza ndi malamulo amene samatumikira chifuno chopindulitsa. Koma lamulo lake limapereka mtundu wachitsogozo chimene chimabweretsa ufulu, mtendere, ndi chisungiko zozikidwa pa unansi woyenera ndi Mulungu ndipo ndi munthu mnzathu.
6, 7. (a) Kodi ndani amene ali mu m’khalidwe wabwino koposa kuchitapo kanthu ponena za kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa ulamuliro? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera chimene chimachitika kwa anthu amene amanyalanyaza malamulo?
6 Koposa munthu wina aliyense, Mulungu amadziŵa ukulu wa chisalungamo cha munthu ndi kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa ulamuliro. Ndipo iye wapereka Mawu ake kuti mosasamala kanthu za mmene awo otsendereza angakhalire apamwamba, adzawaimba mlandu. (Aroma 14:12) M’nthawi yoikika ya Mulungu, “oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” (Miyambo 2:22) Koma sizidzachita ubwino uliwonse kwa ife ngati tikhala osadekha ndi kuswa malamulo.—Aroma 12:17-19.
7 Pausiku wakuperekedwa ndi kumangidwa kwake, Yesu anagogomezera ichi kwa atumwi ake. Chifukwa cha mikhalidwe m’dzikomo, kuphatikizapo kukhalamo kwazirombo, anthu kaŵirikaŵiri ananyamula zida. Chotero pachochitika chimenecho panali malupanga aŵiri pakati pa atumwi a Yesu. (Luka 22:38) Kodi chinachitika nchiyani? Eya, iwo anawona kupotozedwa kwachiwawa kwa chiweruzo cholungama pamene Yesu anali kumangidwa popanda chifukwa. Chotero mtumwi Petro mopsa mtima anasolola lupanga lake nadula khutu la mmodzi wa amunawo. Koma Yesu anabwezeretsa khutu lodulidwalo nadandaulira Petro kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Anthu ambiri, ngakhale m’tsiku lathu, akanapulumutsidwa ku imfa yamwamsanga mwakutsatira chilangizo ichi.—Miyambo 24:21, 22.
Lingaliro Loyenera la Ulamuliro Wadziko
8. (a) Monga momwe kwalongosoledwera pa Aroma 13:1, 2 kodi ndimotani mmene Akristu ayenera kuwonera olamulira adziko? (b) Kodi nchiyani chimene chimatanthauzidwa ndi mawu akutiwo “amakhala mmalo awo aang’ono mololedwa ndi Mulungu”?
8 Polembera kalata Akristu m’Roma, mtumwi Paulo anauziridwa ndi Mulungu kulongosola mmene iwo anayenera kudzisungira mogwirizana ndi olamulira audziko. Iye analemba kuti: “Munthu aliyense agonjere olamulira akulu, pakuti palibe ulamuliro wina kusiyapo wochokera kwa Mulungu; olamulira alipowa amakhala m’malo awo ang’ono mololedwa ndi Mulungu. Chifukwa chake iye amene akutsutsa ulamulirowo watenga malo otsutsa kakonzedwe ka Mulungu; awo amene atenga malo okatsutsa adzalandira chilango kwa iwo eni.” (Aroma 13:1, 2, NW) Kodi izi zikutanthauza kuti Mulungu waika muulamuliro olamuliro adziko amenewa? Baibulo motsimikizirika limayankha kuti ayi! (Luka 4:5, 6; Chivumbulutso 13:1, 2) Koma iwo alipo mololedwa ndi iye. Ndipo ‘malo ang’ono’ amene iwo akhala nawo mkati mwa mbiri ya anthu anatsimikiziridwa ndi Mulungu. Kodi malo antchitowo akhala chiyani?
9. Ngakhale ngati akuluakulu aboma achita machitidwe olakwa, kodi nchifukwa ninji ife tingawasonyeze ulemu?
9 Lemba limene langogwidwa mawu kumenelo limanena kuti ali “akulu.” Motero akuluakulu aboma sayenera kuchitiridwa mopanda ulemu. Malamulo operekedwa ndi iwo sayenera kunyalanyazidwa. Ichi sichitanthauza kuti inu kwenikweni mumasilira anthuwo, ndi kuti mumavomereza kuipa kulikonse kumene iwo angalowetsedwemo. Koma ulemu umasonyezedwa moyenelera chifukwa cha malo antchito amene iwo ali nawo.—Tito 3:1, 2.
10. Kodi ndimotani mmene kukhomedwa kwamisonkho kuyenera kuwonedwera, ndipo chifukwa ninji?
10 Kwakukulukulu, malamulo adziko ngopindulitsa. Iwo amathandiza kusungitsa bata ndipo amatsimikiziritsa mlingo wachitetezo cha anthu ndi chuma chawo. (Aroma 13:3, 4) Ndiponso, kaŵirikaŵiri maboma amapereka misewu, utumiki woyeretsa, chinjirizo lamoto, maphunziro, ndi mautumiki ena amene amapindulitsa anthu. Kodi iwo ayenera kulipilidwa kaamba ka mautumiki amenewa? Kodi ife tiyenera kukhoma misonkho? Kaŵirikaŵiri funsoli limadzutsa malingaliro amphamvu chifukwa cha misonkho yokwera ndi kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwakaŵirikaŵiri kwandalama zaboma. Namonso, m’nthawi ya Yesu, funsoli linali ndi matanthauzo andale zadziko. Koma Yesu sanakhale ndi lingaliro lakuti mkhalidwe umene unalipowo unafunikiritsa kukana kulipira. Polankhula zandalama zimene zinali zitasulidwa ndi Kaisara wa Roma, iye anati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:17-21; Aroma 13:6, 7) Ayi, Yesu sanapereke lingaliro lakuti munthu aliyense akhale lamulo kwa iyemwini.
11, 12. (a) Kodi ndimotani mmene malemba amasonyezera kuti pali ulamuliro wina woti ulingaliridwe? (b) Kodi mukanachitanji ngati olamulira adziko anaturutsa malamulo amene anawombana ndi zofuna za Mulungu, ndipo chifukwa ninji?
11 Komabe, Yesu anasonyeza kuti “Kaisara,” boma ladziko, sanali ulamuliro wokha woyenera kulingaliridwa. “Olamulira akulu” sali akulu kwa Mulungu ndiponso saali olingana naye. Mosemphana ndi zimenezo, iwo ali aang’ono kwambiri kwa iye. Chotero ulamuliro wawo ngwochepa, suli wotheratu. Chifukwa cha chimenechi, kaŵirikaŵiri Akristu ayang’anizana ndi chosankha chovuta. Chiri chosankha chimene inunso muyenera kuyang’anizana nacho. Pamene anthu okhala mu ulamuliro adzifunsilira zimene ziri za Mulungu, kodi mudzachitanji? Ngati iwo aletsa chimene Mulungu amalamula, kodi mudzamvera yani?
12 Atumwi a Yesu mwaulemu koma mwamphamvu analongosola kaimidwe kawo kuziŵalo za khoti lalikulu mu Yerusalemu kuti: “Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziwona ndi kuzimva. . . . Tiyenera kumvera Mulungu koposa Anthu.” (Machitidwe 4:19, 20; 5:29) Nthawi zina maboma apereka ziletso m’nthawi zamaupandu, ndipo izi nzomvekera. Koma nthawi zina ziletso zaboma zingalinganizidwire kudodometsa kulambira kwathu Mulungu ndi kukupangitsa kukhala kosatheka kukwaniritsa mathayo operekedwa ndi Mulunguwo. Pamenepo chiyani? Mawu ouziridwa a Mulungu amayankha kuti: ‘Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu’?
13, 14. (a) Kodi tiyenera kukhala osamalitsa motani kusakhala osamvera malamulo adziko kaamba ka zifukwa zathu chabe? (b) Kuchokera m’Malemba, sonyezani zifukwa za chimenechi.
13 Ngakhale kuli kwakuti kulemekeza thayo iri kwa Mulungu kungaombane ndi zimene “Kaisara,” amafuna, izi ziri zosiyana kwambiri ndi kuswa modzigangira malamulo amene sitimavomerezana nawo. Nzowona kuti, mwalingaliro lathu, malamulo ena angawonekere kukhala osafunika kapena oletsa mosayenera. Koma zimenezo sizimalungamitsa kunyalanyaza malamulo amene samaombana ndi malamulo a Mulungu. Bwanji ngati anthu onse anamvera kokha malamulo amene anawalingalira kukhala opindulitsa kwa iwo? Kukanachititsadi chipolowe.
14 Panthawi zina munthu angalingalire kuti angathe kunyalanyaza ulamuliro ndi kuchita zofuna zake chifukwa chakuti sikukuwonekera kuti adzagwidwa ndi kulangidwa. Koma pali ngozi yaikulu mu ichi. Pamene kuli kwakuti kunyalanyazidwa kwalamulo poyamba kungalowetsemo nkhani zazing’ono, kusalangidwa kwa munthuyo kungampatse chidaliro chakuchita kusayeruzika kokulirapo. Monga momwe Mlaliki 8:11 amalongosolera kuti: “Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.” Koma kodi chifukwa chenicheni chakumverera lamulo chiri chabe kuwopa chilango kaamba ka kusamvera? Kwa Mkristu, payenera kukhala chochititsa champhamvu kwambiri. Mtumwi Paulo anachitcha “chifukwa chokakamiza”—chikhumbo chakukhala ndi chikumbumtima choyera. (Aroma 13:5, NW) Munthu amene chikumbumtima chake chaphunzitsidwa malamulo amakhalidwe abwino Amalemba amadziwa kuti kulondola njira yakusayeruzika kukakhala kuchita “kotsutsa kakonzedwe ka Mulungu.” Mosasamala kanthu kuti kaya anthu ena amadziŵa zimene tikuchita, Mulungu amadziŵa, ndipo ziyembekezo zathu za moyo wamtsogolo zimadalira pa iye.—1 Petro 2:12-17.
15. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kutsogoza munthu mkhalidwe lake kulinga kwa mphunzitsi wasukulu kapena wolemba ntchito? (b) Mwanjira imeneyi, kodi timapewa kusonkhezeredwa ndi mzimu wayani?
15 Ziri chimodzimodzi ndi za lingaliro la wachichipere kulinga kwa mphunzitsi wapasukulu ndi lingaliro la wachikulire kulinga kwa womlemba ntchito wake. Chenicheni chakuti anthu otizinga amachita zinthu zolakwa sichiyenera kukhala chopimira. Kaya mphunzitsi kapena wolemba ntchito akudziŵa zimene timachita sikuyenera kupanga kusiyana kulikonse. Funso nlakuti, Kodi nchiyani chimene chiri choyenera? Kodi nchiyani chimene chiri chokondweretsa Mulungu? Kachiŵirinso, ngati tipemphedwa kuchita zimene siziombana ndi malamulo a Mulungu kapena malamulo amakhalidwe abwino olungama, timavomereza. Kaŵirikaŵiri aphunzitsi apasukulu ali kaŵirikaŵiri oimira a boma ladziko, ndipo motero ali oimira a “olamulira aakulu,” ndipo chotero amayenelera ulemu. Ndipo ponena za olemba ntchito akudziko, lamulo lamakhalidwe abwino Labaibulo pa Tito 2:9, 10 lingagwiritsiridwe ntchito, ngakhale kuli kwakuti pamenepo Paulo analemba za unansi wosiyana, uja wa akapolo ndi ambuyawo. Paulo anati: “Akondweretseni bwino lomwe, . . . mukumasonyeza kukhulupirika kwabwino mokwanira, kotero kuti [inu] mukakometse chiphunzitso cha mpulumutsi wathu Mulungu, m’zinthu zonse.” (Tito 2:9, 10, NW) Potero, timapewa chisonkhezero cha Satana, amene mzimu wake “ukuchita mwa ana akusamvera,” ndipo timapanga maunansi amtendere ndi anthu anzathu.—Aefeso 2:2, 3.
Ulamuliro M’kati mwa Banja
16. Kodi ndichofunika chotani kaamba ka moyo wabanja wogwirizana chimene chikulongosoledwa pa 1 Akorinto 11:3?
16 Banja ndiwo malo ena kumene kusonyeza ulemu kwa olamulira kungapangitse maunansi amtendere. Kaŵirikaŵiri kwambiri ulemu wabwino wotero umasoŵeka, kukumachititsa kunyonyosoka kwamaunansi abanja ndipo kaŵirikaŵiri kusweka kwa mabanja. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuwongolera mkhalidwewo? Lamulo la makhalidwe abwino, monga momwe lalembedwera pa 1 Akorinto 11:3, liri ndi yankho: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wamkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.”
17. (a) Ponena za umutu, kodi malo antchito a mwamuna ndiotani? (b) Kodi ndichitsanzo chabwino chotani ponena za umutu wa mwamuna chimene Kristu anapereka?
17 Tawonani kuti mawu awa akakonzedwe ka Yehova samasonya choyamba ku umutu wamwamuna. Mmalomwake, amasonya ku chenicheni chakuti pali munthu wina amene mwamuna ayenera kuyang’anako kaamba ka chitsogozo, wina wake amene chitsanzo chake iye ayenera kuchitsatira. Wina wake ameneyo ndiye Yesu Kristu. Ndiye mutu wamwamuna. Ndipo m’zochita zake ndi mpingo wake, umene ukuyerekezeredwa ndi mkwatibwi, Kristu anasonyeza njira yopangira chipambano chaumutu wa mwamuna. Chitsanzo chake chabwino kwambiricho chinasonkhezera kulabadira kofunitsitsa mwa atsatiri ake. Pamene anatsogoza, mmalo mwakukhala waukali ndi wovuta kwa otsatira ake, Yesu anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima,” kotero kuti iwo anapeza mpumulo wa miyoyo yawo. (Mateyu 11:28-30) Kodi iye anawanyoza chifukwa cha zolakwa zawo? Mosemphana ndi zimenezo, iye anawapatsa uphungu mwachikondi natayadi moyo wake kuwayeretsera machimo. (Aefeso 5:25-30) Ha ndidalitso lotani nanga ku banja lirilonse kukhala ndi mwamuna amene amayesayesa mowona mtima kutsatira chitsanzo chimenecho!
18. (a) Kodi mkazi angasonyeze m’njira zotani kuti iye amalemekeza ulamuliro wa mwamuna wake? (b) Kodi ndimotani mmene ana ayenera kusonyezera ulemu kumakolo awo, ndipo chifukwa ninji?
18 Pamene muli mutu woterowo m’banja, sikuli kovuta kwa mkazi kuyang’ana kwa mwamuna wake. Ndipo kumvera kumadza mosavutirapo konse kuchokera kwa ana. Koma palinso zochuluka zimene mkazi ndi ana angathandizire kuchimwemwe chabanja. Mwakukhala kwake waphamphu m’kusamalira banja ndiponso mwamzimu wogwirizana, mkaziyo amasonyeza kuti ali ndi “ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” Kodi zimenezo ziri choncho m’banja mwanu? (Aefeso 5:33; Miyambo 31:10-15, 27, 28) Ponena za ana kumvera kofunitsitsa kwa ponse pawiri atate ndi amayi kumasonyeza kuti iwo amalemekeza makolo awo monga momwe afunira Mulungu. (Aefeso 6:1-3) Kodi sipakanakhala mtendere wochuluka kwambiri ndi lingaliro lokulira la chisungiko chaumwini m’banja lotero koposa m’limene mulibe kulemekeza ulamuliro?
19. Ngati inu muli nokha m’banja amene amayesa kutsogozedwa ndi Mawu a Mulungu, kodi muyenera kuchitanji?
19 Mungathandize kupangitsa banja lanu kukhala malo otero. Kaya ziŵalo zina zisankha kuchilikiza njira za Yehova kapena ayi, inu mungatero. Enawo angalabadire kuchitsanzo chanu chabwino. (1 Akorinto 7:16; Tito 2:6-8) Ngakhale ngati iwo satero, zimene mukuchita zidzakhala monga umboni wakulungama kwa njira za Mulungu, ndipo chimenecho sindicho kanthu kena ka phindu lochepa.—1 Petro 3:16, 17.
20, 21. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti ulamuliro wa mwamuna ndi wa makolo suli wotheratu? (b) Chotero, kodi mkazi Wachikristu kapena ana okhulupirira angayang’anizane ndi chosankha chotani, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kuwasonkhezera?
20 Kumbukirani kuti kakonzedwe konse ka ulamuliro wabanja kanayambidwa ndi Mulungu. Motero amuna ayenera kukhala ogonjera kwa Kristu, akazi kwa amuna awo “popeza nkoyenera mwa Ambuye,” ndipo ana kwa makolo awo “pakuti kumeneku nkokondweretsa kwambiri mwa Ambuye.” (Akolose 3:18, 20; 1 Akorinto 11:3) Chotero Mulungu sangasiyidwe m’nkhaniyi, kodi angatero? Ichi chitanthauza kuti ulamuliro wa mwamuna pa mkazi wake, ndi makolo pa ana awo, uli wochepa. Ndiko kuti, ziŵalo zokwatirana Zachikristu ndi ana zimagonjera choyamba kwa Mulungu ndi Kristu, kumvera uphungu wawo. Poyamba kwa ziŵalo za muukwati zosakhulupilira kapena makolo lingaliro limenelo lingakhale losakondweretsa. Koma kwenikweni limachitira ubwino wawo, chifukwa chakuti lidzathandiza kupangitsa wa muukwati wokhulupirirayo ndi ana kukhala odalirika kwambiri ndi a ulemu.
21 Komabe, bwanji ngati mwamuna wabanja anafunsira kuti mkazi wake achite kanthu kena kamene sikakakhala “koyenera mwa Ambuye”? Zimene iye amachita zidzasonyeza kuti kaya iye kwenikweni “amawopa Mulungu wowona” kapena ayi. (Mlaliki 12:13) Momwemonso pamene ana ali achikulire mokwanira kuzindikira ndi kumvera Mawu a Mulungu. Ngati makolo awo akugwirizana nawo m’chikhumbo chawo chakutumikira Yehova, anawo ayenera kupanga chosankha chakuti kaya adzakhala okhulupirika kwa Mulungu kapena kugawana mkhalidwe wa makolo awo amene saali. (Mateyu 10:37-39) Koma kuphatikizapo pa thayo lawo loyambilira kwa Mulungu, ana ayenera kukhala ogonjera mu “chirichonse,” ngakhale ngati kungatanthauze kuchita zinthu zimene iwo samakonda. (Akolose 3:20) Njira iyi yakhalidwe ingakoperedi makolo awo ku makonzedwe a Yehova achipulumutso. Kulidi “kokondweretsa Ambuye” pamene chisonkhezero cha munthu chiri kukhulupirika kwa Yehova ndi njira zake zolungama, mmalo mwakusamvera kochititsidwa ndi mzimu wakusamvera.
Mu Mpingo Wachikristu
22, 23. (a) Kodi ndimotani mmene oyang’anira Achikristu amatumikilira ziŵalo za mpingo? (b) Chotero, kodi ndikhalidwe lotani limene Ahebri 13:17 amanena kuti tiyenera kukhala nalo kulinga kwa iwo?
22 Kukhulupirika kwa Yehova kofananako kuyenera kusonyezedwa mu mkhalidwe wathu kulinga ku mpingo wake Wachikristu ndi awo amene akuusamalira. Yehova wapereka oyang’anira kuweta “gulu lankhosa.” Iwo samalandira malipiro koma amadzipereka chifukwa cha nkhawa yowona mtima kaamba ka abale awo ndi alongo Achikristu. (1 Petro 5:2; 1 Atesalonika 2:7-9) Iwo amathandiza mpingo kuchita ntchito ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Ndiponso, pokhala ndi nkhawa kaamba ka chiŵalo chirichonse champingo, iwo amathandiza amenewa kuphunzira mmene angagwiritsirire ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo m’miyoyo yawo. Ndiponso, ngati chiŵalo chirichonse chitenga njira yolakwa popanda kuizindikira mokwanira, kuyesayesa kumapangidwa kumbweza. (Agalatiya 6:1) Ngati chiŵalocho chinyalanyaza uphungu Wamalemba ndi kupitirizabe m’kuchita cholakwa chachikulucho, oyang’anira amatsimikizira kuti iye akuchotsedwa. Chotero mpingo umatetezeredwa kuchiyambukiro chake choipa.—1 Akorinto 5:12, 13.
23 Moyamikira kakonzedwe ka Yehova kachikondi kameneka kutsimikizira mtendere pakati pa anthu ake, tiyenera kulabadira chilangizo chopezedwa pa Ahebri 13:17 chakuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.”
24, 25. (a) Kodi ndimotani mmene zimene akulu amaphunzitsa ziyenera kuyambukilira mmene timawawonera? (b) Kodi ndiliti ndipo ndikuti kumene tiyenera kugwiritsira ntchito zimene timaphunzitsidwa kuchokera m’Baibulo? Chifukwa ninji?
24 Baibulo limagogomezera kuti chifukwa chachikulu chimene oyang’anira kapena akulu awa amafunikilira ulemu ndicho chakuti iwo akuphunzitsa “Mawu a Mulungu.” (Ahebri 13:7; 1 Timoteo 5:17) Ndipo ponena zamphamvu ya “Mawu” amenewo, Ahebri 4:12, 13 amalongosola kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zifundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingalira ndi zitsimikizo zamtima. Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.”
25 Chotero chowonadi cha m’Mawu a Yehova chimavumbula kusiyana pakati pa zimene munthu angawonekere kukhala ndi zimenedi iye ali. Ngati iye ali ndi chikhulupiliro chowona mwa Mulungu ndi chikhumbo chowona chakukondweretsa Mlengi wake, chisonkhezero chake chidzasonyeza bwino lomwe “ulemelero wa Mulungu” ngakhale pamene sakuwonedwa ndi akulu ampingo. (Aroma 3:23) Iye sakanakhala ndi mbali m’kudzisungira kosagwirizana ndi Malemba kokha chifukwa chakuti sikuli pakati pa zolakwa zazikulu zimene munthu angachotsedwere mu mpingo. Chifukwa chake, ngati aliyense ali ndi chikhoterero chakupeputsa uliwonse wauphungu wopezedwa m’Mawu a Mulungu, iye afunikira kupenda mosamalitsa chimene kwenikweni chiri mkhalidwe wake kwa Mulungu. Kodi iye akukhala ngati munthu uja amene Salmo 14:1 imati: “Wauchitsiru amati”—ayi osati poyera,—koma “mu mtima mwake, ‘Kulibe Mulungu’”?
26, 27. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulingalira mwamphamvu “Mawu alionse” a Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene miyoyo yathu imayambukiridwira pamene ife tisonyeza kulemekeza ulamuliro motero?
26 Poyesedwa ndi Mdyerekezi, Yesu analengeza kuti: “Munthu ayenera kukhala ndi moyo . . . ndi mawu aliwonse oturuka mkamwa mwa Yehova.” (Mateyu 4:4, NW) Kodi inu mumakhulupilira kuti “Mawu aliwonse” a Yehova ali ofunika, kuti palibe alionse amene ayenera kunyalanyazidwa? Kumvera zina za zofunika za Yehova pamene zina zichitiridwa monga zosanunkha kanthu, sikuli kokwanira konse. Mwinamwake tikuchilikiza kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova kapena tikutenga mbali ya Mdyerekezi mwa kudziikira muyeso wathu wachimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa. Achimwemwe ali awo amene amasonyeza kuti amakondadi chilamulo cha Yehova.—Salmo 119:165.
27 Anthu oterowo samagwidwa ndi mzimu wogawanika wadziko. Ndiponso iwo samachita nawo khalidwe lochititsa manyazi la awo amene amakankhira pambali makhalidwe abwino. Kulemekeza Yehova kwakukulu ndi njira zake zolungama kumachititsa miyoyo yawo kukhala yokhazikika. Kuchitira ulemu Yehova ndi njira zake kotero kumawakhozetsa kukhala ndi ulemu woyenelera kaamba ka olamulira audziko, kumene kuli kofunika kaamba ka kukhala ndi moyo kwamtendere.
[Chithunzi patsamba 134]
Atumwi a Yesu anauza khoti lalikulu kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu”