Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Yerusalemu—Maziko a Zochitika za M’Baibulo
PAMENE kuli kwakuti mitundu yambiri iri ndi likulu, mzinda waukulu wokhala ndi mpando wa boma, ophunzira Baibulo angaganizire za Yerusalemu kukhala likulu la umunthu. Ichi chiri tero chifukwa chakuti zinthu zazikulu zimene zinachitika kumeneko ziri zofunika kwambiri kwa tonsefe.
Pamwambapa, mungawone kawonekedwe kamene mukanawona ngati mukanaimirira pa malo okwezeka kum’mwera kwa Yerusalemu.a Zigwa ziŵiri zimakumana cha pamene pali malo a mitengo yobiriŵira modera. Chigwa cha Kedroni chimabwera motsika kuchokera kulamanja; chakumadzulo, kapena kulamanzere, kuli Chigwa cha Hinomu, chimene chinadzutsa dzina la m’Baibulo la Gehena. (Mateyu 10:28; 23:33) Chapakati (powenekera m’malo owunikiridwa ndi dzuŵa kutsogolo kwa malinga alipowo) ndi pamene Mzinda wakale wa Davide unamangidwa. Mkati mwa malingamo muli zimango zosiyana ziŵiri za Chisilamu m’malo a mbiri yakale. Chapafupi kwambiri ndi khomalo pali nyumba yobiriŵira ya mawonekedwe a siliva ya msikiti, ndipo kumbuyo kwake kuli chimango chachikulu chomangidwa cha golidi cha Nyumba ya Thanthwelo.
Koma nchifukwa ninji Yerusalemu, ndipo makamaka malo olinganizidwa pamene zimango za nyumba ziŵirizo tsopano zikuimirira, ziyenera kukhala zofunika kwambiri kwa inu? Chabwino, ndi nkhani ya m’Baibulo yotani imene chithunzi cha nkhosa yamphongo yokodwa mu mtengo chimabweretsa ku malingaliro anu? Mwinamwake ija ya Abrahamu. Inde, anali iye yemwe anapita ndi mwana wake Isake ku Phiri la Moriya, limene mwachiwonekere linali kapena pafupi ndi malo a thanthwe lokwezeka pamene mukuwona nyumba ziŵirizo. Mwachikhulupiriro, Abrahamu anali wofunitsitsa kupereka nsembe mwana wake wokondedwa, koma mngelo anagwira dzanja lake. Kenaka Abrahamu anapeza “nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m’chiyangoyangomo” napereka nsembe iyi “m’malo mwa mwana wake.” Chotero kuyang’ana Yerusalemu kungabweretse m’malingaliro chochitika chochititsa nthumanzi chimenechi.—Genesis 22:1-13.
Nsembe zina zinadzakhalako pambuyo pake pamene Solomo anamanga kachisi yaikulu kwa Yehova pa malo olinganizidwa pamene zimango za nyumbazo ziri tsopano. (2 Mbiri 3:1) Yesani kulingalira Aisrayeli akubwera kuchokera m’mbali zonse za dziko ndi nsembe zawo za nyama kaamba ka mapwando a pa chaka. Lolemekezeka koposa la iwo linali Tsiku Lotetezera. Pa tsikulo, mbuzi imodzi inasankhidwa ndi kutumizidwa “kwa Azazeli m’chipululu,” mothekera kunsi m’Chigwa cha Kedroni ndipo kenaka kum’mwera cha kum’mawa m’chipululu cha Yudeya. Mbuzi ina ndi ng’ombe yamphongo zinaphedwa ndipo mwazi wawo unagwiritsiridwa ntchito m’kupereka nsembe kupanga chotetezera kaamba ka ansembe ndi anthu. Mwazi wina unatengedwa ngakhale kupyola nsalu yochinga kuloŵa m’Malo Opatulikitsa a kachisi. Chotero mungayang’ane pa chithunzi cha mzindawo ndi chimenecho m’malingaliro.—Levitiko 16:1-34.
Nsembe zonsezi m’Yerusalemu zinaloza kutsogolo ku nsembe yangwiro ya Yesu Kristu. Pa usiku wake womalizira pa dziko lapansi, umene unali chifupifupi nthaŵi ya mwezi wathunthu, Yesu anasonkhana ndi ophunzira ake kuchita phwando la Paskha woyenerera womalizira. Umu munali m’chipinda chapamwamba mmene mukulingaliridwa kukhala munali m’malo a pamwamba a mzindawo kulamanzere (kumadzulo) kwa malo a kachisi. Pambuyo pakuti Yesu wakhazikitsa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, anatenga atumwi ake kupita ku Phiri la Azitona, limene liri kudutsa Chigwa cha Kedroni, kum’mawa (kulamanja) kwa kachisi.—Luka 22:14-39.
Monga chothandizira kuwona ichi m’malingaliro, yang’anani pa chithunzi chiri pansichi, chimene chinatengedwa mopenya cha kum’mawa kuchokera mkati mwa Yerusalemu, mothekera kuchokera pa malo pamene Yesu anakhala ndi Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Kuchokera ku lingaliroli, mukuwona kunsi cha kumanzere nyumba (yobiriŵira m’kuwunika kwa mwezi) ya msikiti pa malo a phiri la kachisi. Kutsogolo kum’mawa kuli Chigwa cha Kedroni (pansi pa mzera wowonekera) ndipo kenaka mitengo ya Munda wa Getsemane. Chapamwamba kulamanja kuli Phiri la Azitona.
Mwezi udzakhala chifupifupi wathunthu pa March 22, 1989, pamene mipingo ya Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse idzasonkhana (pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa) kaamba ka Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, kukumbukira imfa yansembe ya Yesu.b Chonde konzani kukapezeka kumeneko. Pa tsiku limenelo, mungafune kusinkhasinkha pa zinazake za zochitika zakale zozikidwa mu Yerusalemu ndi kuzungulira iyo m’chigwirizano ndi kutsanulira moyo wake mu imfa kwa Yesu. Chotero Yesu analemekeza chilunjiko cha Yehova ndi kuwombola mtundu wa anthu okhulupirira kuchoka ku uchimo ndi imfa.—1 Akorinto 11:23-26; Ahebri 9:11-28.
[Mawu a M’munsi]
a 1989 Kalenda ya Mboni za Yehova iri ndi chithunzi chimenechi mu mlingo waukulu.
b Onani Nsanja ya Olonda, June 15,1977, tsamba 383 (Chingelezi), kaamba ka nsonga zowonjezereka kulinga ku kuŵerengera nthaŵi ya kuchita phwando la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.