Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuperekedwa ndi Kutengedwa
PAMENE Pilato, posonkhezeredwa ndi ulemu wachete wa Yesu wozunzidwayo, ayeseranso kummasula, ansembe aakulu akukwiya kopambanitsa. Iwo ngofunitsitsa kusalola china chirichonse kudodometsa cholinga chawo choipa. Chotero akuyambanso kufuula kwawo namati: ‘Mpachikeni, mpachikeni.’
‘Mtengeni iye inu nimumpachike,’ Pilato akuyankha motero mokhumudwa. Mosemphana ndi zinenezo zawo zoyambirira, Ayudawo angakhale ndi ulamuliro wakupha apandu kaamba ka milandu yachipembedzo yomwe njoipa kwenikweni. Kenaka, kwa nthaŵi yachisanu, Pilato akumulengeza Yesu kukhala wopanda liŵongo, nati: ‘Ine sindipeza chifukwa mwa iye.’
Ayudawo, powona kuti zinenezo zawo zandale sizikuphula kanthu, akubwerera ku mlandu wachipembedzo wa kuchitira mwano womwe anaugwiritsira ntchito maola angapo oyambirira pakuzengedwa mlandu kwa Yesu pamaso pa Bwalo la Akulu. ‘Tiri nacho chilamulo ife,’ iwo akutero, ‘ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.’
Chinenezo chimenechi nchatsopano kwa Pilato, ndipo chikumpangitsa kuchita mantha kwambiri. Iye tsopano wazindikira kuti Yesu simunthu wamba, monga momwedi loto la mkazi wake ndi nyonga yodabwitsa ya umunthu wa Yesu zikusonyezera. Koma “Mwana wa Mulungu”? Pilato akudziŵa kuti Yesu achokera ku Galileya. Komabe, kodi iye angakhale anakhalako ndi moyo kalelo? Akumabwerera naye m’nyumba yachifumuyo, Pilato akufunsa kuti: ‘Muchoka kuti?’
Yesu wakhala chete. Koyambirirako anamuuza Pilato kuti iye ndi mfumu, koma kuti Ufumu wake suli wa dziko lino lapansi. Palibe kulongosola kowonjezereka tsopano kumene kudzakhala ndi phindu lirilonse. Komabe, chifukwa cha kunyada, Pilato wakwiyitsidwa ndi kukana kuyankhako, ndipo akumuzazira Yesu ndi mawu akuti: ‘Simulankhula ndi ine kodi? Simudziŵa kodi kuti ulamuliro ndiri nawo wakukumasulani, ndipo ndiri nawo ulamuliro wakukupachikani?’
Yesu akuyankha mwaulemu kuti: ‘Simukadakhala nawo ulamuliro uliwonse pa ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera kumwamba.’ Iye akusonya ku kuperekedwa kwa ulamuliro kwa olamulira aumunthu kochitidwa ndi Mulungu kuti ayendetse zochitika zapadziko lapansi. Yesu akuwonjezera kuti: ‘Chifukwa cha ichi iye wondipereka ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.’ Ndithudi, wansembe wamkulu Kayafa ndi mabwenzi ake limodzi ndi Yudase Isikariote onse ali ndi thayo lalikulu kuposa Pilato la kuchitira Yesu mosalungama.
Posangalatsidwa koposa ndi Yesu ndikuchita mantha kuti mwina Iye angakhale wochokera kwa Mulungu, Pilato akuyambanso kuyesera kummasula Iye. Komabe, Ayudawo akumtsutsa Pilato. Iwo akubwereza chinenezo chawo cha ndale, mochenjera akumawopseza kuti: “Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesa yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.”
Mosasamala kanthu za zitsutso zowopsazo, Pilato atulutsiranso Yesu kubwalo. “Taonani, Mfumu yanu!” iye akuchondereranso.
‘Chotsani, Chotsani, mpachikeni iye!’ ndilo yankho.
‘Ndipachike Mfumu yanu kodi?’ Pilato akufunsa motero mothedwa nzeru.
Ayudawo anakwiya ndi ulamuliro wa Aroma. Iwo akunyozadi ulamuliro wa Roma! Komabe, mwachinyengo, ansembe aakuluwo akuti: “Tiribe Mfumu koma Kaisara.”
Akumawopa kutaya malo ake andale ndi kutchuka kwake, Pilato pomalizira pake akugonjera ku zofuna zosalekeza, zowopseza za Ayudawo. Iye akumpereka Yesu. Asilikali akumvula Yesu malaya ofiirirawo ndikumveka malaya ake. Pamene Yesu akuperekedwa kukapachikidwa, wasenzetsedwa mtengo wake wozunzirapo.
Tsopano ukali mmawa pa Lachisanu, Nisani 14; mwinamwake masana akuyandikira. Yesu sanagonepo chiyambire Lachinayi mmawa, ndipo wavutika ndi zokumana nazo zosautsa zambiri. Momvekera kwenikweni, nyonga yake yatha ndi kulemera kwa mtengo wozunzirapowo. Chotero munthu wongodutsa, Simoni wa ku Kurene m’Afirika, akukakamizidwa kumsenzera iye. Pamene akuyenda, khamu lalikulu la anthu likutsatira, kuphatikizapo akazi ambiri amene akudziguguda mwachisoni ndi kumlirira Yesu.
Akumatembenukira kwa akaziwo, Yesu akuti: ‘Ana aakazi inu a Yerusalemu, musandilirire ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa. Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife. Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?’
Yesu akusonya ku mtengo wa mtundu Wachiyuda, umene udakali ndi uwisi wamoyo chifukwa cha kukhalapo kwa Yesu ndi kukhalapo kwa otsalira amene akumkhulupirira. Koma pamene ameneŵa adzachotsedwa pakati pa mtunduwo, mtengo wakufa mwauzimu wokha ndiwo udzatsala, inde, gulu louma la mtunduwo. Ha, chidzakhala chifukwa cha kulirira chotani nanga pamene magulu ankhondo Achiroma, akumatumikira monga akupha a Mulungu, adzasakaza mtundu Wachiyudawo! Yohane 19:6-17; 18:31; Luka 23:24-31; Mateyu 27:31, 32; Marko 15:20, 21.
◆ Kodi ndi chinenezo chotsutsana ndi Yesu chotani chimene atsogoleri achipembedzowo akupanga pamene zinenezo zawo zandale siziphula kanthu?
◆ Kodi nchifukwa ninji mwinamwake Pilato akuchita mantha kwambiri?
◆ Kodi ndani amene ali ndi tchimo lalikulu la zimene zikumchitikira Yesu?
◆ Kodi ndimotani mmene ansembewo akumpangitsira Pilato kumpereka Yesu kuti aphedwe?
◆ Kodi Yesu akuwauzanji akazi amene akumlirira, ndipo kodi iye atanthauzanji mwakusonya ku mtengo “wauwisi” ndipo kenaka “wouma”?