“Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
PAMENE anali pachikike pa mtengo wophedwerapo, akumafa momva ululu, mpandu anapempha mwamuna wokhala pambali pake kuti: “Yesu, ndikumbukireni pamene mulowa muufumu wanu.” Yesu, ngakhale kuti nayenso anali kufa momva ululu wopweteka, anayankha naati: “Indetu ndikuuza iwe lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:42, 43, NW) Ha, ndichiyembekezo chotonthoza chotani nanga chopatsa munthu womafayo.
Komabe, kodi mwawona kuti, New World Translation—matembenuzidwe ogwidwa mawu m’ndime yapitayo—imaika chizindikiro chakupuma pambuyo pa liwulo “lerolino” pamene ikumasulira mawu ameneŵa onenedwa ndi Yesu? Zimenezi zimapereka lingaliro lakuti ngakhale patsiku la imfa yake ya iyemwini, Yesu anali wokhoza kulonjeza moyo m’Paradaiso kwa mpanduyo. Kumbali ina, The New English Bible imaika chizindikiro chakupuma m’mawu a Yesu mwanjirayi: “Ndikuuza iwe izi: lerolino udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Matembenuzidwe ena ochuluka amagwirizana ndi The New English Bible, akupereka lingaliro lakuti Yesu ndi mpandu womafayo anali kupita ku Paradaiso patsiku lomwe lija. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyana? Ndipo kodi ndikuika chizindikiro chakupuma kuti kumene kuli kolondola?
M’chenicheni, panalibe kuika zizindikiro zakupuma m’malembo apamanja oyambirira a Chigiriki a Baibulo. Chifukwa chake, pamene kuika zizindikiro zakupuma kunayambidwa, ojambula Baibulo ndi otembenuza anafunikira kuziika mogwirizana ndi kumvetsetsa kwawo chowonadi cha Baibulo. Pamenepa, kodi kumasulira kozoloŵereka kuli kolondola? Kodi Yesu ndi wochita zoipa anapita ku Paradaiso pa tsiku limene iwo anamwalira?
Ayi, malinga ndi Baibulo, iwo anapita kumalo otchedwa m’Chigiriki Haʹdes ndi m’Chihebri Sheʹol, onse aŵiri amaloza kumanda wamba a anthu. (Luka 18:31-33; 24:46; Machitidwe 2:31) Ponena za awo okhala kumalowo, Baibulo limati: “Koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingalira, ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda [Chigiriki, Haʹdes], ulikupitako.” Saali paradaiso konse!—Mlaliki 9:5, 10.
Panali patsiku lachitatu pamene Yesu anaukitsidwa kuchokera ku Hades. Kenako, mkati mwa pafupifupi milungu isanu ndi umodzi anawonekera kwa nthaŵi zingapo kwa otsatira ake kuzungulira dziko la Palestina. M’chimodzi cha zochitika zimenezo, Yesu anauza Mariya kuti: “Sindinatha kukwera kwa Atate.” (Yohane 20:17) Chotero, ngakhale panthaŵiyo anali asanafike ku malo alionse omwe akakhoza kutchedwa paradaiso.—Chivumbulutso 2:7.
M’zaka za zana lachitatu C.E.—pamene kugwirizanitsidwa kwa chiphunzitso Chachikristu ndi nthanthi Zachigiriki zinali kuyendera limodzi—Origen anagwira mawu a Yesu kukhala akuti: “Lerolino udzakhala ndi ine m’Paradaiso wa Mulungu.” M’zaka za zana lachinayi C.E., olemba atchalitchi anatsutsa zolimba kuika chizindikiro chakupuma pambuyo pa “lerolino.” Zimenezi zimasonyeza kuti njira yozoloŵereka ya kuŵerenga mawu a Yesu inayamba kalekale. Koma imasonyezanso kuti ngakhale m’zaka za zana lachinayi C.E., mawu a Yesu anali kuŵerengedwa ndi ena mogwirizana ndi njira imene amasulidwira mu New World Translation.
Lerolinonso, ngakhale kuti otembenuza ambiri amaika chizindikiro chakupuma pa Luka 23:43 mogwirizana ndi mwambo watchalitchi, ena amaika chizindikiro chakupuma mofanana ndi New World Translation. Mwachitsanzo, m’matembenuzidwe a Chijeremani olembedwa ndi Profesa Wilhelm Michaelis, mawu a Yesu amaŵerengedwa motere: “Indetu, ndikupatsa iwe chitsimikiziritso ichi lerolino: (Tsiku lina) udzakhala pamodzi ndi ine m’Paradaiso.”
Pamenepa, kodi mawu a Yesu anatanthauzanji kwa wochita zoipayo? Iye angakhale anamva zonenedwa kuti Yesu ndiye Mfumu yolonjezedwa. Mosakaikira, iye anadziŵa dzina la ulemulo “mfumu ya Ayuda” limene Pilato anazokota ndi kupachika pamwamba pa mutu wa Yesu. (Luka 23:35-38) Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo mouma khosi anamkana Yesu, mpandu wolapayo anasonyeza chikhulupiriro chake, akumati: “Yesu, ndikumbukireni pamene mulowa mu ufumu wanu.” Iye sanayembekezere kulamulira ndi Yesu, koma anafuna kupindula ndi ulamuliro wa Yesu. Chifukwa chake, Yesu, ngakhale pa tsiku lovuta koposa limenelo, analonjeza kuti wochita zoipayo akakhala naye m’Paradaiso.
Kodi ndi m’paradaiso uti? M’Baibulo, Paradaiso woyambirira anali munda wonga paki wa Edene umene makolo athu oyamba anautaya. Baibulo limalonjeza kuti Paradaiso wapadziko lapansi ameneyo adzabwezeretsedwanso pansi pa Ufumu wa Mulungu, umene Yesu ndiye Mfumu. (Salmo 37:9-11; Mika 4:3, 4) Chifukwa chake, Yesu adzakhala ndi wochita zoipa uja ndi akufa ena osaŵerengeka pamene adzawaukitsa kuchokera kumanda kumka kumoyo padziko lapansi la paradaiso ndi kumwaŵi wakuphunzira kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kukhala ndi moyo kosatha.—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:11-13; 21:3, 4.