Mapeto a Upandu Ali Pafupi Tsopano!
OFUFUZA amafuna kuthetsa maupandu mwa kusanthula mfungulo zomwe zimavumbula chizindikiritso ndi zolinga za oyambitsawo. Njira ndi maluso a wofufuzayo ziri nkhani za manovel otchuka pa dziko lonse. Ngakhale kuti iye pomalizira pake angakhale wachipambano m’kupeza mpanduyo, ntchito ya wofufuzayo mwachisawawa imayamba pambuyo pa chochitikacho, pambuyo pakuti upanduwo wachitidwa kale.
Monga momwe zingawonedwere ndi kukwera kwa upandu, pa mpandu aliyense wogwidwa, pamakhala ambiri ena omwe atembenukira ku upandu. Chotero zowonjezereka kuposa kokha kuthetsa milandu yochitika kale zifunikira kuchitidwa kuti upandu uthetsedwe. Kodi nchiyani chomwe chidzaletsa anthu kukhala apandu?
Upandu uyenera kuchita ndi makhalidwe. Tiribe vuto m’kulandira kuti kupha anthu, kugwirira chigololo, ndi machitidwe ena a chiwawa ali maupandu. Koma bwanji ponena za kunama pamene tikudzaza chikalata cha msonkho? Kachitidwe koteroko kalinso upandu, popeza kuti kali kosemphana ndi miyezo ya makhalidwe a kuwona mtima. Kuthetseratu upandu kuyenera kutanthauza kuchotseratu machitidwe onse osemphana ndi mkhalidwe wolandirika.
Lingalirani zitsanzo zitatu za Baibulo zomwe zimawunikira osati kokha choyambitsa cha upandu komanso njira mu imene udzathetsedwere.
Mantha Aumulungu Molimbana ndi Nsanje
Chonde onani mawu a wamasalmo Asafu: “Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuwona mtendere wa oipa.” (Salmo 73:3) Inde, nsanje ya kupita patsogolo kwa mpandu ndi njira za moyo zimanyenga ambiri kutsanzira njira zosayeruzika. Kuwunikira upandu pa wailesi ya kanema ndi m’manyuzipepala kumawupanitsa iwo kukhala wolandirika kwenikweni m’malo mosonkhezera udani wa chimene chiri choipa.
Mosasamala kanthu za icho, mlembi wowuziridwa wa Miyambo akuchenjeza kuti: “Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.” Chisonkhezero chenicheni ndi chikhumbo cha munthu chiri muzu wa vutolo. Njira yokhutiritsa koposa yothetsera ilo iri mwa kumangirira mantha aumulungu a kusakondweretsa Yehova Mulungu. “Pakutitu padzakhala mphoto; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.”—Miyambo 23:17, 18.
Chikhulupiriro Molimbana ndi Umbombo
Mu ngululu ya 33 C.E., Yesu anali kuyenda kudutsa mzinda wa Yeriko. Umenewo unali mudzi wa kwawo kwa Zakeyu, amene wolemba Uthenga Wabwino Luka akumulongosola kukhala “mkulu wa amisonkho,” akumawonjezera kuti “anali wachuma.” Boma lachonde lozungulira Yeriko linali gawo loyambirira losonkhanitsa msonkho, ndipo monga momwe kwasonyezedwera ndi mawu enieni a Zakeyu, ntchito yake monga mkulu wa amisonkho inampatsa iye mwaŵi wa kulanda. Koma Zakeyu sanakhalebe mpandu.—Luka 19:1-8.
Zakeyu anathamangira kutsogolo kwa khamu losonkhana mozungulira Yesu ndipo chifukwa cha msinkhu wake waufupi anafuna malo owonekera mwa kukwera mu mtengo wa mkuyu. Yesu anamuwona iye ndi kumuwuza Zakeyu kutsika, popeza Iye akakhala ndi iye pamene anali mu Yeriko. Pambuyo pake, mawu a Zakeyu analengeza kusintha mkhalidwe: “Gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka, ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanayi.” Kubwezera ndalama zotengedwa monyenga kukaphatikizapo zotaika zazikulu. Mwa kulonjeza kuchita ichi, Zakeyu analengeza chikhulupiriro chake mwa Yesu. Inde, kawonedwe kake kosinthika kanabweretsa chotulukapo chozizwitsa, kubwezera kwa chomwe chinatengedwa mopanda lamulo kuwonjezera kuwirikiza nthaŵi zitatu pa mtengo umenewo, kupanga chobwezera chowirikiza kanayi. Chotero Zakeyu anawongolera cholakwa chomwe anachita ndi kupitirirapo, mwa kutsimikizira kuwona kwa njira yake yosinthidwa ya kakhalidwe.—2 Akorinto 7:11.
Anthu Ali Ofunika Koposa Kuposa Katundu
Bwanamkubwa Wachiroma Pilato ananena ponena za Yesu Kristu wopatsidwa mlanduyo kuti: “Ndiribe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.” (Luka 23:4) M’malo mokhoterera ku mkhalidwe wa upandu kuti apeze chuma, mkati mwa utumiki wake wonse wa pa dziko lapansi, Yesu anasonyeza chikondwerero chachikondi mwa anthu. “Powona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:36-38) Mwachiwonekere, Yesu anaika anthu patsogolo pa katundu, ngakhale patsogolo pa chitonthozo ndi zikondwerero za iyemwini. Tikuwonanso ichi kuchokera ku kufunitsitsa kwake ku kudzipereka iyemwini kusamalira kaamba ka ophunzira ake ndi makamu omwe anamfuna iye kaamba ka chilangizo ndi thandizo. (Mateyu 8:20; 14:13-16) Mwa ichi, Yesu anatisiira ife chitsanzo chochitsatira.—1 Petro 2:21.
Kodi chiri chotheka kwa anthu lerolino kutsatira dongosolo limenelo, kusunga anthu anzawo kukhala ofunika koposa kuposa katundu wakuthupi? Tingayankhe motsimikizirika. Lingalirani Mboni za Yehova, tsopano zoposa mamiliyoni atatu ndi kota zamphamvu. Izo zimafuna kukhala ndi maganizo a Kristu ndi kupereka kulongosola kogwira ntchito. Iwo amagwira ntchito mokhazikika kuchotsa m’mitima yawo zikhumbo zoipa zomwe zimatsogolera ena ambiri ku upandu. Asanakhale Mboni, pamene iwo anaphunzira Baibulo ndi kukulitsa chikondi kaamba ka Mulungu, ichi chinakhudza ena a iwo omwe angakhale anali apandu; chinafulumiza ambiri a iwo kupanga kubwezera kaamba ka machitidwe a upandu omwe angakhale anachita kumbuyo. Ayi, oterowo sanachite ichi kuti afalitsidwe koma kotero kuti akhale ndi unansi wamtendere ndi Yehova Mulungu ndipo mwakutero kupindula kuchokera ku chifundo chake chokoma mtima monga momwe chasonyezedwera kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu.—1 Akorinto 2:16; 6:11; 2 Akorinto 5:18-20.
Ndi chikondi kaamba ka anansi awo, Akristu oterowo amatenga nthaŵi kuchezera anthu ena ndi kulongosola mmene mabanja oterowo angayang’anire kutsogolo ku moyo m’mikhalidwe ya Paradaiso pansi pa Ufumu wa Mulungu. Mlungu uliwonse Mboni za Yehova zimachita misonkhano yokhazikika pa Nyumba zawo za Ufumu. Mmodzi yemwe anadziwulula yekha monga mbala analandira chiitano cha kupezeka kukawona chimene misonkhano imeneyi iri. Iye akusimba kuti: “Kunenako zochepa zokha, ndinadabwitsidwa kwambiri. Iyo sinali yosasangalatsa kapena yosungulumwitsa monga momwe ndinayembekezera. Kutentha ndi chikondi, zowonekeratu, mwachiwonekere zinali zenizeni. Ndipo chiyamikiro chimene Mboni zonse zimawonekera kukhala nacho kaamba ka zinthu zauzimu chinali chowonekera.” Iye anali wokondweretsedwa kotero kuti anapitiriza kuyanjana kwake, ndipo ichi chinamthandiza iye kusintha. Kaya mwakhala ophatikizidwa mu upandu kapena ayi, pamene muyanjana ndi atumiki a Mulungu, nanunso mudzapeza chikondwerero chowona chimodzimodzicho mwa anthu m’malo mwa katundu.—Mateyu 22:39.
Upandu—Kodi Unachotsedwa Kale?
Ngati anthu sachitanso monga apandu, kodi chimenecho chikutanthauza kuti iwo ali angwiro? Kutalitali! Mboni za Yehova, mofanana ndi wina aliyense, zimavutika ndi chimo la choloŵa kuchokera kwa kholo lathu laumunthu loyambirira, Adamu. (Aroma 5:12; 1 Yohane 1:8) Koma iwo tsopano ali ogwirizana m’kutumikira Mulungu, monga momwe kwawunikiridwa mu ntchito yawo ya dziko lonse yolalikira ndi kuphunzitsa. Ichi chimasonyeza umboni wamphamvu ku kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya wakuti: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, . . . mitundu idzasonkhana kumeneko.” (Yesaya 2:2) Ndithudi, mamiliyoni akuthamangira ku kulambira kokwezeka kwa Yehova, kufunafuna chilangizo m’njira zake. Inu mungakhale mmodzi wa awo amene akupindula mwa kuyanjana ndi anthu omwe amapeŵa upandu.
Kuchotsa Upandu—Ziyembekezo
Machitachita owonjezereka a upandu m’tsiku lathu m’chenicheni amasonyeza kuyandikira kwa kuloŵereramo kwaumulungu kwa kuchotsa oipa onse, kuphatikizapo oyambitsa onse a upandu. “Pakuti wochita zoipa adzadulidwa . . . katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psyiti; inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.” (Salmo 37:9, 10) Mapeto ku upandu ndithudi ali pafupi tsopano, popeza kuti tikuyandikira ku nthaŵi pamene mpandu woyambirira, Satana Mdyerekezi, adzamangidwa ndi kuikidwa ku pompho. (Chibvumbulutso 20:1-3) Nchosangalatsa chotani nanga mmene icho chiyenera kukhalira kudziŵa kuti kuwopa upandu ndi kupweteka kovutikidwa ndi minkhole yake posachedwapa zidzakhala zinthu zakale!
Komabe, bwanji ponena za mamiliyoni a anthu omwe m’chiwukiriro adzabwerera ku moyo pa dziko lapansi? (Machitidwe 24:15) Ngati iwo adzawumirira pa umunthu umodzimodziwo ndi njira zomwe anali nazo asanafe, kodi iwo sadzayambitsanso m’kuntho watsopano wa upandu? Palibe chifuno cha kuwopera chimenecho. Yesu analonjeza mbala chiwukiriro, akumanena kuti: “Zowonadi ndikuwuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43, NW) Ichi ndithudi chimasonyeza kuti owukitsidwa adzafunikira kupanga masinthidwe; kupanda apo dziko latsopano silidzakhala paradaiso.
Mongadi mmene apandu oipitsitsa afunikira kuthandizidwa asanakhale okhoza kukhazikika m’mudzi popanda kuyambitsa mavuto, momwemonso pansi pa Ufumu wa Mulungu, programu yophunzitsa yaikulu idzathandiza nzika zake kukhala zosunga lamulo. (Chibvumbulutso 20:12, 13) Pokhala ndi mwaŵi wowonekeratu wa kukhala ozunguliridwa ndi nzika za Paradaiso, zomwe zikumvera malamulo a Mulungu, owukitsidwawo adzakumana ndi mikhalidwe ya zachuma yowongoleredwa moyenerera. (Yesaya 65:21-23) Padzakhala olamulira olungama m’mathayo, ndipo ochita zolakwa owumirira aliwonse adzayang’anizana ndi kuchotsedwa kuchoka ku moyo. (Yesaya 32:1; 65:20) Chotero pali chifukwa chokwanira cha kukhulupirira kuti, pomalizira pake, upandu udzatha.
Ngakhale kuti tidakakhala m’dziko lomwe likuzindikiritsidwa ndi upandu, inu mwachidaliro mungawunikire chikhulupiriro mwa Yehova, yemwe akulonjeza kufupa atumiki ake okhulupirika ndi moyo wangwiro m’Paradaiso. Chitani tero tsopano mwa kutenga mwaŵi wa kakonzedwe ka phunziro la Baibulo la pa nyumba laulere loperekedwa ndi Mboni za Yehova. (Yohane 17:3) Nthaŵi yotsatira imene mudzakumana nawo, bwanji osafunsa kaamba ka tsatanetsatane wowonjezereka? Kapena mungalembere ku adresi ya kufupi nanu yondandalitsidwa pa tsamba 2 la magazini ino. Icho ndithudi chiri choyenerera kupanga kuyesayesa, popeza kuti mapeto a upandu ali pafupi tsopano!
[Chithunzi patsamba 5]
Chikhulupiriro cha Zakeyu chinamfulumiza iye kubwezera zomwe analanda
[Chithunzi patsamba 7]
Programu yophunzitsa idzaphunzitsa nzika za Ufumu wa Mulungu kukhala zosunga lamulo