Mutu 20
Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?
1, 2. Kodi tikudziwa motani kuti atumiki a Mulungu akale anakhulupirira chiukiriro?
ATUMIKI A MULUNGU nthawi zonse akhulupirira chiukiriro. Ponena za Abrahamu, amene anakhalako zaka 2,000 Yesu asanabadwe monga munthu, Baibulo limati: “Poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa [mwana wake Isake], ngakhale kwa akufa.” (Ahebri 11:17-19) Pambuyo pake mtumiki wa Mulungu Yobu anafunsa kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Moyankha funso lake lomwe, Yobu anati kwa Mulungu: “Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani.” Motero iye anasonyeza kuti anakhulupirira chikukiriro.—Yobu 14:14, 15.
2 Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anafotokoza kuti: “Zakuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:37, 38) M’Malemba Achikristu Achigiriki liwulo “chiukiriro” likugwiritsiridwa ntchito koposa nthawi 40. Ndithudi, kuuka kwa akufa ndiko chiphunzitso chachikulu Chabaibulo.—Ahebri 6:1, 2.
3. Kodi Malita anasonyeza chikhulupiriro chotani m’chiukiriro?
3 Pamene mlongo wake Lazalo anafa, bwenzi la Yesu Malita anasonyeza chikhulupiriro m’chiukiriro. Atamva kuti Yesu analinkudza, Malita anatuluka kumchingamira. “Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa,” iye anatero. Powona chisoni chake, Yesu anamtonthoza ndi mawuwo: “Mlongo wako adzauka.” Malita anayankha kuti: “Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomariza.”—Yohane 11:17-24.
4-6. Kodi Malita anali ndi zifukwa zotani zokhulupirira chiukiriro?
4 Malita anali ndi zifukwa zamphamvu kaamba ka chikhulupiriro chake m’kuuka. Mwa chitsanzo, iye anadziwa kuti, zaka zambiri zapitazo mneneri wa Mulungu Eliya ndi Elisa, ndi mphamvu ya Mulungu, aliyense adaukitsa mwana. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37) Ndipo anadziwa kuti munthu wina wakufa adauka pamene iye anaponyedwa m’denje nakhudza mafupa a Elisa wakufa. (2 Mafumu 13:20, 21) Koma chimene chidalimbikitsa koposa chikhulupiriro chake m’kuuka chinali chimene Yesu mwiniyo adaphunzitsa ndi kuchita.
5 Malita angakhale anali m’Yerusalemu zosakwanira zaka ziwiri zapitazo, pamene Yesu anatchula mbali imene akakhala nayo m’kuukitsa akufa. Iye anati: “Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:21, 28, 29.
6 Kufikira nthawiyo imene Yesu analankhula mawu amenewo, palibe cholembedwa Chabaibulo chakuti iye adaukitsa aliyense. Koma mwamsanga pambuyo pake iye anaukitsa mnyamata, mwana wa mkazi wina wamasiye mumzinda wa Nayini. Mbiri ya zimenezi inatengeredwa kummwera ku Yudeya, motero Malita anali wotsimikizira kukhala atamva za iko. (Luka 7:11-17) Pambuyo pake, Malita anayeneranso kukhala atamva zimene zinachitika pafupi ndi Nyanja ya Galileya m’nyumba ya Yairo. Mwana wake wamkazi wa usinkhu wa zaka 12 adadwala kwambiri ndipo adafa. Koma Yesu anafika panyumba ya Yairo, iye anapita kwa mwana wakufayo, nati: “Buthu, tauka!” Ndipo iye anaukadi!—Luka 8:40-56.
7. Kodi Yesu anapatsa Malita chitsimikizo chotani chakuti iye angaukitse akufa?
7 Komabe Malita sanayembekezere Yesu kuukitsa mlongo wake pa nthawi imeneyi. Ndicho chifukwa chake iye anati: “Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomariza.” Komabe, kuti asonyeze Malita mbali imene ali nayo m’kuukitsa akufa, Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo iye wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse.” Mwamsanga pambuyo pake Yesu anatengeredwa kumanda kumene Lazalo adaikidwa. “Lazalo, tuluka!” anapfuula. Ndipo Lazalo, amene adali wakufa masiku anai, anatuluka!—Yohane 11:24-26, 38-44.
8. Kodi pali umboni wotani wakuti Yesu anaukitsidwa?
8 Masabata owerengeka pambuyo pake Yesu mwiniyo anaphedwa naikidwa m’manda. Koma iye anakhalamo kokha mbali za masiku atatu. Mtumwi Petro akufotokoza chifukwa chake, kuti: “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tiri mboni ife tonse.” Atsogoleri achipembedzo sanathe kuletsa Mwana wa Mulungu kutuluka m’manda. (Machitidwe 2:32; Mateyu 27:62-66; 28:1-7) Sipangakhale kukayikira kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, pakuti pambuyo pake iye anadzisonyeza wamoyo kwa ambiri a ophunzira ake, nthawi ina kwa okwanira 500 a iwo. (1 Akorinto 15:3-8) Ophunzira a Yesu anakhulupirira chiukiriro mwamphamvu kwambiri chakuti iwo anali ofunitsitsa kuyang’anizana ngakhale ndi imfa kuti atumikire Mulungu.
9. Kodi ndianthu asanu ndi anai otani amene Baibulo limanena kuti anaukitsidwa?
9 Umboni wowonjezereka wakuti akufa angaukitsidwe unaperekedwa pambuyo pake mwa mtumwi Petro ndi Paulo. Choyamba, Petro anaukitsa Tabita, wotchedwanso Dolika, wa mzinda wa Yopa. (Machitidwe 9:36-42) Ndiyeno Paulo anabwezeretsa ku moyo Utiko wachichepereyo, amene adafa pamene anagwa kuchokera pa zenera la nsanja yachiwiri pamene Paulo analinkulankhula. (Machitidwe 20:7-12) Ndithudi ziukiriro zisanu ndi zinai zolembedwa m’Baibulo zimenezi zimapereka umboni wotsimikizirika wakuti akufa angabwezeretsedwe ku moyo!
KODI NDANI ADZAUKITSIDWA?
10, 11. (a) Kodi nchifukwa ninji Mulungu analinganiza chiukiriro? (b) Malinga ndi kunena kwa Machitidwe 24:15, kodi ndimagulu awiri a anthu otani amene adzaukitsidwa?
10 Pachiyambi sichinali chifuno cha Mulungu kuukitsa aliyense, chifukwa chakuti ngati Adamu ndi Hava akanakhalabe okhulupirika palibe akadafunikira kufa. Komano tchimo la Adamu linadzetsa kupanda ungwiro ndi imfa pa aliyense. (Aroma 5:12) Motero kuti atheketsere aliyense wa ana a Adamu kulandira moyo wosatha, Yehova Mulungu analinganiza chiukiriro. Koma kodi nchiyani chimene chimatsimikiziritsa kaya munthu akuukitsidwa kapena ayi?
11 Baibulo limafotokoza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Zimenezi zingadabwitse ena. ‘Kubwezeretseranji ku moyo “osalungama”?’ iwo angadabwe. Chimene chinachitika pamene Yesu anali pachikike pa mtengo wophedwerapo chidzatithandiza kuyankha funso limeneli.
12, 13. (a) Kodi Yesu anapereka lonjezo lotani kwa mpandu? (b) Kodi “Paradaiso” amene Yesu anamlankhula ali kuti?
12 Amuna oyandikana ndi Yesu amenewa ndiapandu. Mmodzi wa iwo wangotsiriza kumchitira chipongwe, kuti “Ndiwe Kristu, kodi sichoncho? Dzipulumutse ndi ife.” Komabe, mpandu winayo akukhulupirira Yesu. Iye akutembenukira kwa iye ndipo akuti: “Ndikumbukireni pamene mulowa mu ufumu wanu.” Atatero, Yesu akulonjeza kuti: “Ndithudi ndikukuuza lerolino, Udzakhala nane m’Paradaiso.”—Luka 23:39-43, NW.
13 Koma kodi Yesu akutanthauzanji pamene akuti: “Udzakhala nane m’Paradaiso”? Kodi Paradaiso ali kuti? Eya, kodi paradaiso amene Mulungu anapanga pachiyambi anali kuti? Anali padziko lapansi, kodi sichoncho? Mulungu anaika anthu awiri oyambawo m’paradaiso wokongola wotchedwa munda wa Edene. Motero pamene tiwerenga kuti mpandu wakale ameneyu adzakhala m’Paradaiso, tiyenera kuchitira chinthunzithuzi m’maganizo mwathu dziko lapansi lino likupangidwa kukhala malo okongola okhalamo, pakuti liwulo “paradaiso” limatanthauza “munda” kapena “paki.”—Genesis 2:8, 9.
14. Kodi Yesu adzakhala ndi mpandu wakaleyo m’Paradaiso m’njira yotani?
14 Ndithudi Yesu Kristu, sadzakhala padziko lapansi pompano limodzi ndi mpandu wakaleyo. Ayi, Yesu adzakhala kumwamba akumalamulira monga mfumu pa Paradaiso wapadziko lapansi. Motero iye adzakhala ndi munthu ameneyo m’lingaliro lakuti Iye adzamuukitsa kwa akufa ndi kusamalira zowosa zake, zakuthupi ndi zauzimu zomwe. Koma kodi nchifukwa ninji Yesu adzalola munthu amene anali mpandu kukhala m’Paradaiso?
15. Kodi “osalungama” akuukitsidwiranji?
15 Nzowona kuti munthu ameneyu anachita zinthu zoipa. Iye anali “wosalungama.” Ndiponso, iye anali wosadziwa chifuniro cha Mulungu. Koma kodi iye akanakhala mpandu ngati akadadziwa zifuno za Mulungu? Kuti tidziwe, Yesu adzaukitsa munthu wosalungama ameneyu, kuphatikizapo mamiliyoni zikwi zambiri za ena amene anafa osadziwa. Mwa chitsanzo, m’zaka mazana ambiri zapitazo anthu ambiri anafa amene sanadziwe kuwerenga ndi amene sadawone Baibulo. Koma iwo adzaukitsidwa ku Sheol, kapena Hade. Ndiyeno, m’dziko lapansi laparadaiso, iwo adzaphunzitsidwa chifuniro cha Mulungu, ndipo iwo adzakhala ndi mpata wa kusonyeza kuti iwo amakondadi Mulungu mwa kuchita chifuniro chake.
16. (a) Kodi ndani mwa akufa amene sadzaukitsidwa? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuyesa kuganizira zinthu? (c) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala nkhawa yathu yaikulu?
16 Zimenezi sizitanthauza kuti aliyense adzalandira chiukiriro. Baibulo limasonyeza kuti Yudase Iskariote, amene anapereka Yesu, sadzatero. Chifukwa cha kuipa kwake kwadala, Yudase akutchedwa “mwana wa chitayiko.” (Yohane 17:12) Iye anapita ku Gehena wophiphiritsira kumene kulibe chiukiriro. (Mateyu 23:33) Anthu amene mwadala akuchita chimene chiri choipa atadziwa chifuniro cha Mulungu angakhale akuchimwira mzimu woyera. Ndipo Mulungu sadzaukitsa awo amene akuchimwira mzimu wake woyera. (Mateyu 12:32; Ahebri 6:4-6; 10:26, 27) Komabe, popeza kuti Mulungu ndiye Woweruza, palibe chifukwa chakuti ife tiyese kuganizira kaya anthu ena oipa m’nthawi zakale kapena zamakono adzaukitsidwa kapena ayi. Mulungu akudziwa amene ali m’Hade ndi amene ali m’Gehena. Popeza za ife, tiyenera kuchita zirizonse zimene tingathe kuti tikhale mtundu wa anthu amene Mulungu akufuna m’dongosolo lake latsopano.—Luke 13:24, 29.
17. Kodi ndani amene sadzafunikira kuukitsidwa kuti alandire moyo wosatha?
17 Tchenicheni nchakuti sionse amene akulandira moyo wosatha adzafunikira kuukitsidwa. Atumiki a Mulungu ambiri okhala ndi moyo tsopano “m’masiku otsiriza” ano a dongosolo la zinthu adzapyola Harmagedo. Ndiyeno, monga mbali ya “dziko [lapansi] latsopano” lolungama, iwo sadzafunikiranso kufa. Zimene Yesu ananena kwa Malita zingakhale zowona m’njira yeniyeni kwa iwo: “Ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse.”—Yohane 11:26; 2 Timoteo 3:1.
18. Kodi ndani amene ali “olungama” amene adzaukitsidwa?
18 Kodi ndani amene ali “olungama” amene ayenera kuukitsidwa? Amenewa adzaphatikizapo atumiki a Mulungu okhulupirika amene anakhalako Yesu Kristu asanadze kudziko lapansi. Ambiri a anthu amenewa akutchulidwa maina mu Ahebri chaputala 11. Iwo sanayembekezere kupita kumwamba, koma anayembekezera kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Ndiponso pakati pa “olungama” oti aukitsidwe pali atumiki a Mulungu okhulupirira amene amwalira m’zaka zaposachedwapa. Mulungu adzalinganiza kuti chiyembekezo chawo cha kukala ndi moyo kosatha padziko lapansi chikupezedwa mwa kuwaukitsa kwa akufa.
NTHAWI NDI MALO OUKITSIDWIRA
19. (a) Kodi Yesu anali woyamba kuukitsidwa m’lingaliro lotani? (b) Kodi ndani amene akuukitsidwa kenako?
19 Yesu Kristu akutchedwa “woyamba kuukitsidwa kwa akufa.” (Machitidwe 26:23, NW) Zimenezi zikutanthauza kuti iye anali woyamba kuukitsidwa mwa awo amene sakafunikira kufanso. Ndiponso, iye anali woyamba kuukitsidwa monga munthu wauzimu. (1 Petro 3:18) Koma Baibulo limatiuza kuti kukakhala ena, likumati: “Aliyense m’malo ake: Kristu zipatso zoundukula, pambuyo pake awo amene ali a Kristu mkati mwa kukhalapo kwake.” (1 Akorinto 15:20-23, NW) Motero m’chiukiriro ena akaukitsidwa ena ake asanaukitsidwe.
20. (a) Kodi ndani amene ali “awo a Kristu”? (b) Kodi iwo akulandira chiukiriro chotani?
20 “Awo amene ali a Kristu” ndiwo ophunzira okhulupirika 144,000 osankhidwa kulamulira naye mu Ufumuwo. Ponena za chiukiriro chawo chakumwamba, Baibulo limati: “Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri iribe ulamuliro; komatu . . . adzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.”—Chivumbulutso 20:6; 14:1, 3.
21. (a) Kodi “kuuka koyamba” kukuyamba liti? (b) Kodi ndani amene mosakayikira aukitsidwira kale ku moyo wakumwamba?
21 Motero motsatizana ndi kuuka kwa Kristu, a144, 000 ndiwo otsatirapo kuukitsidwa. Iwo ali ndi mbali “m’kuuka koyamba,” kapena “chiukiriro choyambirira.” (Afilipi 3:11, NW) Kodi chimenechi chikuchitika liti? “Mkati mwa kukhalapo kwake,” Baibulo limatero. Monga momwe taphunzirira m’mitu yoyambirirayo, kukhalapo kwa Kristu kunayamba m’chaka cha 1914. Motero “tsiku” la “kuuka koyamba” kwa Akristu okhulupirika kwa kumwamba lafika kale. Mosakayikira atumwi ndi Akristu ena oyambirira aukitsidwira kale ku moyo wakumwamba.—2 Timoteo 4:8.
22. (a) Kodi ndaniso amene adzakhala ndi mbali “m’kuuka koyamba”? (b) Kodi iwo akuukitsidwa liti?
22 Koma pali Akristu okhala ndi moyo tsopano mkati mwa kukhalapo kosawoneka kwa Kristu amene ali ndi chiyembekezo chimodzimodzichi cha kulamulira kumwamba ndi Kristu. Iwo ndiwo otsala, otsalira a 144,000. Kodi iwo akuukitsidwa liti? Iwo safunikira kugona mu imfa, koma iwo amaukitsidwa nthawi yomweyo pamene iwo afa. Baibulo limafotokoza kuti: “Sitidzagona tonse [mu imfa], koma tonse tidzasandulika, m’kaphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa.”—1 Akorinto 15:51, 52; 1 Atesalonika 4:15-17.
23. Kodi Baibulo limafotokoza motani kusinthira ku moyo wauzimu?
23 Ndithudi, “kuuka koyamba” kwa kumoyo wakumwamba kumeneku nkosawoneka ndi maso aanthu. Ndiko kuukira ku moyo monga zolengedwa zauzimu. Baibulo limafotokoza kusinthira ku moyo wauzimuko motere: “Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi; lifesedwa m’mnyozo, liukitsidwa m’ulemerero; . . . . Lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu.”—1 Akorinto 15:42-44.
24. (a) Kodi ndikuuka kotani kumene kukutsatira “kuuka koyamba”? (b) Kodi nchifukwa ninji kukutchedwa “kuuka koposa”?
24 Komabe, kanenedwe kenikeniko “kuuka koyamba” kamasonyeza kuti kwina kudzatsatira. Kumeneku ndiko kuukira ku moyo padziko lapansi laparadaiso ponse pawiri kwa anthu olungama ndi osalungama. Kumeneku kudzachitika pambuyo pa Harmagedo. Kudzakhala “kuuka koposa” koposa kuja kwa anyamata oukitsidwa ndi Eliya ndi Elisa ndi kwa ena amene anaukitsidwa padziko lapansi pa nthawi ina. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ngati awo oukitsidwa pambuyo pa Harmagedo asankha kutumikira Mulungu iwo sadzafunikiranso kufa.—Ahebri 11:36.
CHOZIZWITSA CHA MULUNGU
25. (a) Kodi nchifukwa ninji siliri thupi limene linafa limene likuukitsidwa? (b) Kodi nchiyani chimene chikuukitsidwa, ndipo kodi nchiyani chimene chikuperekedwa kwa awo amene akuukitsidwa?
25 Munthu atafa, kodi chimaukitsidwa nchiyani? Sithupi limodzimodzilo limene linafa. Baibulo limasonyeza zimenezi pamene limafotokoza chiukiriro cha kumoyo wakumwamba. (1 Akorinto 15:35-44) Ngakhale awo amene akuukitsidwira ku moyo padziko lapansi samalandira thupi limodzimodzilo limene iwo anali nalo pamene iwo anakhala ndi moyo kale. Thupilo mwinamwake linawola ndi kubwerera ku nthaka. M’kupita kwa nthawi zopanga thupi lakufalo zingakhale zitakhala mbali ya zinthu zina zamoyo. Motero Mulungu samaukitsa thupi limodzimodzilo koma munthu yemweyo amene anafa. Kwa anthu amene akupita kumwamba, iye amapereka thupi latsopano lauzimu. Kwa awo amene akuukitsidwa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi, iye amapereka thupi lenileni latsopano. Thupi lenileni latsopano limeneli mosakayikira lidzakhala lolingana ndi limene munthuyo anali nalo asanafe kotero kuti iye adzazindikiridwa ndi awo amene anamdziwa.
26. (a) Kodi nchifukwa ninji chiukiriro chiri chozizwitsa chodabwitsa kwambiri? (b) Kodi ndizotumba zotani za anthu zimene zingatithandize kumvetsetsa kukhoza kwakukulu kwa Mulungu kukumbukira anthu amene afa?
26 Chiukiriro chiridi chozizwitsa chodabwitsa. Munthu amene anafa angakhale atasonkhanitsa kuchuluka kwakukulu kwa chidziwitso ndi nzeru ndi zikumbukiro zambiri mkati mwa nthawi yamoyo. Anakulitsa umunthu umene unampangitsa kukhala wosiyana ndi munthu wina aliyense amene anakhalako chiyambire. Komabe Yehova Mulungu amakumbukira chinthu chirichonse, ndipo adzabwezeretsa munthu wathunthu ameneyu pamene Iye amuukitsa: Monga momwe Baibulo likunenera ponena za akufa oti aukitsidwe: “Onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:38) Anthu angajambule mawu ndi zithunzinthuzi za anthu, ndi kuwalizanso nthawi yaitali anthuwo atafa. Koma Yehova angathe, ndipo kwenikweni, adzabwezeretsa ku moyo anthu onse amene akukhala ndi moyo m’chikumbukiro chake!
27. Kodi ndimafunso otani onena za chiukiriro amene tidzayankhidwa pambuyo pake?
27 Baibulo limatiuza zina zambiri ponena za moyo m’Paradaiso akufa ataukitsidwa. Mwa chitsanzo, Yesu anatchula anthu akutulukira, ena ku “kuuka kwa moyo” ndi enanso ku “kuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:29) Kodi anatanthauzanji? Ndipo kodi mkhalidwe udzakhala wosiyana kwa “olungama” amene akuukitsidwa ndi umene udzakhala wa “osalungama”? Kulingaliridwa kwa Tsiku Lachiweruzo kudzatiyankhira mafunso oterowo.
[Zithunzi patsamba 167]
“Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka”
Eliya anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye
Elisa anaukitsa mwana
Munthu wina amene anakhudza mafupa a Elisa anauka
[Zithunzi patsamba 168]
Anthu oukitsidwa ndi Yesu:
Mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Nayini
Lazalo
Mwana wamkazi wa Yairo
[Zithunzi patsamba 169]
Ena amene anaukitsidwa:
Dolika
Yesu mwini
Utiko
[Chithunzi patsamba 170]
Kodi Paradaiso amene Yesu analonjeza wochita zoipayo ali kuti?