Kachisi Wauzimu Wamkulu wa Yehova
“Tili naye [mkulu wa ansembe, NW] wotere, . . . mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene [Yehova, NW] anachimanga, si munthu ayi.”—AHEBRI 8:1, 2.
1. Kodi ndi makonzedwe achikondi otani amene Mulungu anapangira anthu ochimwa?
YEHOVA MULUNGU, mwa chikondi chake chachikulu pa anthu, anapereka nsembe yochotsa machimo a dziko. (Yohane 1:29; 3:16) Panafunikira kusamutsa moyo wa Mwana wake woyamba kubadwa kuchokera kumwamba kuuloŵetsa m’mimba ya namwali wachiyuda wotchedwa Mariya. Mngelo wa Yehova anafotokozera Mariya mwachimvekere kuti mwana amene adzamkhalira pathupi “[a]dzatchedwa Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:34, 35) Yosefe, amene anatomerana ndi Mariya, anauzidwa za kukhaliridwa pathupi kozizwitsa kwa Yesu nadziŵa kuti ameneyuyo “adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”—Mateyu 1:20, 21.
2. Kodi Yesu anachitanji pamene anali pafupifupi zaka 30, ndipo chifukwa ninji?
2 Pamene Yesu anali kukula, ayenera kukhala atazindikira zina za mfundo zimenezi zonena za kubadwa kwake kozizwitsa. Anadziŵa kuti Atate wake wakumwamba anamkonzera ntchito yopulumutsa miyoyo yoti achite padziko lapansi. Chotero, monga munthu wachikulire wazaka pafupifupi 30, Yesu anafika kwa mneneri wa Mulungu Yohane kuti adzabatizidwe mu mtsinje wa Yordano.—Marko 1:9; Luka 3:23.
3. (a) Kodi Yesu anatanthauzanji ndi mawu akuti “Nsembe ndi chopereka simunazifuna”? (b) Kodi ndi chitsanzo chapadera chotani chimene Yesu anapereka kwa onse ofuna kukhala ophunzira ake?
3 Yesu anali kupemphera panthaŵi ya ubatizo wake. (Luka 3:21) Malinga ndi umboni, kuyambira panthaŵi imeneyi ya moyo wake, anakwaniritsa mawu a Salmo 40:6-8, monga momwe mtumwi Paulo pambuyo pake anasonyezera kuti: “Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera ine.” (Ahebri 10:5) Motero Yesu anasonyeza kuzindikira kwake kuti Mulungu ‘sanafune’ nsembe zanyama kupitiriza kuperekedwa pakachisi wa Yerusalemu. M’malo mwake, anazindikira kuti Mulungu anali atamkonzera thupi laumunthu langwiro, Yesuyo, kuti alipereke monga nsembe. Zimenezi zinali kudzachotsa kufunika kulikonse kwa nsembe zanyama. Posonyeza chikhumbo chake chochokera mumtima cha kugonjera chifuniro cha Mulungu, Yesu anapitiriza kupemphera kuti: “Taonani, ndafika, (pamutu pake pa buku palembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.” (Ahebri 10:7) Nchitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga cha kulimba mtima ndi kudzipereka kopanda dyera chimene Yesu anapereka patsikulo kaamba ka onse amene adzakhala ophunzira ake!—Marko 8:34.
4. Kodi Mulungu anasonyeza motani kuvomereza kwake kudzipereka nsembe kwa Yesu?
4 Kodi Mulungu anasonyeza kuti wavomereza pemphero laubatizo la Yesu? Tiyeni tilole mmodzi wa atumwi a Yesu atiyankhe: “Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira iye, ndipo anapenya mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa iye; ndipo onani, mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 3:16, 17; Luka 3:21, 22.
5. Kodi nchiyani chimene guwa la nsembe looneka la pakachisi linachitira chithunzi?
5 Kuvomereza kwa Mulungu thupi la Yesu kaamba ka nsembe kunatanthauza kuti, m’lingaliro lauzimu, guwa la nsembe lalikulu kuposa limene linali m’kachisi wa Yerusalemu linali litaonekera. Guwa looneka la nsembe limene anali kuperekerapo nyama za nsembe linachitira chithunzi guwa la nsembe lauzimu limenelo, limene kwenikweni linali “chifuniro” cha Mulungu kapena makonzedwe a kuvomereza moyo waumunthu wa Yesu monga nsembe. (Ahebri 10:10) Nchifukwa chake mtumwi Paulo anakhoza kulembera Akristu anzake kuti: “Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema [kapena, kachisi] alibe ulamuliro wa kudyako.” (Ahebri 13:10) Mwa mawu ena, Akristu oona amapindula ndi nsembe yotetezera machimo imeneyi yoposa, imene ansembe achiyuda ambiri anakana.
6. (a) Kodi nchiyani chimene chinaonekera panthaŵi ya ubatizo wa Yesu? (b) Kodi dzina laulemulo Mesiya, kapena Kristu, limatanthauzanji?
6 Kudzozedwa kwa Yesu ndi mzimu woyera kunatanthauza kuti Mulungu tsopano analinganiza makonzedwe onse a kachisi wake wauzimu, Yesu akumatumikira monga Mkulu wa Ansembe. (Machitidwe 10:38; Ahebri 5:5) Wophunzira Luka anauziridwa kutchula chaka chenicheni cha chochitika chosaiŵalika chimenechi kukhala “chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara.” (Luka 3:1-3) Chimenecho chimagwirizana bwino ndi chaka cha 29 C.E.—masabata 69 enieni a zaka, kapena zaka 483, kuyambira pamene Mfumu Aritasasta anapereka lamulo lakuti malinga a Yerusalemu amangidwenso. (Nehemiya 2:1, 5-8) Malinga ndi ulosi, “wodzozedwayo, ndiye kalonga” akaonekera m’chaka chimenecho chonenedweratu. (Danieli 9:25) Malinga ndi umboni, Ayuda ambiri anali kuzindikira zimenezi. Luka amasimba kuti “anthu anali kuyembekezera” za kuonekera kwa Mesiya, kapena Kristu, maina aulemu a mawu achihebri ndi achigiriki amene ali ndi tanthauzo lofanana lakuti, “wodzozedwa.”—Luka 3:15.
7. (a) Kodi ndi liti pamene Mulungu anadzoza “Malo Opatulikitsa,” ndipo zimenezi zinatanthauzanji? (b) Kodi chinachitikanso nchiyani kwa Yesu panthaŵi ya ubatizo wake?
7 Panthaŵi ya ubatizo wa Yesu, malo okhala a Mulungu anadzozedwa, kapena kupatulidwa pambali, monga “Malo Opatulikitsa” m’kakonzedwe ka kachisi wamkulu wauzimu. (Danieli 9:24) “Chihema choona [kapena kachisi], chimene [Yehova] anachimanga, si munthu ayi” chinayamba kugwira ntchito. (Ahebri 8:2) Ndiponso, kupyolera m’kubatizidwa kwake ndi madzi ndi mzimu woyera, munthuyo Yesu Kristu anabadwanso monga Mwana wa Mulungu wauzimu. (Yerekezerani ndi Yohane 3:3.) Zimenezi zinatanthauza kuti Mulungu panthaŵi yake adzaitanira Mwana wake kumoyo wakumwamba, kumene adzatumikirako ali kudzanja lamanja la Atate wake monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe “nthaŵi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.”—Ahebri 6:20; Salmo 110:1, 4.
Malo Opatulikitsa Akumwamba
8. Kodi mpando wachifumu wa Mulungu kumwamba tsopano unakhala ndi mbali zatsopano zotani?
8 Patsiku la ubatizo wa Yesu, mpando wachifumu wakumwamba wa Mulungu unakhala ndi mbali zina. Kudziŵikitsidwa kwa nsembe yangwiro yaumunthu yotetezera machimo a dziko kunagogomezera chiyero cha Mulungu mosiyana ndi mkhalidwe wochimwa wa munthu. Chifundo cha Mulungu chinasonyezedwanso mwa njira yakuti tsopano anali wokonzekera kupembedzeka. Motero mpando wachifumu wa Mulungu kumwamba unakhala ngati chipinda chamkatikati cha kachisi, mmene mkulu wa ansembe anali kuloŵamo kamodzi pachaka ndi mwazi wa nyama kuti atetezere tchimo m’njira yophiphiritsira.
9. (a) Kodi nsalu yolekanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa inachitira chithunzi chiyani? (b) Kodi Yesu analoŵa motani kupyola nsalu yotchinga ya kachisi wauzimu wa Mulungu?
9 Nsalu yotchinga imene inalekanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa inachitira chithunzi thupi la Yesu. (Ahebri 10:19, 10) Linali chopinga chimene chinaletsa Yesu kuloŵa pamaso pa Atate wake pamene anali munthu padziko lapansi. (1 Akorinto 15:50) Panthaŵi ya imfa ya Yesu, “chinsalu chotchinga cha m’kachisi chinang’ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi.” (Mateyu 27:51) Zimenezi zinasonyeza mwamphamvu kuti chopinga chimene chinaletsa Yesu kuloŵa kumwamba tsopano chinali chitachotsedwa. Patapita masiku atatu, Yehova Mulungu anachita chozizwitsa chapadera. Anaukitsa Yesu kwa akufa, osati monga munthu wa nyama ndi mwazi amene angafe, koma monga cholengedwa chauzimu chaulemerero ‘chokhalako nthaŵi yosatha.’ (Ahebri 7:24) Patapita masiku makumi anayi, Yesu anakwera kumwamba naloŵa mu “Malo Opatulikitsa” enieni, “kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.”—Ahebri 9:24.
10. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Yesu anapereka mtengo wa nsembe yake kwa Atate wake wakumwamba? (b) Kodi kudzozedwa ndi mzimu woyera kunatanthauzanji kwa ophunzira a Kristu?
10 Kodi Mulungu anavomereza mtengo wa mwazi wa Yesu wokhetsedwa kukhala chotetezera machimo a dziko? Indedi iye anatero. Umboni wa zimenezi unafika patapita masiku 50 Yesu atauka, patsiku la phwando la Pentekoste. Mzimu woyera wa Mulungu unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu 120 amene anasonkhana m’Yerusalemu. (Machitidwe 2:1, 4, 33) Monga Mkulu wa Ansembe wawo, Yesu Kristu, iwo tsopano anali odzozedwa kutumikira monga “ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu” m’makonzedwe a Mulungu a kachisi wamkulu wauzimu. (1 Petro 2:5) Ndiponso, odzozedwa ameneŵa anapanga mtundu watsopano, “mtundu woyera mtima” wa Mulungu wa Israyeli wauzimu. Kuyambira pamenepo, maulosi onse a zinthu zabwino ponena za Israyeli, monga ngati a lonjezo la “pangano latsopano” lolembedwa pa Yeremiya 31:31, anayamba kugwira ntchito pa mpingo wachikristu wodzozedwa, “Israyeli wa Mulungu” weniweni.—1 Petro 2:9; Agalatiya 6:16.
Mbali Zina za Kachisi Wauzimu wa Mulungu
11, 12. (a) Kodi bwalo la ansembe linachitira chithunzi chiyani kwa Yesu, ndipo kodi ilo nchiyani kwa otsatira ake odzozedwa? (b) Kodi mkhate wa madzi umachitira chithunzi chiyani, ndipo umagwiritsiridwa ntchito motani?
11 Ngakhale kuti Malo Opatulikitsa anachitira chithunzi “m’mwamba momwe,” mmene muli mpando wachifumu wa Mulungu, mbali zina zonse za kachisi wauzimu wa Mulungu nzogwirizana ndi zinthu za padziko lapansi. (Ahebri 9:24) Mu kachisi wa mu Yerusalemu, munali bwalo lamkati la ansembe lokhala ndi guwa la nsembe ndi mkhate waukulu wa madzi, umene ansembe anali kusambamo asanayambe kuchita utumiki wopatulika. Kodi zinthu zimenezi zikuchitira chithunzi chiyani m’kakonzedwe ka kachisi wauzimu wa Mulungu?
12 Kwa Yesu Kristu, bwalo lamkati la ansembe linachitira chithunzi mkhalidwe wake wopanda uchimo monga Mwana wa Mulungu waumunthu wangwiro. Mwa kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu, otsatira odzozedwa a Kristu amayesedwa olungama. Motero, Mulungu moyenera angachite nawo zinthu monga ngati kuti alibe uchimo. (Aroma 5:1; 8:1, 33) Chifukwa chake, bwalo limeneli limachitiranso chithunzi mkhalidwe wonenedwa kukhala wolungama waumunthu umene aliyense payekha wa ansembe oyera mtimawo ali nawo pamaso pa Mulungu. Panthaŵi imodzimodziyo, Akristu odzozedwa akali opanda ungwiro ndipo okhoza kuchimwa. Mkhate wa madzi wa m’bwalowo umachitira chithunzi Mawu a Mulungu, amene Mkulu wa Ansembe amagwiritsira ntchito kusambitsira ansembe oyera mtima mopita patsogolo. Mwa kuvomereza kusambitsidwa kumeneku, iwo akhala ndi kaonekedwe kabwino kwambiri kamene kamalemekeza Mulungu ndi kukokera anthu akunja m’kulambira kwake koyera.—Aefeso 5:25, 26; yerekezerani ndi Malaki 3:1-3.
Malo Opatulika
13, 14. (a) Kodi Malo Opatulika a kachisi amachitira chithunzi chiyani kwa Yesu ndi otsatira ake odzozedwa? (b) Kodi choikapo nyali chagolidi chimachitira chithunzi chiyani?
13 Chipinda choyamba cha kachisi chimachitira chithunzi mkhalidwe wapamwamba kuposa uja wa bwalo. Kwa munthu wangwiroyo Yesu Kristu, chinachitira chithunzi kubadwanso kwake monga Mwana wa Mulungu wauzimu woyembekezera kubwerera kumoyo wakumwamba. Atayesedwa olungama pa maziko a kukhulupirira kwawo mwazi wokhetsedwa wa Kristu, otsatira odzozedwa ameneŵa amakhalanso ndi mzimu wa Mulungu wapadera wogwira ntchito pa iwo. (Aroma 8:14-17) Kupyolera “mwa madzi [ndiko kuti, ubatizo wawo] ndi mzimu,” ‘amabadwa mwatsopano’ monga ana a Mulungu auzimu. Pokhala otero, amakhala ndi chiyembekezo choukitsidwira ku moyo wakumwamba monga ana a Mulungu auzimu, ngati apitirizabe kukhala okhulupirika kufikira imfa.—Yohane 3:5, 7; Chivumbulutso 2:10.
14 Ansembe amene anatumikira m’Malo Opatulika apadziko lapansi sanaonekere kwa olambira okhala kunja. Mofananamo, Akristu odzozedwa ali ndi mkhalidwe wauzimu umene sagaŵana ndi ena kapena umene unyinji wa olambira Mulungu sungaumvetse, amene chiyembekezo chawo chili cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. Choikapo nyali chagolidi cha m’chihema chimachitira chithunzi mkhalidwe wounikiridwa wa Akristu odzozedwa. Mzimu woyera wa Mulungu, mofanana ndi mafuta a m’nyali, umagwira ntchito ya kuunikira pa Baibulo kulimveketsa. Kuzindikira kumene Akristu amakupeza pa zimenezi, samangokusunga. M’malo mwake, amamvera Yesu, amene anati: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. . . . Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:14, 16.
15. Kodi nchiyani chimene mkate wa pa gome la mkate woonekera umachitira chithunzi?
15 Kuti akhalebe mumkhalidwe wounikiridwa umenewu, Akristu odzozedwa ayenera nthaŵi zonse kudya chochitiridwa chithunzi ndi mkate wa pa gome la mkate woonekera. Magwero awo aakulu a chakudya chauzimu ndiwo Mawu a Mulungu, amene iwowo amayesayesa kuŵerenga ndi kuwasinkhasinkha tsiku ndi tsiku. Yesu analonjezanso kuwapatsa “zakudya panthaŵi yake” kupyolera mwa “kapolo [wake] wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) “Kapolo” ameneyu ndiye gulu lonse la Akristu odzozedwa padziko lapansi amene akhalako panthaŵi iliyonse. Kristu wagwiritsira ntchito gulu la odzozedwa limeneli kufalitsa chidziŵitso pa kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo ndi kupereka chitsogozo chapanthaŵi yake pa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo watsiku ndi tsiku wamakono. Chifukwa chake, Akristu odzozedwa moyamikira amadya chakudya chonse chauzimu choperekedwa chimenecho. Koma chichirikizo cha moyo wawo wauzimu chimadalira pa zoposa kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu m’maganizo ndi m’mtima mwawo. Yesu anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Mofananamo, Akristu odzozedwa amapeza chikhutiro mwa kulimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu chovumbulidwa tsiku ndi tsiku.
16. Kodi nchiyani chimene utumiki wochitidwa pa guwa la nsembe lofukizapo umachitira chithunzi?
16 Mmaŵa ndi madzulo, wansembe anapereka nsembe ya zofukiza kwa Mulungu pa guwa la nsembe lofukizapo m’Malo Opatulika. Panthaŵi imodzimodziyo, olambira osakhala ansembe anali kupemphera kwa Mulungu pamene anali chiimire m’mabwalo a kachisi wake. (Luka 1:8-10) “Zofukiza,” Baibulo limafotokoza motero, “ndizo mapemphero a oyera mtima.” (Chivumbulutso 5:8) “Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu,” wamasalmo Davide analemba motero. (Salmo 141:2) Akristu odzozedwa nawonso amaŵerengera kwambiri mwaŵi wawo wa kufikira Yehova m’pemphero kupyolera mwa Yesu Kristu. Mapemphero aphamphu amene amachokera mumtima ali ngati zofukiza za fungo lokoma. Akristu odzozedwa amatamandanso Mulungu m’njira zina, kugwiritsira ntchito milomo yawo kuphunzitsa ena. Chipiriro chawo poyang’anizana ndi mavuto ndi umphumphu wawo poyesedwa zili zinthu zokondweretsa kwambiri kwa Mulungu.—1 Petro 2:20, 21.
17. Kodi nchiyani chimene chinaloŵetsedwamo pokwaniritsa chithunzi chaulosi chimene chinaperekedwa mwa kuloŵa koyamba m’Malo Opatulikitsa kwa mkulu wa ansembe pa Tsiku Lotetezera?
17 Pa Tsiku Lotetezera, mkulu wa ansembe wa Israyeli anali kuloŵa m’Malo Opatulikitsa ndi kufukiza zofukiza pa mbale yagolidi ya makala amoto. Anafunikira kuchita zimenezi asanapititse mwazi wa nsembe za uchimo. Pokwaniritsa chithunzi chaulosi chimenechi, mwamunayo Yesu anasunga umphumphu wonse kwa Yehova Mulungu asanapereke moyo wake nsembe yachikhalire kaamba ka machimo athu. Motero iye anasonyeza kuti munthu wangwiro atha kusunga umphumphu wake kwa Mulungu mosasamala kanthu za chitsenderezo chilichonse chimene Satana angamuikire. (Miyambo 27:11) Pamene anayesedwa, Yesu anagwiritsira ntchito pemphero “ndi kulira kwakukulu ndi misozi . . . ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu.” (Ahebri 5:7) M’njira imeneyi analemekeza Yehova monga Mfumu ya chilengedwe chonse yolungama ndi yoyenera. Mulungu anafupa Yesu mwa kumuukitsa kwa akufa kuloŵa m’moyo wakumwamba wosafa. M’malo ameneŵa apamwamba, Yesu amaika mtima pa chifukwa chachiŵiri cha kudza kwake kudziko lapansi, ndiko kuti, kuyanjanitsa anthu ochimwa olapa ndi Mulungu.—Ahebri 4:14-16.
Ulemerero Woposa wa Kachisi Wauzimu wa Mulungu
18. Kodi Yehova wabweretsa motani ulemerero wapadera m’kachisi wake wauzimu?
18 “Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo,” ananeneratu motero Yehova. (Hagai 2:9) Mwa kuukitsa Yesu kukhala Mfumu yosafa ndi Mkulu wa Ansembe, Yehova anabweretsa ulemerero wapadera m’kachisi wake. Tsopano Yesu ali ndi udindo wa kupereka “kwa onse akumvera iye . . . chipulumutso chosatha.” (Ahebri 5:9) Oyamba kusonyeza kumvera kumeneko anali ophunzira 120 amene analandira mzimu woyera pa Pentekoste mu 33 C.E. Buku la Chivumbulutso linaneneratu kuti ana auzimu ameneŵa a Israyeli potsirizira pake adzakwanira 144,000. (Chivumbulutso 7:4) Atafa, ambiri a iwo anafunikira kugona m’manda a anthu onse, akumayembekezera nthaŵi ya kukhalapo kwa Yesu mu mphamvu yaufumu. Kuŵerengera zaka kwa ulosi kwa mu Danieli 4:10-17, 20-27 kumasonyeza 1914 kukhala nthaŵi ya Yesu ya kuyamba kulamulira pakati pa adani ake. (Salmo 110:2) Kwa zaka makumi ambiri nthaŵiyo isanafike, Akristu odzozedwa anayembekezera mwachidwi kufika kwa chakacho. Nkhondo yadziko yoyamba ndi masoka ake pa anthu zinapereka umboni wakuti Yesu anakhazikitsidwadi pa mpando wachifumu monga Mfumu mu 1914. (Mateyu 24:3, 7, 8) Posapita nthaŵi, nthaŵi yakuti “chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu” itafika, Yesu anakwaniritsa lonjezo kwa ophunzira ake odzozedwa amene anali atagona mu imfa lakuti: “Ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha.”—1 Petro 4:17; Yohane 14:3.
19. Kodi otsalira a 144,000 amaloŵa motani ku Malo Opatulikitsa akumwamba?
19 Ziŵalo za 144,000 za ansembe oyera mtima sizinamalizidwebe zonse kuikidwa chizindikiro ndi kusonkhanitsidwa kukakhala kwawo, kumwamba. Otsalira a iwo akali ndi moyo padziko lapansi mumkhalidwe wauzimu wochitiridwa chithunzi ndi Malo Opatulika, olekanitsidwa ndi malo opatulika a Mulungu ndi “nsalu yotchinga,” kapena chopinga, cha matupi awo anyama. Pamene ameneŵa afa ali okhulupirika, amaukitsidwa nthaŵi yomweyo monga zolengedwa zauzimu zosafa kukagwirizana ndi aja a 144,000 amene ali kale kumwamba.—1 Akorinto 15:51-53.
20. Kodi ndi ntchito iti yofunika imene otsalira a ansembe oyera mtima akuchita panthaŵi ino, ndipo ndi zotulukapo zotani?
20 Pokhala ndi ansembe ambiri chotero otumikira pamodzi ndi Mkulu wa Ansembe kumwamba, kachisi wauzimu wa Mulungu walandira ulemerero wowonjezereka. Zikali choncho, otsalira a ansembe oyera mtima akuchita ntchito yofunika padziko lapansi. Kupyolera mwa kulalikira kwawo, Mulungu ‘akugwedeza amitundu onse’ ndi mawu achiweruzo chake, monga momwe kunanenedweratu pa Hagai 2:7. Panthaŵi imodzimodziyo, mamiliyoni ambiri a olambira olongosoledwa kukhala “zofunika za amitundu onse” akuloŵa m’mabwalo apadziko lapansi a kachisi wa Yehova. Kodi ameneŵawo amayenerera motani m’makonzedwe a kulambira a Mulungu, ndipo kodi ndi ulemerero wina wotani wamtsogolo wa kachisi wake wauzimu umene tingayembekezere? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
Mafunso a Kupenda
◻ Kodi Yesu anapereka chitsanzo chapadera chotani mu 29 C.E.?
◻ Kodi ndi makonzedwe otani amene anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E.?
◻ Kodi nchiyani chimene Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa amachitira chithunzi?
◻ Kodi kachisi wauzimu wamkulu walemekezedwa motani?
[Chithunzi patsamba 17]
Pamene Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E., kachisi wauzimu wamkulu wa Mulungu anayamba kugwira ntchito