Ndani Adzakhala Wovomerezedwa ndi Yehova?
“Gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu . . . ; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.”—AFILIPI 2:12, 13.
1, 2. Ndi mu mkhalidwe wotani mmene Yesu analandira chilengezo cha chivomerezo chaumulungu, ndipo nchifukwa ninji ichi chiyenera kutikondweretsa?
PANALI posinthira zinthu m’mbiri. Yohane Mbatizi anakhala akulalikira uthenga wa Mulungu ndi kumiza olapa m’madzi. Kenaka munthu anamufikira amene Yohane anamudziŵa kukhala wolungama; iye anali Yesu. Iye analibe chimo kaamba ka limene anafunikira kulapa, komabe iye anafunsa kuti abatizidwe ‘kuti akwaniritse chilungamo chonse.’—Mateyu 3:1-15.
2 Yohane atagonjera modekha, ndipo Yesu atatuluka m’madzi, “miyamba inatseguka kwa iye, ndipo anapenya mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda.” Choposa chimenecho, panali “mawu ochokera ku miyamba akuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa, [yemwe ndavomereza, NW].’ “ (Mateyu 3:16, 17; Marko 1:11) Chiri chigamulo chotani nanga! Tonsefe timasangalala ndi kusangalatsa wina wake amene timalemekeza. (Machitidwe 6:3-6; 16:1, 2; Afilipi 2:19-22; Mateyu 25:21) Tangolingalirani, kenaka, mmene mukamverera ngati Mulungu Wamphamvuyonse analengeza kuti, ‘Ndakuvomerezani!’
3. Nchiyani chomwe tiyenera kukhala odera nacho nkhaŵa ponena za chivomerezo cha Mulungu?
3 Kodi chiri chothekera kwa munthu kukhala wovomerezedwa ndi Mulungu lerolino? Mwachitsanzo, tengani munthu amene ‘alibe chiyembekezo ndipo alibe Mulungu m’dziko,’ akumakhala “oyesedwa alendo a moyo wa Mulungu.” (Aefeso 2:12; 4:18) Kodi iye angasinthe kuchokera ku mkhalidwe umenewo kupita ku mkhalidwe wodalitsidwa wa kukhala wovomerezedwa ndi Yehova? Ngati ndi tero, motani? Tiyeni tiwone.
Kodi Mawu Ake Anatanthauzanji?
4. (a) Ndi liti limene liri lingaliro la liwu la Chigriki kaamba ka “kuvomerezedwa” m’chilengezo cha Mulungu? (b) Nchifukwa ninji kugwiritsidwa ntchito m’nkhaniyi kuli kosangalatsa mwapadera?
4 Zolembera za Uthenga Wabwino wa mawu a Mulungu akuti “Ndavomereza [Yesu]” zimagwiritsira ntchito verebu la Chigriki eu·do·keʹo. (Mateyu 3:17; Marko 1:11; Luka 3:22) Ilo limatanthauza “kukhala wokondweretsedwa bwino, kulingalira moyanjika, kutenga chikondwerero mu,” ndipo mtundu wake wa nauni uli ndi lingaliro lakuti “chifuno chabwino, chisangalalo chabwino, chiyanjo, chifuno, chikhumbo.” Eu·do·keʹo siliri lolekezera ku chivomerezo chaumulungu. Mwachitsanzo, Akristu mu Makedoniya ‘anakondweretsedwa’ kugawana mwa za chuma ndi ena. (Aroma 10:1; 15:26; 2 Akorinto 5:8; 1 Atesalonika 2:8; 3:1) Komabe, chivomerezo chimene Yesu analandira chinasonyezedwa ndi Mulungu, osati anthu. Mawu amenewa amagwiritsiridwa ntchito kulozera kwa Yesu kokha pambuyo pa kubatizidwa. (Mateyu 17:5; 2 Petro 1:17) Mosangalatsa, Luka 2:52 amagwiritsira ntchito liwu losiyanako—khaʹris—m’kulankhula za Yesu monga wachichepere wosabatizidwa yemwe analandira “chiyanjo” kuchokera kwa Mulungu ndi anthu.
5. (a) Ndimotani mmene chiriri chowonekera kuti anthu opanda ungwiro angavomerezedwe ndi Mulungu? (b) Ndani omwe ali “anthu okondwera nawo”?
5 Kodi chirinso chothekera kaamba ka anthu opanda ungwiro monga ife kupeza chivomerezo cha Mulungu? Mwachimwemwe, yankho liri inde. Pamene Yesu anabadwa, angelo analengeza kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo [eu·do·kiʹas].” (Luka 2:14) M’Chigriki chenicheni, angelo anali kuyimba za dalitso lomadza “kwa anthu olingalira bwino” kapena “anthu amene Mulungu wawavomereza.”a Profesa Hans Bietenhard akulemba za kugwiritsira ntchito kwa en an·throʹpois eu·do·kiʹas: “Mawuwo amalozera kwa anthu osangalatsa bwino kwa Mulungu . . . sitiri, chotero, kuchita pano ndi ubwino wa anthu . . . Tikuchita ndi ubwino wa ulamuliro chisomo cha Mulungu, chomwe chimasankha kaamba ka icho chokha anthu kaamba ka chipulumutso.” Chotero, monga mmene Mboni za Yehova zakhala zikulongosola kwa nthaŵi yaitali, Luka 2:14 amasonyeza kuti kupyolera m’kudzipereka ndi ubatizo, chiri chothekera kwa anthu opanda ungwiro kukhala anthu okondwera, anthu ovomerezedwa ndi Mulungu!b
6. Nchiyani chomwe tikufunikirabe kuphunzira ponena za chivomerezo cha Mulungu?
6 Inu mungazindikire, ngakhale kuli tero, kusiyana komwe kulipo pakati pa kukhala ‘adani a Mulungu ndi maganizo pa ntchito zomwe ziri zoipa’ ndi kukhala ovomerezedwa monga oyanjana a Mulungu wathu wa chilungamo ndi wanzeru. (Akolose 1:21, NW; Salmo 15:1-5) Chotero, ngakhale kuti mungamasulidwe kumva kuti anthu angakhale ovomerezedwa, inu mungafune kudziŵa chimene chikukhudzidwa. Tingaphunzire zambiri ponena za ichi kuchokera m’zochita zakale za Mulungu.
Iye Analandira Anthu
7. Eksodo 12:38 amapereka chisonyezero chotani ponena za mkhalidwe wa Mulungu?
7 Kwa zaka mazana angapo chisanachitidwe chilengezo cha pa Luka 2:14, Yehova analandira anthu kubwera ndi kudzamulambira iye. Ndithudi, Mulungu anali kuchita kotheratu ndi mtundu wa Israyeli, womwe unali wodzipereka kwa iye. (Eksodo 19:5-8; 31:16, 17) Kumbukirani, ngakhale ndi tero, kuti pamene Israyeli anatukuka ukapolo wa chiIgupto, “anthu ambiri osakanizana anapita nawo.” (Eksodo 12:38, NW) Osakhala Aisrayeli amenewo omwe angakhale anali ndi zochita ndi anthu a Mulungu ndi kuchitira umboni miliri pa Igupto tsopano anasankha kupita ndi Israyeli. Ena mwachidziŵikire anakhala atembenuki otheratu.
8. Ndi mitundu iŵiri iti ya alendo omwe anakhala mu Israyeli, ndipo nchifukwa ninji panali kusiyana mmene Aisrayeli anachitira nawo?
8 Pangano la Lamulo linavomereza mkhalidwe wa osakhala Aisrayeli mu unansi kwa Mulungu ndi anthu ake. Alendo ena anali okhala omwe anangokhala kokha m’dziko la Israyeli, kumene iwo anafunikira kumvera malamulo oyambirira, onga ngati aja otsutsa kupha ndi ofunikira kusunga Sabata. (Nehemiya 13:16-21) M’malo mokupatira okhala m’dziko amenewo monga abale, m’Israyeli anasonyeza kuchenjera kolingalirika pamene anali kulankhula kapena kuchita ndi iwo, popeza kuti anali asanakhalebe mbali ya mtundu wa Mulungu. Mwachitsanzo, pamene kuli kwakuti m’Israyeli sanavomerezewe kugula ndi kudya mtembo wa nyama yosakhetsedwa mwazi yomwe inafa yokha, alendo oterowo omwe sanali atembenuki akachita tero. (Deuteronomo 14:21; Ezekieli 4:14) M’kupita kwa nthaŵi ena a alendo odzakhala amenewa akatsatira njira ya alendo ena omwe anakhala atembenuki odulidwa. Kokha pamenepo ndi pamene iwo anachitiridwa monga abale m’kulambira kowona, oŵerengera kusunga Lamulo lonse. (Levitiko 16:29; 17:10; 19:33, 34; 24:22) Rute, m’Moabu, ndi Namani, wakhate wa ku Siriya, anali osakhala Aisrayeli omwe Mulungu anawavomereza.—Mateyu 1:5; Luka 4:27.
9. Ndimotani mmene Solomo anatsimikizira mkhalidwe wa Mulungu kulinga kwa alendo?
9 M’masiku a Mfumu Solomo, tikuwonanso mkhalidwe wolonjera wa Mulungu kulinga kwa osakhala Aisrayeli. Pamene anali kupereka kachisi, Solomo anapemphera kuti: “Ndiponso kunena za mlendo, osati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m’dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu . . . akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika ku nyumba ino; mverani inu m’mwamba mokhala inu, . . . kuti anthu onse a dziko lapansi adziŵe dzina lanu, kuwopa inu monga mumatero anthu anu Aisrayeli.” (1 Mafumu 8:41-43) Inde, Yehova analandira mapemphero a alendo owona mtima omwe anafunafuna kaamba ka iye. Mwinamwake awa nawonso akaphunzira malamulo ake, kugonjera ku kachitidwe ka kudulidwa, ndipo kukhala ziwalo zolandiridwa za anthu ake odalitsidwa.
10. Ndimotani mmene Ayuda akanachitira ndi mdindo wa ku Aitiopiya, ndipo nchifukwa ninji m’dulidwe unampindulitsa iye?
10 Munthu mmodzi amene anachita ichi m’nthaŵi zakale anali wosunga chuma wa Mfumukazi Kandake ku Aitiopiya wakutali. Mwachidziŵikire, pamene iye choyamba anamva za Ayuda ndi kulambira kwawo, njira yake ya moyo kapena njira za chipembedzo zinali zosalandirika kwa Yehova. Chotero Ayuda anayenera kusonyeza mlingo wa kulekelera pamene mlendo ameneyu pakati pawo anali kuphunzira Lamulo kuti adziŵe zifuno za Mulungu. Iye mwachidziŵikire anapita patsogolo ndi kupanga masinthidwe ofunikira kuyeneretsedwa kaamba ka m’dulidwe. Machitidwe 8:27 amatiwuza ife kuti iye “anadza ku Yerusalemu kudzapemphera.” (Eksodo 12:48, 49) Ichi chikasonyeza kuti iye anali mtembenuki wotheratu. Iye chotero anali mu mkhalidwe wa kulandira Mesiya ndi kukhala wophunzira wake wobatizidwa, mwakutero kukhala mumzere ndi chifuno chopita patsogolo cha Mulungu.
Osakhulupirira ndi Mpingo Wachikristu
11, 12. (a) Ndi kusintha kowonjezereka kotani kumene kunachitika pamene m’Aitiopiyayo anabatizidwa? (b) Ndimotani mmene ichi chinaliri chogwirizana ndi Afilipi 2:12, 13?
11 Yesu anawuza otsatira ake: “Chifukwa chake mukani phunzitsani anthu amitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Mtembenuki wa ku Aitiopiya wotchulidwa kaleyu anali ndi chidziŵitso cha Yehova ndi cha mzimu wake woyera. Chotero pamene Filipo anamthandiza iye kumvetsetsa ndi kulandira Yesu monga Mwana wa Mulungu wa umesiya, iye akabatizidwa. Iye chotero akakhala chiwalo chovomerezedwa cha anthu a Yehova omwe anali kutsatira Kristu. Mwachibadwa, iye akakhala woŵerengera kwa Mulungu, wofunikira ‘kusunga zinthu zose zolamulidwa’ kaamba ka Akristu. Koma ndi kuŵerengera kumeneku kunabwera chiyembekezo chozizŵitsa: chipulumutso!
12 Pambuyo pake, Paulo analemba kuti Akristu onse anafunikira ‘kugwirira ntchito chipulumutso chawo ndi mantha ndi kunthunthumira.’ Komabe, chinali chothekera kuchita chimenecho, “pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha [chisangalalo chabwino, NW] chake [eu·do·kiʹas], ndiye Mulungu.”—Afilipi 2:12, 13.
13. Ndimotani mmene Akristu akanachitira ndi awo omwe sanali ofulumira kubatizidwa monga mdindo wa ku Aitiopiya?
13 Si onse amene anabwera m’chigwirizano ndi Akristu owona amene anali okonzekera ndi oyeneretsedwa monga munthu wa ku Aitiopiya ameneyo kuyenda mofulumira ku ubatizo. Ena, osakhala Ayuda kapena atembenuki, anali ndi chidziŵitso chochepera kapena analibiretu cha Yehova ndi njira zake; ndipo panalibenso mkhalidwe wotsogozedwa ndi miyezo yake. Ndimotani mmene iwo akachitidwira? Akristu anayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu. Iye ndithudi sana limbikitse kapena ngakhale kulekelera chimo. (Yohane 5:14) Komabe, iye anali wololera kulinga kwa ochimwa omwe anakokedwera kwa iye ndi omwe anakhumba kubweretsa njira zawo m’chigwirizano ndi zija za Mulungu.—Luka 15:1-7.
14, 15. Pambali pa Akristu odzozedwa, ndi mtundu wotani wa anthu omwe anapezeka ku misonkhano mu Korinto, ndipo ndimotani mmene iwo anasiyanirana ponena za kupita patsogolo kwauzimu?
14 Kunena kuti Akristu anachita mololera ndi awo omwe anali kuphunzira ponena za Mulungu chiri chomvekera bwino kuchokera ku ndemanga za Paulo ponena za misonkhano mu Korinto. M’kukambitsirana kugwiritsira ntchito kwa mphatso zozizwitsa za mzimu zomwe poyambirira zinazindikiritsa Chikristu kukhala chokhala ndi dalitso la Mulungu, Paulo anatchula “okhulupirira” ndi “osakhulupirira.” (1 Akorinto 14:22) “Okhulupirira” anali awo omwe analandira Kristu ndipo anabatizidwa. (Machitidwe 8:13; 16:31-34) “Akorinto ambiri anamva nakhulupirira nabatizidwa.”—Machitidwe 18:8.
15 Mogwirizana ndi 1 Akorinto 14:24, ‘anthu osakhulupirira kapena osaphunzira’ anabweranso ku misonkhano mu Korinto ndipo anali olandiridwa kumeneko.c Mwachidziŵikire, iwo anasiyanasiyana ponena za kupita kwawo patsogolo m’kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu. Ena angakhale anali kuchitabe chimo. Ena angakhale anapeza muyezo wa chikhulupiriro, kupanga kale masinthidwe ena m’miyoyo yawo, ndipo, ngakhale asanabatizidwe, anayamba kuwuza ena ponena za zimene anaphunzira.
16. Ndimotani mmene anthu oterowo akapindulira kuchokera ku kukhala pakati pa Akristu pa misonkhano ya mpingo?
16 Ndithudi, palibe aliyense wa osabatizidwa amenewa amena anali “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Ngati zakumbuyo zawo zinaphatikizapo zophophonya zowopsya za makhalidwe ndi zauzimu, icho mwachimvekere chinawatengera iwo onthaŵi kusinthira ku miyezo ya Mulungu. Pa nthaŵiyo, kokha ngati iwo sanayesere mwa nkhalwe kukhotetsa chikhulupiriro ndi chiyero cha mpingo, iwo anali olandiridwa. Chimene anawona ndi kumva pa misonkhano ‘[chikawadzudzula iwo, NW]’ pamene ‘zobisika za mitima yawo zinawonekera.’—1 Akorinto 14:23-25; 2 Akorinto 6:14.
Kukhalabe Ovomerezedwa ndi Mulungu kaamba ka Chipulumutso
17. Luka 2:14 anali ndi kukwaniritsidwa kotani m’zana loyamba?
17 Kupyolera m’kulalikira kwapoyera kwa Akristu obatizidwa m’zana loyamba, zikwi zingapo zinamva mbiri yabwino. Iwo anaika chikhulupiriro m’zimene anamva, kulapa za njira yawo yakale, ndipo anabatizidwa, kupanga “chilengezo chapoyera kaamba ka chipulumutso.” (Aroma 10:10-15, NW; Machitidwe 2:41-44; 5:14; Akolose 1:23) Panalibe chikaikiro chakuti obatizidwawo kubwerera m’nthaŵi imeneyo anali ndi chivomerezo cha Yehova, popeza kuti iye anawadzoza iwo ndi mzimu woyera, kuwatenga iwo monga ana auzimu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga [mwa chisangalalo chabwino, NW] [eu·do·kiʹan] cha chifuniro chake.” (Aefeso 1:5) Chotero, mkati mwa zana limenelo chomwe chinaloseredwa ndi angero pa kubadwa kwa Yesu chinayamba kutsimikizira kukhala chowona kuti: “Mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo [kapena, anthu amene ali ndi chivomerezo cha Mulungu].”—Luka 2:14.
18. Nchifukwa ninji Akristu odzozedwa sakanatengera mosasamala kaimidwe kawo kovomerezedwa ndi Mulungu?
18 Kuti asungirire mtendere umenewo, chinali choyenerera kaamba ka “anthu okondwera nawo” amenewo “kugwirira ntchito chipulumutso [chawo] ndi mantha ndi kunthunthumira.” (Afilipi 2:12) Chimenecho sichinali chopepuka, popeza kuti anali adakali anthu opanda ungwiro. Iwo akayang’anizana ndi ziyeso ndi zitsenderezo za kuchita cholakwa. Ngati iwo anagonjera ku kuchita cholakwa, iwo akataya chivomerezo cha Mulungu. Chotero, Yehova mwachikondi anakonza kaamba ka abusa auzimu omwe ponse paŵiri akathandiza ndi kuchinjirirza mipingo.—1 Petro 5:2, 3.
19, 20. Ndi makonzedwe otani amene Mulungu anapanga kotero kuti akristu obatizidwa akapitiriza kukhala atumiki ake ovomerezedwa?
19 Akulu a mu mpingo oterowo akatenga ku mtima uphungu wa Paulo: “Abale ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu mubweze woteroyo mu mzimu wa chifatso, ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.” (Agalatiya 6:1) Monga mmene tingamvetsetsere, munthu yemwe atenga sitepi lofunika koposa la ubatizo akakhala woŵerengera mokulira, mongadi mmene chinaliri chowona kwa mlendo yemwe anakhala mtembenuki wodulidwa mu Israyeli. Mosasamala kanthu za chimenecho, ngati Mkristu wobatizidwa analakwa, iye akanapeza thandizo lachikondi mkati mwa mpingo.
20 Gulu la akulu mu mpingo lingapereke thandizo kwa mmodzi yemwe agwera m’kuchita cholakwa kokulira. Yuda analemba kuti: “Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo; koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto. Koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane nawonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.” (Yuda 22, 23) Chiwalo chobatizidwa cha mpingo chomwe chinathandizidwa mwa njira imeneyi chingapitirize kusangalala ndi chivomerezo cha Yehova ndi mtendere umene angelo analankhula pa kubadwa kwa Yesu.
21, 22. Nchiyani chomwe chikatulukapo ngati wina wake akakhala wochimwa wosalapa, ndipo ndimotani mmene ziwalo zokhulupirika za mpingo zikachitira?
21 Ngakhale kuti siziri zofala, panali nthaŵi zina pamene wochita cholakwayo anal wosalapa. Kenaka akulu akayenera kumuchotsa iye kuti achinjirize chiyero cha mpingo kuchokera ku kudetsedwa. Chimenecho chinawoneka ndi mwamuna wobatizidwa mu Korinto yemwe anawumirira m’maunansi a chisembwere. Paulo anachenjeza mpingo kuti: “Musayanjane ndi achigololo, si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi kapena ndi osirira ndi okwatula kapena ndi opembedza mafano. Pakuti m’kutero, mukatuluke m’dziko lapansi. Koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo kapena wosirira kapena wopembedza mafano kapena wolalatira kapena woledzera kapena wolanda ngakhale kukadya naye wotere iai.”—1 Akorinto 5:9-11.
22 Popeza munthu wa ku Korintoyo anatenga sitepi lofunika koposa la ubatizo, kukhala wovomerezedwa ndi Mulungu ndipo chiwalo cha mpingo, kuchotsedwa kwake kunali nkhani yowopsya kwambiri. Paulo anasonyeza kuti Akristu sanayenera kuyanjana naye, popeza kuti iye anakana kaimidwe kake kovomerezeka ndi Mulungu. (Yerekezani ndi 2 Yohane 10, 11.) Petro analemba ponena za ochotsedwa oterowo: “Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo ndi poizindikira kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yowona: ‘Garu wabwerera ku masanzi ake.’”—2 Petro 2:21, 22.
23. M’zana loyamba, nchiyani chomwe chinali mkhalidwe wachisawawa pakati pa Akristu ponena za kusungirira kuvomerezedwa kwa Mulungu?
23 Yehova mwachidziŵikire sakanawonanso anthu oterowo kukhala ovomerezedwa, popeza kuti iwo anachotsedwa kaamba ka kukhala ochita cholakwa osalapa. (Ahebri 10:38; yerekezani ndi 1 Akorinto 10:5.) Mwachiwonekere, kokha ochepera anachotsedwa. Ambiri omwe anapeza “chisomo ndi mtendere wochokera kwa Mulungu” ndipo ‘analandiridwa ngati ana monga umo kunakomera chifuniro chake’ anakhala okhulupirika.—Aefeso 1:2, 5, 8-10.
24. Ndi mbali yotani ya nkhaniyi yomwe imafunikira chisamaliro chathu chowonjezereka?
24 Chimenecho chiridi tero m’nthaŵi yathu inonso. Tiyeni tilingalire, ngakhale ndi tero, mmene ‘osakhulupirira kapena anthu osaphunzira’ angathandizidwire kukhala ovomerezedwa ndi Mulungu lerolino ndi chimene chingachitidwe kuthandiza iwo ngati alakwa m’njiramo. Nkhani yotsatirayi idzachita ndi nkhani zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezani ndi “men-whom-he-approves, [anthu amene amawavomereza],” New Testament, lolembedwa ndi George Swann; “men with whom he is pleased, [anthu amene akondwera nawo],” The Revised Standard Version.
b Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1965, masamba 243-256.
c “ἄπιστος (apistos, ‘wosakhulupirira’) ndi ιδιώτης (idiōtēs, ‘wopanda kumvetsetsa,’ ‘wofunsa’) onse aŵiriwo ali m’gulu la osakhulupirira m’kusiyanitsa ku kupulumutsidwa kwa tchalitchi cha Chikristu.”—The Expositor’s Bible Commentary, Volyumu 10, tsamba 275.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Mogwirizana ndi Malemba, chiyambire liti ndipo ndi mwanjira yotani mmene anthu angavomerezedwere ndi Mulungu?
◻ Nchiyani chomwe chinali kawonedwe ka Mulungu ka alendo pakati pa anthu ake, koma kodi nchifukwa ninji Aisrayeli anafunikira kulinganiza chenjezolo ndi kulolera?
◻ Nchiyani chomwe tingatsirize kuchokera ku chenicheni chakuti “osakhulupirira” anabwera ku misonkhano Yachikristu mu Korinto?
◻ Ndimotani mmene Mulungu wapangira kakonzedwe kuthandiza Akristu obatizidwa kukhala atumiki ake ovomerezedwa?