Mmene Kubadwa kwa Yesu Kumabweretsera Mtendere
ULOSI wolengeza za “mtendere pakati pa anthu amene [Mulungu] amakondwera nawo” si wokhawo umene unakhudza kubadwa kwa Yesu. Kuwonjezera pa zimene angelo analengeza kwa abusa omwe anadabwa, amithenga ochokera kumwamba anauzanso Mariya ndi mwamuna wake, Yosefe, mauthenga a Mulungu onena za kubadwa kwa Yesu. Kukambirana za mauthengawa kungatithandize kuzindikira zambiri zokhudza kubadwa kwa Yesu ndiponso kumvetsa tanthauzo lenileni la lonjezo la angelo lakuti padzakhala mtendere pakati pa anthu.
Yesu asanabadwe, ngakhalenso Mariya asanakhale ndi pakati, mngelo, yemwe Baibulo limamutchula kuti Gabrieli, anafika kwa Mariya. Mngeloyo analonjera Mariya kuti: “Mtendere ukhale nawe, wodalitsika koposatu iwe, Yehova ali nawe.” Mukhoza kuona kuti zimenezi zinam’dabwitsa kwambiri Mariya ndipo mwina anachita mantha pang’ono. Kodi moni woterewu ungatanthauze chiyani?
Gabrieli anafotokoza kuti: “Mvetsera! Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu nadzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu pa nyumba ya Yakobo kwa muyaya, mwakuti ufumu wake sudzatha konse.” Mariya anafunsa kuti zimenezi zingatheke bwanji popeza kuti, iyeyo monga namwali, sanali kugona ndi mwamuna. Gabrieli anayankha kuti adzakhala ndi pakati kudzera mwa mzimu woyera wa Mulungu. Mwanayu sadzakhala mwana wamba ayi.—Luka 1:28-35.
Mfumu Yonenedweratu
Mawu a Gabrieli ayenera kuti anathandiza Mariya kumvetsa kuti mwana yemwe adzabereke ndi amene maulosi akale anamuneneratu. Gabrieli atanena kuti Yehova adzapatsa mwana wa Mariya “mpando wachifumu wa Davide atate wake” ziyenera kuti zinapangitsa Mariya, pamodzi ndi Myuda aliyense wodziwa malemba, kuganiza zimene Mulungu analonjeza kwa Mfumu Davide ya Isiraeli.
Kudzera mwa mneneri Natani, Yehova anauza Davide kuti: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.” (2 Samueli 7:4, 16) Ponena za Davide, Yehova anati: “Ndidzakhalitsanso mbewu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba. Mbewu yake idzakhala ku nthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.” (Salmo 89:20, 29, 35, 36) Choncho, sizinangochitika mwangozi kuti Mariya ndiponso Yosefe achokere ku banja la Davide.
Si maulosi amenewa okha a m’Malemba Achihebri amene analosera za mwana wachifumu wa Davide. Mariya ayenera kuti anadziwanso za ulosi wa Yesaya wakuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”—Yesaya 9:6, 7.
Choncho, zimene Gabrieli ananena kwa Mariya zimakhudza zambiri osati kubadwa kozizwitsa kwa mwana wamwamuna kokha ayi. Mwana wake anali amene adzalowe Ufumu wa Mfumu Davide. Anali amene adzakhale wolowa wachikhalire wa Ufumu woikidwa ndi Mulungu. Maulosi a Gabrieli okhudza ntchito yam’tsogolo ya Yesu ali ndi tanthauzo lalikulu kwambiri kwa ife tonse.
Yosefe atadziwa kuti amene adzakhale mkazi wake anali ndi pakati, anasankha kuthetsa chibwenzi chawo. Iyeyo anadziwa kuti mwanayo sanali wake chifukwa chakuti iye ndi chibwenzi chakecho anali asanagonepo limodzi. Mukhoza kuona kuti zinamuvuta Yosefe kukhulupirira zimene Mariya anafotokoza za mmene anakhalira ndi pakati. Nkhani yolembedwa mu Uthenga Wabwino imati: “Mngelo wa Yehova anamuonekera m’maloto ndi kunena kuti: ‘Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba, chifukwa chakuti pathupi alinapopa pachitika mwa mphamvu ya mzimu woyera. Adzabereka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamutche Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.’”—Mateyo 1:20, 21.
Baibulo silinena ngati Yosefe anamvetsa bwino kapena ayi mmene mwanayo ‘adzapulumutsire anthu ake ku machimo awo.’ Komabe, uthengawu unali wokwanira kumutsimikizira Yosefe kuti mayi woyembekezerayo sanachimwe. Anachita monga mngeloyo anamuuzira ndipo anatengera Mariya kunyumba, womwe unali ngati mwambo wa ukwati.
Zimene zimapezeka m’Malemba ena zimatithandiza kumvetsa zimene mngelo uja ankatanthauza. Kuchiyambi kwa mbiri ya anthu, mngelo wina wopanduka anatsutsa kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Malemba Achiheberi amasonyeza kuti mwa zinthu zimene wopandukayo ananena, anati njira ya Mulungu yolamulirira inali yosalungama ndipo palibe munthu amene adzakhalabe wokhulupirika kwa Yehova akayesedwa. (Genesis 3:2-5; Yobu 1:6-12) Adamu anali mmodzi mwa anthu amene sanakhalebe wokhulupirika. Chifukwa chochimwa iyeyo anapatsira anthu onse uchimo, ndipo chifukwa cha uchimowo iwo amafa. (Aroma 5:12; 6:23) Koma, Yesu anabadwa wopanda uchimo chifukwa chakuti amayi ake sanakhale ndi pakati mwa kugona ndi mwamuna. Mwa kupereka mofunitsitsa moyo wake wangwiro monga dipo lolingana ndendende ndi moyo umene Adamu anataya, Yesu anatha kupulumutsa anthu ku machimo awo n’kuwapatsa chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha.—1 Timoteyo 2:3-6; Tito 3:6, 7; 1 Yohane 2:25.
Mu utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anasonyeza pang’ono mmene zinthu zidzakhalire, zotsatirapo za uchimo zikadzachotsedwa. Iye anachiritsa matenda a mtundu uliwonse ngakhale kuukitsa akufa kumene. (Mateyo 4:23; Yohane 11:1-44) Zozizwitsazo zinangoonetsa pang’ono zimene adzachita m’tsogolo. Yesu iye mwini anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [anga] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
Lonjezolo la kuukitsidwa kwa akufa m’tsogolo likusonyeza mmene kubadwa kwa Yesu ndipo makamaka imfa yake zilili zofunikira kwambiri kwa ife. Lemba la Yohane 3:17 limanena kuti, Mulungu anatumiza Mwana wake m’dziko “kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.” Nkhani yabwino imeneyi ikutikumbutsa za uthenga uja umene unalengezedwa kwa abusa omwe anali kuyang’anira ziweto zawo, usiku umene Yesu anabadwa.
“Uthenga Wabwino wa Chimwemwe Chachikulu”
Unalidi “uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu” kwa anthu pamene angelo analengeza za kubadwa kwa “Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.” (Luka 2:10, 11) Mwanayu anali amene adzakhale Mesiya, Mneneri ndi Woweruza wamkulu yemwe anthu a Mulungu anakhala akuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Deuteronomo 18:18; Mika 5:2) Moyo ndi imfa yake padziko lapansi zidzakhala zofunika kwambiri pa kutsimikizira kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Ndicho chifukwa chake angelo anati: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba.”—Luka 2:14.
Yesu, yemwe Baibulo limamutcha “Adamu womalizira,” anasonyeza kuti munthu akhoza kukhala wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atayesedwa koopsa. (1 Akorinto 15:45) Mwa kutero anatsimikizira kuti Satana ndi wabodza woipa kwambiri. Zimenezi zinakondweretsa angelo okhulupirika kumwamba.
Koma, tiyeni tibwerere ku funso lija lakuti, “Kodi pali chiyembekezo chenicheni choti zimene angelo analengeza pa usiku umene Yesu anabadwa zidzakwaniritsidwa?” Tingayankhe mwamphamvu kuti inde! Mtendere ndi wofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi, chimene chikuphatikizapo kubwezeretsa paradaiso. Cholingacho chitakwaniritsidwa padziko lonse lapansi, anthu onse adzakhala achikondi ndi okhulupirika. Choncho, kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Yehova kukutanthauzanso kuwonongedwa kwa otsutsa onse a ulamuliro wa Yehova. Nkhaniyi si yabwino kwa anthu amene amaikira kumbuyo Satana ponena kuti mfundo za Yehova n’zoipa. Iwowa adzawonongedwa.—Salmo 37:11; Miyambo 2:21, 22.
Onani kuti angelo sanauze abusawo kuti anthu onse adzakhala ndi mtendere ndipo Mulungu adzakondwera nawo. Koma, analengeza za “mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.” Izi zikutanthauza anthu amene Mulungu amawavomereza n’kukondwera nawo. Anthu amene amasonyeza chikhulupiriro choona mwa Yehova amakhala otsatira okhulupirika a Yesu, ndipo amatsanzira iye. Amuna ndi akazi otere amakhala owolowa manja ndi omvetsetsana tsiku lililonse, osati pamasiku ochepa chabe pachaka.
Kutsanzira Khristu Chaka Chonse
Mphamvu ya uthenga wabwino womwe Yesu analalikira yakhudza miyoyo ya anthu ochuluka kwambiri. Ambiri ayamba kugwiritsa ntchito mfundo zachikhristu pambali iliyonse ya moyo wawo. Anthu amene kale makamaka ankangodziganizira ayamba kuganizira zimene Yesu akanachita ngati akanakumana ndi zimene iwowo akukumana nazo. Anthu ena amene kale ankaona zinthu zimene ali nazo ndiponso zosangalatsa za moyo ngati zofunika kwambiri, ayamba kuzindikira kufunika kwa zinthu zauzimu ndiponso kufunika kouza anzawo zimenezi. Anthu amene amachita zimenezi amayesetsa kukhala owolowa manja ndi okoma mtima chaka chonse. Kodi si zimene mungayembekezere kwa Akhristu oona?
Ngati anthu onse oona mtima akanaganiza kwambiri za tanthauzo ndi kufunika kwa uthenga wa mtendere womwe angelo aja analengeza ndi kuchita mogwirizana ndi zimenezi, dziko likanakhala labwino kwambiri.
Maulosi okhudza kubadwa kwa Yesu amatsimikizira anthu amene Mulungu amakondwera nawo kuti angathe kusangalala ndi mtendere weniweni kwamuyaya. Kodi si zimene mukufuna? Tingakhale otsimikiza kuti ulosi wabwino wa mtendere womwe angelo analengeza pa kubadwa kwa Yesu udzakwaniritsidwadi. M’malo moti anthu azingokhala ndi mtendere m’maganizo panyengo ya Khirisimasi pokha, adzakhaladi mwamtendere kwamuyaya.
[Zithunzi patsamba 7]
Anthu angathe ndipo ayenera kutsanzira Khristu chaka chonse