MUTU 21
Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti
YESU ANAWERENGA MPUKUTU WA YESAYA
ANTHU A KU NAZARETI ANAFUNA KUPHA YESU
Mosakayikira anthu anasangalala kwambiri Yesu atabwereranso ku Nazareti. Yesu ankagwira ntchito ya ukalipentala ali m’derali koma pa nthawiyi n’kuti patapita chaka chimodzi kuchokera pamene anabatizidwa ndi Yohane. Koma tsopano anthu ambiri ankamudziwa ngati munthu amene amachita zinthu zamphamvu ndi zozizwitsa. Anthu a ku Nazareti ankafunitsitsa kuona Yesu akuchita zinthu zozizwitsa.
Yesu atapita ku sunagoge, monga mwa chizolowezi chake, anthu ambiri ankayembekezera kuona zinthu zodabwitsa. Mwambowu unayamba ndi pemphero ndipo kenako anawerenga mabuku a Mose monga mmene zinkakhalira “m’masunagoge sabata lililonse.” (Machitidwe 15:21) Pa mwambowu, ankawerenganso mbali zina za mabuku a aneneri. Mosakayikira, Yesu ataimirira kuti ayambe kuwerenga, anazindikira anthu ambiri omwe ankakumana nawo pa nthawi imene ankasonkhana nawo m’sunagogeyu. Kenako anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya ndipo anapeza pamene pamanena za Wodzozedwa ndi mzimu wa Yehova. M’Baibulo mawu amenewa amapezeka pa Yesaya 61:1, 2.
Yesu anawerenga za mmene Wodzozedwayo adzalengezere za ufulu kwa anthu ogwidwa ukapolo, kutsegula maso a akhungu komanso za kubwera kwa chaka chokomera Yehova. Atatero, Yesu anapereka mpukutuwo kwa wotumikira m’sunagogemo n’kukhala pansi. Anthu onse anamuyang’anitsitsa. Kenako analankhula kwa kanthawi ndithu ndipo ananenanso kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”—Luka 4:21.
Anthu anadabwa kwambiri ndi “mawu ogwira mtima otuluka pakamwa pake,” ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?” Koma Yesu atazindikira kuti anthuwo akufuna kuti awachitire zozizwitsa ngati zimene anamva akuchita m’madera ena, ananena kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao. Zinthu zimenezo uzichitenso kwanu kuno.’” (Luka 4:22, 23) N’kutheka kuti anthuwa ankaona kuti zikanakhala bwino Yesu akanayamba kuchiritsa anthu akwawo. Koma chifukwa chakuti sanachite zimenezo, ankaona kuti Yesu waachita chipongwe.
Yesu atadziwa zimene anthuwa ankaganiza, anawauza zinthu zimene zinachitika m’nthawi ya ana a Isiraeli. Anawauza kuti m’nthawi ya Eliya kunali akazi amasiye ambiri ku Isiraeli komabe Eliya sanatumidwe kwa akaziwo. M’malomwake anapita kwa mkazi wamasiye amene sanali Mwisiraeli. Mkaziyu ankakhala ku Zarefati, tauni yomwe inali kufupi ndi Sidoni. Kumeneko Eliya anaukitsa mwana wa mayiyo. (1 Mafumu 17:8-16) Yesu anawauzanso kuti m’nthawi ya Elisa, ku Isiraeli kunali akhate ambiri, koma mneneriyo anachiritsa Namani wa ku Siriya yemwe ankadwala khate.—2 Mafumu 5:1, 8-14.
Kodi anthuwo anatani atazindikira kuti zimene Yesu ananenazo zinasonyeza kuti iwowo anali anthu odzikonda komanso opanda chikhulupiriro? Anthuwo anakwiya kwambiri moti anaimirira n’kumutulutsira kunja kwa mzinda. Anapita naye pamwamba pa phiri lomwe anamangapo mzinda wa Nazareti kuti akamuponye kuphedi. Koma Yesu anawapulumuka n’kuthawa. Zitatero, Yesu anapita ku Kaperenao kumpoto chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya.