MUTU 15
‘Anagwidwa ndi Chifundo’
1-3. (a) Kodi Yesu anachita chiyani opemphetsa awiri amene anali ndi vuto losaona atamupempha kuti awathandize? (b) Kodi mawu akuti “atagwidwa ndi chifundo” akutanthauza chiyani? (Onani mawu am’munsi.)
ANTHU awiri amene anali ndi vuto losaona anali m’mphepete mwa msewu pafupi ndi mzinda wa Yeriko. Tsiku lililonse ankabwera pamalowo ndipo ankakhala pamalo abwino pamene ankadziwa kuti pamadutsa anthu ambiri n’kumapempha ndalama. Koma tsiku lina anakumana ndi zinthu zina zimene zinasintha kwambiri moyo wawo.
2 Mwadzidzidzi, opemphetsawo anamva phokoso la anthu. Popeza kuti anali osaona, sankadziwa chimene chinkachitika ndipo mmodzi wa iwo anafunsa kuti adziwe. Iye anauzidwa kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” Yesu anali pa ulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu ndipo gulu la anthu linkamutsatira. Anthu opemphetsawo atamva kuti Yesu akudutsa, anayamba kufuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” Gulu la anthulo linakwiya ndipo linawauza kuti akhale chete, koma sanamvere chifukwa iwo ankafunitsitsa kuti awathandize.
3 Yesu anamva kufuula kwawo ngakhale kuti gulu la anthulo linkasokosa kwambiri. Ndiye kodi iye anatani? Pa nthawiyi, anali ndi zinthu zambiri zimene zinkamudetsa nkhawa mumtima mwake. Panali patangotsala mlungu umodzi wokha kuti aphedwe ndipo ankadziwa kuti posachedwa, azunzidwa komanso kuphedwa mwankhanza ku Yerusalemu. Komabe, iye sananyalanyaze anthu osaona omwe ankafuulawo. Choncho, iye anaima n’kulamula kuti anthu osaonawo awabweretse kwa iye. Iwo anamupempha kuti: “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona.” Yesu “atagwidwa ndi chifundo,” anagwira maso awo ndipo anayamba kuona.a Nthawi yomweyo, iwo anayamba kumutsatira.—Luka 18:35-43; Mateyu 20:29-34.
4. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi wakuti iye “adzamvera chisoni munthu wonyozeka”?
4 Si nthawi yokhayi imene Yesu anachitira ena chifundo. Iye anasonyeza kambirimbiri ndiponso nthawi zosiyanasiyana kuti wagwidwa ndi chifundo ndipo ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu. Ulosi wa m’Baibulo umati iye “adzamvera chisoni munthu wonyozeka.” (Salimo 72:13) Mogwirizana ndi mawu amenewa, Yesu ankazindikira mwamsanga mavuto a anthu ndipo sankadikira kuti achite kumupempha kuti awathandize. Chifundo ndi chimene chinkamuchititsa kuti azilalikira. Tsopano tiyeni tione mmene mabuku a Uthenga Wabwino amasonyezera kuti Yesu anali wachifundo. Tiona zimenezi kuchokera pa zimene ankalankhula komanso kuchita. Tionanso mmene ifeyo tingasonyezere chifundo ngati mmene Yesu anachitira.
Yesu Ankamvera Chisoni Anthu Ena
5, 6. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu anali munthu wachifundo?
5 Yesu ankamva chisoni kwambiri akaona anthu akuvutika. Iye ankamvetsa mmene anthu ovutikawo akumvera ndipo ankawamvera chisoni. Ngakhale kuti iye anali asanakumanepo ndi mavuto ngati amenewo, zinkamukhudza kwambiri moti ankamva ululu ngati mmene anthuwo ankamvera. (Aheberi 4:15) Mwachitsanzo, pamene ankachiritsa mayi amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, Yesu anafotokoza kuti ‘matendawo anali aakulu.’ Zimenezi zikusonyeza kuti iye ankadziwa kuti mayiwo akuvutika kwambiri. (Maliko 5:25-34) Ataona Mariya ndi anthu ena akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro, anakhudzidwa kwambiri ndi chisoni chawo ndipo anavutika kwambiri mumtima mwake. Ngakhale ankadziwa kuti watsala pang’ono kuukitsa Lazaro, Yesu anamva chisoni kwambiri mpaka anagwetsa misozi.—Yohane 11:33, 35.
6 Pa nthawi ina, munthu wakhate anapita kwa Yesu n’kumudandaulira kuti: “Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Kodi Yesu, amene anali munthu wangwiro yemwe sanadwalepo, anatani? Anamumvera chisoni kwambiri munthu wakhateyo, ndipo mpake kuti Baibulo limanena kuti, “anagwidwa chifundo.” (Maliko 1:40-42) Kenako anachita chinthu chodabwitsa kwambiri. Iye ankadziwa bwino kuti mogwirizana ndi Chilamulo, anthu akhate anali odetsedwa ndipo sankayenera kukhala pafupi ndi anthu ena. (Levitiko 13:45, 46) Yesu akanatha kuchiritsa munthuyo ngakhale osamukhudza. (Mateyu 8:5-13) Koma iye anasankha kukhudza munthu wakhateyo ndi kumuuza kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo, khatelo linatheratu. Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti ndi munthu wachifundo kwambiri.
7. N’chiyani chingatithandize kuti tizimvera ena chisoni, nanga tingasonyeze bwanji zimenezi?
7 Monga Akhristu tikulimbikitsidwa kuti tizimvera ena chifundo ngati mmene Yesu ankachitira. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizimverana chisoni.’b (1 Petulo 3:8) Zingakhale zovuta kuti timvetse mavuto ndiponso ululu wa anthu amene akudwala matenda aakulu kapena amene akuvutika maganizo, makamaka ngati ifeyo sitinakumanepo ndi mavuto ngati amenewo. Koma kumbukirani kuti sizidalira kuti tikumane ndi mavuto amene mnzathu akukumana nawo kuti timvetse mmene akuvutikira. Mwachitsanzo, Yesu ankamvetsa mmene odwala akuvutikira ngakhale kuti iyeyo sanadwalepo. Nanga tingatani kuti tizimvetsa mavuto amene anthu akukumana nawo? Anthu amene akuvutikawo akamatiuza mavuto awo tizimvetsera modekha ndiponso tiziyerekezera kuti nafenso tili ndi mavuto ngati awowo. Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanamva bwanji ndikanakhala kuti ndakumana ndi mavuto ngati amenewa?’ (1 Akorinto 12:26) Ena akamavutika, tiziyesetsa kuwamvera chisoni mwamsanga, tikatero tidzatha ‘kulankhula molimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa.’ (1 Atesalonika 5:14) Nthawi zina tingagwetse misozi posonyeza kuti tili ndi chisoni chifukwa cha mavuto amene mnzathu akukumana nawo, osati kungomuuza kuti nafenso zatikhudza. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Muzilira ndi anthu amene akulira.”—Aroma 12:15.
8, 9. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amaganizira ena?
8 Yesu anali wokoma mtima ndipo akamachita zinthu ankaganizira mavuto amene anthu ankakumana nawo. Mwachitsanzo, kumbukirani nthawi imene anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losamva komanso losalankhula. Mwina ataona kuti munthuyo akuchita manyazi, Yesu anachita chinthu chapadera chimene sanachite pamene ankachiritsa anthu ena. Iye “anatenga munthuyo n’kuchoka naye pagulu la anthulo kupita naye pambali.” Kenako anamuchiritsa popanda anthu oonerera.—Maliko 7:31-35.
9 Yesu anachitanso zinthu zosonyeza kuganizira ena pamene anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losaona n’kumupempha kuti amuchiritse. Iye “anagwira dzanja la munthu wosaonayo, n’kupita naye kunja kwa mudzi,” ndipo kumeneko anamuchiritsa mwapang’onopang’ono. Mwina zimenezi zinathandiza munthuyu kuti azolowere pang’onopang’ono kuona kuwala ndi zinthu zosiyanasiyana zimene anali asanazionepo. (Maliko 8:22-26) Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti amaganizira kwambiri anthu ena.
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhudzidwa ndi mmene ena akumvera?
10 Popeza ndife otsatira a Yesu, tizisonyeza kuti timakhudzidwa ndi mmene ena akumvera. Choncho tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula, chifukwa tikudziwa kuti kulankhula mosaganiza bwino kumakhumudwitsa ena. (Miyambo 12:18; 18:21) Akhristu amene amaganizira ena amapeweratu kulankhula mawu a mwano, onyoza ndiponso okhadzula. (Aefeso 4:31) Akulu, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhudzidwa ndi mmene ena akumvera? Mukamapereka malangizo, muzilankhula mokoma mtima kuti anthuwo aone kuti mumawalemekeza. (Agalatiya 6:1) Makolo, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhudzidwa ndi mmene ana anu amamvera? Mukamalangiza ana anu kapena kuwapatsa chilango, muziyesetsa kuchita zimenezi m’njira yoti musawachititse manyazi.—Akolose 3:21.
Yesu Ankathandiza Anthu Ngakhale Asanamupemphe
11, 12. Kodi ndi nkhani ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti Yesu sankadikira kupemphedwa kuti athandize anthu?
11 Sikuti nthawi zonse Yesu ankadikira kuti anthu amupemphe kuti awachitire chifundo. Ndipotu munthu wachifundo amathandiza anthu mwa kufuna kwake ndipo sadikira kuti achite kupemphedwa. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Yesu ankathandiza ena chifukwa anali wachifundo. Mwachitsanzo, gulu la anthu litakhala naye masiku atatu osadya, Yesu sanadikire kuti wina achite kumuuza kuti anthuwo ali ndi njala, kapena kumupempha kuti awathandize. Nkhaniyi imati: “Yesu anaitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: ‘Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni, chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita ndi njala chifukwa angalenguke panjira.’” Kenako mwa kufuna kwake, Yesu anadyetsa gulu la anthulo mozizwitsa.—Mateyu 15:32-38.
12 Tiyeni tione nkhani ina imene inachitika mu 31 C.E. Yesu ali pafupi ndi mzinda wa Naini, anakumana ndi anthu akulira. Anthuwo ankatuluka mumzindawo atanyamula maliro a ‘mwana wamwamuna yekhayo wa mkazi wa masiye,’ ndipo mwina ankapita kumanda apafupi amene anali m’mbali mwa phiri. N’zodziwikiratu kuti mayiyo anali ndi chisoni kwambiri mumtima mwake. Iye ankapita kukaika maliro a mwana wake wamwamuna yekhayo, ndipo analibe mwamuna amene akanamuthandiza kulira. Pagulu la anthu lonselo, Yesu ‘anaona mayiwo,’ amene tsopano anali mkazi wamasiye ndiponso wopanda mwana. Zimene anaonazo zinamukhudza kwambiri ndipo ‘anawamvera chisoni’ mayiwo. Palibe amene anapempha Yesu kuti athandize mayiwo, koma anawathandiza chifukwa cha chifundo chake. Choncho, “anayandikira n’kugwira chithathacho” ndipo anaukitsa mnyamatayo. Kodi kenako chinachitika n’chiyani? Yesu sanauze mnyamatayo kuti akhale m’gulu la anthu amene ankamutsatira koma “anamupereka kwa mayi ake.” Iye anachita zimenezi pofuna kuonetsetsa kuti pakhale munthu wosamalira mkazi wamasiyeyo.—Luka 7:11-15.
13. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu, amene sankadikira kuti anthu achite kumupempha kuti awathandize?
13 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? N’zoona kuti sitingadyetse anthu mozizwitsa kapena kuukitsa akufa. Komabe, tingatsanzire Yesu pothandiza anthu amene akuvutika ngakhale kuti sanatipemphe. Mwachitsanzo, Mkhristu mnzathu angakhale ndi vuto lalikulu la zachuma kapena ntchito ingamuthere. (1 Yohane 3:17) Komanso nyumba ya mkazi wamasiye ingafunike kukonzedwa mwamsanga. (Yakobo 1:27) Mwinanso tingadziwe banja limene laferedwa ndipo likufunika kulimbikitsidwa kapena kuthandizidwa m’njira ina yake. (1 Atesalonika 5:11) Tikaona anthu ena amene akufunikiradi kuthandizidwa, tisamadikire kuti achite kutipempha kuti tiwathandize. (Miyambo 3:27) Chifundo chidzatichititsa kuti tiwathandize ngati tingakwanitse kutero. Tisaiwale kuti zinthu zochepa zimene tingachite mokoma mtima kapena mawu olimbikitsa amene tingalankhule kuchokera pansi pa mtima angasonyeze kuti ndife achifundo.—Akolose 3:12.
Chifundo Chinkachititsa Kuti Yesu Azilalikira
14. N’chifukwa chiyani Yesu ankaona kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yofunika kwambiri?
14 Monga mmene taonera m’gawo lachiwiri la buku lino, Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolalikira uthenga wabwino. Iye anati: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) N’chifukwa chiyani ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri? Chifukwa chachikulu n’chakuti amakonda Mulungu. Koma panalinso chifukwa china: Chifundo chimene Yesu anali nacho chinamuchititsa kuona kuti anthu ena anali ndi njala yauzimu ndipo anawathandiza. Pa njira zonse zimene iye anasonyezera chifundo, panalibe njira yofunika kwambiri kuposa kuthetsa njala yauzimu ya anthu ena. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawalalikira. Kuchita zimenezi kutithandiza kuti tionenso bwino zifukwa zimene zimatichititsa kugwira nawo ntchito yolalikira.
15, 16. Fotokozani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawalalikira.
15 Mu 31 C.E., patatha zaka pafupifupi ziwiri akuchita mwakhama utumiki wake, Yesu anawonjezera utumikiwu poyamba “ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse” ya ku Galileya. Zimene anaona zinamukhudza kwambiri. Mtumwi Mateyu anafotokoza kuti: “Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mateyu 9:35, 36) Yesu ankamvera chisoni anthu wamba ndipo ankadziwa bwino kwambiri kuti sankasamalidwa mwauzimu. Yesu ankadziwanso kuti atsogoleri achipembedzo, amene anayenera kuweta anthuwa, sankawasamalira n’komwe koma ankangowazunza. Choncho Yesu anagwidwa ndi chifundo ndipo ankayesetsa mwakhama kuti alalikire anthuwo uthenga wopatsa chiyembekezo. Panalibe chinthu chabwino chimene anthuwo ankafunikira kuposa kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.
16 Zinthu zina zofanana ndi zimenezi zinachitika patapita miyezi ingapo, mu 32 C.E., nthawi ya Pasika itatsala pang’ono kufika. Pa nthawiyi, Yesu ndi atumwi ake anakwera ngalawa kupita tsidya lina la nyanja ya Galileya kuti akapume kwaokha. Koma gulu la anthu linathamanga m’mbali mwa nyanja ndipo linakafika ngalawa ija isanafike. Kodi Yesu ataona anthuwo anachita chiyani? Nkhaniyi imati: “Atatsika anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni, chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe m’busa. Ndiye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:31-34) Apanso Yesu “anawamvera chisoni” poona kuti anali ndi njala yauzimu. Mofanana ndi “nkhosa zimene zilibe m’busa,” anthuwo anali ndi njala yauzimu chifukwa atsogoleri achipembedzo anangowasiya kuti azizisamalira okha. Yesu sankangolalikira kuti akwaniritse udindo wake, koma ankalalikira chifukwa chakuti anali wachifundo.
17, 18. (a) N’chiyani chimatichititsa kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira? (b) Kodi tingatani kuti tizimvera ena chifundo?
17 Popeza ndife otsatira a Yesu, kodi n’chiyani chimene chimatichititsa kugwira nawo ntchito yolalikira? Monga mmene tinaonera m’Mutu 9 wa buku lino, tinapatsidwa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mateyu 28:19, 20; 1 Akorinto 9:16) Koma tisamagwire ntchito imeneyi pofuna kungokwaniritsa udindo umene tapatsidwa. Chofunika kwambiri n’chakuti tizigwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu chifukwa choti timakonda Yehova. Timalalikiranso chifukwa timachitira chifundo anthu amene sadziwa zimene ife timakhulupirira. (Maliko 12:28-31) Choncho, kodi tingatani kuti tizimvera ena chifundo?
18 Tiziona anthu ngati mmene Yesu ankawaonera. Iye ankawaona kuti anali “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” Mwachitsanzo, yerekezerani kuti mwapeza kamwana kankhosa katasochera. Kamwana kankhosako kali ndi njala komanso ludzu chifukwa palibe m’busa woti akatsogolere kumene kuli msipu ndi madzi. Kodi simungakamvere chisoni? Kodi simungayesetse kuchita zonse zimene mungathe kuti mukapatse chakudya ndi madzi? Kamwana kankhosako kali ngati anthu ambiri amene sanamvebe uthenga wabwino. Abusa a zipembedzo zonyenga sakuthandiza anthu awo ndipo anthuwo ali ndi njala komanso ludzu lauzimu moti alibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo. Koma ifeyo tili ndi chilichonse chimene iwo angafune. Tili ndi chakudya chauzimu chopatsa thanzi ndiponso madzi otsitsimula a choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Yesaya 55:1, 2) Tikamaganizira njala yauzimu imene anthu amenewa ali nayo, timawamvera chisoni kwambiri. Mofanana ndi Yesu tikamamvera anthu chisoni tidzayesetsa kuwauza uthenga wa Ufumu wopatsa chiyembekezo.
19. Kodi tingathandize bwanji munthu yemwe tikuphunzira naye Baibulo, amene tikuona kuti wakwanitsa zonse zofunikira kuti ayambe kugwira nawo ntchito yolalikira?
19 Kodi tingathandize bwanji ena kuti azitsanzira Yesu? Tiyerekezere kuti mukufuna kulimbikitsa munthu yemwe mumaphunzira naye Baibulo amene wakwanitsa zonse zofunikira kuti ayambe kugwira nawo ntchito yolalikira. Kapenanso mwina mukufuna kuthandiza munthu amene anasiya kulalikira kuti ayambenso kugwira nawo ntchitoyi. Kodi anthu amenewa tingawathandize bwanji? Tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azifunitsitsa kugwira nawo ntchitoyi. Kumbukirani kuti choyamba, Yesu “anawamvera chisoni” anthu kenako anayamba kuwaphunzitsa. (Maliko 6:34) Choncho, tikathandiza wophunzira Baibulo wathu komanso anthu amene anasiya kulalikira kuti azimvera ena chisoni, adzakhala ofunitsitsa kuchokera pansi pa mtima kuti akhale ngati Yesu ndipo adzayamba kugwira nawo ntchito youza ena uthenga wabwino. Mwina tingawafunse kuti: “Kodi uthenga wa Ufumu unasintha bwanji moyo wanu kuti ukhale wabwino? Nanga bwanji anthu amene sanamvebe uthenga umenewu, kodi nawonso sakufunika kuuzidwa? Ndiye inuyo mungatani kuti muthandize anthu amenewo?” Komabe, chifukwa chachikulu chimene chimalimbikitsa munthu kugwira nawo ntchitoyi ndi kukonda Mulungu ndiponso mtima wofunitsitsa kumutumikira.
20. (a) Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu akhale wotsatira wa Yesu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?
20 Kuti munthu akhale wotsatira wa Yesu amafunika kuchita zambiri, osati kumangotsanzira zimene iye ankanena komanso kuchita. Tiyenera kukhala ndi “maganizo” ngati amene iye anali nawo. (Afilipi 2:5) Ndipo tili ndi mwayi chifukwa Baibulo limasonyeza maganizo ndiponso mtima umene Yesu anali nawo, womwe unkamuchititsa kulankhula komanso kuchita zinthu zosiyanasiyana. Tikadziwa “maganizo a Khristu,” tidzaphunzira kukhala anthu achifundo ndipo tidzachitira ena zinthu ngati mmene Yesu ankachitira. (1 Akorinto 2:16) M’mutu wotsatira, tikambirana njira zosiyanasiyana zimene Yesu anasonyezera chikondi makamaka kwa otsatira ake.
a Anthu ena amati mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “atagwidwa ndi chifundo,” ndi ena mwa mawu amphamvu kwambiri m’Chigiriki osonyeza kumvera ena chisoni. Buku lina limati mawu amenewa “samangosonyeza kumva chisoni kokha ukaona anthu amene akuvutika, koma amatanthauzanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuwathandiza komanso kuthetsa mavuto awo.”
b Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘tizimverana chisoni,’ kwenikweni amatanthauza kuti “tizivutikira limodzi.”