MUTU 38
Yohane Ankafuna Kumva Kuchokera kwa Yesu
YOHANE M’BATIZI ANKAFUNA KUDZIWA ZA UDINDO WA YESU
YESU ANANENA ZINTHU ZABWINO ZOKHUDZA YOHANE
Yohane M’batizi anali atakhala m’ndende kwa pafupifupi chaka chimodzi ndipo pa nthawi yonseyi ankamva zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita. Tangoganizani mmene Yohane anamvera ophunzira ake atamuuza kuti Yesu waukitsa mwana wa mzimayi wamasiye wa ku Naini. Komabe Yohane ankafuna kumva yekha kuchokera kwa Yesu kuti zimenezi zinkatanthauza chiyani. Choncho Yohane anatuma ophunzira ake awiri kuti akafunse Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?”—Luka 7:19.
Kodi funso limeneli linali lodabwitsa? Inde. Tikutero chifukwa Yohane anali munthu wodzipereka ndipo pafupifupi zaka ziwiri m’mbuyomo pamene ankabatiza Yesu, anaona mzimu wa Mulungu ukutsika n’kuima pamutu pa Yesu komanso anamva mawu ochokera kwa Mulungu ovomereza kuti Yesu ndi mwana wake. Komabe musaganize kuti chikhulupiriro cha Yohane chinali chitachepa. Zikanakhala choncho, Yesu sakananena zinthu zabwino zokhudza Yohane ngati mmene anachitira pa nthawiyi. Koma ngati Yohane anali ndi chikhulupiriro cholimba, ndiye n’chifukwa chiyani anafunsa funso limeneli?
N’kutheka kuti Yohane ankafuna kuti amve kuchokera kwa Yesuyo kuti analidi Mesiya. Kudziwa zimenezi kukanalimbitsa chikhulupiriro chake pa nthawi imene ankavutika m’ndende. Ndipo funso limene Yohane anafunsali linali lomveka. Iye ankadziwa za maulosi a m’Baibulo omwe ankasonyeza kuti Wodzozedwa wa Mulungu adzakhala mfumu komanso kuti adzapulumutsa anthu. Koma pa nthawiyi Yohane anali atakhala m’ndende kwa miyezi yambiri kuchokera pamene Yesu anabatizidwa. N’chifukwa chake Yohane ankafuna kudziwa ngati padzabwerenso munthu wina pambuyo pa Yesu, yemwe adzakwaniritse zonse zimene zinanenedwa kuti Mesiya adzachita akadzabwera.
M’malo mongouza ophunzira a Yohane kuti, ‘Inde, ndine amene mwakhala mukumuyembekezera,’ Yesu anasonyeza umboni woti Mulungu ankamutsogolera moti ankachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana. Kenako anauza ophunzira a Yohane kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mukumva ndi kuona: Akhungu akuonanso, olumala akuyendayenda, akhate akuyeretsedwa ndipo ogontha akumva. Akufa akuukitsidwa, ndipo kwa aumphawi uthenga wabwino ukulengezedwa.”—Mateyu 11:4, 5.
N’kuthekanso kuti Yohane anafunsa funso limeneli chifukwa ankayembekezera kuti Yesu achita zinthu zambiri kuposa zimene ankachita pa nthawiyo komanso kuti mwina amutulutsa m’ndendemo. Koma Yesu anamuuza kuti asayembekezere zinthu zambiri kuposa zimene ankachitazo.
Ophunzira a Yohane atachoka, Yesu anauza gulu la anthu kuti Yohane sanali mneneri wamba. Iye ananena kuti Yohane anali “mthenga” wa Yehova amene anatchulidwa mu ulosi wopezeka pa Malaki 3:1. Ananenanso kuti Yohane anali mneneri Eliya yemwe anatchulidwa pa Malaki 4:5, 6. Yesu anafotokoza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mwa onse obadwa kwa akazi, sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.”—Mateyu 11:11.
Ponena kuti munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa Yohane, Yesu ankasonyeza kuti Yohane sakalamulira nawo mu Ufumu wakumwamba. Yohane anakonza njira ya Yesu koma anamwalira Yesuyo asanatsegule njira ya kumwamba. (Aheberi 10:19, 20) Komabe, Yohane anali mneneri wokhulupirika wa Mulungu ndipo adzakhala nzika ya Ufumu wa Mulungu padziko lapansi.