Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kodi Yohane Analibe Chikhulupiriro?
YOHANE Mbatizi, yemwe wakhala ali m’ndende kwa chifupifupi chaka chimodzi tsopano, akulandira ripoti lonena za kuukitsidwa kwa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Naini. Koma Yohane akufuna kumva mwachindunji kuchokera kwa Yesu ponena za chinthu chozizwitsa ichi, chotero, iye akutumiza awiri a akuphunzira ake kukafunsa: “Kodi ndinu Wakudzayo kapena tiyang’anire wina?“
Limeneli lingawonekere kukhala funso lachilendo makamaka popeza Yohane anawona mzimu wa Mulungu ukutsikira pa Yesu ndipo anamva mawu a Mulungu achitsimikiziro pamene anali kumbatiza iye chifupifupi zaka ziwiri zapita. Funso la Yohane lingapangitse ena kufikira malongosoledwe akuti chikhulupiriro chake chinali chofooka. Koma ichi sichiri tero. Yesu sakanalankhula mokwezeka ponena za Yohane, chomwe akuchita pa nthawi ino, ngati Yohane anayamba kukaikira. Ndi chifukwa ninji, nanga, Yohane akufunsa funso limeneli?
Mwinamwake Yohane akungofuna kokha chitsimikiziro kuchokera kwa Yesu kunena kuti iye ndiye Mesiya. Ichi chingakhale chilimbikitso chokulira kwa Yohane pamene akuvutika m’ndende. Koma mwachiwonekere pali zina zake zochuluka ku funso la Yohane kuposa chimenechi. lye mwachidziwikire akufuna kudziwa ngati pali wina wake wakudzanso, mlowa m’malo, monga momwe kunaliri, yemwe adzamaliza kukwaniritsidwa kwa zinthu zonse zomwe zinanenedweratu kuti zidzakwaniritsidwa ndi Mesiya.
Malinga ndi maulosi a Baibulo amene Yohane ali wozolowerana nawo, Wodzozedwa wa Mulungu adzayenera kukhala mfumu, Mpulumutsi. Koma Yohane adakali kusungidwa m’ndende, ngakhale miyezi yambiri pambuyo pa kubatizidwa kwa Yesu. Chotero Yohane mwachiwonekere akufunsa Yesu: “Kodi ndinu amene mudzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu ku mphamvu za kunja, kapena kodi pali wina wosiyana, mlowa m’malo, amene tiyenera kudikirira kudzakwaniritsa maulosi onse onena za ulemerero wa Mesiya?’
M’malo mowuza ophunzira a Yohane, ‘Kwenikweni ndinedi amene anayenera kudza’ Yesu mu ora lofananalo akupereka chisonyezero chowonekera kwambiri mwakuchiritsa anthu ochuluka matenda ndi kudwala kosiyanasiyana. Kenaka iye akuwauza ophunzirawo: “Mukani, muuze Yohane zimene mwaziwona ndi kuzimva; anthu akhungu alandira kuwona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino. Ndipo odala iye amene sakhumudwa chifukwa cha ine.”
M’mawu ena, popeza funso la Yohane linasonyeza kuyembekezera kwa Yesu kuchita mokulira ndi mmene iye akuchitira, monga ngati kumupulumutsa Yohane iye mwini, Yesu akumuuza Yohane kusayembekezera zokulira kuposa izi.
Pamene ophunzira a Yohane achoka, Yesu atembenukira kwa khamu ndi kuliuza kuti Yohane ali “mthenga” wa Yehova wonenedweratu pa Malaki 3:1 ndiponso ali m’neneri Eliya wonenedweratu pa Malaki 4:5, 6. lye mwakutero akumlemekeza Yohane kukhala monga wofanana ndi m’neneri aliyense yemwe anakhalako asanakhale iye, akumalongosola:
“Ndinena kwa inu, mwa akubadwa mwa akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane Mbatizi, koma iye amene ali wamng’ono mu Ufumu wa kumwamba ali wamkulu woposa iye. Koma kuyambira masiku a Yohane Mbatizi kufikira tsopano Ufumu wa kumwamba uli chonulirapo chomwe anthu akulinga, ndipo kwa awo akukanikiza patsogolo akupwaira iwo.”
Pano Yesu akusonyeza kuti Yohane sakakhala mu Ufumu wa kumwamba, popeza wochepa ali wokulira kuposa Yohane. Yohane anakonza njira kaamba ka Yesu, koma imfa yake ichitika Kristu asanachiike chipangano, kapena chigwirizano, ndi ophunzira ake omwe akakhala olamulira anzake mu Ufumu wake. Ichi ndi chifukwa chake Yesu akunena kuti Yohane sakakhala mu Ufumu wa ku mwamba. M’malomwake Yohane akakhala nzika ya pa dziko lapansi ya Ufumu wa Mulungu. Luka 7:18-30, NW; Mateyu 11:2-15.
◆ Kodi nchifukwa ninji Yohane akufunsa kuti kaya Yesu ali iye Wakudzayo kapena pali wina wake wosiyana yemwe akayenera kuyembekezeredwa?
◆ Ndi maulosi ati amene Yesu akunena kuti Yohane anawakwaniritsa?
◆ Kodi nchifukwa ninji Yohane Mbatizi sakakhala kumwamba ndi Yesu?