Moyo wa Anthu Akale—Mlimi
“[Yesu] anauza ophunzira ake kuti: ‘Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.’”—MATEYU 9:37, 38.
NTHAWI zambiri Yesu akamaphunzitsa mfundo zofunika kwambiri za choonadi ankagwiritsa ntchito mafanizo okhudza zimene mlimi amachita komanso zipangizo zaulimi. (Mateyu 11:28-30; Maliko 4:3-9; Luka 13:6-9) Kodi n’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Chifukwa anthu ambiri a m’dera limene iye ankakhala anali alimi. Anthu ambiri amene ankamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa ankatsatira njira zaulimi zimene zinakhala zikutsatiridwa kwa nthawi yaitali. Iwo ankamvetsa mosavuta zimene Yesu ankaphunzitsa chifukwa ankawafotokozera mogwirizana ndi zinthu zimene iwowo ankachita tsiku ndi tsiku. Yesu ankawadziwa bwino anthuwo ndipo iwo ankakhudzidwa mtima ndi zimene iye ankaphunzitsa.—Mateyu 7:28.
Tingamvetse bwino mafanizo a Yesu komanso nkhani zina za m’Baibulo ngati titadziwa mmene mlimi wa m’nthawi ya Yesu ankachitira zinthu pa ulimi wake. Tiyenera kudziwa mbewu zimene ankabzala, zipangizo zimene ankagwiritsa ntchito, komanso zovuta zimene ankakumana nazo pa ntchito yake.
Yerekezerani kuti mukumuona mlimi akugwira ntchito yake. Tikukupemphani kuti muziwerenga malemba amene aikidwa m’nkhaniyi ndi kuona zomwe mukuphunzirapo.
Nthawi Yofesa
Mlimi akuima pakhomo pa nyumba yake m’mamawa ndipo akutchinga maso ake poopa kuwala kwa dzuwa. Iye akumva kafungo ka chinyezi chifukwa cha mvula imene yagwa n’kufewetsa nthaka imene inali youma kwambiri ndi dzuwa. Nthawi yolima yafika ndipo iye akupachikira paphewa lake pulawo yathabwa yomwe inkakhala yopepuka n’kuuyamba ulendo wa kumunda.
Atafika kumeneko, iye akusonkhanitsa ng’ombe zake n’kuziika pagoli la pulawo kenako n’kuzikusa kuti ziyambe kulima. Khasu lachitsulo lapulawoyo likudula nthaka yomwe ndi yamiyala. Khasuli siligalauza nthaka koma limangoing’amba n’kupanga tingalande tating’ono (1). Mlimiyu akuyesetsa kuti apange tingalande towongoka choncho sakuyang’ana m’mbuyo chifukwa zimenezo zingachititse kuti pulawoyo ikhotere kumbali. (Luka 9:62) Iye akuyesetsa kuti asapitirire malire a munda wake komanso akuyesetsa kukonza bwino mundawo kuti adzakolole zochuluka.
Popeza wapanga tingalande munda wonsewo, tsopano iye ndi wokonzeka kuyamba kufesa mbewu zake. Mlimiyu akunyamula kathumba ka balere m’dzanja lake lamanzere ndipo akumatapa ndi dzanja lake lamanja mbewuzo n’kumazimwaza m’mundamo (2). Iye akuyesetsa kuti mbewuzo zigwere “panthaka yabwino.”—Luka 8:5, 8.
Atamaliza kufesa, akuyamba kukwirira mbewuzo. Mlimiyo akumangirira nthambi za mitengo yaminga kung’ombe ndipo ng’ombezo zikamakwakwaza nthambizo m’mundamo zikukwirira mbewuzo. Pa nthawiyi mbalame zabwera kale n’kumasokosa kwinaku zikujompha mbewu zimene sizinakwiriridwe. Kenako patapita nthawi, mlimiyo akugwiritsa ntchito kachipangizo kokhala ngati khasu (3) kupalira mbewuzo komanso kuchotsa udzu umene ungalepheretse mbewuzo kukula bwino.—Mateyu 13:7.
Nthawi Yokolola
Padutsa miyezi ndipo mvula yakhala ikugwa bwino. Tsopano ndi nthawi yokolola balere moti dzuwa likawala, maso a mbewuzo akumatuluka ndipo akuchititsa kuti munda wonsewo uzioneka woyera.—Yohane 4:35.
Pa nthawi yokolola mlimi ndi banja lake lonse amakhala otanganidwa kwambiri. Mlimiyo amagwira balere ndi dzanja lake lamanzere pamene kumanja kumakhala chikwakwa chimene amadulira balereyo (4). Ena amatolera balereyo n’kumumanga mitolo (5), akatero amakweza mitoloyo pabulu kapena mu ngolo (6) n’kupita naye pamalo opunthira mbewu a m’mudzimo.
Pa nthawiyi, dzuwa likuwala kwambiri ndipo ukayang’ana kumwamba, komwe kulibe mitambo, likungooneka ngati chibowo. Kenako banjali likupita pansi pa mtengo wa mkuyu kuti lipume pang’ono. Pamenepo iwo akukamba nkhani n’kumaseka uku akudya mkate, tirigu wowamba, maolivi, nkhuyu zouma ndiponso mphesa zouma zoumba pamodzi. Pomaliza akumwera madzi otunga pakasupe.—Deuteronomo 8:7.
Pafupi ndi mundawu pali munda wina ndipo m’munda umenewu muli anthu amene akukunkha (7). Ena mwa anthu amenewa ndi osauka ndipo alibe minda yawoyawo.—Deuteronomo 24:19-21.
Kenako mlimi uja akumwaza mitolo ya balere ija pamalo opunthira mbewu, omwe ankakhala okwera komanso ogangatika kwambiri. Ndiyeno popuntha ankagwiritsa ntchito chipangizo chinachake cholemera chomwe chinkakokedwa ndi ng’ombe mozungulira malowo (8). (Deuteronomo 25:4) Chipangizo chopunthirachi chinkakhala ndi miyala komanso tizitsulo takuthwa timene tinkadula mapesi a balereyo.
Kenako mlimi uja ankadikira kuti kunja kuyambe kuda. (Rute 3:2) Kachisisira kakayamba, ankatenga ‘fosholo youluzira mankhusu’ (9) yomwe ankauluzira balereyo. Fosholoyo ankaipisa pansi pa mulu wa balere uja kenako n’kumaitukulira m’mwamba. (Mateyu 3:12) Balere ankagwera pansi ndipo mankhusu ankauluka ndi mphepo. Iye ankachita zimenezi mpaka atamaliza balere yense amene ali pamalopo.
Dzuwa likatuluka, mkazi ndi ana aakazi a mlimiyo ankayamba kupeta mbewuzo (10). Ankapeta kuti achotse miyala ndipo balere amene apetayo ankamuika m’dengu koma zinyalala ankazitaya. Balere amene akolola ankamusungira m’mbiya (11). Chaka chimenecho kukakhala kuti kuli zokolola zochuluka balere wotsala ankamusunga m’nkhokwe zimene ankachita kukumba pansi.
Ali pamalo opunthira mbewuwo, mlimiyo akudziwongola kwinaku akuyang’ana minda ina yozungulira mudziwo. Iye akuona minda imene mwangotsala ziputu zokhazokha ndipo uwu ndi umboni wa ntchito yaikulu imene alimi agwira. Akuonanso anthu ogwira ntchito m’minda akusamalira minda ya mphesa, maolivi, makangaza komanso nkhuyu. Kenako mlimiyu akuimikirana dzanja ndi munthu wina yemwe akulima m’munda wapafupi. M’munda mwa munthuyu muli zinthu monga nkhaka, mphodza, nyemba, nandolo komanso anyezi wamitundumitundu. Kenako mlimi uja akuyang’ana kumwamba n’kupereka pemphero lachidule lochokera pansi pa mtima lothokoza Mulungu chifukwa cha zinthu zabwino zimene wamupatsa.—Salimo 65:9-11.
[Zithunzi patsamba 28-30]
(Onani m’magazini yeniyeni)