Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kugwiritsira Ntchito Korona?
“MARIYA ndi Korona ndizo njira zabwino kwambiri zofikira Mulungu Wamphamvuyonse m’pemphero.”—Jean.
“Ngati munafunikira thandizo lirilonse kwa Mariya, ilo lingapezedwe bwino kwambiri mwakugwiritsira ntchito Korona. Ine sindingapite kulikonse popanda iyo!”—Kevin.
“Tinaphunzitsidwa kuti muyenera kupemphera kwa Mulungu kupyolera mwa Mariya.”—Jeannine, yemwe kale anali m’virigo Wachikatolika.
Kodi pali maziko enieni a chidaliro chathithithi choterocho pa Korona? Kodi Mulungu, Kristu, kapena Mariya amavomereza kuigwiritsira ntchito? Kodi nchiyani chimene mbiri yakale ndi Mawu Opatulika a Mulungu amanena za iyo?
Anthu ambiri amene amagwiritsira ntchito Korona amakhulupirira kuti kachitidweko kanayambika ndi Chikristu. Komabe, umboni wa m’mbiri umavumbula kuti kachitidwe ka kubwerezabwereza mapemphero ndi kuwaŵerenga pa unyolo wamikanda kanayambika Chikristu chisanakhale. Pochitira ndemanga pa chiyambi cha Korona, The World Book Encyclopedia ikusimba motere: “Mikanda ya pemphero njakalekale, ndipo mwinamwake inagwiritsidwa ntchito choyambirira ndi Abuda. Onse aŵiri Abuda ndi Asilamu amaigwiritsira ntchito m’mapemphero awo.” The Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti mikanda ya pemphero idali yofala ponseponse kwa osakhala Akristu kwa zaka mazana ambiri ndipo inagwiritsiridwa ntchito Tchalitchi Chachikatolika chisanayambe kugwiritsira ntchito Korona.
Mariya ndi Korona
Mariya akutchedwa “Mfumukazi ya Korona Woyera.” Iye watukulidwa m’kulangiza Akatolika “Kupemphera ndi Korona.” Korona yotchuka kwambiri, “Korona ya Namwali Mariya Wodalitsika,” inayambira m’zaka za zana la 12 C.E. ndipo inafikira pachimake m’zaka za zana la 15. Korona ndi Mariya ndizo chinthu chimodzi, popeza kuti iye akulingaliridwa kukhala m’chilikizi wa Korona ndi kwa amene kufunika kwakukulu kukuperekedwa m’pemphero.
Kodi nchifukwa ninji pali chigogomezero chonsecho pa Mariya ndi Korona? Poyankha akuluakulu Achikatolika amalozera ku chimene mngelo Gabrieli anati kwa iye: “Kondwerani, mwana wamkazi woyanjidwa iwe! Ambuye ali nawe.” (Luka 1:28, The New American Bible) Mariya anazindikira kuti mbali yake m’kukhala ndi pakati m’kubadwa kwa Yesu, ngakhale kuti inali yofunika, inali yochepera italinganizidwa ndi malo okwezeka amene Mwana amene akabalayo akalandira. Ponena za iye, mngelo Gabrieli anapitiriza kuti: “Ulemu wake udzakhala waukulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Ambuye Mulungu adzampatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. . . . Ulamuliro wake udzakhala wopanda mapeto.”—Luka 1:32, 33, NAB.
Onani kuti chisamaliro chinalunjikitsidwa, osati kwa Mariya, koma pa Mwanayo yemwe akakhala m’mimba mwa mayiyo—Yesu. Iye ndiye amene akakhala wamkulu ndi kulamulira monga Mfumu. (Afilipi 2:9, 10) Palibe nchimodzi chomwe chimene chanenedwa ponena za kuikidwa kwa Mariya monga “Mfumukazi ya Korona Woyera.” Komabe, Mariya analandiradi dalitso; iye anakhala mayi wa Yesu.—Luka 1:42.
Mariya sadali mkazi wodzikuza, wofunafuna kutchuka. Iye anali wachimwemwe ndi wokhutira kukhala mlambiri wodzichepetsa wa Mulungu Wam’mwambamwamba. Mkhalidwe wake wachifatso, wogonjera wavumbulidwa ndi kayankhidwe kake aka kwa mngelo Gabrieli: “Ndine mdzakazi [kapolo] wa Ambuye.” (Luka 1:38, The Jerusalem Bible) M’moyo wake wonse, Mariya anatsimikizira kukhala mkazi wowona mtima wa chikhulupiriro, wokonda chilungamo, wophunzira wokhulupiririka ndi wokhulupirika wa Yesu Kristu yemwe anagwirizana ndi alambiri anzake m’kulambira Mulungu Wamphamvuyonse modzichepetsa. Akristu oyambirira anapemphera limodzi ndi Mariya, osati kwa iye.—Machitidwe 1:13, 14.
Pemphero ndi Korona
Akristu amalilingalira pemphero kukhala makonzedwe amtengo koposa a Mlengi—mphatso yeniyeni yoyenera kunyadiridwa. Pemphero ndilo kukambitsirana kwaulemu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Ilo liyenera kufotokoza malingaliro athu amkatikati ndi maganizo apamtima. “Pemphero liyenera kukhala kufotokoza kwa ubwenzi wa munthu ndi Mulungu,” ikutero New Catholic Encyclopedia. Kupembedzera Mulungu sikuyenera kukhala chizoloŵezi chopanda tanthauzo, ndipotu sitiyenera kumamatira gwagwagwa ku njira zina zosankhidwa za mawu oloŵezedwa.—Mateyu 6:7, 8.
Kodi Korona amathandizira ku mapemphero atanthauzo oterowo? Jeannine akunena kuti kubwerezabwereza mawu akuti “Atamandidwe Mariya” pa Korona “kumakhala kubwerezabwereza kwapakamwa.” Kubwerezabwereza mawu amodzimodziwo pa Korona sikunam’bweretse chifupi ndi Mulungu. Wina yemwe kale adali m’virigo Wachikatolika, Lydia anati: “Sindinapeze chirichonse chomangirira m’kubwerezabwereza Korona. Ndinkakonda kuŵerenga mabuku onena za chipembedzo.” Mapemphero obwerezabwereza samatumikira chifuno chaphindu chirichonse, popeza kuti Mulungu walonjeza kuti: “Asanatchule kanthu, ndidzawayankha.” (Yesaya 65:24, NAB; Mateyu 6:7, 8, 32) Mulungu Wamphamvuyonse amayamikira ndi kuyankha mapembedzero amene amanenedwa ndi cholinga chabwino ndi omwe amachokera mumtima woona ndi wotsimikiza. Korona simathandiza munthu kumfikira Mulungu ndi mapemphero atanthauzo, ochokera mumtima.—Salmo 119:145; Ahebri 10:22.
Mmene Tingamfikire Mulungu
Njira yokha yovomerezedwa yofikira kwa “Wakumva pemphero” ndiyo kupyolera mwa Yesu Kristu. (Salmo 65:2) Yesu anaphunzitsa mosabisa kuti: “Ndine Njira, Chowonadi ndi Moyo. Palibe yemwe angadze kwa Atate koma kupyolera mwa ine.” (Yohane 14:6, JB) Mariya sanaitanidwe kudzagawana thayo ili ndi kutumikira monga nkhoswe. Ngati Mariya anapatsidwa mwaŵi wapadera uwu, ndithudi Yehova akanachidziŵitsa.—Ahebri 4:14-16; 1 Yohane 2:1, 2.
Korona ndi mapemphero obwerezabwereza oloŵezedwa zinayambira kunja kwa maiko odzitcha Achikristu. Kupemphera kwa Mariya kumanyalanyaza chimene Yesu anaphunzitsa, kuti ‘palibe munthu adza kwa Atate koma kupyolera mwa [iye].’ Motero, Korona ndi Mariya sindizo njira ya Mulungu yakumfikira Iye m’pemphero.