Mapindu a Kukonda Mawu a Mulungu
“Uikonde [nzeru], idzakuchinjiriza. . . . Idzakutengera ulemu pamene uifungatira.”—MIYAMBO 4:6, 8.
1. Kodi kukondadi Mawu a Mulungu kumaphatikizapo kuchita chiyani?
KUŴERENGA Baibulo n’kofunika kwambiri kwa Mkristu. Komabe, kuliŵerenga kokhako sikusonyeza chikondi cha pa Mawu a Mulungu. Bwanji ngati munthu amaŵerenga Baibulo komano n’kumachita zinthu zimene Baibulo limatsutsa? N’zosakayikitsa kuti sakonda Mawu a Mulungu m’njira imene wolemba Salmo 119 anawakondera. Kukonda Mawu a Mulungu kunam’pangitsa kukhala mogwirizana ndi zimene Mawuwo amafuna.—Salmo 119:97, 101, 105.
2. Kodi ndi mapindu otani amene amadza ndi nzeru yozikidwa pa Mawu a Mulungu?
2 Kukhala mogwirizana ndi zofuna za Mawu a Mulungu kumafuna nthaŵi zonse kulamulira maganizo ndi moyo wako. Kuchita zimenezo kumasonyeza nzeru yaumulungu, imene imatanthauza kugwiritsa ntchito chidziŵitso ndi kumvetsa kopezedwa mwa kuphunzira Baibulo. “Uikonde [nzeru], idzakutchinjiriza. Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira. Idzaika chisada cha chisomo pam’tu pako; idzakupatsa korona wokongola.” (Miyambo 4:6, 8, 9) Chimenecho n’chilimbikitsotu chabwino kwambiri choti tikulitse chikondi cha pa Mawu a Mulungu ndi kutsogozedwa ndi Mawuwo! Kodi pali amene sakufuna kutchinjirizidwa, kukwezedwa, ndi kulemekezedwa?
Otchinjirizidwa ku Kuwonongedwa Kotheratu
3. Kusiyana ndi kale lonse, n’chifukwa chiyani Akristu afunikira kutchinjirizidwa, ndipo kwa yani?
3 Kodi munthu amatchinjirizidwa motani ndi nzeru yopezeka mwa kuphunzira ndi kutsatira Mawu a Mulungu? Chinthu choyamba n’chakuti amatchinjirizidwa kwa Satana Mdyerekezi. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti apulumutsidwe kwa woipayo, Satana. (Mateyu 6:13) Lerolino, kufunika kwa kuphatikiza pempho limeneli m’mapemphero athu n’kwakukuludi. Satana ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba chaka cha 1914 chitafika, ndiye n’chifukwa chake Satana ali ndi “udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Mmene nthaŵi yamutheramu tsopano, mkwiyo wake uyenera kuti uli pachimake pamene akuyesetsa mosaphula kanthu kuchita nkhondo pa awo “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.”—Chivumbulutso 12:17.
4. Kodi Akristu amatchinjirizidwa motani ku chitsenderezo cha Satana ndi misampha yake?
4 Ndi mkwiyo wakewo, Satana akupitirizabe kudzutsira atumiki achikristu ameneŵa mavuto ndi kuyambitsa chizunzo chankhanza kapena kupingapinga ntchito yawo mwa njira zina. Akufunanso kukopa olengeza Ufumu kuti asumike maganizo awo pazinthu monga kutchuka kwakudziko, kukonda moyo wa phee, kupeza chuma chakuthupi, ndi kukondetsa zosangalatsa, m’malo mwa ntchito yolalikira Ufumu. Kodi n’chiyani chimatchinjiriza atumiki okhulupirika a Mulungu kuti asagonje ndi chitsenderezo cha Satana kapena kuti asakodwe m’misampha yake? Inde, pemphero, unansi waumwini wathithithi ndi Yehova, ndi chikhulupiriro chakuti malonjezo ake n’ngotsimikizirika n’zofunika. Koma zonsezi n’zogwirizana ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu ndi kutsimikiza mtima kulabadira zikumbutso za m’Mawuwo. Zikumbutso zimenezi zimadza mwa kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zothandizira kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano yachikristu, kumvera uphungu wa m’Malemba wochokera kwa wokhulupirira mnzathu, kapena mwakungosinkhasinkha mwapemphero pa mapulinsipulo a Baibulo amene mzimu wa Mulungu watikumbutsa.—Yesaya 30:21; Yohane 14:26; 1 Yohane 2:15-17.
5. Kodi nzeru yozikidwa pa Mawu a Mulungu imatitchinjiriza motani?
5 Awo amene amakonda Mawu a Mulungu amatchinjirizidwa m’njira zinanso. Mwachitsanzo, amapeŵa kuvutika mtima komanso matenda enieni amene amadza chifukwa cha kumwa mankhwala osokoneza bongo, kusuta fodya, ndi chiwerewere. (1 Akorinto 5:11; 2 Akorinto 7:1) Sawononga maunansi a anthu mwa kuchita miseche kapena kuyankhula monyoza. (Aefeso 4:31) Komanso sakhala okayika chifukwa chokonda mafilosofi onyenga a nzeru ya dziko. (1 Akorinto 3:19) Mwa kukonda Mawu a Mulungu, amatchinjirizidwa ku zinthu zimene zingawawonongetsere unansi wawo ndi Mulungu ndi kuwatayitsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Amatanganidwa ndi kuthandiza anansi awo kuti akhale ndi chikhulupiriro m’malonjezo abwino kwambiri amene ali m’Baibulo, podziŵa kuti potero ‘adzadzipulumutsa iwo okha ndi iwo akumva iwo.’—1 Timoteo 4:16.
6. Kodi nzeru yozikidwa pa Mawu a Mulungu ingatitchinjirize motani ngakhale pamene tili pamavuto?
6 Zoonadi, aliyense, ngakhale anthu amene amakonda Mawu a Mulungu amakhudzidwa ndi “nthaŵi ndi zochitika zamwadzidzidzi.” (Mlaliki 9:11, NW) N’zodziŵikiratu kuti ena pakati pathu adzakumana ndi masoka achilengedwe, kudwala matenda akayakaya, kuchita ngozi, kapena kumwalira mwadzidzidzi. Koma ngakhale zitatero, ndife otchinjirizidwa. Palibe tsoka limene lingawononge kotheratu munthu amene amakondadi Mawu a Mulungu. Chotero, sitiyenera kuda nkhaŵa mopambanitsa ndi zimene zingadzachitike m’tsogolo. Titachita zonse zotiteteza, ndi bwino kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndi kusalola kupanda chisungiko kwa moyo wamakono kutilanda mtendere wathu. (Mateyu 6:33, 34; Afilipi 4:6, 7) Kumbukirani kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha chiukiriro ndi moyo wabwino kwambiri pamene Mulungu ‘adzapanga zonse zikhale zatsopano.’—Chivumbulutso 21:5; Yohane 11:25.
Sonyezani Kuti Ndinu “Nthaka Yokoma”
7. Ndi fanizo lotani limene Yesu anauza makamu amene anadza kudzamumvetsera?
7 Kufunika kwa kukhala ndi malingaliro oyenera pa Mawu a Mulungu kunasonyezedwa bwino m’limodzi la mafanizo a Yesu. Pamene Yesu anali kulalikira uthenga wabwino m’Palestina yense, makamu ankasonkhana kuti amumvetsere. (Luka 8:1, 4) Koma si onse amene anakondadi Mawu a Mulungu. Mosakayikira, ena anadza kudzamumvetsera chifukwa chakuti ankafuna kuona zozizwitsa kapena chifukwa chakuti ankasangalala ndi maphunzitsidwe ake ochititsa chidwiwo. Chotero, Yesu anauza makamuwo fanizo lakuti: “Anatuluka wofesa kukafesa mbewu zake; ndipo m’kufesa kwake zina zinagwa m’mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m’mlengalenga zinatha kuzidya. Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinafota msanga, chifukwa zinalibe mnyontho. Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa. Ndipo zina zinagwa panthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi.”—Luka 8:5-8.
8. M’fanizo la Yesu, kodi mbewu n’chiyani?
8 Fanizo la Yesu linasonyeza kuti anthu adzalabadira kulalikira kwa uthenga wabwino m’njira zosiyanasiyana, malinga ndi mmene mtima wa womvetserayo ulili. Mbewu imene ikufesedwayo ndiwo “mawu a Mulungu.” (Luka 8:11) Kapena, monga momwe nkhani ina imasimbira fanizolo, mbewuyo ndi “mawu a Ufumu.” (Mateyu 13:19) Yesu anagwiritsa ntchito mawu onse aŵiri, popeza kuti nkhani yaikulu m’Mawu a Mulungu ndi ya Ufumu wakumwamba wolamulidwa ndi Yesu Kristu monga Mfumu umene Yehova adzagwiritsa ntchito kukweza uchifumu wake ndi kuyeretsa dzina lake. (Mateyu 6:9, 10) Chotero, kwenikweni, mbewu ndiwo uthenga wabwino wa Mawu a Mulungu, Baibulo. Mboni za Yehova zimagogomezera uthenga wa Ufumu umenewu pamene zifesa mbewu motsanzira Wofesa woyambayo, Yesu Kristu. Kodi zimapeza kulabadira kotani?
9. Kodi n’chiyani chimatanthauzidwa ndi mbewu zomwe zikugwera (a) m’mbali mwa njira? (b) pathanthwe? (c) pakati pa minga?
9 Yesu anati mbewu zina zikugwera m’mbali mwa njira ndipo zikupondedwa. Zimenezi zikuimira anthu otanganitsidwa kwambiri moti mbewu za Ufumu sizikutha kuzika mizu m’mitima yawo. Asanayambe kukonda Mawu a Mulungu, “akudza Mdyerekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.” (Luka 8:12) Mbewu zina zikugwera pathanthwe. Zimenezi ndiwo anthu amene amakopeka ndi uthenga wa m’Baibulo koma salola kuti ukhudze mitima yawo. Akakumana ndi chitsutso kapena akalephera kutsatira uphungu wa Baibulo, “angopatuka” chifukwa chakuti sanazike mizu. (Luka 8:13) Ndiyeno pali awo amene amamva mawu koma “nkhaŵa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo” zimawafooketsa. M’kupita kwa nthaŵi, mofanana ndi zomera zokoledwakoledwa ndi minga, iwo ‘sakhwima.’—Luka 8:14.
10, 11. (a) Kodi nthaka yabwino imaimira yani? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tisunge’ Mawu a Mulungu m’mitima yathu?
10 Ndiyeno pali mbewu zomwe zimagwera panthaka yabwino. Ameneŵa ndiwo anthu amene amalandira uthengawo ndi “mtima woona ndi wabwino.” Mwachibadwa, aliyense wa ife amafuna kudziona kuti ali m’gulu limeneli. Koma pomalizira pake, ndi kuweruza kwa Mulungu kumene kudzasonyeza zonse. (Miyambo 17:3; 1 Akorinto 4:4, 5) Mawu ake amanena kuti timasonyeza kuti tili ndi “mtima woona ndi wabwino” mwa zochita zathu kuyambira tsopano mpaka imfa yathu kapena mpaka pamene Mulungu adzathetsa dongosolo loipa la zinthu limeneli. Ngati poyamba talabadira uthenga wa Ufumu, zimenezo zili bwino. Komabe, awo amene ali ndi mtima woona ndi wabwino amalandira Mawu a Mulungu “nawasunga . . . , nabala zipatso ndi kupirira.”—Luka 8:15.
11 Njira yokha yotsimikizirika yosungira Mawu a Mulungu m’mitima yathu ndiyo kuwaŵerenga ndi kuwaphunzira patokha komanso mogwirizana ndi okhulupirira anzathu. Zimenezi zimaphatikizapo kugwiritsa ntchito mokwanira chakudya chauzimu choperekedwa kudzera m’makonzedwe oikidwa kuti asamalire zinthu zauzimu za otsatira oona a Yesu. (Mateyu 24:45-47) Mwa njira imeneyo, awo amene amasunga Mawu a Mulungu m’mitima yawo amasonkhezeredwa ndi chikondi kuti ‘abale zipatso ndi kupirira.’
12. Kodi zipatso zimene tiyenera kubala ndi kupirira n’ziti?
12 Kodi nthaka yabwino imabala zipatso zotani? Mwachilengedwe, mbewu zimakula kukhala zomera zobala zipatso zimenenso zili ndi mbewu zofananazo, zimene zingafesedwenso kuti zibale zipatso zina. Mofananamo, kwa awo amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, mbewu ya mawu imamera mwa iwo, kuwapangitsa kupita patsogolo mwauzimu kufikira pamene iwonso angafese mbewu m’mitima ya ena. (Mateyu 28:19, 20) Ndipo ntchito yawo yofesa imachitidwa ndi kupirira kwakukulu. Yesu anasonyeza kufunika kwa kupirira pofesa mbewu pamene anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:13, 14.
“Kubala Zipatso mu Ntchito Yonse Yabwino”
13. Kodi ndi pemphero lotani limene Paulo anapereka limene linagwirizanitsa zipatso ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu?
13 Mtumwi Paulo nayenso anakambapo za kufunika kwa kubala zipatso, ndipo anagwirizanitsa kubala zipatso ndi Mawu a Mulungu. Anapemphera kuti okhulupirira anzake “[a]kadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”—Akolose 1:9, 10; Afilipi 1:9-11.
14-16. Mogwirizana ndi pemphero la Paulo, kodi okonda Mawu a Mulungu amabala zipatso zotani?
14 Chotero Paulo akusonyeza kuti cholinga si kungokhala ndi chidziŵitso cha m’Baibulo. M’malo mwake, kukonda Mawu a Mulungu kumatisonkhezera ‘kuyenda moyenera Ambuye’ mwa kupitirizabe “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.” Ntchito yabwino yake iti? Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiyo ntchito yofunika kwambiri ya Akristu m’masiku otsiriza ano. (Marko 13:10) Kuwonjezera apo, awo amene amakonda Mawu a Mulungu amayesetsa nthaŵi zonse kuchirikiza ntchitoyi ndi ndalama zawo. Amasangalala nawo mwayi umenewu podziŵa kuti “Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Zopereka zawo zimathandiza pa kuyendetsa nyumba za Beteli zoposa zana limodzi zimene zimapereka chitsogozo cha ntchito yolalikira Ufumu ndiponso zina zimene zimapanga mabaibulo ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo. Zopereka zawo zimathandiziranso pa zowonongedwa za pa misonkhano yaikulu yachikristu ndi pakutumiza oyang’anira oyendayenda, amishonale, ndi alaliki ena a nthaŵi zonse.
15 Ntchito zinanso zabwino zimaphatikizapo kumanga ndi kusamalira nyumba za kulambira koona. Kukonda Mawu a Mulungu kumasonkhezera olambira ake kuonetsetsa kuti Nyumba Zamisonkhano ndi Nyumba za Ufumu sizikusiyidwa zosasamalidwa. (Yerekezani ndi Nehemiya 10:39.) Popeza kuti dzina la Mulungu limaonekera patsogolo pa nyumba zimenezi, n’kofunika kwambiri kuti mkati ndi kunja zizikhala zoyera ndi zaudongo ndi kutinso khalidwe la awo amene amalambira m’nyumba zimenezi lisakhale lodzetsa chitonzo. (2 Akorinto 6:3) Akristu ena amatha kuchita zowonjezeka. Kukonda Mawu a Mulungu kumawasonkhezera kuyenda maulendo ataliatali kuti akamange nawo nyumba zatsopano zolambiriramo m’mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi kumene kukufunika thandizo chifukwa cha umphaŵi kapena kusoŵa kwa anthu a maluso ofunika.—2 Akorinto 8:14.
16 “Kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino” kumaphatikizaponso kusamalira maudindo apabanja ndi kudera nkhaŵa Akristu anzathu. Kukonda Mawu a Mulungu kumatisonkhezera kuzindikira mwamsanga zosoŵa za “apabanja la chikhulupiriro” ndi “kusonyeza kudzipereka kwaumulungu pabanja [lathu].” (Agalatiya 6:10; 1 Timoteo 5:4, 8, NW) Pachifukwa chimenechi, ndi ntchito yabwino kuchezera odwala ndi kutonthoza olira. Ndipo akulu a mumpingo ndi Makomiti Olankhulana ndi Zipatala amachita ntchito yabwino zedi pothandiza anthu amene akuyang’anizana ndi mavuto azachipatala! (Machitidwe 15:29) Ndiyeno masoka akuwonjezeka—ena achilengedwe komanso ena ochitika chifukwa cha kupusa kwa anthu. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Mboni za Yehova zadzipangira mbiri yabwino m’mbali zambiri za dziko lapansi popereka chithandizo mwamsanga kwa okhulupirira anzawo ndi anthu ena ovutika chifukwa cha masoka ndi ngozi. Zonsezi ndi zipatso zabwino zimene okonda Mawu a Mulungu amasonyeza.
Mapindu Aulemerero Am’tsogolo
17, 18. (a) Kodi kufesa mbewu za Ufumu kukukwaniritsanji? (b) Kodi ndi zochitika zogwedeza dziko ziti zimene okonda Mawu a Mulungu adzaona posachedwapa?
17 Kufesa mbewu za Ufumu kukupitirizabe kudzetsa mapindu aakulu kwa anthu. M’zaka zino anthu oposa 300,000 chaka chilichonse alola kuti uthenga wa m’Baibulo uzike mizu m’mitima yawo moti apatulira miyoyo yawo kwa Yehova ndi kusonyeza zimenezi mwa ubatizo wa m’madzi. Iwo adzakhalatu ndi tsogolo laulemerero kwambiri!
18 Posachedwapa, okonda Mawu a Mulungu akudziŵa kuti Yehova Mulungu adzaimirira kuti akulitse dzina lake. ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wapadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, adzawonongedwa. (Chivumbulutso 18:2, 8) Kenako, awo amene sakufuna kutsatira Mawu a Mulungu adzaphedwa ndi Mfumuyo, Yesu Kristu. (Salmo 2:9-11; Danieli 2:44) Pambuyo pake, Ufumu wa Mulungu udzadzetsa mpumulo wosatha pochotsapo upandu, nkhondo, ndi masoka ena. Sikudzakhalanso kofunika kutonthoza anthu chifukwa cha zinthu zopweteketsa mtima, matenda, ndi imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.
19, 20. Kodi ndi tsogolo laulemerero lotani limene okondadi Mawu a Mulungu adzakhala nalo?
19 Ndiyeno, okonda Mawu a Mulungu adzakwaniritsatu ntchito zabwino zaulemerero zedi! Opulumuka Armagedo adzayamba ndi ntchito yosangalatsa yosintha dziko lapansili kukhala paradaiso. Iwo adzakhala ndi mwayi wosangalatsa wokonzekera zofunika za anthu akufa amene tsopano akugona m’manda ndiponso ali m’chikumbukiro cha Mulungu kuti adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Panthaŵi imeneyo, chitsogozo changwiro chidzafika kwa okhala padziko lapansi kuchokera kwa Ambuye Mfumu Yehova, kudzera mwa Mwana wake wokwezedwayo, Yesu Kristu. ‘Mabuku adzatsegulidwa,’ kuvumbula malangizo a Yehova a moyo wa m’dziko latsopano.—Chivumbulutso 20:12.
20 Panthaŵi yoikidwa ya Yehova, gulu lonse la Akristu okhulupirika odzozedwa likadzalandira mphotho yawo yakumwamba monga “oloŵa [nyumba] anzake a Kristu.” (Aroma 8:17) Mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, anthu onse padziko lapansi amene amakonda Mawu a Mulungu adzakonzedwa kukhala ndi malingaliro ndi thupi langwiro. Akadzakhalabe okhulupirika pamayesero omalizira, adzafupidwa ndi moyo wosatha ndipo adzaloŵa mu “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21; Chivumbulutso 20:1-3, 7-10) Imeneyotu idzakhala nthaŵi yosangalatsa zedi! Ndithudi, kaya Yehova watipatsa chiyembekezo chakumwamba kapena cha padziko lapansi, chikondi chosatha cha pa Mawu ake ndi kutsimikiza mtima kukhala mogwirizana ndi nzeru yaumulungu kudzatitchinjiriza tsopano. Ndiponso m’tsogolo ‘kudzatipatsa ulemu chifukwa tikukufungatira.’—Miyambo 4:6, 8.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi kukonda Mawu a Mulungu kudzatitchinjiriza motani?
◻ Kodi mbewu ya m’fanizo la Yesu n’chiyani, ndipo imafesedwa motani?
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti ndife “nthaka yokoma”?
◻ Kodi ndi mapindu otani amene anthu okonda Mawu a Mulungu angayembekezere?
[Chithunzi patsamba 16]
Mbewu ya m’fanizo la Yesu imaimira uthenga wabwino umene uli m’Mawu a Mulungu
[Mawu a Chithunzi]
Garo Nalbandian
[Chithunzi patsamba 17]
Mboni za Yehova zimatsanzira Wofesa Mbewu Wamkulu
[Zithunzi patsamba 18]
Opulumuka Armagedo adzasangalala ndi zipatso za dziko lapansi