Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kupha Munthu Mkati mwa Phwando Lokumbukira Tsiku Lobadwa
PAMBUYO pa kupereka malangizo kwa atumwi ake, Yesu akuwatumiza iwo ku magawo awo awiri awiri. Mwinamwake pachibalePetrd ndi Andreya anapitira pamodzi, monga mmene anachitira Yakobo ndi Yohane; Filipo ndi Bartolomeyo, Tomasi ndi’ Mateyu, Yakobo’ ndi Tadeyo, ndi Simoni ndj Yudasiisikariote. Awiri awiri asanu ndi mmodzi a olalikirawo akulengeza mbiri yabwino ya UfUmu ndi kuchita zozizwitsa za kuchiritsa kulikonse kumene apita.
Panthawiyi, Yohane Mbatizi adakali m’ndende. lye wakhala kumeneko kwa chifupifupi zaka ziwiiri tsopano.’ Mungakumbukire kuti Yohane analalalikira kuti Chinali cholakwa kwa Herod, Antipa kutenga’ Herodiya, mkazi wambale wake Filipo monga mkaziwake. Popeza Herode Antipa andzilalikira kukhala akutsatira Chilamulo cha Mose, Yohane moyenerera anavumbulutsa chigwirizano cha chigololo chimenechi. Chinali chifukwa cha ichi kuti Herode anapangitsa Yohane kuponyedwa m’ndende, mwinamwake pachikakamizo cha Herodiya.
Herode Antipa anazindikira kutiYohane anali munthu wolungama ndipo anamvetsera kwa iye ndi chisangalalo. Chotero iye sakudziwa chochita naye. Herodiya, ku mbali ina, amamuda Yohane ndipo anafunafuna kumupha iye. Pomalizira, mwawi umene anakhala akudikira unafika
Mwamsanga isanafike Paskha ya 32 C. E„ Herode akonzekera chikumbukiro chachikulu cha tsiku lake lakubadwa. Amene asonkhana kaamba kaphwandolo ali anthu amaudindo apamwamba ndi nduna za nkhondo za Herode, limodzinso ndi nzika zotchuka za mu Galileya. Pamene madzulo afika, Salome, mwana wamkazi wamng’ono wa Herodiya mwa mwamuna wake wakale Filipo, watumizidwakukavina kaamba ka alendo. GUlu la amunawo lasangalatsidwa ndi kuvina kwake, kumene mosakaikira kunali kodzutsa chikondi.
Herode wasangalatsidwa kwambiri ndi Salome. ‘Tapempha kwa ine chirichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe,” iye akulengeza tero. lye akulumbira: “chirichonse ukandipempha ndidzakupatsa, ngakhale kukugawira ufumu wanga”
Asanayankhe, Salome akupita panja kukafunsa mayi wake. “Ndidzapempha chiyani? iye akufunsa.
Mwawi pomalizira!Mutu wa yohane Mbatizi,” Herodiya akuyankha mosasinkhasinkha
Mwamsanga Salome akubwerera kwa Herode ndi kupempha: “Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi m’mbizi”
Herode amva chisoni chachikulu. koma chakuti alendo ake amva lumbiro lake, iye ali ndi manyazi, kusapereka ichi, ngakhale kuti ichi chikatanthauza kupha munthu wosachimwa mwamsanga odula anthu atumizidwa kundende ndimalangizo ake osasangalatsa Posakhalitsa iye akubwera ndi mutu wa Yohane Mbatizi m’mbizi, ndi kuwupereka iwo kwa Salome, lye, kenaka, autenga iwo kwa mayi wake. Pamene ophunzira a Yohane amva chimene chachitika, iwo akubwera ndi kuchotsa thupi lake ndi kuika ilo m’manda, ndipo kenaka asimba nkhaniyo kwa Yesu.
Pambuyo pake, pamene Herode amva za kuchiritsa anthu kwa Yesu ndi kutulutsa ziwanda, iye achita mantha, kuwopa kuti Yesu m’chenicheni ali Yohane amene waukitsidwa kuchokera kwa akufa. Pambuyo pa chimenecho, iye mokulira akukhumba kuwona Yesu, osati kuti akamve ulaliki wake, koma kukatsimikizira kaya mantha ake anali ndi maziko kapena ayi. Mateyu 10:1-5; 11:1; 14:1-12; Marko 6:14-29; Luka 9:7-9.
◆ Nchifukwa ninji Yohane ali m’ndende, ndipo kodi nchifukwa ninji Herode sakufuna kumupha iye?
◆ Kodi ndimotani mmene Herodiya pomalizira ali wokhoza kupha Yohane? !
◆ Pambuyo pa imfa ya Yohane, kodi nchifukwa ninji Herode akufuna kuwonaYesu?
[Chithunzi chachikulu patsamba 31]