Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Mozizwitsa Adyetsa Zikwi
ATUMWI 12 angosangalala kumene ndi ulendo wolalikira wozizwitsa kuzungulira mu Galileya. Tsopano, mwamsanga pambuyo pa kuphedwa kwa Yohane, iwo akubwerera kwa Yesu ndi kunena zokumana nazo zawo zosangalatsa. Kuwona kuti iwo ali otopa ndi kuti anthu ambiri akubwera ndi kupita kotero kuti alibe ngakhale nthaŵi ya kudya, Yesu akuti: ‘Tiyeni tipite ku malo atokha kumene mungapume.’
Akukwera ngalawa yawo, mwinamwake pafupi ndi Kapernao, iwo akulunjika ku malo akutali, mwachiwonekere kum’mawa kwa Yordano kupitirira Betsaida. Anthu ambiri, ngakhale kuli tero, akuwona iwo pamene akuchoka, ndipo ena adziŵa ponena za icho. Onsewo athamangira kutsogolo pamtunda, ndipo pamene ngalawa ifika, iwo ali pamenepo kuwachingamira.
Akutuluka m’ngalawa ndi kuwona khamu lalikulu, Yesu agwidwa ndi chifundo chifukwa anthuwo ali ngati nkhosa zopanda mbusa. Chotero iye akuchiritsa odwala awo ndi kuyamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
Mwamsanga nthaŵi itha, ndipo ophunzira a Yesu afika kwa iye ndi kunena kuti: “Malo ano nga chipululu, ndi dzuŵa lapendeka ndithu. Muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.”
Komabe, mkuyankha Yesu akuti: “Apatseni kudya ndinu.” Kenaka, popeza Yesu anadziŵa kale chimene akachita, iye anamuyesa Filipo, mwakumfunsa kuti: “Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?”
Kuchokera ku kayang’anidwe ka Filipo mkhalidwewo uli wosatheka. Nkulekelanji, popeza kuti pali amuna chifupifupi 5,000, ndipo mwinamwake anthu oposa 10,000 kuŵerenganso akazi ndi ana! “Mikate ya marupiya atheka mazana aŵiri [rupiya inali malipiro a nthaŵiyo] siikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono,” ayankha Filipo.
Mwinamwake kuti asonyeze kusatheka kwa kudyetsa anthu ambiri chotero, Andreya akudzipereka: “Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiŵiri,” akuwonjezera: “Koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?”
Koma popeza iri nthaŵi yangululu, mwamsanga pambuyo pa Paskha wa 32 C.E., pali udzu wobiriŵira wambiri. Chotero Yesu anauza ophunzira ake kuuza anthu kuti akhale pa udzupo mu magulu a 50 ndi a 100. Iye atenga mikate isanuyo ndi tinsomba tiŵirito, kuyang’ana kumwamba, ndipo apereka dalitso. Kenaka ayamba kunyema mkatewo ndi kugawa tinsombato. Iye akupereka izi kwa ophunzira ake, amene, kenaka, agawira izo kwa anthu. Modabwitsa, anthu onse adya kufikira kukhuta!
Pambuyo pake Yesu akuuza ophunzira ake: “Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.” Pamene akuchita tero, iwo adzaza mitanga 12 ndi makombo kuchokera ku zimene iwo adya! Mateyu 14:13-21; Marko 6:30-44; Luka 9:10-17; Yohane 6:1-13.
◆ Nchifukwa ninji Yesu akufuna malo obisika kaamba ka atumwi ake?
◆ Ndi kuti kumene Yesu akutenga ophunzira ake, ndipo kodi nchifukwa ninji chifuno chawo chakupuma sichinakwaniritsidwe?
◆ Pamene dzuŵa lapendeka, nchiyani chimene ophunzira akufulumiza, koma ndimotani mmene Yesu asamalira anthuwo?