MUTU 65
Yesu Anaphunzitsa Anthu Ena Ali pa Ulendo Wopita ku Yerusalemu
MATEYU 8:19-22 LUKA 9:51-62 YOHANE 7:2-10
MMENE AZICHIMWENE AKE A YESU ANKAMUONERA
KUFUNIKA KWA NTCHITO ZOKHUDZA UFUMU
Yesu analalikira komanso kuchita zozizwitsa zambiri ku Galileya chifukwa ndi kumene anapeza anthu ambiri amene ankamvetsera uthenga wake poyerekeza ndi ku Yudeya. Komabe Ayuda “anayamba kufunafuna njira yomuphera” atachiritsa munthu wina pa mwambo wa Pasika ku Yerusalemu.—Yohane 5:18; 7:1.
Koma pa nthawiyi unali mwezi wa September kapena October m’chaka cha 32 C.E. ndipo Chikondwerero cha Misasa (kapena kuti Chikondwerero cha Zokolola) chinali chitayandikira. Chikondwererochi chinkachitika kwa masiku 7 ndipo pa tsiku la 8 ankachita msonkhano wopatulika. Chikondwererochi chinkachitika kumapeto kwa nyengo yokolola ndipo imeneyi inali nthawi yosangalala komanso yothokoza Yehova chifukwa cha zokololazo.
Azichimwene ake a Yesu, omwe mayina awo anali Yakobo, Simoni, Yosefe komanso Yuda anauza Yesu kuti achoke ‘apite ku Yudeya.’ Ku Yerusalemu ndi kumene kunali ku likulu la chipembedzo chachiyuda. Ndipo pa nthawi ya zikondwerero zitatu zomwe zinkachitika chaka chilichonse, mumzindawu munkadzaza anthu. Azichimwene ake a Yesu atadziwa kuti ku chikondwererochi kudzapitanso anthu ambiri anauza Yesu kuti: “Pakuti palibe amene amachita kanthu mseri koma n’kumafuna kudziwika ndi anthu. Ngati inu mumachita zimenezi, mudzionetsere poyera kudzikoli.”—Yohane 7:3,4.
Pa nthawiyi azichimwene ake a Yesuwa “sanali kumukhulupirira” kuti ndi Mesiya. Komabe iwo ankafuna kuti anthu amene adzapite kuchikondwererocho akamuone akuchita zodabwitsa. Yesu anazindikira kuti kuchita zimenezi kunali koopsa choncho anawauza kuti: “Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa. Inuyo nyamukani mupite ku chikondwereroko. Ine sindipitako panopa, chifukwa nthawi yanga yoyenera sinafike.”—Yohane 7:5-8.
Patadutsa masiku angapo azichimwene ake a Yesu atanyamuka ndi gulu la anthu ena, Yesu ndi atumwi ake ananyamuka koma mosaonekera kwa anthu ambiri. Iwo sanadutse njira ya kufupi ndi mtsinje wa Yorodano, yomwe anthu ambiri ankakonda kudutsa. M’malomwake anadutsa njira yachidule yodzera m’chigawo cha Samariya. Yesu anadziwa kuti adzafuna malo ogona pofika ku Samariya choncho anatumiza anthu kuti akafufuze ndi kukonzeratu malowo. Atafika pamalo ena ku Samariya anthu akumeneko sanawalandire bwino komanso anakana kuwapatsa malo chifukwa anadziwa kuti Yesu akupita ku Yerusalemu kumwambo wachiyuda ndipo sakhalitsa kwawoko. Chifukwa cha zimenezi Yakobo ndi Yohane anakwiya kwambiri ndipo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi mukufuna tiwaitanire moto kuchokera kumwamba kuti uwanyeketse?” (Luka 9:54) Yesu anawadzudzula chifukwa chokhala ndi maganizo amenewo ndipo anapitiriza ulendo wawo.
Ali m’njira anakumana ndi mlembi wina amene anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.” (Mateyu 8:19, 20) Yesu ananena zimenezi pofuna kumuthandiza mlembiyo kudziwa kuti akadzakhala wotsatira wake adzakumana ndi mavuto. Zikuoneka kuti mlembiyu anali wonyada kwambiri moti sanalole kukhala moyo woterowo. Ndiyetu aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingalolere kuvutika chifukwa chokhala wotsatira wa Yesu?’
Yesu anakumananso ndi munthu wina ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Koma munthuyo anayankha kuti: “Ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.” Yesu ankadziwa mmene zinthu zinalili pamoyo wa munthuyo choncho anamuuza kuti: “Aleke akufa aike akufa awo, koma iwe pita kukalengeza ufumu wa Mulungu kwina kulikonse.” (Luka 9:59, 60) Bambo ake a munthuyu anali asanamwalire. Tikutero chifukwa akanakhala kuti pa nthawiyo bambowo anali atamwalira, munthuyo akanakhala ali kumaliro a bambo akewo ndipo sakanakumana ndi Yesu. Munthuyo sanali wokonzeka kuika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba pa moyo wake.
Pamene ankayandikira ku Yerusalemu anakumananso ndi munthu wina amene anauza Yesu kuti: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika a m’banja langa.” Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wogwira pulawo koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo sayenera ufumu wa Mulungu.”—Luka 9:61, 62.
Aliyense amene akufuna kukhala wophunzira wa Yesu ayenera kuika maganizo ake onse pa ntchito zokhudza Ufumu. Ngati munthu amene akuyendetsa pulawo sakuyang’ana kutsogolo komwe akupita sangalime mzera woongoka. Ndipo ngati atasiya pulawoyo pansi kuti ayang’ane kumbuyo, ndiye kuti ntchito yonse singayende. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene zingachitikire munthu amene akuyenda panjira yopita ku moyo wosatha koma n’kumayang’ana kumbuyo kuti aone zinthu za m’dziko loipali. Munthuyu angasokonezeke n’kuchoka panjira yopita ku moyo wosatha.