Chikondi cha pa Mnansi Nchotheka
FANIZO la Yesu Kristu la Msamariya linasonyeza zimene chikondi chenicheni cha pa mnansi chimatanthauzadi. (Luka 10:25-37) Yesu anaphunzitsanso kuti: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndiili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”—Mateyu 22:37-39.
Mofanana ndi anthu ambiri, kodi mumakuona kukhala kovuta kukonda mnansi wanu wa fuko lina losiyana ndi lanu? Mwina zili choncho chifukwa chakuti mwaphunzira ponena za tsankho ndi chisalungamo kapena kuti zimenezi zinakuchitikirani. Mwina inuyo kapena wokondedwa wanu munachitiridwa nkhanza ndi anthu a mtundu wina.
Popeza Yesu anasonyeza kuti limodzi la malamulo a Mulungu nlakuti tikonde mnansi wathu, kuyenera kukhala kotheka kulaka udani waukulu wotero. Njira yochitira zimenezo ndiyo kuona anthu mmene Mulungu ndi Kristu amawaonera. Mogwirizana ndi nkhaniyi tiyeni tipende chitsanzo cha Yesu ndi Akristu oyambirira.
Chitsanzo Chabwino cha Yesu
Ayuda a m’zaka za zana loyamba anali ndi udani waukulu pa Asamariya, anthu okhala m’dera la pakati pa Yudeya ndi Galileya. Panthaŵi ina otsutsa Achiyuda mwamwano anafunsa Yesu kuti: “Kodi sitinenetsa kuti inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiŵanda?” (Yohane 8:48) Lingaliro la kuda Asamariya linali lamphamvu mwa iwo moti Ayuda ena anatembereradi Asamariya poyera m’masunagoge napemphera tsiku ndi tsiku kuti Asamariya asakapatsidwe moyo wosatha.
Mosakayikira kudziŵa chidani chimenechi chozika mizu mwa iwo kunasonkhezera Yesu kupereka fanizo la Msamariya amene anadzisonyeza kukhala mnansi weniweni mwakusamalira mwamuna Wachiyuda womenyedwa ndi achifwamba. Kodi ndimwanjira ina yotani imene Yesu akanayankhira pamene mwamuna Wachiyuda wodziŵa bwino Chilamulo cha Mose anamfunsa kuti: “Ndipo mnansi wanga ndani?” (Luka 10:29) Eya, Yesu akanayankha mwachindunji kuti: ‘Mnansi wako sali chabe Myuda mnzako komanso anthu ena, ngakhale Msamariya.’ Komabe, Ayuda akanakuona kukhala kovuta kuvomereza zimenezo. Chotero iye anasimba fanizo la Myuda amene anachitiridwa chifundo ndi Msamariya. Motero Yesu anathandiza omvetsera Achiyuda kuzindikira okha kuti chikondi chowona cha pa mnansi chikasonyezedwanso kwa anthu osakhala Ayuda.
Yesu analibe malingaliro a kuda Asamariya. Akumayenda m’Samariya panthaŵi ina, anapuma pachitsime pamene ophunzira ake anapita kumzinda wapafupi kukagula chakudya. Pamene mkazi Wachisamariya anadza kudzatunga madzi, iye anati: “Undipatse ine ndimwe.” Popeza kuti Ayuda ndi Asamariya samadyerana, mkaziyo anafunsa kuti: “Bwanji inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya?” Pamenepo Yesu anapereka umboni kwa iye, akumalengezadi poyera kuti anali Mesiya. Mkaziyo analabadira mwakupita mumzinda ndi kukaitana ena kudza ndi kumvetsera kwa iye. Chotulukapo? “M’mudzi muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira iye.” Nchotulukapo chabwino chotani nanga chotsatirapo chifukwa chakuti Yesu sanadodometsedwe ndi mkhalidwe wa maganizo wofala wa Ayuda anzake!—Yohane 4:4-42.
Mulungu Alibe Tsankho
Chinali chifuno cha Mulungu kuti Yesu angolalikira kwakukulukulu kwa Ayuda okha, “nkhosa zotayika za banja la Israyeli.” (Mateyu 15:24) Chotero, otsatira ake oyambirira anali Ayuda. Koma patangopita zaka zitatu pambuyo pa kutsanulidwa kwa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E., Yehova anamveketsa bwino lomwe kuti anafuna Ayuda okhulupirira kufutukulira ntchito yakupanga ophunzira kwa anthu amitundu, Akunja.
M’kuganiza kwa Ayuda, kukonda Msamariya monga munthu mwini kukakhala kovuta kwambiri. Ndipo kukakhala kovutirapo kusonyeza chikondi cha pa mnansi kwa Akunja osadulidwa, anthu amene sanali oyandikana kwambiri ndi Ayuda monga momwe analiri Asamariya. Pofotokoza mkhalidwe wa maganizo wa Ayuda kwa Akunja, The International Standard Bible Encyclopaedia imati: “Timapeza, m’nthaŵi za mu NT[Chipangano Chatsopano], mtundu wopambanitsa wa kuipidwa, kunyodola ndi chidani. Iwo [Akunja] anaonedwa kukhala odetsedwa, amene kunali kosaloleka kuyanjana nawo. Anali adani a Mulungu ndi anthu Ake, kwa amene chidziŵitso cha Mulungu chinamanidwa kusiyapo ngati anakhala otembenuka, ndipo ngakhale atatero, monga m’nthaŵi zamakedzana, sakanaloledwa kukhala ziŵalo zenizeni. Ayuda analetsedwa kuwapatsa uphungu, ndipo ngati anafunsa za Mulungu anayenera kutembereredwa.”
Ngakhale kuti ambiri anali ndi malingaliro ameneŵa, Yehova anachititsa mtumwi Petro kuona masomphenya mmene anauzidwa ‘kusayesa chinthu wamba chimene Mulungu anayeretsa.’ Ndiyeno Mulungu anamuuza kupita kunyumba kwa Korneliyo Wakunja. Petro anapereka umboni wonena za Kristu kwa Korneliyo, banja lake, ndi Akunja ena. “Zowona,” Petro anatero, “ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Petro akali kulalikira, mzimu woyera unatera pa okhulupirira atsopanowo, amene anabatizidwa pambuyo pake nakhala otsatira oyamba Akunja a Kristu.—Machitidwe, chaputala 10.
Otsatira Achiyuda analandira kusinthaku, akumazindikira kuti lamulo la Yesu la “kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse” silinali kwa Ayuda okha m’maiko onse koma linaphatikizapo Akunja. (Mateyu 28:19, 20, NW; Machitidwe 11:18) Akumalaka malingaliro alionse otsutsa Akunja amene anali nawo, iwo analinganiza mkupiti wa kulalikira kupanga ophunzira mwa amitundu. Zaka zosakwanira 30 pambuyo pake, kunali kotheka kunena kuti mbiri yabwino idalalikidwa kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akolose 1:23.
Amene anali kupititsa patsogolo ntchito yolalikira imeneyi anali mtumwi Paulo, iye mwiniyo Mkristu Wachiyuda. Asanakhale wotsatira wa Kristu, anali chiŵalo chokangalika cha gulu lachipembedzo la Afarisi. Iwo sanangonyoza Akunja okha koma ngakhale anthu wamba a mtundu wawo. (Luka 18:11, 12) Koma Paulo sanalole malingaliro amenewo kumlepheretsa kusonyeza chikondi cha pa mnansi kwa ena. Mmalomwake, anakhala “mtumwi wa anthu amitundu [Akunja],” akumapereka moyo wake pantchito ya kupanga ophunzira m’maiko onse a m’dera la Mediterranean.—Aroma 11:13.
Mkati mwa kuchita utumiki wake, Paulo anaponyedwa miyala, kumenyedwa, ndi kuikidwa m’ndende. (Machitidwe 14:19; 16:22, 23) Kodi zochitika zankhanza zotero zinamchititsa kuipidwa ndi kunena kuti anali kutaya nthaŵi yake pakati pa amitundu ndi mafuko ena? Kutalitali. Iye anadziŵa kuti panali anthu owona mtima omwazikana m’mafuko onse ambiri a m’nthaŵi yake.
Pamene Paulo anapeza Akunja amene anali ofunitsitsa kuphunzitsidwa njira za Mulungu, anawakonda. Mwachitsanzo, iye analembera Atesalonika kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu siuthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Mawu owona mtima ameneŵa amasonyeza kuti Paulo anakondadi Atesalonika Akunja ndipo sanalole kalikonse kuwononga chimwemwe cha unansi wabwino ndi iwo.
Chikondi cha pa Mnansi Chikusonyezedwa
Lerolino, mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, awo amene amadzigwirizanitsa ndi mpingo Wachikristu amakulitsa chikondi cha pa mnansi kwa anthu a mafuko onse. Mwakukulitsa lingaliro laumulungu ponena za ena ndi mwakulalikira mbiri yabwino kwa iwo, Akristu owona afutukula chidziŵitso chawo cha anthu amene sakanaŵadziŵa. Ndiponso ali ndi chikondi cha ubale pa iwo. (Yohane 13:34, 35) Zimenezi zingakuchitikireni nanunso.
Chikondi chotero chilipo pakati pa Mboni za Yehova, ngakhale kuti zimapezeka m’maiko 229 ndipo zapangidwa ndi “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Monga gulu la abale lapadziko lonse, ali ogwirizana pa kulambira Yehova, kukana kwawo kutenga mbali m’kulimbana ndi maudani a ufuko, ndi kukana kwawo kukondera kumene kumabera anthu maunansi abwino ndi anthu anzawo.
Yanjanani ndi Mboni, ndipo mudzaona mmene anthu a mafuko onse akuchitira chifuno cha Mulungu. Mudzaona chikondi cha pa mnansi chikusonyezedwa pamene zilengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Inde, ndipo m’mipingo yawo, mudzakumana ndi anthu okoma mtima ndi owona mtima amene amasonyeza ndi miyoyo yawo kuti aphunziradi kukonda mnansi wawo.
[Chithunzi patsamba 6]
M’mipingo ya Mboni za Yehova, mudzapeza anthu achimwemwe a mafuko onse
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Kufika kwa Msamariya Wachifundo pa Nyumba ya Alendo/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.