Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Msamariya Waunansi
YESU mwinamwake ali pafupi ndi Betaniya, mudzi wachifupifupi makilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu. Mwamuna yemwe ali katswiri mu Chilamulo cha Mose akumufikira iye ndi funso, akumafunsa kuti: “Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?”
Yesu akuzindikira kuti munthuyo, loya, sakufunsa kokha kaamba ka chidziŵitso koma chifukwa akukhumba kumuyesa iye. Cholinga cha loyayo mwinamwake chingakhale kumpangitsa Yesu kuyankha m’njira imene idzalakwira malingaliro a Ayuda. Chotero Yesu akumpangitsa loyayo kuchimwa iyemwini, akumafunsa: “M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uŵerenga bwanji?”
M’kuyankha, loyayo, akumasonyeza chidziŵitso chachilendo, akugwira mawu kuchokera ku malamulo a Mulungu pa Deuteronomo 6:5 ndi Levitiko 19:18, akumanena kuti: “‘Udzikonda [Yehova] Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi mphamvu yako yonse ndi nzeru zako zonse,’ ndi, ‘mnansi wako monga iwe mwini.’”
“Wayankha bwino,” Yesu akuyankha. “Chita ichi ndipo udzakhala ndi moyo.”
Loyayo, ngakhale kuli tero, sanakhutiritsidwe. Yankho la Yesu siliri lachindunji mokwanira kaamba ka iye. Iye akufuna chitsimikiziro kuchokera kwa Yesu kuti kawonedwe kake kali kolondola ndipo chotero iye ali wolungama m’kuchita kwake ndi ena. Chotero, iye akufunsa: “Ndipo mnansi wanga ndani?”
Ayuda amakhulupirira kuti liwu lakuti “mnansi” limagwira ntchito kokha kwa Ayuda anzawo, monga mmene mawu ozungulira lemba la Levitiko 19:18 akuwonekera kusonyeza. M’chenicheni, pambuyo pake ngakhale mtumwi Petro ananena kuti: “Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu M’yuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina.” Chotero loyayo, ndipo mwinamwake ophunzira a Yesu nawonso, akukhulupirira kuti ali olungama ngati achitira Ayuda anzawo chifundo, popeza, m’kawonedwe kawo, osakhala Ayuda sali kwenikweni anansi awo.
Popanda kulakwira amvetseri ake, ndimotani mmene Yesu angawongolere kawonedwe kawo? Iye akukamba nkhani, mwinamwake yozikidwa pa chochitika chenicheni. “Munthu wina [M’yuda],” Yesu akulongosola, “anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko ndipo anagwa m’manja a achifwamba, amene anamvula zovala namkwapula, nachoka, atamsiya wofuna kufa.”
“Ndipo, kudangotero kuti,” Yesu akupitiriza, “wansembe wina anatsika njirayo, ndipo, pa kumuwona iye, anapita mbali ina. Momwemonso M’levi, pofika pamenepo ndi kumuwona, anapita mbali ina. Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pa iye ndipo, pakumuwona, anagwidwa chifundo.”
Ansembe ambiri ndi owathandiza awo Achilevi pa kachisi amakhala mu Yeriko, mtunda wa makilomita 23 pa msewu wowopsya womwe umatsetsereka mamita 900 kuchokera kumene iwo anatumikira pa kachisi mu Yerusalemu. Ansembe ndi Alevi akanayembekezeredwa kuthandiza M’yuda mnzawo m’tsoka. Koma iwo sakutero. M’malomwake, Msamariya akutero. Ayuda amadana ndi Asamariya mokulira kotero kuti posachedwapa anatukwana Yesu m’mawu amphamvu mwakumutcha iye “Msamariya.”
Nchiyani chimene Msamariyayo akuchita kuthandiza M’yudayo? “Nadza kwa iye,” Yesu akunena, “namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo. Ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha nadza naye ku nyumba ya alendo namsungira. Ndipo mmawa mwake anatulutsa marupiya atheka aŵiri [chifupifupi malipiro a masiku aŵiri], napatsa mwininyumba ya alendo, nati, ‘Msungeni iye, ndipo chirichonse umpatsa koposa, ine pobwera ndidzakubwezera iwe.’”
Pambuyo pokamba nkhaniyo, Yesu akufunsa loyayo: “Ndi uti wa awa atatu uyesa iwe anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?”
Akumadzimva wosakhazikika ponena za kupereka ulemu kwa Msamariya, loyayo akuyankha chabe kuti: “Iye wakumchitira chifundo.”
“Pita nuchite iwe momwemo,” Yesu akumaliza tero.
Ngati Yesu akanawuza loyayo mwachindunji kuti omwe sanali Ayuda analinso anansi ake, munthuyo sakanakana kokha kuvomereza ichi koma ambiri m’khamu mwinamwake akanatenga mbali yake m’kukambitsirana ndi Yesu. Nkhani yowona m’moyo weniweni imeneyi, ngakhale kuli tero, imachipangitsa icho kukhala chodziŵikiratu m’njira yosatsutsika kuti anansi athu amaphatikiza anthu pambali pa awo a fuko lathu ndi mtundu. Ndi njira yozizwitsa chotani nanga ya kuphunzitsira imene Yesu ali nayo! Luka 10:25-37; Machitidwe 10:28; Yohane 4:9; 8:48.
◆ Kodi ndi mafunso otani amene loya anafunsa Yesu, ndipo nchiyani chimene mwachiwonekere chiri cholinga chake m’kufunsa?
◆ Ndi ndani amene Ayuda anakhulupirira kuti anali anansi awo, ndipo nchifukwa chotani chimene chiripo cha kukhulupirira kuti ngakhale ophunzira anagawana kawonedwe kameneka?
◆ Ndimotani mmene Yesu anafikiritsira kawonedwe kolondola kotero kuti loyayu sakanakana iko?