-
Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi WabwinoNsanja ya Olonda—1998 | July 1
-
-
Anachita Chifuniro cha Yehova
Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi Wabwino
M’TSIKU la Yesu, panali udani waukulu pakati pa Ayuda ndi Akunja. M’kupita kwa nthaŵi, Mishnah yachiyuda inaphatikizapo ngakhale lamulo lomwe linali kuletsa akazi achiisrayeli kuti asamathandize akazi osakhala Ayuda panthaŵi yobala mwana, popeza kuti kuteroko kukanakhala kuthandizira kudzetsa munthu wina Wakunja m’dziko.—Abodah Zarah 2:1.
Asamariya ndi Ayuda anali paubale weniweni pa zonse ziŵiri chipembedzo ndi mtundu kusiyana ndi Akunja. Komatu iwo anali kuonedwanso monga odetsedwa. “Ayuda sayenderana nawo Asamariya,” analemba motero mtumwi Yohane. (Yohane 4:9) Ndithudi, Talmud inali kuphunzitsa kuti “mkate wopatsidwa ndi Msamariya ngwodetsedwa kwambiri kuposa nyama ya nkhumba.” Ayuda ena anali kugwiritsira ntchito dzina lakuti “Msamariya” monga mawu onyoza ndi kutonza.—Yohane 8:48.
-
-
Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi WabwinoNsanja ya Olonda—1998 | July 1
-
-
Yesu anapitiriza kunena kuti: “Msamariya wina ali paulendo wake anadza pali iye.” Mosakayika konse, kutchulidwa kwa Msamariya kunapangitsa kuti wachilamuloyo akhale tcheru kwambiri. Kodi Yesu adzavomereza kuti mtundu umenewu uyenera kuonedwabe monga wodetsedwa? Mosiyana ndi zimenezo, ataona wapaulendo wovulazidwayo, Msamariyayo “anagwidwa chifundo.” Yesu anati: “Nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye panyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.b Ndipo mmaŵa mwake anatulutsa malupiya atheka aŵiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.”—Luka 10:33-35.
-