Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Uphungu kwa Marita, ndi Malangizo pa Pemphero
MKATI mwa ntchito ya utumiki wa Yesu m’Yudeya, iye akuloŵa m’mudzi wa Betani. Kuno ndi kumene Marita, Mariya, ndi mbale wawo Lazaro amakhala. Mwinamwake Yesu anakumana ndi atatu amenewa kumayambiriro mu utumiki wake ndipo chotero ali kale mabwenzi achifupi ndi iwo. M’chochitika chirichonse, Yesu tsopano akupita kunyumba ya Marita ndipo akulandiridwa ndi iye.
Marita ali wofunitsitsa kupereka kwa Yesu zinthu zabwino koposa zimene ali nazo. Ndithudi, uli ulemu wabwino kukhala ndi Mesiya wolonjezedwa atachezera kunyumba ya wina! Chotero Marita akukhala wodzilowetsamo m’kukonza chakudya chokonzedwa mopambanitsa ndi kuwona ku tsatanetsatane wina wokonzedwa kumpanga Yesu kukhala wosangalala ndipo wopumula moposerapo.
Kumbali ina, mbale wa Marita Mariya akhala pa mapazi a Yesu ndi kumvetsera kwa iye. Patapita kanthaŵi, Marita akufika ndi kunena kwa Yesu: “Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze, tsono, kuti andithandize.”
Koma Yesu akukana kunena chirichonse kwa Mariya. M’malomwake, iye akupatsa uphungu Marita kaamba ka kukhala wodera nkhaŵa mopambanitsa ndi zinthu za kuthupi. “Marita, Marita,” iye akudzudzula mwachifundo, “uda nkhaŵa nuvutika ndi zinthu zambiri. [Zinthu zochepa, ngakhale ndi tero zikufunika, kapena kokha chimodzi, (NW)].” Yesu akunena kuti sichiri choyenera kuthera nthaŵi yochuluka kukonzekera zakudya zochuluka kaamba ka chakudya chimodzi. Kokha zinthu zochepa kapena ngakhale kokha mbale imodzi ya chakudya iri yokwanira.
Malingaliro a Marita ali abwino; iye akufuna kukhala wolandira alendo wochereza. Komabe, ndi chisamaliro chake chodera nkhaŵa ku makonzedwe akuthupi, iye akuphonya mwaŵi wa kulandira malangizo aumwini kuchokera kwa Mwana weniweni wa Mulungu! Chotero Yesu akumaliza kuti: “Pakuti Mariya, anasankha dera lokoma, limene silidzachotsedwa kwa iye.”
Pambuyo pake, pa chochitika china, wophunzira akufunsa Yesu: “Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.” Mwinamwake wophunzira ameneyu sanalipo chifupiifupi chaka chimodzi ndi theka kumayambiriro pamene Yesu anapereka pemphero la chitsanzo mu Ulaliki wake wa pa Phiri. Chotero Yesu akubwereza malangizo ake kenaka akupitiriza kupereka fanizo kuti agogomezere kufunika kwa kukhala owumirira m’pemphero.
“Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake,” Yesu akuyamba, “nadzapita kwa iye pakati pa usiku nadzati kwa iye, “Bwenzi, ndibwereke mikate itatu, popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndiribe chompatsa’? Ndipo iyeyu wa mkatimo poyankha akati, “Usandivuta. Pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa.’ Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma lake adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azisowa.”
Ndi kuyerekeza kumeneku Yesu sakutanthauza kunena kuti Yehova Mulungu sali wofunisitsa kuyankha ku mapembedzero, monga mmene linaliri bwenzi m’nkhani yake. Ayi, koma iye akuchitira fanizo kuti ngati bwenzi losafunitsitsa lidzayankha ku zopempha zowumirira, ndi mokulira chotani nanga Atate wathu wakumwamba wachikondi adzachitira! Chotero Yesu akupitiriza: “Ndipo ndinena ndi inu, [Pitirizani kupempha, ndipo adzakupatsani; pitirizani kufunafuna, ndip mudzapeza; pitirizani kugogoda, ndipo adzakutsegulirani, (NW)]. Pakuti yense wakupempha alandira, ndi wofunayo apeza, ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.”
Yesu kenaka akulozera kwa atate opanda ungwiro, a umunthu ochimwa, akumanena kuti: “Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha nsomba, adzamninkha njoka m’malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira, kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa kumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akupempha iye!” Ndithudi, ndi chilimbikitso chosonkhezera chotani nanga chimene Yesu akupereka cha kukhala owumirira m’pemphero. Luka 10:38-11:13.
◆ Nchifukwa ninji Marita akupita ku makonzedwe opambanitsa kaamba ka Yesu?
◆ Nchiyani chimene Mariya akuchita, ndipo nchifukwa ninji Yesu akumuyamikira iye m’malo mwa Marita?
◆ Nchiyani chimene chinamsonkhezera Yesu kubwereza malangizo ake pa pemphero?
◆ Ndimotani mmene Yesu anachitira chitsanzo chifuno cha kukhala owumirira m’pemphero?