MUTU 18
‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’
1, 2. Fotokozani mmene ulendo wa Mariya unalili komanso chomwe chinapangitsa kuti ukhale wovuta kwa Mariyayo.
MARIYA anali atayenda kwa maola ambiri pa ulendo wopita ku Betelehemu. Kenako anayamba kutembenukira uku ndi uku ali pamsana pa bulu yemwe anakwera pa ulendowu. Mwamuna wake Yosefe ankayenda patsogolo n’cholinga choti azitsogolera buluyo. Pa nthawiyi n’kuti Mariya ali woyembekezera ndipo ankamva mwana akusunthasuntha m’mimba mwake.
2 Baibulo limanena kuti pa nthawiyi Mariya n’kuti ali “wotopa ndi pakati.” (Luka 2:5) Pamene ankadutsa m’minda yosiyanasiyana, n’kutheka kuti panali alimi ena amene anali m’minda yawo ndipo ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani mayi wotopa chonchi ali pa ulendo. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mariya ayende ulendo wautali chonchi kuchoka kwawo ku Nazareti?
3. Kodi Mariya anapatsidwa ntchito yotani, nanga m’nkhaniyi tiphunzira zotani?
3 Miyezi ingapo m’mbuyomo, mayi wachiyudayu anapatsidwa ntchito yapadera kwambiri. Ntchito yake inali yoti abereke mwana yemwe adzakhale Mesiya, Mwana wa Mulungu. (Luka 1:35) Koma mwanayo atatsala pang’ono kubadwa, panachitika zinthu zina zimene zinapangitsa kuti ayende ulendowu. Mariya anakumana ndi zinthu zambiri zoyesa chikhulupiriro chake. Tiyeni tione zimene zinam’thandiza kuti akhalebe wokhulupirika.
Ulendo Wopita ku Betelehemu
4, 5. (a) N’chiyani chinachititsa kuti Yosefe ndi Mariya apite ku Betelehemu? (b) Kodi lamulo limene Kaisara anapereka linachititsa kuti ulosi uti ukwaniritsidwe?
4 Pa nthawiyi, panali anthu ambiri amene ankapita kumizinda ya kwawo. Kaisara Augusto anali atapereka lamulo loti m’dzikomo muchitike kalembera, choncho aliyense anayenera kupita kumzinda wa kwawo kukalembetsa. Kodi Yosefe anatani atamva lamulo limeneli? Nkhaniyi imati: “Yosefe nayenso anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti, n’kupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi m’fuko la Davide.”—Luka 2:1-4.
5 N’zosadabwitsa kuti Kaisara anapereka lamuloli pa nthawi imeneyi, chifukwa ulosi wina umene unalembedwa zaka pafupifupi 700 m’mbuyomo, unalosera kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Panali mzinda wina wotchedwa Betelehemu womwe unali pamtunda wa makilomita 11 kuchokera ku Nazareti. Koma ulosiwu unanena mwachindunji kuti Mesiya adzabadwira ku “Betelehemu Efurata.” (Werengani Mika 5:2.) Kuchokera ku Nazareti kudzera ku Samariya, umenewu unali ulendo wa makilomita 130 ndipo njira yake inali yodutsa m’mapiri. Kumeneku n’kumene Yosefe anayenera kupita, chifukwa n’kumene kunali kumudzi kwa Mfumu Davide. Yosefe ndi mkazi wake Mariya anali mbumba za Davide.
6, 7. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinapangitsa kuti ulendo wopita ku Betelehemu ukhale wovuta kwa Mariya? (b) Kodi Mariya ankasankha bwanji zochita atakwatiwa ndi Yosefe? (Onaninso mawu a m’munsi.)
6 Popeza Mariya anali ndi pakati, mwina zinali zovuta kuti agwirizane ndi maganizo a Yosefe oti apite ku Betelehemu pomvera lamuloli. Tikutero chifukwa iyi inali nthawi yoti nyengo yachilimwe yatsala pang’ono kutha ndipo mvula yamawawa ikanatha kugwa nthawi ina iliyonse. Komanso mzinda wa Betelehemu unali m’dera lokwera kwambiri moti zinali zovuta kuti munthu amene wayenda kale ulendo wa masiku angapo alimbanenso ndi chitunda chimenechi. Ndiye poti Mariya anali wotopa, mwina akanatenga masiku ochulukirapo kuposa pamenepa chifukwa akanamafunikira kupuma pafupipafupi. Komanso pa nthawi ngati imeneyi mayi aliyense woyembekezera amafuna kukhala kunyumba, pafupi ndi achibale komanso anzake oti amuthandize nthawi yochira ikafika. Kunena zoona, Mariya anafunika kulimba mtima kuti ayende ulendo umenewu.
7 Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, Mariya anapitabe ndi mwamuna wake chifukwa Baibulo limanena kuti Yosefe anapita “kukalembetsa limodzi ndi Mariya.” Limanenanso kuti Mariya ‘anamanga banja ndi Yosefe malinga ndi pangano.’ (Luka 2:4, 5) Posankha zochita, Mariya ankakumbukira kuti ndi munthu wapabanja. Iye ankadziwa kuti Yosefe ndiye mutu wa banja lake ndipo ankakwaniritsa udindo wake wochirikiza zimene mwamuna wakeyo wasankha.a Motero iye anagonjera ndipo sanalole kuti nkhani imeneyi iyese chikhulupiriro chake.
8. (a) Fotokozani chinthu chinanso chimene chinachititsa Mariya kulola kupita ku Betelehemu ndi Yosefe. (b) N’chifukwa chiyani tingati Mariya ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu onse okhulupirika?
8 Ngakhale kuti Baibulo silinena, n’kutheka kuti Mariya anamvera mwamuna wake chifukwa choti ankadziwa za ulosi wonena kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Tikutero chifukwa choti zikuoneka kuti atsogoleri achipembedzo ngakhalenso anthu wamba ambiri ankadziwa ulosi umenewu. (Mat. 2:1-7; Yoh. 7:40-42) Ndipotu Mariya anali mtsikana wodziwa Malemba. (Luka 1:46-55) Kaya Mariya anachita zimenezi pomvera mwamuna wake, pomvera lamulo la boma, chifukwa chodziwa ulosi wa Yehova, kapena pa zifukwa zonsezi, mfundo ndi yakuti iye anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Yehova amasangalala kwambiri ndi amuna komanso akazi amene ali ndi mtima wodzichepetsa ndiponso womvera. Masiku ano, pomwe anthu ambiri saona kuti kumvera n’kofunika, Mariya ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu onse okhulupirika.
Kubadwa kwa Khristu
9, 10. (a) Kodi Mariya ndi Yosefe ayenera kuti ankaganizira chiyani pamene ankayandikira mzinda wa Betelehemu? (b) N’chifukwa chiyani Yosefe ndi Mariya anagona m’khola?
9 Mtima wa Mariya uyenera kuti unakhala m’malo atayamba kuona mzinda wa Betelehemu. Pa nthawiyi n’kuti iye ndi mwamuna wake akukwera zitunda kudutsa minda ya maolivi. Maolivi anali m’gulu la mbewu zimene zinkakololedwa komalizira. N’kutheka kuti atangoona mzindawo, anayamba kuganizira za mbiri yake. Unali mzinda waung’ono kwambiri moti sunkaikidwa m’gulu la mizinda ya ku Yuda, monga mmene mneneri Mika ananenera. Komabe kumeneku n’kumene Boazi, Naomi, ndi Davide anabadwira zaka zoposa 1,000 m’mbuyomo.
10 Mariya ndi Yosefe atafika, anapeza kuti mzindawu unali utadzaziratu ndi anthu ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa anthuwa malo onse ogona anali atatha.b Choncho chifukwa chosowa pogwira, anaganiza zongogona m’khola. Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji kuona mkazi wake akuyamba kubuula ndi ululu wobereka kwa nthawi yoyamba? Ndipotu kumbukirani kuti zonsezi zinkachitikira m’khola.
11. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti azimayi onse angamvetse mavuto amene Mariya anakumana nawo? (b) Kodi Yesu ndi “woyamba kubadwa” m’njira ziti?
11 Mayi aliyense angathe kumvetsa mavuto amene Mariya anakumana nawo. Pa nthawiyi n’kuti patapita zaka 4,000 kuchokera pamene Yehova ananeneratu kuti akazi onse azidzamva ululu pobereka, chifukwa cha uchimo umene anthu anatengera kwa Adamu ndi Hava. (Gen. 3:16) Choncho Mariya nayenso anamva ululu woterewu pobereka. Luka sanafotokoze mavuto onse amene Mariya anakumana nawo pobereka, m’malomwake anangoti: “Anabereka mwana wake woyamba wamwamuna.” (Luka 2:7) Uyu anali “mwana woyamba” wa Mariya, mwa ana osachepera 7 amene iye anabereka. (Maliko 6:3) Komabe mwana ameneyu anali wosiyana kwambiri ndi anzake onsewo. Sikuti iye anangokhala mwana woyamba wa Mariya, koma analinso Mwana wa Yehova “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Akol. 1:15.
12. Kodi Mariya anagoneka kuti mwana wake, nanga zimene zinachitikadi zimasiyana bwanji ndi zithunzi ndiponso masewero ambiri a kubadwa kwa Yesu?
12 Apa Luka anatchulapo mfundo imene imanenedwa ndi anthu ambiri, yakuti: “Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto.” (Luka 2:7) Zithunzi ndiponso masewero ambiri a kubadwa kwa Yesu, amaonetsa zimenezi m’njira yokokomeza kwambiri. Koma izi si zimene zinachitikadi. Musaiwale kuti banjali linagona m’khola ndipo muyenera kuti munali monunkha komanso mwauve, monga mmene makola ambiri amakhalira. Palibe makolo amene angasankhe kuti mwana wawo akabadwire m’khola ngati patakhala malo ena abwinopo. Makolo ambiri amafuna ana awo akhale ndi zinthu zabwino kwambiri komanso azikhala pamalo abwino. Ndiye kodi mukuganiza kuti Mariya ndi Yosefe akanakhala ndi mwayi wosankha, sakanafuna kuti mwana wawo, yemwe analinso Mwana wa Mulungu, abadwire malo abwino kwambiri?
13. (a) Kodi Mariya ndi Yosefe anachita chiyani poyesetsa kusamalira mwana wawo? (b) Mofanana ndi Yosefe komanso Mariya, kodi makolo anzeru amaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?
13 Ngakhale kuti zinthu zinali chonchi, iwo sanakhumudwe koma anayesetsa kuchita zimene akanatha posamalira mwanayo. Mwachitsanzo, Mariya anakulunga bwinobwino mwanayo ndi nsalu n’kumugoneka modyera ziweto. Sanaganizire kwambiri za mavuto ake mpaka kulephera kuchita zimene akanatha posamalira mwana wakeyo. Iye ndi mwamuna wake ankadziwanso kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kuyesetsa kusamalira mwana wawoyo mwauzimu. (Werengani Deuteronomo 6:6-8.) Masiku anonso, makolo anzeru amaona kuti kusamalira ana awo mwauzimu m’dziko loipali n’kofunika kwambiri.
Yosefe ndi Mariya Analimbikitsidwa ndi Abusa
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani abusa ankafunitsitsa kuona Yesu? (b) Kodi abusa anatani ataona Yesu m’khola?
14 Kenako mwadzidzidzi panatulukira abusa omwe anabwera m’kholamo kuti adzaone banjalo, koma makamaka mwanayo. Abusa amenewa ankachita kuonekeratu kuti anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Iwo anali atathamanga kuchokera kumapiri kumene ankadyetsa ziweto zawo.c Makolo a mwanayo anadabwa kwambiri ndi kufika kwa abusawa koma abusawo anafotokoza zinthu zodabwitsa zimene anaona. Ananena kuti ali kuphiriko, mwadzidzidzi kunabwera mngelo pakati pa usiku ndipo ulemerero wa Yehova unawawalira ponsepo. Kenako mngeloyo anawauza kuti Khristu, kapena kuti Mesiya, wabadwa ku Betelehemu. Anawauzanso kuti mwanayo akam’peza modyera ziweto atakutidwa munsalu. Kenako panachitika chinthu chinanso chodabwitsa kwambiri. Iwo anaona chigulu cha angelo chikuimba za ulemerero wa Yehova.—Luka 2:8-14.
15 N’chifukwa chake abusawa, omwe anali anthu wamba, anafika ku Betelehemu akuthamanga. Ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona khandalo litagona modyera ziweto, ngati mmene mngelo uja anawauzira. Ataona zimenezi, anayamba kuuza anthu ena nkhani yabwinoyi. Iwo ‘anafotokoza zimene anauzidwa ndipo onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anali kuwauza.’ (Luka 2:17, 18) N’zoonekeratu kuti atsogoleri achipembedzo sankawawerengera abusa ngati anthu ofunika. Koma zimene zinachitikazi, zinasonyeza kuti Yehova ankawawerengera kwambiri anthuwa chifukwa anali odzichepetsa komanso okhulupirika. Koma kodi Mariya analimbikitsidwa bwanji ndi kufika kwa alendowa?
Yehova ankawawerengera kwambiri abusa chifukwa anali odzichepetsa komanso okhulupirika
16. Kodi Mariya anasonyeza bwanji kuti anali mtsikana woganiza kwambiri, ndipo zimenezi zinam’thandiza bwanji?
16 Pa nthawiyi Mariya ayenera kuti anali wofooka chifukwa anali atangobereka kumene, komabe anamvetsera mwachidwi mawu onse amene abusawo ankanena. Komanso “Mariya anasunga mawu onsewa ndi kuganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.” (Luka 2:19) Mariya anali munthu woganiza kwambiri. Iye anadziwa kuti uthenga wa mngeloyo unali wofunika kwambiri. Mulungu wake, Yehova, ankafuna kuti azindikire kuti mwana amene anaberekayo sanali munthu wamba. Choncho, sikuti Mariya anangomvetsera zimene abusawo ananena. Iye anasunga mumtima mwake mawu onse amene anauzidwawo kuti aziwaganizirabe mpaka m’tsogolo. Mfundo imeneyi ikusonyeza zimene zinam’thandiza Mariya kukhala ndi chikhulupiriro cholimba pa moyo wake wonse.—Werengani Aheberi 11:1.
17. Pa nkhani ya choonadi cha m’Baibulo, kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Mariya?
17 Kodi inuyo mukufunitsitsa kutsatira chitsanzo cha Mariya? Yehova watipatsa Baibulo momwe muli Mawu ake. Koma tingapindule ndi Mawu akewa ngati tikuchita nawo chidwi. Tingasonyeze chidwi chimenechi pophunzira Baibulo nthawi zonse. Tisamaliwerenge ngati buku wamba, koma tizidziwa kuti Baibulo ndi Mawu ouziridwa ndi Mulungu. (2 Tim. 3:16) Kenako, mofanana ndi Mariya, tiyenera kusunga mumtima mwathu zimene tikuwerengazo, n’kumaganizira tanthauzo lake. Tikamasinkhasinkha zinthu zimene timawerenga m’Baibulo, n’kumaona njira zimene tingagwiritsire ntchito malangizo a Yehova pa moyo wathu, chikhulupiriro chathu chidzalimba.
Mawu Enanso Amene Mariya Anasunga
18. (a) Yesu atakwanitsa masiku 8, kodi Mariya ndi Yosefe anatsatira bwanji Chilamulo cha Mose? (b) Kodi nsembe imene Yosefe ndi Mariya anapereka kukachisi ikusonyeza bwanji kuti anali osauka?
18 Mwana uja atakwanitsa masiku 8, anadulidwa potsatira Chilamulo cha Mose, ndipo Mariya ndi Yosefe anam’patsa dzina loti Yesu, potsatira zimene mngelo anawauza. (Luka 1:31) Atakwanitsa masiku 40, anapita naye kukachisi ku Yerusalemu, mtunda wa makilomita 10 kuchokera ku Betelehemu. Atafika kumeneko anapereka nsembe yoyeretsa. Nsembe imene iwo anapereka inali njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, mogwirizana ndi nsembe imene Chilamulo chinkalola kuti anthu osauka azipereka. Iwo sanachite manyazi poona kuti sanakwanitse kupereka nsembe zimene makolo ena ankapereka. Ndipotu atafika kukachisiku analimbikitsidwa kwambiri.—Luka 2:21-24.
19. (a) Kodi Simiyoni anauza Mariya mawu enanso otani amene iye anawasunga mumtima mwake? (b) Kodi Anna anatani ataona Yesu?
19 Ali kumeneko, munthu wina wokalamba dzina lake Simiyoni anawapeza n’kumuuza Mariya mawu enanso amene iye anawasunga mumtima mwake. Simiyoni analonjezedwa kuti sadzafa asanaone Mesiya, ndipo mzimu woyera unamuthandiza kuzindikira kuti Yesu ndi amene anali Mpulumutsi wolonjezedwayo. Iye anamuuzanso Mariya kuti tsiku lina adzamva chisoni kwambiri chifukwa cha zimene zidzachitike. Anauza Mariya kuti adzamva ululu ngati kuti lupanga lalitali lalasa moyo wake. (Luka 2:25-35) Ngakhale kuti mawu amenewa anali ochititsa mantha, n’kutheka kuti ndi amene anamuthandiza Mariya kupirira zimenezi zitachitika pambuyo pa zaka 30, pamene mwana wake anaphedwa. Simiyoni atachoka, panabweranso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna. Iye ataona Yesu, anayamba kunena za mwanayu kwa aliyense amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.—Werengani Luka 2:36-38.
20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yosefe ndi Mariya anachita bwino kupita ndi Yesu kukachisi ku Yerusalemu?
20 Mariya ndi Yosefe anachita bwino kwambiri kupita ndi mwana wawo kukachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Zimenezi zinathandiza mwanayo kuti atakula azikondanso kupita kukachisi wa Yehova. Monga taonera, ali kukachisiko anapereka kwa Mulungu nsembe komanso anauzidwa mawu olimbikitsa kwambiri. N’zosakayikitsa kuti Mariya anachoka kumeneko chikhulupiriro chake chitalimba ndiponso atamva mawu ambiri oti awaganizire ndiponso kuuza anthu ena.
21. Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba ngati cha Mariya?
21 Masiku anonso n’zosangalatsa kwambiri kuona makolo akutsatira chitsanzo chimenechi. Nthawi zonse makolo a Mboni za Yehova amatenga ana awo popita kumisonkhano yachikhristu. Makolowa amayesetsa kuchita zimene angathe ponena mawu olimbikitsa kwa okhulupirira anzawo. Ndipo akamachoka kumisonkhanoyo amakhala atalimbikitsidwa, ali osangalala ndiponso ali ndi zinthu zambiri zabwino zoti akauze ena. Timasangalala kwambiri kusonkhana ndi makolo oterewa. Tikamachita zimenezi, chikhulupiriro chathu chimalimba ngati mmene zinalili ndi Mariya.
a Taonani kusiyana kwa mawu a m’lembali ndi mawu ofotokoza ulendo wa Mariya wa m’mbuyomo. Ponena za ulendowu, Malemba amati: “Mariya ananyamuka . . . n’kupita” kwa Elizabeti. (Luka 1:39) Pa nthawiyi Mariya anangonyamuka, sanam’funse kaye Yosefe, chifukwa anali asanakwatirane. Komano atakwatirana, Yosefe ndi amene akutchulidwa ngati mwini wa ulendo uliwonse umene ayendera limodzi.
b Masiku amenewo mzinda uliwonse unkakhala ndi malo ogona anthu apaulendo.
c Mfundo yakuti pa nthawiyi abusawa anali kuphiri ndi ziweto zawo ikutsimikizira zimene Baibulo limasonyeza, zoti Khristu sanabadwe m’mwezi wa December chifukwa pa nthawiyi ziweto sankapita nazo kutali. Choncho Khristu ayenera kuti anabadwa chakumayambiriro kwa October.